Phunziro 7
Phunziro Limapindulitsa
1. Kodi phunziro limatikonzekeretsa chiyani?
1 Kodi mungakonde kuona chikhulupiriro chanu chikuwonjezeka, kuona chikondi chanu kwa Mulungu chikukhala champhamvu kwambiri, kukulitsa luntha lanu la kuzindikira ndi zipatso zoŵirikiza za khama lanu pautumiki? Kupita patsogolo kumene mungakhale nako m’mbali zonsezi kumadalira kwambiri mmene mumachitira phunziro laumwini ndi la banja. Phunziro loterolo lili mbali yofunika kopambana pamiyoyo yathu monga Akristu. Silimangotikonzekeretsa kutumikira Mulungu tsopano, komanso ndi mbali yokonzekera moyo m’dziko latsopano la Mulungu. Kodi inuyo panokha mumaphunzira mmene munayenera kuchitira?—Mat. 4:4.
2, 3. Kodi nthaŵi ya phunziro tingaipeze motani?
2 Kaŵirikaŵiri vuto limakhala kupeza nthaŵi yokwanira yochitira phunziro. Komabe n’kotheka kuligonjetsa vutolo. Ngati muona kuti pologalamu yanu ya phunziro ifunikira kuwongolera, pendani zochita zanu za mlungu ndi mlungu. Si kwenikweni kuti mungapeze nthaŵi yochuluka yopanda chochita nayo. Koma Baibulo limatifulumiza ‘kuwombola nthaŵi’ pantchito zina. (Aef. 5:15-17, NW) Ngati muli ndi TV, bwanji osalemba nthaŵi imene mumawononga poionerera pa mlungu wathunthu? Mungadabwe ndi kuchuluka kwa nthaŵi yogwiritsidwa ntchito m’njira imeneyo. Kodi mumawononga nthawi yochuluka motani pa “nkhani zosafunikira” kwenikweni patelefoni, kucheza ndi anansi kapena kuŵerenga nyuzipepala kapena magazini adziko? Kodi ina ya nthaŵi imeneyi mlungu ndi mlungu ingaperekedwe ku phunziro limene lingakhale lopindulitsa kosatha? Phunziro loterolo mungakhale nalo masana, madzulo kapena nthaŵi ina iliyonse imene ingakukhalireni bwino. Kaŵirikaŵiri munthu amapeza nthaŵi ya zinthu zofunika kwambiri kwa iye, ndipo mosapeneka konse, phunziro la Mawu a Mulungu lili pakati pa “zinthu zofunika kwambiri” kwa munthu amene amalemekeza unansi wake ndi Yehova.—Afil. 1:9-11, NW; Miy. 2:1-5.
3 Ngakhale kuti poyamba kungakhale kovuta kuti mukhazikike pansi ndi kusumika maganizo pa phunziro, m’kupita kwa nthaŵi kumafeŵerapo ndi kuyamba kukukondweretsani moŵirikiza. Koma mufunikira kuzindikira kufunika kwake, kupatula nthaŵi ya kuphunzira nthaŵi zonse komano kuikirapo khama.
4, 5. Kodi phunziro limaphatikizapo chiyani, ndipo chifukwa chiyani kuli koyenera kuyamba phunziro ndi pemphero?
4 Phunziro liyenera kuchitidwa ndi cholinga chokhoza kudzakumbukira nkhani ndi kuifotokoza momvekera bwino. Kuŵerenga wamba, ngakhale kuti kuli ndi malo ake pamoyo wathu, sindiko phunziro. Phunziro limafuna kufufuza, kusinkhasinkha ndi kugwiritsa ntchito zophunziridwazo. Musamaŵerenge zochuluka kwambiri moti n’kulephera kumvetsa. Mukatero phunziro lanu lidzakhala losagwira mtima ndi losapindulitsa. M’malo mwake, khalani ndi nthaŵi yofufuza ndi kusinkhasinkha. Komabe, konzekerani kuŵerenga zokwanira kotero kuti muone kuti mukuphunzirapodi kanthu kena.
5 Wophunzira wachikristu sadalira luso la iye mwini kuti apeze njira yodziŵira zinthu zakuya za Mawu a Mulungu a choonadi. Amazindikira kuti pamafunika chithandizo cha mzimu woyera wa Mulungu, komanso gulu la Mulungu la atumiki odzipereka, ndi Mawu enieniwo a Mulungu. Ndicho chifukwa chake n’kofunika kupempha dalitso la Mulungu panthaŵi za phunziro mwa pemphero.—Yak. 1:5; Luka 11:9-13.
6, 7. Kodi ndi malingaliro otani othandiza amene angayesedwe kuti tipindule kwambiri ndi kuŵerenga Baibulo kwa banja?
6 Phunziro la Baibulo. Pasukulu ya Utumiki Wateokalase pamakhala gawo la kuŵerenga Baibulo mlungu ndi mlungu. Mutha kuchita zimenezi monga banja, kumaŵerenga chaputala chimodzi kapena ziŵiri za Baibulo madzulo. Kuti mupindule nako kuŵerenga kumeneku, woŵerengayo kapena wina aliyense alongosole mfundo yaikulu ya ndimeyo. Ngati mukuŵerenga panokha nkhaniyo, khalani ndi nthaŵi ya kusinkhasinkha pa lingaliro lofotokozedwalo, mmene likugwirizanira ndi chaputala chonsecho ndi mmene likukhudzira moyo wanu.
7 Mutatha kuŵerenga Baibulo, ngati mfundo sizinamveke bwino, pezani nthaŵi yokafufuza. Mwinamwake ganizo kapena lingaliro la lemba linalake linali losamvekera bwino kwa inu. Kodi mungadziŵe bwanji zowonjezera pa lembalo? Choyamba mungaone gawo lotchedwa Scripture Index m’ma Watch Tower Publications Indexes kuti mupeze kumene lembalo lafotokozedwa. Ngati funso lanu lili pa liwu lina m’lembalo monga ngati “Sanctification (kuyeretsa)” kapena “Babylon the Great (Babulo Wamkulu),” mungapeze mawu ena olongosola mwa kuyang’ana pa gawo lotchedwa Subject Index m’ma Watch Tower Publications Indexes a palaibulale yanu. Mungatsatire dongosolo limodzimodzilo pofuna kudziŵa za munthu wina kapena malo otchulidwa m’Baibulo. Mungapezenso chidziŵitso chonena za anthu ndi malo m’buku la Insight on the Scriptures kapena mwa kungoona pa mpambo wa malemba ondandalikidwa mwa dongosolo la alifabeti kumapeto kwa Baibulo lanu lachingelezi ndiyeno kuŵerenga malemba osonyezedwawo.
8, 9. Kodi mayankho pa mafunso a Baibulo tingawapeze motani, ndipo tiyenera kufunafunanso chiyani kuwonjezera pa mayankhowo?
8 Kufufuza mayankho. Nthaŵi zina paulendo wobwereza kapena paphunziro la Baibulo funso lingabuke limene simuli wotsimikiza kuyankha kwake. Kufufuza pamafunso oterowo kungachitidwe panthaŵi ya phunziro laumwini lakunyumba. Mwa njira imeneyi mudzakhala wotsimikiza kuti ‘mukulunjika nawo bwino mawu a choonadi.’ (2 Tim. 2:15) Mwa kuchita khama pang’ono, yankho lokhutiritsa kaŵirikaŵiri limapezeka. Choyamba, ngati chimene mukufuna ndi malongosoledwe a lemba linalake, ŵerengani kaye nkhaniyo. Kodi nkhaniyo ikunena za chiyani ndipo mfundo yake ya lembalo n’njotani? Mutadziŵa zimenezo, mwakonzeka tsopano kuyang’ana pa gawo lotchedwa Scripture Index m’ma Watch Tower Publications Indexes kuti mupeze chithandizo chowonjezera. Kodi funsolo lili pa chiphunzitso kapena pa ulosi, kapena kodi likunena za kugwiritsa ntchito mapulinsipulo a Malemba pamoyo wa wophunzirayo? Zigawo zonse ziŵiri za Subject Index ndi Scripture Index za m’ma Watch Tower Publications Indexes zingakuthandizeni kupeza chidziŵitso chimene mukuchifunacho.
9 Pamene mwakhutira kuti mwapeza yankho, dzifunseni umboni umene muli nawo. Kodi mudzayankha mwakungotchula mfundo imene mwina womvetsera wanu angaone kuti munangokhulupirira popanda zifukwa zomvekera bwino, kapena kodi mukuona kufunika kwa kupereka zifukwa zofotokozedwa m’mabuku a Sosaite? Kodi mungapereke chitsanzo choonetsa kuti yankholo n’loona? Amene mwam’fikirayo angafune kuti mufotokoze zifukwa zanu kapena kuti mupereke umboni wa m’Malemba. Kodi mungalongosole mfundoyo mwa fanizo? Kodi muli ndi mafunso otsogolera amene mungawagwiritse ntchito kuthandiza wophunzirayo kufika pa ganizo loyenera? Mutaiphunzira nkhaniyo, mudzakhala wokhoza kupereka yankho logwira mtima.
10, 11. Perekani malingaliro a kakonzekeredwe ka phunziro la Nsanja ya Olonda ndi phunziro la buku la mpingo.
10 Kukonzekera phunziro la “Nsanja ya Olonda.” M’mayiko ena Nsanja ya Olonda simapezeka nthaŵi zonse chifukwa cha ziletso pa ntchito ya mboni za Yehova. M’malo oterowo abale amangobwerera m’makope akale kapena kudalira zimene akuzikumbukira m’maphunziro am’mbuyo. Kodi mungakumbukire mfundo zazikulu m’makope aposachedwapa a Nsanja ya Olonda amene mwawaphunzira? Tiyenera kuphunzira ndi cholinga chodzakumbukira mfundozo kuti tidzazigwiritse ntchito m’tsogolo, kaya pamiyoyo yathu kapena mu utumiki wakumunda.
11 Nkopindulitsa kuŵerenga magazini kuyambira kuchikutiro mpaka kuchikutiro mutangowalandira, kuti mupeze mfundo zazikulu za nkhaniyo. Ndiyeno, nthaŵi itayandikira yoti mukaphunzire nkhaniyo kumpingo, ndi bwino kubwereramonso m’nkhani panokha kapena kukambirana monga banja. Pochita zimenezo, choyamba onani mutu wa nkhaniyo, lemba lake lalikulu ndi timitu ta m’kati m’zilembo zakuda. Mukatero mumakhala ndi chithunzi chonse cha nkhaniyo ndipo mudzatha kuona kugwirizana kwa mfundo za m’ndime iliyonse. Tsopano ŵerengani phunziro lonselo ndime ndi ndime, mukumapeza mayankho a mafunso ndi kuchonga mfundo zazikulu zokha zodzakumbukira m’tsogolo. Pamene mutsiriza ndime iliyonse, ngati muona kuti simungayankhe funsolo m’mawu anu, ndi bwino kuŵerenganso ndimeyo kuti mukhoze kuyankha. Perekani chisamaliro pazifukwa za m’Malemba za mayankho operekedwa, mukumaŵerenga malemba osagwidwa mawu ndi kuchonga amene mudzafuna kuyankhapo pamsonkhano. Mutamaliza ndime zonse za kamutu kam’kati, imani pang’ono ndi kupenda mmene mfundozo zathandizira kufotokoza nkhani yonseyo. Chitaninso zimenezo kumapeto kwa nkhaniyo. Dzifunseni kumene mungagwiritse ntchito zimene mwaphunzira, mmene zikukhudzira moyo wanu kapena mmene mungazifotokozere kwa munthu wina. Mwakutero, simudzakhala mukuchonga chabe mayankho, komanso mudzapeza nzeru ndi luntha. (Miy. 4:7) Komanso chisangalalo chanu paphunziro la Nsanja ya Olonda pamodzi ndi mpingo chidzawonjezeka kwambiri. Tsatirani dongosolo lofananalo pokonzekera phunziro la buku la mpingo.
12-14. Kodi n’chifukwa chiyani phunziro la banja lili lofunika kwambiri, ndipo ndi nkhani zotani zimene zingaphunziridwe?
12 Phunziro la banja. Koposa zonse, tsimikizirani kuti makonzedwe anu a kuphunzira akuphatikizapo banja lanu kotero kuti aliyense apindule kwathunthu. Kodi chingakhale chikondi ngati mutu wa banja aphunzira mwakhama kwinaku mkazi wake ndi ana alikufa ndi njala yauzimu? Mutu wa banja ali ndi udindo wa ‘kusunga ake, makamaka apabanja lake,’ osati mwakuthupi chabe komanso mwauzimu. (1 Tim. 5:8, NW) Nzeru ya kuphunzitsa ana Baibulo akali aang’ono ikuoneka mu uphungu wa Miyambo 22:6 wakuti: “Phunzitsa mwana poyamba njira yake; ndipo angakhale atakalamba sadzachokamo.” Musaganize kuti mwana wanu n’ngwamng’ono kwambiri moti sangapindule kanthu. Ana amaphunzira kuyambira paukhanda. (2 Tim. 3:15) Amene amapita patsogolo mofulumira kwambiri m’banja, ali aja amene amakhala ndi chizoloŵezi cha kupatula nthaŵi yoŵerengera pamodzi monga banja ndi kuphunziranso pamodzi. Chofunika kwambiri ndicho kuchita mokhazikika.
13 Kodi mumakambirana lemba la tsiku ndi banja lanu, kuwalola kukambapo ndi kufunsa mafunso kuti mutsimikizire ngati iwo akumvetsa? Zimenezi zingapatse banja lanu chakudya chauzimu chopatsa thanzi. Mabanja ambiri amachita zimenezo pa nthaŵi ya chakudya. Komanso, banja lililonse lifunikira kupatula nthaŵi ya phunziro la banja lotalikirapo la mlungu ndi mlungu. Angakhale madzulo kapena nthaŵi ina iliyonse yoyenera. Pamafunika nthaŵi yokwanira kuti mumvetse nkhani zambiri za Baibulo, kuti mupende mbali zake zosiyanasiyana ndi kuzikhomereza pamtima. Phunziro la banja lokhazikika limalola nonsenu kupindula nalo phunziro loterolo. Kodi mumakhala nalo phunziro la banja lotero? Ngati silili chinthu cha nthaŵi zonse m’banja mwanu, bwanji osakambirana nkhaniyo ndi banja lonse leroli ndi kuchitapo kanthu kuti zimenezi zikhale mbali ya moyo wanu?—Aef. 6:4; Deut. 6:4-7.
14 Ngati ana ali aang’ono kwambiri, ndi bwino kuphatikizapo nkhani zophunzira limodzi zimene iwonso akhoza kuzimvetsa ndipo zowathandiza. Koma ngakhale nkhani yovuta kwambiri mungakambirane m’njira yoti n’kuloŵetsamo ana ndi mafunso okhweka apatalipatali pa mfundo imene angamvetse. Mabanja ambiri amakonzekera phunziro la Nsanja ya Olonda panthaŵi ya phunziro lawo la banja. Koma nkhani iliyonse yoyenera zosoŵa za banja ingaphunziridwe paphunziro la banja. Kuphunzira koteroko kumalimbitsa zomangira za banja ndi kukulitsa chiyamikiro chauzimu.
15-17. Kodi phunziro lokhazikika lili ndi mphotho zotani?
15 Mphotho za khama. Mphotho imodzi yamwamsanga ya phunziro lakhama ndiyo kukulitsa luso la kukumbukira zinthu kupyolera m’khama ndi kusonkhezereka. Mu utumiki wakumunda ndi pamisonkhano yampingo kumakhala kwapafupi kukumbukira ndi kulongosola mfundo zimene zaphunziridwa. Timakhoza kuyankha pamtima mafunso a okondwerera atsopano, ndi kusonyeza mofulumira malemba amene amachirikiza mayankho athu. Koma koposa zimenezo, phunziro limatipatsa chidziŵitso chokwanira cha Mawu a Mulungu chopindulitsa kwambiri. Limatipatsa chikhulupiriro cholimba, luntha la kuzindikira mapulinsipulo a Baibulo ndi chimwemwe choŵirikiza cha kutumikira Yehova.—Aheb. 5:14.
16 Anthu anzeru amaika patsogolo zinthu zokhudza moyo wawo wauzimu. Zinthu zazing’ono zingakankhidwire pambali akasoŵa nthaŵi, koma osati phunziro la Mawu a moyo. Amene amakhala ndi lingaliro limeneli ndi amene Yehova amalonjeza kuti ‘udzandipeza.’ (1 Mbiri 28:9) Zimenezi zidzakhala choncho ngati muphunzira, osati chabe kupeza chidziŵitso cha m’mutu, koma kuchiloŵetsa mumtima mwanu. Lolani kuti chikondi chanu ndi chiyamikiro chanu kwa Yehova ndi ntchito zake zodabwitsa chikule pamene mukuphunzira Mawu ake.
17 Cholinga chenicheni chimene atumiki a Mulungu amaphunzirira chikusonyezedwa bwino m’pemphero la mtumwi Paulo, lolembedwa pa Akolose 1:9, 10 kuti: “Kuti mukadzazidwe ndi chizindikiritso cha chifuniro chake mu nzeru zonse ndi chidziŵitso cha mzimu, kuti mukayende koyenera Ambuye kukam’kondweretsa monsemo, ndi kubala zipatso mu ntchito yonse yabwino, ndi kukula m’chizindikiritso cha Mulungu.”