Achinyamata—kulitsani Luso Lanu la Kuzindikira!
‘Chakudya chotafuna chili cha anthu akulu misinkhu, amene mwa kuchita nazo anazoloŵeretsa zizindikiritso zawo [“anakulitsa luso lawo la kuzindikira, mwa kuligwiritsa ntchito,” NW] posiyanitsa chabwino ndi choipa.’—AHEBRI 5:14.
1, 2. (a) Kodi mkhalidwe wathu lero uli motani pouyerekeza ndi wa Akristu akale a ku Efeso? (b) Kodi ndi mikhalidwe yotani imene ingakutetezeni ku ngozi, ndipo mungaikulitse motani?
“PENYANI bwino umo muyendera, si monga opanda nzeru, koma monga anzeru; akuchita machawi, popeza masiku ali oipa.” (Aefeso 5:15, 16) Chilembereni mtumwi Paulo mawuŵa zaka zikwi ziŵiri zapitazo, ‘anthu oipa ndi onyenga aipa chiipire.’ Tikukhala ‘m’nthaŵi zoŵaŵitsa,’ kapena nthaŵi “zodzala ndi zoopsa,” malinga n’kunena kwa Baibulo lina.—2 Timoteo 3:1-5, 13; Phillips.
2 Komabe, mutha kuthaŵa zoopsa zimene zingakubisalireni mwa kukulitsa ‘kuchenjera, . . . kudziŵa ndi kulingalira.’ (Miyambo 1:4) Miyambo 2:10-12 imati: ‘Pakuti nzeru ikaloŵa m’mtima mwako, moyo wako udzakondwera ndi kudziŵa, kulingalira kudzakudikira, kuzindikira kudzakutchinjiriza; kukupulumutsa ku njira yoipa, kwa anthu onena zokhota.’ Koma kodi mungaikulitse motani mikhalidwe imeneyo? Ahebri 5:14 amati: “Chakudya chotafuna chili cha anthu akulu misinkhu, amene mwa kuchita nazo anazoloŵeretsa zizindikiritso zawo [“anakulitsa luso lawo la kuzindikira, mwa kuligwiritsa ntchito”] kusiyanitsa chabwino ndi choipa.” Mofanana ndi luso lina lililonse, kuzoloŵera kugwiritsa ntchito luso la kuzindikira kumafuna kuphunzira. Liwu lachigiriki limene Paulo anagwiritsa ntchito kwenikweni limatanthauza ‘kuphunzitsidwa muja amachitira katswiri wa maseŵero apidigoli.’ Kodi kuphunzirako mumakuyamba motani?
Kuphunzira Luso la Kuzindikira
3. Kodi mungagwiritse ntchito motani luso lanu la kuzindikira pofuna kupanga chosankha?
3 Onani kuti luso lanu la kuzindikira—kukhoza kwanu kuzindikira chabwino ndi choipa—mumaliphunzira mwa “kuligwiritsa ntchito” luso limenelo. Pofuna kusankha chinthu, mukhoza kusankha mopusa ngati mungolota zinthu, kapena kuchita mwaphuma, kapenanso ngati mungotsatira zimene ambiri amachita. Kuti musankhe mwanzeru, muyenera kugwiritsa ntchito luso lanu la kuzindikira. Motani? Choyamba, mwa kupenda mkhalidwewo mosamalitsa ndi kumvetsa zonse zophatikizidwamo. Funsani mafunso ngati kuli kofunikira. Dziŵiranitu zimene mungafune kuchita. Miyambo 13:16 imati: “Yense wochenjera amachita mwanzeru; koma wopusa aonetsa utsiru.” Kenako, yesani kuona ndi malamulo ati kapena malangizo a Baibulo amene akukhudzidwa. (Miyambo 3:5) Komabe, kuti muchite zimenezi mufunikira kulidziŵa bwino Baibulo. N’chifukwa chake Paulo amatilimbikitsa kudya “chakudya chotafuna”—kuphunzira “kupingasa, ndi utali, ndi kukwera” ndi kuya kwa choonadi.—Aefeso 3:18.
4. N’chifukwa chiyani kudziŵa mapulinsipulo a Mulungu kuli kofunika kwambiri?
4 Kuchita zimenezo n’kofunika kwambiri, pakuti tili opanda ungwiro ndi okonda kuchimwa. (Genesis 8:21; Aroma 5:12) “Mtima ndiwo wonyenga koposa, ndi wosachiritsika,” amatero Yeremiya 17:9. Popanda malangizo a Mulungu kuti atitsogolere, tikhoza kudzinyenga tokha ndi kuona chinthu choipa kukhala chabwino—chabe chifukwa thupi lathu lachilakalaka chinthucho. (Yerekezani ndi Yesaya 5:20.) Wamasalmo analemba kuti: “Mnyamata adzayeretsa mayendedwe ake bwanji? Akawasamalira monga mwa mawu anu. Malangizo anu andizindikiritsa; chifukwa chake ndidana nawo mayendedwe onse achinyengo.”—Salmo 119:9, 104.
5. (a) N’chifukwa chiyani achinyamata ena amatsatira mayendedwe achinyengo? (b) Kodi mtsikana wina anatenga bwanji choonadi kukhala chakechake?
5 Achinyamata ena amene akulira m’mabanja achikristu atsatira mayendedwe achinyengo. Kodi chifukwa chake n’chiyani? Kodi chingakhale chifukwa chakuti oterowo ‘sanazindikire chimene chili chifuno cha Mulungu, chabwino ndi chokondweretsa, ndi changwiro’? (Aroma 12:2) Ena atha kumafika kumisonkhano limodzi ndi makolo awo ndi kuthanso kutchula ziphunzitso zina zoyambirira za m’Baibulo. Koma pamene afunsidwa kulongosola umboni wa chikhulupiriro chawo kapena kuti afotokoze zina mwa zinthu zozama za m’Mawu a Mulungu, chidziŵitso chawo chimapezeka kukhala chopereŵera momvetsa chisoni. Achinyamata oterowo akhoza kusokeretsedwa mosavuta. (Aefeso 4:14) Ngati zili choncho kwa inu, bwanji osakhala ndi mtima wofuna kusintha? Mlongo wina wachitsikana akukumbukira kuti: “Ndinayamba kufufuza. Ndinadzifunsa kuti, ‘Ndingadziŵe bwanji kuti ichi ndicho chipembedzo choona? Nanga ndingadziŵe motani kuti alikodi Mulungu wotchedwa Yehova?’”a Popenda Malemba mosamalitsa anakhutira kuti zimene anaphunzira kwa makolo ake zinalidi zoona!—Yerekezani ndi Machitidwe 17:11.
6. Kodi ndi motani mmene ‘mungatsimikizire chokondweretsa Ambuye,’ Yehova?
6 Pokhala ndi chidziŵitso cha mapulinsipulo a Yehova, kudzakhala kosavuta kwa inu “kuyesera [“kutsimikiza,” NW] chokondweretsa Ambuye n’chiyani.” (Aefeso 5:10) Koma bwanji ngati simuli wotsimikiza za chimene muyenera kuchita pankhani ina? Pemphani Yehova kuti akutsogolereni. (Salmo 119:144) Yesani kukambirana nkhaniyo ndi makolo anu kapena Mkristu wachikulire. (Miyambo 15:22; 27:17) Mutha kupezanso chithandizo chabwino mwa kufufuza m’Baibulo ndi m’zofalitsa za Watch Tower. (Miyambo 2:3-5) Pamene mugwiritsa ntchito kwambiri luso lanu la kuzindikira, m’pamenenso lidzakhala lakuthwa kwambiri.
Kuonetsa Kuzindikira Pankhani ya Zosangalatsa
7, 8. (a) Kodi mungagwiritse ntchito motani luso lanu la kuzindikira posankha kupita kapena kusapita ku macheza? (b) Kodi lingaliro la Baibulo n’lotani pankhani ya zosangalatsa?
7 Tsopano tiyeni tione mmene mungagwiritsire ntchito luso lanu la kuzindikira m’mikhalidwe ina. Mwachitsanzo, tinene kuti mwaitanidwa ku macheza ena ake. Mwina mwachita kulandira kalata yoitanira anthu kumachezawo. M’kalatamo atchula kuti kumeneko kudzakhala achinyamata a Mboni ambiri. Koma kudzakhala kulipira pofuna kuthandiza pa ndalama zimene zawonongedwa. Kodi mukayenera kupita?
8 Eya, gwiritsani ntchito luso lanu la kuzindikira. Choyamba, dziŵani zenizeni za machezawo. Kodi adzakhala aakulu motani? Kodi kudzakhala ndani kumeneko? Adzayamba nthaŵi yanji? Nanga adzatha nthaŵi yanji? Kodi akonza zochitika zotani kumeneko? Kodi adzayang’anira machezawo ndani? Kenako, fufuzani, yang’anani “Social Gatherings (Macheza),” ndi “Entertainment (Zosangalatsa)” mu Watch Tower Publications Index.b Kodi kafukufuku wanu angavumbule chiyani? Choyamba, angavumbule kuti Yehova sadana ndi kusonkhana kwa anthu kuti asangalale ndi macheza abwino. Ndi iko komwe, Mlaliki 8:15 amanena kuti limodzi ndi kugwira ntchito zolimba, “munthu alibe kanthu kabwino pansi pano, koma kudya ndi kumwa, ndi kusekera.” Eya, ngakhale Yesu Kristu weniweniyo anakhala nawo pa zakudya zapadera ndi paukwati umodzi. (Luka 5:27-29; Yohane 2:1-10) Ngati achitika moyenerera, macheza akhoza kukhala opindulitsa.
9, 10. (a) Kodi macheza ena angakhale ndi ngozi zotani? (b) Ndi mafunso otani amene muyenera kudzifunsa musanasankhe kupita kapena kusapita kumacheza?
9 Komabe, macheza osakonzedwa mosamala angapute mavuto. Pa 1 Akorinto 10:8, timaŵerenga za mmene mayanjano oipa anatsogolera ku dama ndi kuphedwa kwa “[Aisrayeli osakhulupirika] tsiku limodzi zikwi makumi aŵiri ndi zitatu.” Chenjezo lina lotsegula maganizo tikulipeza pa Aroma 13:13 pamene pamati: “Tiyendeyende koyenera, monga usana; sim’madyerero ndi kuledzera ayi, sim’chigololo ndi chonyansa ayi, simundewu ndi nkhwidzi ayi.” (Yerekezani ndi 1 Petro 4:3.) Zoona, sitingaike muyezo pano wa chiŵerengero cha anthu amene ayenera kufika pamacheza. Koma zochitika zasonyeza kuti ngati macheza akhala aakulu kwambiri, kuwayang’anira kwake kumakhalanso kovuta. Koma macheza a ukulu woyenera, komanso olinganizidwa bwino sakonda kusintha n’kukhala “mapwando osadziletsa.”—Agalatiya 5:21, Byington.
10 Mosakayikira, kafukufuku wanuyo adzabutsa mafunso enanso, monga akuti: Kodi kumachezako kudzakhalanso Akristu achikulire? Ndani kwenikweni, akulipirira machezawo? Kodi cholinga cha machezawo ndi kulimbikitsa mayanjano abwino kapena kuthandiza munthu wina kuti apeze phindu la ndalama? Kodi pali ziletso zilizonse kwa amene aitanidwa kumeneko? Ngati machezawo akachitika kumapeto kwa mlungu, kodi adzatha nthaŵi yabwino kotero kuti ofikapo akathe kupita mu utumiki wachikristu tsiku lotsatira? Ngati kudzakhala nyimbo ndi kuvina, kodi zidzakhala zoyenerana ndi makhalidwe achikristu? (2 Akorinto 6:3) Kudzifunsa mafunso oterowo kungakhale kovuta. Koma Miyambo 22:3 imachenjeza kuti: “Wochenjera aona zoipa, nabisala; koma achibwana angopitirira, nalipitsidwa.” Inde, mukhoza kuleŵa mikhalidwe yoopsa mwa kugwiritsa ntchito luso lanu la kuzindikira.
Kuzindikira Posankha Maphunziro Anu
11. Kodi achinyamata angagwiritse ntchito motani luso lawo la kuzindikira pokonza tsogolo lawo?
11 Baibulo limanena kuti n’kwanzeru kukonzekera tsogolo lanu. (Miyambo 21:5) Kodi mwakambirana ndi makolo anu za tsogolo lanu? Mwinamwake mukufuna kudzayamba utumiki wa nthaŵi zonse monga mpainiya. Kunena zoona, palibe ntchito ina iliyonse imene ingakhale yokhutiritsa kuposa imeneyo. Ngati mukuphunzira njira zabwino zochitira phunziro laumwini komanso kudziŵa maluso ena a mu utumiki, dziŵani kuti mukukonzekera ntchito yosangalatsa kwambiri. Kodi mwaganizirapo za mmene muzipezera chithandizo pamoyo wanu mutayamba utumikiwo? Ngati mungadzaganize zokhala ndi banja m’tsogolo, kodi mudzakwanitsa kusamalira udindo wowonjezera umenewo? Kuti musankhe bwino zofunikira kuchita pankhani zimenezo, m’pofunika kugwiritsa ntchito luso la kuzindikira.
12. (a) Kodi mabanja ena achitanji kuti zinthu ziwayendere malinga ndi kusintha kwa mkhalidwe wa zachuma? (b) Kodi kuchita maphunziro owonjezera kumasemphana ndi cholinga cha upainiya? Fotokozani.
12 M’madera ena kumakhalabe kotheka kuloŵa ntchito yophunzirira pantchito pomwepo. Alipo achinyamata ena amene aphunzira bizinesi ya banja lawo kapena kuphunzitsidwa ndi anzawo achikulire amene ali ndi mabizinesi. Ena akuchita makosi akusukulu amene angadzawathandize m’tsogolo muno. Kumadera kumene mwayi umenewu kulibe, makolo atapenda nkhaniyo mosamalitsa, angakonze kuti ana awo alandire maphunziro owonjezera pambuyo pa sukulu yasekondale. Kukonzekereratu maudindo a munthu m’njira imeneyi kuti akadzakula adzawasamalire bwino ndipo makamaka kuti adzakhoze kuchita utumiki waupainiya kwa nthaŵi yaitali, sikusemphana ndi kuika patsogolo Ufumu wa Mulungu. (Mateyu 6:33) Ndipo maphunziro owonjezera salepheretsa cholinga cha upainiya. Mwachitsanzo, kwa nthaŵi yaitali mtsikana wina wa Mboni ankafuna kuchita upainiya. Atamaliza sukulu ya sekondale, makolo ake—apainiya okhazikika—anakonza kuti mwana wawoyo ayambe maphunziro owonjezera. Mtsikanayo anatha kuchita upainiya kwinaku akuchita maphunzirowo, ndipo tsopano anaphunzira luso la ntchito imene ikum’thandiza pamoyo wake pamene akupitiriza upainiya wake.
13. Kodi mabanja ayenera kuŵerengera motani mtengo wa maphunziro owonjezera?
13 Ponena za maphunziro owonjezera, banja lililonse lili ndi ufulu komanso udindo wosankha zimene lingachite. Pamene maphunzirowo asankhidwa bwino, akhoza kukhala othandiza kwambiri. Komanso, akhoza kukhalanso msampha. Ngati mukuganiza za maphunziro oterowo, kodi cholinga chanu n’chiyani? Kodi mukufuna kukonzekereratu mmene mungadzasamalire bwino maudindo anu mukadzakula? Kapena, kodi ‘mukungodzifunira nokha zinthu zazikulu’? (Yeremiya 45:5; 2 Atesalonika 3:10; 1 Timoteo 5:8; 6:9) Nanga bwanji za maphunziro owonjezera osachitira panyumba, mwina kukakhala kukoleji kapena ku yunivesite? Kodi chimenecho chingakhale chanzeru poganizira chenjezo la Paulo lakuti “mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma”? (1 Akorinto 15:33; 2 Timoteo 2:22) Kumbukiraninso kuti “yafupika nthaŵi” yotsalayo. (1 Akorinto 7:29) Kodi ndi nthaŵi yochuluka motani imene mudzaipereka ku maphunziro amenewo? Kodi adzakutengerani zaka zochuluka za unyamata wanu? Ngati zilidi choncho, kodi mudzagwiritsa ntchito motani langizo la Baibulo lakuti “ukumbukirenso Mlengi wako masiku a unyamata wako”? (Mlaliki 12:1) Ndiponso, kodi maphunziro amene mukuwachitawo adzakusiyirani mpata woti muchitire ntchito zofunika kwambiri zachikristu, monga kusonkhana, utumiki wakumunda, ndi phunziro laumwini? (Mateyu 24:14; Ahebri 10:24, 25) Ngati luso lanu la kuzindikira n’lakuthwa, simudzaiŵala zolinga zanu zauzimu pamene inuyo limodzi ndi makolo anu mukonza tsogolo lanu.
Kukhala Paubwenzi Wotomerana Wolemekezeka
14. (a) Kodi ndi malangizo otani amene angathandize otomerana pankhani yosonyezana chikondi? (b) Kodi otomerana ena alephera motani kugwiritsa ntchito luso la kuzindikira pankhani imeneyi?
14 Mbali ina yofuna luso lanu la kuzindikira ndi ubwenzi wotomerana. N’kwachibadwa kufuna kusonyeza chikondi kwa munthu amene mumam’samala. Mwachionekere, otomerana akhalidwe labwino aja a m’Nyimbo ya Solomo anachitirana machitidwe ena osonyezana chikondi asanakwatirane. (Nyimbo ya Solomo 1:2; 2:6; 8:5) Lerolinonso, otomerana ena angaone kuti sikulakwa kugwirana manja, kupsompsonana, ndi kukumbatirana, makamaka pamene ukwati wawo uli pafupi. Koma kumbukirani: “Wokhulupirira mtima wakewake ali wopusa.” (Miyambo 28:26) Mwatsoka lake, otomerana ambiri alephera kugwiritsa ntchito luso la kuzindikira ndipo adziloŵetsa m’mikhalidwe yoikana pachiyeso. Chifukwa cha zimenezo, machitachita osonyezana chikondi apitirira malire ndipo afika posadziletsa; zotsatirapo zake zakhala machitidwe osayenera mpaka chisembwere chenicheni.
15, 16. Kodi ndi machenjezo anzeru ati amene otomerana angawasamale pofuna kukhala ndi ubwenzi wolemekezeka?
15 Choncho ngati muli paubwenzi wotomerana ndi wina, mungachite mwanzeru kupeŵa kukhala aŵiriŵiri panokha m’malo osayenera. Kungakhale bwino kwambiri kusangalala ndi bwenzi lanulo pakati pa anzanu ena kapena m’malo apoyera. Otomerana ena amakhala ndi wina wowaperekeza. Ndiponso, lingalirani mawu a pa Hoseya 4:11 akuti: “Vinyo, ndi vinyo watsopano, zichotsa mtima.” Moŵa ungafooketse luso la kuzindikira la otomeranawo ndi kuwapangitsa kuchita zinthu zimene pambuyo pake zingawanong’onezetse bondo.
16 Miyambo 13:10 imati: “Kudzikuza kupikisanitsa; koma omwe anauzidwa uphungu ali ndi nzeru.” Inde, ‘uzanani uphungu’ ndi kukambirana mmene muzichitira zinthu. Ikani malire pa machitidwe anu osonyezana chikondi, aliyense polemekeza malingaliro ndi chikumbumtima cha mnzake. (1 Akorinto 13:5; 1 Atesalonika 4:3-7; 1 Petro 3:16) Kukambirana nkhani imeneyi kungakhale kovuta poyamba, koma mwakutero mungapeŵe mavuto aakulu amene angabukepo m’tsogolo muno.
Kuphunzitsidwa ‘Kuyambira Ubwana’
17. N’chifukwa chiyani Davide anauza Yehova kuti “mwandikhalira wokhulupirika kuyambira ubwana wanga”? Ndipo pali phunziro lanji kwa achinyamata a lero?
17 Kupeŵa misampha ya Satana kumafuna kuti muzikhala tcheru nthaŵi zonse—ndipo nthaŵi zina, kumafuna kulimba mtima kwambiri. Zoona, nthaŵi zina mungapeze kuti mukukhala wosiyana osati ndi anzanu okha, komanso ndi dziko lonse. Wamasalmo Davide anapemphera kuti: “Inu ndinu chiyembekezo changa, Ambuye Yehova; mwandikhalira wokhulupirika kuyambira ubwana wanga. Mulungu, mwandiphunzitsa kuyambira ubwana wanga; ndipo kufikira lero ndilalikira zodabwitsa zanu.” (Salmo 71:5, 17)c Davide akudziŵika chifukwa cha kulimba mtima kwake. Koma kodi anakhala nako liti? Pamene anali mnyamata! Ngakhale asanagonjetse Goliate, chochitika chimene anatchuka nacho kwambiri, Davide anali atasonyezapo kale kulimba mtima kwake poteteza nkhosa za atate wake pamene anapha mkango komanso chimbalangondo. (1 Samueli 17:34-37) Komabe, Davide anapereka thamo lonse kwa Yehova pa kulimba mtima kulikonse kumene anakusonyeza, ndipo anamuuza kuti “mwandikhalira wokhulupirika kuyambira ubwana wanga.” Luso la Davide lodalira Yehova linam’theketsa kugonjetsa chiyeso chilichonse chomwe anakumana nacho. Inunso mudzaona kuti ngati mudalira Yehova, adzakupatsani kulimba mtima ndi nyonga ‘yolakira dziko lapansi.’—1 Yohane 5:4.
18. Kodi ndi langizo lotani limene likuperekedwa kwa achinyamata a lerolino?
18 Achinyamata anzanu zikwizikwi akhala olimbika mtima ndipo tsopano akutumikira monga ofalitsa uthenga wabwino obatizidwa. Timayamikira Yehova chifukwa cha chikhulupiriro ndi kulimba mtima zimene achinyamatanu mwasonyeza! Khalanibe otsimikiza mtima pothaŵa chidetso cha dzikoli. (2 Petro 1:4) Pitirizanibe kugwiritsa ntchito luso lanu la kuzindikira limene mwaliphunzira m’Baibulo. Kuteroko kudzakutetezani ku tsoka tsopano lino ndipo kudzatsimikizira chipulumutso chanu cham’tsogolo. Ndithudi, monga tidzaonera m’nkhani yomaliza, mukhoza kukhala ndi moyo wopambana.
[Mawu a M’munsi]
a Onani nkhani yakuti “Achinyamata Akufunsa Kuti . . . Kodi Ndingapange Bwanji Choonadi Kukhala Changachanga?” mu Galamukani! ya November 8, 1998.
b Nkhani yakuti “Zosangulutsa Pocheza—Sangalalani ndi Mapinduwo, Peŵani Misampha” imene inatuluka mu Nsanja ya Olonda ya August 15, 1992, ili ndi mfundo zothandiza pankhani imeneyi.
c Salmo 71 likuoneka kuti linapitirizidwa kuchokera ku Salmo 70, limene timawu tapamwamba tikusonyeza kuti ndi salmo la Davide.
Mafunso Obwereramo
◻ Kodi wachinyamata angakulitse motani luso lake la kuzindikira?
◻ Kodi wachinyamata angagwiritse ntchito motani luso lake la kuzindikira pankhani ya macheza achikristu?
◻ Kodi ndi zinthu ziti zofunika kuziganizira posankha maphunziro?
◻ Kodi anthu otomerana angapeŵe bwanji msampha wa chisembwere?
[Zithunzi patsamba 15]
Kuphunzira kufufuza kudzakuthandizani kukulitsa luso lanu la kuzindikira
[Chithunzi patsamba 16]
Macheza aang’ono savuta kuwayang’anira komanso sakonda kusintha n’kukhala mapwando osadziletsa
[Chithunzi patsamba 16]
Makolo ayenera kuthandiza ana awo kusankha maphunziro
[Chithunzi patsamba 17]
Kucheza pakati pa anthu ena kumakhala chitetezo kwa mabwenzi otomerana