“Idzani Kuno kwa Ine . . . Ndipo Ine Ndidzakupumulitsani Inu”
Mmene Anthu Akuwonjezekera Pakufunika Nyumba Zina Mwamsanga
“IDZANI kuno kwa Ine . . . ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu,” anatero Yesu Kristu. (Mateyu 11:28) Pempho labwinotu kwambiri limeneli kuchokera kwa Mutu wa mpingo wachikristu. (Aefeso 5:23) Tikaganizira mawu ameneŵa, timayamikira kwambiri misonkhano yathu yachikristu yomwe imatipatsa mpumulo pocheza ndi abale ndi alongo athu auzimu. Timavomereza mawu a wamasalmo amene anayimba kuti: “N’kokoma ndi kokondweretsa ndithu kuti abale akhale pamodzi!”—Salmo 133:1.
Inde, amene timakhala nawo pamisonkhano yolambirayi ndiwo anthu abwino kwambiri kucheza nawo ndipo macheza oterowo amakhala abwino komanso osangalatsa mwauzimu. Mpake kuti mtsikana wina wachikristu anati: “Ndimakhala kusukulu tsiku lonse, ndipo imanditopetsa kwambiri. Koma misonkhano ili ngati chitsime cha madzi m’chipululu, komwe ndimapeza mpumulo ndi mphamvu zopitiranso kusukulu mmawa mwake.” Mtsikana wina wa ku Nigeria anati: “Ndaona kuti kucheza kwambiri ndi anthu amene amakonda Yehova kumandithandiza kuyandikira kwa iye.”
Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova yakwanuko ndiwo malo a kulambira koona m’deralo. M’madera ambiri, misonkhano imachitikira m’Nyumba ya Ufumu kaŵiri mlungu uliwonse, ndipo amene akuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova tikuwalimbikitsa kumafika mwamsanga kuti azipindula ndi macheza abwino kumeneko.—Ahebri 10:24, 25.
Zikufunika Mwamsanga
Komabe, si Mboni za Yehova zonse zomwe zili ndi Nyumba ya Ufumu yabwino. Kuwonjezeka kwa olengeza Ufumu padziko lonse kwachititsa kuti Nyumba za Ufumu zina zifunike mwamsanga. Nyumba zambiri zikufunikabe makamaka m’mayiko amene akutukuka kumene.—Yesaya 54:2; 60:22.
Mwachitsanzo: Mumzinda womwe ndi likulu la dziko la Democratic Republic of Congo munali Nyumba za Ufumu khumi zokha pa mipingo 290 imene ili mumzindawo. Nyumba za Ufumu zambiri zikufunika mwamsanga m’dzikolo. Ku Angola, mipingo yambiri imasonkhana panja chifukwa chakuti kuli Nyumba za Ufumu zochepa chabe. Vuto limeneli lili m’mayiko ena ambiri.
Choncho, kuchokera mu 1999, pali dongosolo lomwe lakonzedwa lothandiza kumanga Nyumba za Ufumu m’mayiko osauka. Pofuna kuthandiza pa ntchito yomangayi m’mayiko ameneŵa, Mboni zodziŵa bwino ntchitoyi zadzipereka kuigwira. Mboni zimenezi mofunitsitsa pamodzi ndi zina za m’dera lomwe nyumbazo akuzimanga, zimagwirira ntchito limodzi ndipo zotsatira zake zimakhala zolimbikitsa kwambiri. Motero, Mboni za m’deralo zimapindula kwambiri chifukwa cha luso lomwe zimaphunzira. Izi zikuthandiza kuthetsa vuto la kuchepa kwa Nyumba za Ufumu m’mayiko awo.
Choncho, gulu lomanga Nyumba za Ufumu limalandira malangizo othandiza kugwiritsa ntchito njira ndiponso zipangizo zomwe zimapezeka kumaloko. Cholinga sindicho kungomanga Nyumba za Ufumu zambiri zomwe zikufunika, komanso kukhala ndi pulogalamu yomazikonza mosavuta zikawonongeka pogwiritsa ntchito zipangizo zopezeka kumaloko.—2 Akorinto 8:14, 15.
Ntchito Yolimbikitsa Kwambiri
Kodi zotsatira za ntchito yomanga nyumba zolambiriramo imeneyi n’zotani? Kumayambiriro kwa chaka cha 2001, lipoti lochokera ku Malawi linati: “Zomwe zachitika m’dziko lino n’zochititsa chidwi kwambiri. Miyezi iŵiri ikubwerayi tidzamaliza Nyumba za Ufumu zina zambiri.” (Zithunzi 1 ndi 2) M’dziko la Togo, anthu odzipereka anamanga Nyumba za Ufumu zambiri zabwino m’miyezi yaposachedwapa. (Chithunzi 3) Anthu odzipereka omwe akugwira ntchito yabwinoyi akuthandizanso kumanga Nyumba za Ufumu zabwino ku Mexico, Brazil, ndi mayiko ena.
Mipingo ikuona kuti Nyumba ya Ufumu akaimanga, anthu akumeneko amazindikira kuti Mboni za Yehova zikhazikika. Zikuoneka kuti ambiri ankachita mphwayi kusonkhana ndi Mboni mpaka pamene nyumba yabwino yolambiriramo anaimanga. Mpingo wa Nafisi mu Malawi unapereka lipoti lakuti: “Popeza tsopano tili ndi Nyumba ya Ufumu yabwino, ulaliki ukuyenda bwino kwambiri moti timayambitsa maphunziro a Baibulo mosavuta.”
Anthu a mumpingo wa Krake ku Benin ankawaseka kwambiri mmbuyomu chifukwa Nyumba yawo ya Ufumu inali yachikalekale poyerekeza ndi matchalitchi ena. (Chithunzi 4) Tsopano mpingowo uli ndi Nyumba ya Ufumu yabwino kwambiri yomwe ikulemekezetsa kulambira koona. (Chithunzi 5) Mpingo umenewu uli ndi olengeza Ufumu 34 ndipo anthu osachepera 73 amafika pa misonkhano ya Lamlungu. Koma anthu okwana 651 anafika patsiku lopatulira Nyumba ya Ufumuyo. Ambiri mwa anthu ameneŵa anali a m’tauni amene anachita chidwi kwambiri poona kuti Mboni zamanga nyumbayo kwanthaŵi yochepa chabe. Poona zomwe zachitika mmbuyomu pankhani yomangayi, nthambi ya ku Zimbabwe inalemba kuti: “Mwezi umodzi womwe takhala tikumanga Nyumba ya Ufumu, anthu nthaŵi zambiri amawonjezeka moŵirikiza.”—Zithunzi 6 ndi 7.
Mosakayikira, Nyumba za Ufumu zatsopano zambiri ndizo malo amene Akristu odzipatulira komanso anthu achidwi amapezako mpumulo wauzimu. Mpingo wina ku Ukraine utayamba kugwiritsa ntchito Nyumba ya Ufumu yatsopano, Mboni ina kumeneko inati: “Tili ndi chimwemwe chosefukira. Taona ndi maso athu mmene Yehova amathandizira anthu ake. Tsopano chidaliro chathu choti Yehova apitiriza kutithandiza n’cholimba kwambiri.”
[Bokosi/Zithunzi pamasamba 10, 11]
Tikuyamikira Kwambiri Thandizo Lanu
Mboni za Yehova n’zokondwa kwambiri chifukwa cha kuyenda msanga kwa ntchito yomanga Nyumba za Ufumu zatsopano zomwe zikufunika mwamsanga padziko lonse lapansi. Kuwonjezeka kwa olambira a Yehova m’mayiko osiyanasiyana kukuchititsa kuti Nyumba zina za Ufumu zatsopano zizimangidwabe mpaka m’tsogolo. Inde, m’chaka cha utumiki cha 2001, mipingo yosachepera pa 32 anali kuikhazikitsa mlungu uliwonse. Mipingo imeneyi ikufuna malo olambiriramo.
Mwina mungafunse kuti: ‘Kodi ndalama zomangira Nyumba za Ufumu zatsopano makamaka m’mayiko amene abale ali osauka zimachokera kuti?’ Yankho lake limakhudza mbali ziŵiri, thandizo la Mulungu komanso kuwolowa manja kwa anthu.
Malinga ndi lonjezo lake, Yehova akutsanulira mzimu wake woyera kwa atumiki ake umene umawathandiza “kuti achite zabwino, kukhala ochuluka mu ntchito zabwino, kukhala owolowa manja, okonzeka kugaŵira ena.” (1 Timoteo 6:18, NW) Mzimu wa Mulungu umalimbikitsa Mboni za Yehova kuthandizira pa ntchito yolalikira Ufumu m’njira iliyonse. Izo zimagwiritsa ntchito nthaŵi yawo, mphamvu zawo, ndi zinthu zina pantchito zachikristu.
Mzimu wofunitsitsa kupereka mowolowa manja umalimbikitsa Mboni komanso anthu ena amene amathandiza ndi ndalama pantchito yomanga imeneyi. Kuwonjezera pa kulipirira zofunika mumpingo wawo, iwo amaperekanso ndalama zothandizira ntchito yomanga m’mayiko ena padziko lapansi.
Mumpingo uliwonse, muli mabokosi amene analembapo mooneka bwino kuti: “Zopereka za Ntchito ya Padziko Lonse—Mateyu 24:14.” Munthu aliyense atha kuponya m’mabokosi ameneŵa ndalama mwaufulu ngati akufuna kutero. (2 Mafumu 12:9) Timayamikira kwambiri zopereka zonse kaya zambiri kapena zochepa. (Marko 12:42-44) Ndalama zimenezi zimagwira ntchito zosiyanasiyana zomwe zikufunika, kuphatikizapo ntchito yomanga Nyumba za Ufumu. Ndalamazi sizigwira ntchito yolipirira akuluakulu a Mboni za Yehova chifukwa chakuti izo zilibe anthu oterowo amene amalipidwa.
Kodi ndalama zomwe anthu amapereka pantchito ya padziko lonse zimagwiradi ntchito yake? Inde zimagwira. Nthambi ya ku Liberia, dziko lomwe munali nkhondo yapachiweniweni, inapereka lipoti lakuti Mboni zambiri m’dzikolo sizili pantchito ndipo zili pamavuto aakulu azachuma. Kodi anthu a Yehova m’dzikolo angamange bwanji nyumba zabwino zolambiriramo? Nthambiyo inati: “Zopereka za abale m’mayiko ena zidzathandiza pantchitoyi. Limenelitu ndi dongosolo lanzeru komanso labwino kwambiri.”
Abale m’mayiko ameneŵa nawonso amapereka ngakhale kuti ndi osauka. Dziko la Sierra Leone mu Africa linapereka lipoti lakuti: “Abale kuno akuthandiza kwambiri pantchitoyi ndipo mokondwera amagwiritsa ntchito mphamvu zawo komanso amapereka kangachepe komwe ali nako kuthandizira ntchito yomanga Nyumba za Ufumu.”
Ntchito yonseyi potsirizira pake imalemekeza Yehova. Abale a ku Liberia ananena mokondwera kuti: “Ntchito yomanga nyumba zabwino zolambiriramo m’dziko lonse lino idziŵitsa anthu kuti kulambira koona kukhazikika komanso dzina lalikulu la Mulungu wathu likwezeka ndi kulemekezeka.”