Tizilemekeza Malo Athu Olambirira Yehova
“Kudzipereka kwambiri panyumba yanu kudzandidya.”—YOH. 2:17.
1, 2. (a) Kodi kale atumiki a Yehova ankagwiritsa ntchito malo ati pomulambira? (b) Kodi Yesu ankaona bwanji kachisi wa Mulungu ku Yerusalemu? (c) Kodi tikambirana chiyani m’nkhaniyi?
ATUMIKI a Mulungu amakhala ndi malo olambirira ndipo izi zinayamba kalekale. Mwachitsanzo, Abele ayenera kuti ankapereka nsembe zake paguwa. (Gen. 4:3, 4) Nowa, Abulahamu, Isaki, Yakobo ndi Mose anamanganso maguwa a nsembe. (Gen. 8:20; 12:7; 26:25; 35:1; Eks. 17:15) Yehova anauza Aisiraeli kuti amange chihema. (Eks. 25:8) Patapita nthawi, anamanganso kachisi kuti azilambiramo Yehova. (1 Maf. 8:27, 29) Ayuda atabwerera ku ukapolo ku Babulo, ankasonkhana m’masunagoge. (Maliko 6:2; Yoh. 18:20; Mac. 15:21) Akhristu oyambirira ankasonkhana m’nyumba za anthu a mumpingo. (Mac. 12:12; 1 Akor. 16:19) Masiku ano, Akhristu padziko lonse amalambira Yehova ndiponso kuphunzira Mawu ake m’Nyumba za Ufumu.
2 Yesu ankakonda kwambiri kachisi wa Yehova ku Yerusalemu ndipo Baibulo limasonyeza kuti iye anakwaniritsa lemba lakuti: “Kudzipereka kwambiri panyumba yanu kwandidya.” (Sal. 69:9; Yoh. 2:17) Koma sitinganene kuti Nyumba ya Ufumu ndi ‘nyumba ya Yehova’ ngati mmene zinalili ndi kachisi ku Yerusalemu. (2 Mbiri 5:13; 33:4) Ngakhale zili choncho, m’Baibulo muli mfundo zosonyeza zimene tiyenera kuchita polemekeza Nyumba ya Ufumu. M’nkhaniyi tikambirana mfundozi. Tikambirananso zimene tingachite pothandiza kuti Nyumba za Ufumu zizimangidwa, kuyeretsedwa komanso kukonzedwa.a
TIZILEMEKEZA KWAMBIRI MISONKHANO YATHU
3-5. (a) Kodi cholinga cha Nyumba ya Ufumu n’chiyani? (b) Kodi tiyenera kusonyeza makhalidwe otani tikakhala pa misonkhano?
3 Nyumba ya Ufumu ndi malo amene timakumana mlungu uliwonse kuti tiziphunzitsidwa ndi Yehova komanso kumulambira. Pamalowa timalimbikitsidwa ndiponso kulandira malangizo othandiza amene gulu la Yehova limatipatsa. Onse amene amafika pa Nyumba ya Ufumu amaitanidwa ndi Yehova ndiponso Mwana wake. Tiyenera kuona kuti ‘kudzadya patebulo la Yehova’ ndi mwayi wa mtengo wapatali.—1 Akor. 10:21.
4 Yehova amaona kuti misonkhano ndi yofunika kwambiri, choncho amatiuza kuti tisaleke kusonkhana. (Werengani Aheberi 10:24, 25.) Popeza timalemekeza Yehova, sitiyenera kujomba ku misonkhano popanda zifukwa zomveka. Tikamakonzekera ndiponso kuyankha pa misonkhano timasonyeza kuti timaiyamikira kwambiri.—Sal. 22:22.
5 Zimene timachita tikakhala pa Nyumba ya Ufumu ndiponso poisamalira, zingasonyeze kuti timalemekeza Yehova kapena ayi. Tikakhala pa misonkhano tiyenera kuchita zinthu mogwirizana ndi dzina la Yehova lomwe limalembedwa pa chikwangwani cha Nyumba ya Ufumu.—Yerekezerani ndi 1 Mafumu 8:17.
6. Kodi anthu ena ananena zotani atafika pa Nyumba ya Ufumu? (Onani chithunzi patsamba 27.)
6 Tikamachita zinthu mwaulemu pamalo athu olambirira, anthu ena omwe si Mboni amaona. Mwachitsanzo bambo wina ku Turkey anati: “Nditafika pa Nyumba ya Ufumu ndinachita chidwi kwambiri ndi mmene malowo ankaonekera. Anthu ake anavala mwaulemu, anali ansangala ndipo anandilandira bwino.” Munthuyo anayamba kufika pa misonkhano yonse ndipo kenako anabatizidwa. Pofuna kutsegulira Nyumba ya Ufumu mumzinda wina ku Indonesia, abale anaitana anthu ena apafupi, meya wa mzindawu ndiponso akuluakulu ena aboma kuti adzaione. Meyayo anachita chidwi kwambiri poona kuti Nyumba ya Ufumu ndi yomangidwa bwino ndiponso malowo ndi okongola kwambiri. Iye anati: “Nyumbayi ndi yaukhondo kwambiri ndipo zikusonyeza kuti mumakhulupirira kwambiri Mulungu.”
7, 8. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timalemekeza Yehova pa misonkhano?
7 Tiyenera kuvala ndiponso kudzikongoletsa mwaulemu pofuna kusonyeza kuti timalemekeza Yehova amene watiitanira ku misonkhano. Koma zikuoneka kuti ena amakhwimitsa kwambiri zinthu pomwe ena amachita zinthu motayirira ngati kuti ali kunyumba. N’zoona kuti Yehova amafuna kuti anthu asamamangike pa Nyumba ya Ufumu. Koma tiyenera kupewa kutumizirana mauthenga pafoni, kudya, kumwa kapena kuchita chilichonse chimene chingasokoneze ena. Makolo ayenera kuphunzitsa ana awo kuti asamathamangethamange kapena kusewera pa Nyumba ya Ufumu.—Mlal. 3:1.
8 Yesu anakwiya ataona anthu akugulitsa zinthu m’kachisi ndipo anawathamangitsa. (Yoh. 2:13-17) Nazonso Nyumba za Ufumu si malo ochitirapo malonda koma ndi malo oti tiziphunzitsidwa ndiponso kulambira Yehova. Choncho sitiyenera kuchita zinthu zosemphana ndi cholinga cha Nyumba ya Ufumu.—Yerekezerani ndi Nehemiya 13:7, 8.
NTCHITO YOMANGA NYUMBA ZA UFUMU
9, 10. (a) Fotokozani mmene ntchito yomanga Nyumba za Ufumu yayendera. (b) Kodi gulu la Yehova limathandiza bwanji mipingo imene singakwanitse kumanga Nyumba ya Ufumu?
9 Gulu la Yehova likuchita zambiri pothandiza kuti Nyumba za Ufumu zambirimbiri zimangidwe. Abale ndi alongo odzipereka ndi amene amagwira ntchito yopanga mapulani, kumanga ndiponso kukonza zowonongeka. Kuyambira pa November 1, 1999, Nyumba za Ufumu zoposa 28,000 zamangidwa padziko lonse. Apa tinganene kuti pa zaka 15 zapitazi, pafupifupi Nyumba za Ufumu 5 zinkamangidwa tsiku lililonse.
10 Gulu la Yehova limayesetsa kugwiritsa ntchito bwino ndalama zimene ena amapereka kuti Nyumba za Ufumu zimangidwe m’madera osiyanasiyana. Izi n’zogwirizana ndi mfundo ya m’Malemba yakuti zochuluka zimene ena ali nazo zithandizire pa zimene ena akusowa “kuti pakhale kufanana.” (Werengani 2 Akorinto 8:13-15.) Zotsatira zake n’zakuti Nyumba za Ufumu zokongola zamangidwa m’mipingo imene payokha sikanakwanitsa.
11. (a) Kodi abale ena ananena zotani atamangiridwa Nyumba ya Ufumu? (b) Kodi inuyo mumamva bwanji mukaganizira zoti abale ndi alongo amasangalala akamangiridwa Nyumba ya Ufumu?
11 Abale ena mumpingo wina ku Costa Rica atamangiridwa Nyumba ya Ufumu anati: “Tikamaona Nyumba ya Ufumu yathu sitimvetsa ngakhale pang’ono. Zimangokhala ngati kutulo. Nyumbayo inamangidwa n’kumaliza chilichonse m’masiku 8 okha. Zonsezi zinatheka chifukwa chothandizidwa ndi Yehova, zimene gulu lake lachita komanso khama la abale ndi alongo odzipereka. Kunena zoona nyumbayi ndi mphatso yamtengo wapatali imene Yehova watipatsa. Timainyadira kwambiri.” Kodi inuyo mumamva bwanji mukaganizira zoti anthu m’mayiko ambiri akusangalala chifukwa chokhala ndi Nyumba za Ufumu? Zikuonekeratu kuti Yehova akudalitsa ntchito yomanga nyumbazi. Tikutero chifukwa chakuti Nyumba ya Ufumu ikangomangidwa anthu ambiri amabwera kudzasonkhanamo.—Sal. 127:1.
12. Kodi inuyo mungathandize bwanji pa ntchito yomanga Nyumba za Ufumu?
12 Abale ndi alongo ambiri akhalapo ndi mwayi wogwira nawo ntchito yomanga Nyumba za Ufumu ndipo amasangalala kwambiri. Kaya ifenso tingagwire nawo ntchitoyi kapena ayi, tikhoza kuthandiza popereka ndalama zathu. Kale, ntchito zokhudza malo olambirira zinkayenda bwino chifukwa cha zinthu zimene anthu ankapereka. Ndi mmene zililinso masiku ano ndipo zimenezi zimalemekeza kwambiri Yehova.—Eks. 25:2; 2 Akor. 9:7.
NYUMBA YA UFUMU IZIKHALA YAUKHONDO
13, 14. Kodi ndi mfundo za m’Malemba ziti zimene zimasonyeza kuti tiyenera kuyeretsa Nyumba ya Ufumu?
13 Nyumba ya Ufumu ikamangidwa, tiyenera kuisamalira kuti izilemekeza Mulungu wadongosolo amene timamulambira. (Werengani 1 Akorinto 14:33, 40.) Yehova amafuna kuti anthu ake azikhala oyera. Choncho tiyenera kukhala anthu aukhondo, amaganizo oyera, amakhalidwe abwino ndiponso osadetsedwa ndi kulambira konyenga.—Chiv. 19:8.
14 Tikamayeretsa Nyumba ya Ufumu, sitichita manyazi kuitana anthu ku misonkhano yathu. Anthu akabwera ku misonkhano amaonadi kuti timalambira Mulungu woyera amene adzakonza zinthu padzikoli kuti likhalenso loyera.—Yes. 6:1-3; Chiv. 11:18.
15, 16. (a) Kodi ndi zinthu ziti zimene zingachititse kuti ntchito yoyeretsa Nyumba ya Ufumu ikhale yovuta? (b) N’chifukwa chiyani kuyeretsa Nyumba za Ufumu ndi kofunika kwambiri? (c) Kodi mumpingo wanu akulu akonza zotani kuti Nyumba ya Ufumu iziyeretsedwa ndipo tonsefe tiyenera kuchita chiyani?
15 Anthufe timakhala ndi maganizo osiyana pa nkhani ya ukhondo. Izi zimachitika chifukwa cha kumene timachokera. Kumadera ena kumakhala fumbi ndi matope ambiri kapena zimavuta kupeza madzi, sopo ndiponso zinthu zina zoyeretsera. Koma kaya zinthu zili bwanji kwathuko, Nyumba za Ufumu ziyenera kukhala zaukhondo kwambiri chifukwa ndi malo olambirira Yehova.—Deut. 23:14.
16 Kuti tikhale ndi Nyumba ya Ufumu yaukhondo, tiyenera kuchita zinthu mwadongosolo. Akulu ayenera kuonetsetsa kuti pali ndandanda ya anthu oyeretsa komanso zinthu zokwanira zoyeretsera. Malo ena amafunika kuyeretsedwa pafupifupi pomwe malo ena mwa apa ndi apo. Ndiyeno akulu ayenera kuonetsetsa kuti malo alionse akusamaliridwa bwinobwino. Koma aliyense mumpingo ayenera kuthandiza pa ntchito yofunika imeneyi.
TIZIKONZA ZINTHU ZOWONONGEKA PA NYUMBA YA UFUMU
17, 18. (a) Kodi ndi malemba ati amene angatilimbikitse kukonza zinthu zimene zawonongeka pamalo amene timalambira Yehova? (b) N’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kukonza Nyumba za Ufumu?
17 Atumiki a Yehova amayesetsanso kukonza zinthu zimene zawonongeka pa Nyumba za Ufumu. Pamene Yehoasi ankalamulira ku Yuda, anauza ansembe kuti agwiritse ntchito ndalama zimene anthu anapereka kuti akonze ming’alu ya nyumba ya Yehova. (2 Maf. 12:4, 5) Patapita zaka zoposa 200, Mfumu Yosiya anagwiritsanso ntchito ndalama zimene zinaperekedwa kukachisi kuti akonze zinthu zimene zinawonongeka.—Werengani 2 Mbiri 34:9-11.
18 Abale kumaofesi a nthambi ena amaona kuti mipingo sinazolowere kukonza zinthu zimene zawonongeka m’Nyumba za Ufumu. Mwina n’chifukwa chakuti m’maderawo mulibe abale ambiri amene ali ndi luso lokonza zinthu kapena amasowa ndalama zothandizira pa ntchitoyi. Koma vuto ndi lakuti tikalephera kukonza Nyumba za Ufumu, zikhoza kuwonongeka mwamsanga ndipo izi zinganyozetse dzina la Yehova. Choncho tiyeni tonsefe tiziyesetsa kukonza zimene zawonongeka. Tikatero Yehova adzalemekezedwa komanso ndalama zimene Akhristu anzathu amapereka sizidzapita pachabe.
19. Kodi inuyo panopa muziyesetsa kuchita chiyani pa Nyumba ya Ufumu?
19 Nyumba ya Ufumu ikamangidwa imaperekedwa kwa Yehova. Choncho si nyumba ya munthu kapena ya mpingo. M’nkhaniyi taona mfundo za m’Malemba zotilimbikitsa kusamalira Nyumba za Ufumu kuti zizikhala zogwirizana ndi cholinga chake. Choncho tiyeni tizilemekeza malo amene timalambira Yehova. Tiziperekanso ndalama zothandiza pa ntchito yomanga Nyumba za Ufumu zina. Komanso tizigwira mwakhama ntchito yoyeretsa ndi kukonza nyumbazi. Tikatero ndiye kuti tikutsanzira Yesu amene ankakonda ndiponso kulemekeza kwambiri nyumba ya Yehova.—Yoh. 2:17.
a M’nkhaniyi tikambirana za Nyumba za Ufumu koma mfundo zake zikukhudzanso malo alionse amene timasonkhana kuti tilambire Mulungu.