‘Limba Nayoni Nkhondo Yabwino ya Chikhulupiriro’
KODI pali msilikali aliyense amene angakhumudwe panthaŵi ya nkhondo atauzidwa kuti: “Inu bwererani kaye kunyumba, mukacheze ndi mkazi ndiponso banja lanu”?
Msilikali wina m’masiku a Mfumu Davide ya ku Israyeli anauzidwa zimenezo. Uriya Mhiti anaitanidwa ndi mfumu yeniyeniyo ndipo inam’limbikitsa kubwerera kunyumba. Koma Uriya anakana kupita kunyumba kwake. Atam’funsa chifukwa chomwe anakanira, Uriya anayankha kuti likasa la chipangano lomwe linkaphiphiritsira kukhalapo kwa Mulungu ndiponso asilikali achiisrayeli anali kunkhondo. Ndipo anafunsa kuti: “Potero ndikapita ine kodi ku nyumba yanga kuti ndidye, ndimwe, ndigone ndi mkazi wanga?” Uriya ankaona kuti n’kupanda nzeru kuchita zimenezi panthaŵi yovuta ngati imeneyo.—2 Samueli 11:8-11.
Zomwe Uriya anachitazi zikutipatsa mafunso ofunika kwambiri, chifukwa nafenso tikukhala m’nthaŵi ya nkhondo. Panopo kukuchitika nkhondo yosiyana kwambiri ndi zonse zimene mayiko akhala akumenya. Ndi nkhondo yoopsa kwambiri tikaiyerekeza ndi nkhondo zikuluzikulu ziŵiri zapadziko lonse, ndipo inuyo ikukukhudzani. N’kosavuta kuti munthu avulalepo pankhondoyi ndipo mdaniyo ngochititsa mantha kwambiri. Pankhondoyi palibe kuwomberana zipolopolo kapena kuponyerana mabomba, koma m’pofunika ukatswiri kwambiri.
Musanayambe kumenya nawo nkhondoyi, muyenera kudziŵa ngati ndi bwino kumenya nawo ndiponso cholinga chake cha nkhondoyi. Kodi nkhondoyi ikuyenerana ndi mphoto yake? Cholinga cha nkhondo yapaderayi chinafotokozedwa ndi mtumwi Paulo m’kalata yomwe analembera Timoteo, kuti: “Limba nayo nkhondo yabwino ya chikhulupiriro.” Zoonadi, pankhondoyi simuyenera kutchinjiriza linga ayi, koma “chikhulupiriro,” choonadi chonse chachikristu chomwe chafotokozedwa m’Baibulo. Mwachionekere, kuti mumenye nkhondo ya chikhulupiriro ndi kupambana muyenera kutsimikiza kuti “chikhulupiriro” chimenechi n’choona.—1 Timoteo 6:12.
Msilikali wanzeru amayesetsa kudziŵa mdani wake. Pankhondoyi, mdani ndi Satana. Iye akudziŵa bwino njira zomenyera nkhondoyi chifukwa wakhala zaka zambiri akuchita zimenezi ndipo ali ndi zipangizo ndiponso zida zochuluka kwambiri. Iye ndi woposa anthu. Satana ndi wankhanza, wachiwawa, ndiponso ndi wachinyengo. (1 Petro 5:8) Zida zopangidwa ndi anthu komanso ukatswiri ndi ukathyali wawo sizingachite kanthu kwa mdani ameneyu. (2 Akorinto 10:4) Kodi n’chiyani chimene mungagwiritse ntchito pomenya nkhondoyi?
Chida chachikulu ndi ‘lupanga la Mzimu, lomwe ndilo Mawu a Mulungu.’ (Aefeso 6:17) Mtumwi Paulo anasonyeza mmene lupangali limathandizira. Anati: “Mawu a Mulungu ali amoyo, ndi ochitachita, ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse, napyoza kufikira kugaŵira moyo ndi mzimu, ndi zimfundo ndi mafuta a m’mafupa, nazindikiritsa zolingirira ndi zitsimikizo za mtima.” (Ahebri 4:11, 12) Kunena zoona, chida chakuthwa kwambiri komanso chosaphonya ngakhale pang’ono, moti chingathe kuloŵa mpaka m’maganizo ndi m’zolinga za munthu, chiyeneradi kugwiritsidwa ntchito mwaluso ndiponso mosamala.
Muyenera kuti mukudziŵa zoti asilikali angakhale ndi zida zapamwamba kwambiri, koma zidazo zingakhale zopanda pake ngati asilikaliwo sakutha kuzigwiritsira ntchito bwino. Zilinso chimodzimodzi ndi inu. Mukufunika malangizo kuti mugwiritse ntchito bwino lupanga lanu. N’zosangalatsa kuti pali akatswiri ankhondoyi omwe angatiphunzitse kamenyedwe kake. Yesu anatcha akatswiri ophunzitsa anzawo ameneŵa kuti ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” yemwe wapatsidwa udindo wopereka chakudya chauzimu, kapena kuti malangizo apanthaŵi yake kwa otsatira a Yesu. (Mateyu 24:45) Mungazindikire kagulu ka kapolo ameneyu mwa kuona mmene kakuphunzitsira mwakhama ndiponso kuchenjeza anthu panthaŵi yake za njira zomwe mdaniyu akugwiritsa ntchito. Umboni ukusonyeza kuti kagulu kameneka ndi ka anthu odzozedwa ndi mzimu a mumpingo wachikristu wa Mboni za Yehova.—Chivumbulutso 14:1.
Kagulu ka kapolo kameneka kachita zambiri kuwonjezera pa kupereka malangizo. Kasonyeza mtima wa mtumwi Paulo, amene analembera mpingo wa ku Tesalonika, kuti: “Tinakhala ofatsa pakati pa inu, monga mmene mlezi afukata ana ake a iye yekha; kotero ife poliralira inu, tinavomera mokondwera kupereka kwa inu si Uthenga Wabwino wa Mulungu wokha, komanso moyo wathu, popeza mudakhala okondedwa kwa ife.” (1 Atesalonika 2:7, 8) Zili kwa msilikali aliyense wachikristu kugwiritsa ntchito maphunziro abwino ameneŵa.
Zida Zonse Zankhondo
Pali zida zonse zankhondoyi zophiphiritsira zoti zikutetezeni. Mungapeze mndandanda wa zidazi pa Aefeso 6:13-18. Msilikali wochenjera sangapite kunkhondo ngati zina mwa zida zake zauzimu zikusoŵa kapena n’zofunika kukonzedwa.
Mkristu amafunika kukhala ndi zida zonse zankhondo zomuteteza, koma chikopa cha chikhulupiriro ndicho chofunika kwambiri. N’chifukwa chake Paulo analemba kuti: ‘Koposa zonse mudzitengerenso chikopa cha chikhulupiriro, chimene mudzakhoza kuzima nacho mivi yonse yoyaka moto ya woipayo.’—Aefeso 6:16.
Chikopa, chomwe chingathe kubisa thupi lonse, chikuimira kulimba kwa chikhulupiriro. Muyenera kukhulupirira zolimba malangizo a Yehova, ndi kuwalandira osakayikira n’komwe kuti malonjezo ake onse adzakwaniritsidwa. Muziona ngati kuti malonjezowo akwaniritsidwa kale. Musakayikire ngakhale pang’ono kuti dziko lonse la Satanali liwonongedwa posachedwapa, kuti dzikoli lidzasintha n’kukhala paradaiso, ndiponso kuti anthu omvera Mulungu adzakhalanso angwiro.—Yesaya 33:24; 35:1, 2; Chivumbulutso 19:17-21.
Komabe, pankhondo yaikulu yomwe ili mkatiyi mukufunikanso kukhala ndi mnzanu. Pankhondo, asilikali a mbali imodzi amagwirizana kwambiri akamalimbikitsana ndiponso kutetezana, nthaŵi zina ngakhalenso kupulumutsana ku imfa kumene. Ndi bwino kwambiri kukhala ndi anzanu, koma kuti mupambane pankhondo iyi, mukufunika kukhala paubwenzi ndi Yehova mwiniyo. N’chifukwa chake Paulo anamaliza mndandanda wake wa zida zankhondowu ndi mawu akuti: “Mwa pemphero lonse ndi pembedzero mupemphere nthaŵi yonse mwa Mzimu.”—Aefeso 6:18.
Timasangalala kwambiri kukhala ndi bwenzi lapamtima. Timayesetsa kukhala naye. Mwa kulankhula nthaŵi zonse ndi Yehova m’pemphero, iye amakhala weniweni kwa ife, monga bwenzi lodalirika. Wophunzira Yakobo akutilimbikitsa kuti: “Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu.”—Yakobo 4:8.
Njira Zimene Mdaniyu Akugwiritsa Ntchito
Nthaŵi zina kulimbana ndi dzikoli kungakhale ngati kuyenda m’dera lomwe akwiriramo mabomba. Mdani angachokere kulikonse ndipo angakugwireni mwadzidzidzi. Koma khalani ndi chikhulupiriro chakuti Yehova wapereka zonse zofunika kuti mutetezedwe.—1 Akorinto 10:13.
Mdaniyu cholinga chake chingakhale kutsutsa mfundo za choonadi za m’Baibulo zomwe ndi zofunika kwambiri pa chikhulupiriro chanu. Ampatuko angagwiritse ntchito mawu okoma, osyasyalika, ndiponso mfundo zopotoka pofuna kukugonjetsani. Koma sikuti amakhala akukufunirani zabwino. Miyambo 11:9 imati: “Wonyoza Mulungu [“wampatuko,” NW] awononga mnzake ndi m’kamwa mwake; koma olungama adzapulumuka pakudziŵa.”
Kungakhale kulakwa kuganiza kuti mufunika kumvetsera anthu ampatuko kapena kuŵerenga mabuku awo kuti muthe kuwatsutsa. Mfundo zawo zopotoka komanso zoipa zingakuwonongeni mwauzimu ndipo zingakhudze chikhulupiriro chanu monga chilonda chonyeka mofulumira. (2 Timoteo 2:16, 17) M’malo mwake, tsanzirani mmene Mulungu amachitira ndi ampatuko. Ponena za Yehova, Yobu anati: “Wonyoza Mulungu [“wampatuko,” NW] sadzafika pamaso pake.”—Yobu 13:16.
Mdaniyu angayese njira ina, ndipo iyi ndi njira imene wakhala akupindula nayo ndithu. Pangakhale chisokonezo ngati asilikali omwe ali pa ligubo la nkhondo akopeka kutayana ndi anzawo, n’kupita kukachita zachiwerewere.
Zosangalatsa za m’dzikoli, monga mafilimu ndi mapulogalamu a pa TV osonyeza zinthu zoipa komanso nyimbo zaphokoso kwambri, ndi msampha wamphamvu kwambiri. Ena amati angaonere zinthu zolaula kapena kuŵerenga mabuku olaula popanda chilichonse chowachitikira. Koma mwamuna wina amene nthaŵi zonse ankaonera mavidiyo olaula koopsa ananena mosapsatira mawu kuti: “Munthu suiwala zimene waonazo, ukamaziganizira kwambiri chilakolako chochita zomwe unaonazo chimakula . . . Mafilimu ameneŵa amakuganizitsani kuti mukumanidwa chinachake.” Kodi n’koyenera kudziika dala pangozi yovulazidwa ndi msampha wosaonekera umenewu?
Chida china chimene mdaniyu ali nacho ndicho kukopeka ndi chuma. Zingakhale zovuta kuzindikira vuto lake chifukwa chakuti tonse timafunika kukhala ndi katundu. Timafunika kukhala ndi nyumba, chakudya, komanso zovala; ndipo sikuti m’polakwika kukhala ndi zinthu zabwino. Vuto lagona pa mmene munthu amaonera zinthuzo. N’zotheka kuika patsogolo ndalama m’malo mwa zinthu zauzimu. Tikhoza kukhala okonda ndalama. Koma ndi bwino kumadzikumbutsa za zinthu zimene chuma sichingachite. Sichikhalitsa, pamene chuma chauzimu chidzakhala mpaka muyaya.—Mateyu 6:19, 20.
Asilikali akamadzikayikira, sipakhala chiyembekezo choti apambana. “Ukalefuka tsiku la tsoka mphamvu yako ichepa.” (Miyambo 24:10) Kulefuka ndi chida chimene Satana wakhala akuchigwiritsa ntchito kwambiri. Kuvala ‘chisoti chimene ndi chiyembekezo cha chipulumutso’ kudzakuthandizani kuti musalefuke. (1 Atesalonika 5:8) Yesani kukhala ndi chikhulupiriro cholimba ngati cha Abrahamu. Atauzidwa kuti apereke nsembe Isake, mwana wake mmodzi yekhayo, Abrahamu sananyinyirike. Ankakhulupirira kuti Mulungu adzakwaniritsa lonjezo Lake lodalitsa mitundu yonse mwa mbewu yake ndiponso kuti Mulungu akanatha kuukitsa Isake kwa akufa pakanafunika kutero, n’cholinga choti akwaniritse lonjezolo.—Ahebri 11:17-19.
Musasiye Kumenya Nkhondo
Ena omwe kwa nthaŵi yaitali akhala akumenya nkhondoyi molimba mtima angakhale atayamba kulema ndipo chifukwa cha zimenezi sakumenya nkhondoyi mwatcheru ngati kale. Chitsanzo cha Uriya, yemwe tam’tchula koyambirira kwa nkhani ino, chingathandize onse omwe akumenya nawo nkhondoyi kusabwerera m’mbuyo. Ambiri mwa asilikali anzathu achikristu akumana ndi mavuto, miyoyo yawo ili pangozi, kapena akuvutika ndi chisanu ndiponso njala. Mofanana ndi Uriya, ndi bwino kuti tisamaganizire zinthu zonse zabwino zomwe tingapeze panopo kapena kugonjera chikhumbo chokhala moyo wa mwanaalirenji. Tiyenera kukhalabe ndi gulu lankhondo la Yehova lapadziko lonse la asilikali okhulupirika ndi kulimba nayo nkhondoyi mpaka titadzalandira madalitso omwe atisungira.—Ahebri 10:32-34.
Zingakhale zoopsa kwambiri ngati titayirira, mwina poganizira kuti kutiukira komaliza kudakali kutali kwambiri. Chitsanzo cha Mfumu Davide chikusonyeza kuopsa kwake. Pachifukwa china iye anatsala asilikali ake atapita ku nkhondo. Chotsatira chake chinali chakuti, Davide anachita tchimo lalikulu lomwe linam’soŵetsa mtendere ndiponso kum’dzetsera mavuto moyo wake wonse.—2 Samueli 12:10-14.
Kodi m’poyenera kumenya nawo nkhondoyi, kulimba nayo, kulolera kunyozedwa, ndi kusiya zosangalatsa za m’dzikoli zomwe sizabwino? Amene akumenyabe nkhondoyi bwinobwino amavomereza kuti zinthu zomwe dzikoli limapereka zingaoneke zokopa, ngati kanthu konyezimira kwambiri kokongoletsera chinthu, koma kuzionetsetsa bwino muona kuti zilibe phindu kwenikweni. (Afilipi 3:8) Ndiponso nthaŵi zambiri mapeto a zosangalatsa zimenezo amakhala mavuto ndiponso kugwira fuwa lamoto.
Mkristu amene akumenya nawo nkhondo yauzimuyi amakhala paubwenzi wolimba ndi mabwenzi enieni, chikumbumtima choyera, ndiponso amayembekezera zinthu zabwino kwambiri. Akristu odzozedwa ndi mzimu akuyembekezera moyo wosafa kumwamba limodzi ndi Kristu Yesu. (1 Akorinto 15:54) Ambiri mwa asilikali achikristu akuyembekezera moyo wangwiro m’dziko lapansi laparadaiso. Kunena zoona, m’pomveka kuchita chilichonse kuti tipeze mphoto imeneyi. Ndipo mosiyana ndi nkhondo zadziko, tidzapambana nkhondoyi ngati tipitiriza kukhala okhulupirika. (Ahebri 11:1) Koma mapeto a dongosolo lomwe lili m’manja mwa Satanali ndi chiwonongeko chotheratu.—2 Petro 3:10.
Pamene mukulimba nayo nkhondoyi, kumbukirani mawu a Yesu akuti: “Limbikani mtima; ndalilaka dziko lapansi Ine.” (Yohane 16:33) Iye analigonjetsa mwa kukhala tcheru ndiponso kukhala wolimba panthaŵi yoyesedwa. Ifenso tingachite chimodzimodzi.
[Mawu Otsindika patsamba 27]
Pankhondoyi palibe kuwomberana zipolopolo kapena kuponyerana mabomba, koma m’pofunika ukatswiri kwambiri
[Mawu Otsindika patsamba 30]
Tidzapambana nkhondoyi ngati tipitiriza kukhala okhulupirika
[Chithunzi patsamba 26]
Chisoti cha chipulumutso chidzatithandiza kuti tisalefuke
Gwiritsani ntchito chikopa cha chikhulupiriro kuti muzimitse ‘mivi yoyaka moto’ ya Satana
[Chithunzi patsamba 28]
“Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu”
[Chithunzi patsamba 29]
Tiyenera kukhala ndi chikhulupiriro kuti malonjezo a Mulungu adzakwaniritsidwa