Kodi Mavuto Amene Mumakumana Nawo Amalamulira Moyo Wanu?
MAVUTO ndi ofala kwambiri “nthaŵi zoŵaŵitsa” zino. (2 Timoteo 3:1) Mavuto ena angakhale a kanthaŵi ndipo amatha. Ena angakhale kwa miyezi kapenanso zaka zambiri. Choncho, ambiri amamva ngati mmene anamvera Davide wamasalmo, amene analirira Yehova kuti: “Masautso a mtima wanga akula: munditulutse m’zondipsinja.”—Salmo 25:17.
Kodi mukulimbana ndi mavuto othetsa nzeru? Ngati mukutero, Baibulo lingakuthandizeni ndi kukulimbikitsani. Tiyeni tikambirane za moyo wa atumiki aŵiri okhulupirika a Yehova amene anathana ndi mavuto awo. Atumikiwo ndi Yosefe ndi Davide. Mwa kupenda mmene iwo anachitira ndi mavuto awo, tingaphunzirepo mfundo zimene zidzatithandiza kupirira mavuto ngati amene iwo anakumana nawo.
Anakumana ndi Mavuto Aakulu
Nthaŵi imene Yosefe anakwanitsa zaka 17, anali pa vuto lalikulu m’banja mwawo. Abale ake anaona kuti Yakobo, atate wawo, “anam’konda [Yosefe] koposa abale ake onse.” Chifukwa cha zimenezi, iwo “anamuda iye, ndipo sanathe kulankhula ndi iye mwamtendere.” (Genesis 37:4) Titha kuona mmene zimenezi zinam’vutitsira maganizo kwambiri Yosefe. M’kupita kwa nthaŵi, abale akewo anamuda kwambiri mpaka anam’gulitsa kukhala kapolo.—Genesis 37:26-33.
Ali kapolo ku Igupto, mkazi wa mbuye wake anali kufuna kuti Yosefeyo agone naye koma iye anakana. Pokhumudwa kuti Yosefe wam’kana, mkaziyo ananamizira Yosefe kuti anafuna kum’gwirira. Yosefe ‘anamuika m’kaidi’ kumene “anapweteka miyendo yake ndi matangadza; [ndipo] anam’goneka m’unyolo.” (Genesis 39:7-20; Salmo 105:17, 18) Koma ndiye anavutika bwanji! Kwa zaka pafupifupi 13, Yosefe anakhala kapolo kapenanso mkaidi chifukwa cha kupanda chilungamo kwa ena, kuphatikizapo a pabanja lakwawo.—Genesis 37:2; 41:46.
Nayenso Davide wa ku Israyeli wakale anakumana ndi mavuto ali mnyamata. Kwa zaka zambiri, anakakamizika kukhala ndi moyo wothaŵathaŵa, chifukwa chakuti Mfumu Sauli anali kum’saka ngati nyama. Nthaŵi zonse moyo wa Davide unali pangozi. Nthaŵi ina iye anapita kwa Ahimeleki wansembe kuti akapezeko chakudya. (1 Samueli 21:1-7) Sauli atadziŵa kuti Ahimeleki anathandiza Davide, analamula kuti Ahimeleki komanso ansembe onse ndi mabanja awo aphedwe. (1 Samueli 22:12-19) Kodi mukuona mmene Davide anavutikira mtima poganiza kuti mbali ina iye ndi amene anachititsa zimenezi?
Taganizani mavuto ndi kuzunzika zimene Yosefe ndi Davide anapirira zaka zambiri zonsezo. Mwa kupenda mmene iwo anachitira ndi mavuto awo, tingaphunzirepo mfundo zabwino. Tiyeni tikambirane mfundo zitatu zimene tikuphunzira pa chitsanzo cha amuna ameneŵa.
Musasunge Chakukhosi ndi Mkwiyo
Choyamba, amuna okhulupirika ameneŵa sanafune kusunga mkwiyo ndi chakukhosi. Pamene Yosefe anali mkaidi, zikanakhala zosavuta kwa iye kukhala wokwiya chifukwa cha abale ake amene anam’pereka, mwina kukonza za mmene akanawakhaulitsira abale akewo akanakumana nawonso. Koma tikudziŵa bwanji kuti Yosefe analibe maganizo oipa ngati amenewo? Taonani zimene iye anachita atakhala ndi mpata wokhaulitsa abale ake amene anabwera ku Igupto kudzagula tirigu. Nkhaniyo imati: ‘[Yosefe] analira . . . Ndipo Yosefe analamulira kuti [antchito ake] adzaze zotengera zawo [za abale ake] ndi tirigu, ndi kubweza ndalama zawo, aliyense m’thumba mwake, ndi kuwapatsa phoso la panjira.’ Nthaŵi ina pamene anatuma abale ake kukatenga atate wawo ndi kubwera nawo ku Igupto, Yosefe anawalimbikitsa ndi mawu akuti: “Musakangane panjira.” Mwa zimene analankhula ndi kuchita, Yosefe anaonetsa kuti sanalole mkwiyo kapena kusunga chakukhosi kulamulira moyo wake.—Genesis 42:24, 25; 45:24.
Davide nayenso sanasungire Mfumu Sauli chakukhosi. Kaŵiri konse Davide anali ndi mpata wa kupha Sauli. Koma pamene anyamata ake anam’sonkhezera kutero, Davide anati: “Mulungu andiletse kuchitira ichi mbuye wanga, wodzozedwa wa Yehova, kum’samulira dzanja langa, popeza iye ndiye wodzozedwa wa Yehova.” Davide anasiya nkhaniyo m’manja mwa Yehova, ndipo anauza anyamata akewo kuti: “Pali Yehova, Yehova adzam’kantha iye; kapena tsiku la imfa yake lidzafika; kapena adzatsikira kunkhondo, nadzafako.” Nthaŵi ina, Sauli ndi mwana wake Jonatani atamwalira, Davide mpaka anapeka nyimbo ya maliro, kudandaula za imfa yawo. Mofanana ndi Yosefe, Davide sanasunge chakukhosi.—1 Samueli 24:3-6; 26:7-13; 2 Samueli 1:17-27.
Kodi timasunga chakukhosi ndi mkwiyo tikapwetekedwa chifukwa cha kupanda chilungamo kwa ena? Zimenezi zingathe kuchitika mosavuta. Ngati tilola mtima wathu kutilamulira, zotsatira zake zingakhale zowononga kuposa kusoŵa chilungamo kumene anatichitirako. (Aefeso 4:26, 27) Ngakhale kuti tingakhale ndi mphamvu pang’ono kapena tingakhale tilibe mphamvu zoletsa zimene ena angachite, tili ndi mphamvu zolamulira mmene ife tingachitire ngati ena sanatichitire chilungamo. Ngati tili ndi chikhulupiriro chakuti Yehova panthaŵi yake adzasamalira nkhaniyo, sizivuta kusasunga chakukhosi ndi mkwiyo.—Aroma 12:17-19.
Chitani Zimene Mungathe Ngakhale Muli Pamavuto
Mfundo yachiŵiri imene tingaphunzirepo n’njakuti tisalole mavuto athu kutilepheretsa kuchita zimene tingathe. Tingamavutike chifukwa chongoganizira zimene sitingathe kuchita mpaka kuiŵala zimene tingathe kuchita. Zikatero ndiye kuti mavuto athuwo ayamba kutilamulira. Zoterezi zikanam’chitikira Yosefe. Koma iye anasankha kuchita zimene akanatha ngakhale anali pamavuto. Ali kapolo, Yosefe “anapeza ufulu pamaso [pa mbuye wake], ndipo anam’tumikira iye; ndipo anamuyesa iye woyang’anira pa nyumba yake.” Ali mkaidi, Yosefe anachita chimodzimodzi. Chifukwa chakuti Yehova anadalitsa Yosefe ndiponso Yosefeyo anali wakhama, “woyang’anira kaidi anapereka m’manja a Yosefe akaidi onse okhala m’kaidimo, ndipo zonse iwo anazichita mmenemo, iye ndiye wozichita.”—Genesis 39:4, 21-23.
Zaka zimene Davide anali kuthaŵathaŵa, iyenso anachita zimene akanatha ngakhale anali pamavuto. Pamene anali kukhala m’chipululu cha Parana, iye ndi anyamata ake anateteza nkhosa za Nabala kwa achifwamba. Wina mwa abusa a Nabala anati: “Iwo anatikhalira ngati linga usana ndi usiku, nthaŵi yonse tinali nawo ndi kusunga nkhosazo.” (1 Samueli 25:16) Nthaŵi ina, akukhala ku Zikilaga, Davide analanda midzi imene munali adani a Israyeli kumwera, ndipo anawonjezera malire a Yuda.—1 Samueli 27:8; 1 Mbiri 12:20-22.
Kodi tikufunika khama kuti tichite zimene tingathe ngakhale tili pamavuto? N’zoona kuti zingativute kuchita zimenezo, koma tingapambane. Mtumwi Paulo ataganiza za moyo wake analemba kuti: “Ndaphunzira ine, kuti zindikwanire zilizonse ndili nazo. . . . Konseko ndi m’zinthu zonse ndaloŵa mwambo wakukhuta, ndiponso wakumva njala; wakusefukira, ndiponso wakusoŵa.” Kodi Paulo anatha bwanji kuona moyo mwa njira imeneyi? Chifukwa chakuti iye anapitiriza kudalira Yehova. Iye anavomereza kuti: “Ndikhoza zonse mwa Iye wondipatsa mphamvuyo.”—Afilipi 4:11-13.
Dikirani Yehova
Mfundo yachitatu imene tikuphunzirapo n’njakuti tiyenera kudikira Yehova m’malo mogwiritsa ntchito njira zosemphana ndi Malemba kuti tithetse mavuto athu. Wophunzira Yakobo analemba kuti: “Chipiriro chikhale nayo ntchito yake yangwiro, kuti mukakhale angwiro ndi opanda chilema, osasoŵa kanthu konse.” (Yakobo 1:4) Tiyenera kulola chipiriro ‘kukhala nayo ntchito yake yangwiro’ mwa kulola chiyeso kupitirira mpaka chonse chitatha popanda kutsatira njira zosemphana ndi Malemba kuti chiyesocho chithe msanga. Tikalola chiyesocho kupitirira, ndiye kuti chikhulupiriro chathu chidzayesedwa ndi kuyengedwa, ndipo mphamvu yake yolimbitsa munthu idzaonekera. Ndi mmene kupirira kwa Yosefe ndi Davide kunalili. Iwo sanayese kupeza njira zawozawo zothetsera mavuto awo zoti Yehova sakanakondwera nazo. Koma anayesetsa kuchita zimene akanatha ngakhale anali pamavuto. Iwo anadikira Yehova, ndipo analandira madalitso aakulu. Yehova anawagwiritsa ntchito onse aŵiri kulanditsa ndi kutsogolera anthu ake.—Genesis 41:39-41; 45:5; 2 Samueli 5:4, 5.
Ifenso tingakumane ndi mavuto amene angatiyese kuchita zinthu zosemphana ndi Malemba pofuna kuwathetsa. Mwachitsanzo, kodi ndinu wokhumudwa chifukwa chakuti simunapezebe munthu woyenera kumanga naye banja? Ngati limeneli ndi vuto lanu, musayese ngakhale pang’ono kuswa lamulo la Yehova la kukwatira “mwa Ambuye.” (1 Akorinto 7:39) Kodi ukwati wanu uli pamavuto? M’malo motengera mzimu wa dziko umene umalimbikitsa anthu kupatukana ndi kusudzulana, yesetsani kuthandizana kuthetsa mavuto anuwo. (Malaki 2:16; Aefeso 5:21-33) Kodi zikukuvutani kusamalira banja lanu chifukwa cha vuto la zachuma? Kudikira Yehova kumatanthauzanso kuti mupeŵe kuchita ntchito zokayikitsa kapena zosaloleka pofuna kuti mupeze ndalama. (Salmo 37:25; Ahebri 13:18) Inde, tonsefe tiyenera kulimbikira kuchita zimene tingathe ngakhale tili pamavuto kuti Yehova apeze potidalitsira. Pamene tikutero, tisasiye kudikira Yehova kuti apereke njira yabwino yothetsera mavuto athuwo.—Mika 7:7.
Yehova Adzakuthandizani
Kusinkhasinkha mmene anthu a m’Baibulo ngati Yosefe ndi Davide analimbanirana ndi zokhumudwitsa ndi mavuto ena kungatithandize kwambiri. Ngakhale kuti nkhani zawo zikufotokozedwa m’masamba angapo m’Baibulomo, ziyeso zawo zinachitika zaka zambiri. Ndiye tadzifunsani kuti: ‘Kodi atumiki a Mulungu ngati ameneŵa anatha bwanji kupirira mavuto awo? Zinatheka bwanji kuti anakhalabe osangalala? Kodi anafunika kukhala ndi makhalidwe otani?’
Ndi bwinonso kuganiza za kupirira kwa atumiki a Yehova a masiku ano. (1 Petro 5:9) Chaka chilichonse magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! amakhala ndi nkhani zambiri za moyo wa anthu osiyanasiyana. Kodi mumaŵerenga ndi kusinkhasinkha zitsanzo za Akristu okhulupirika ameneŵa? Komanso, m’mipingo mwathu muli anthu amene akupirira mavuto mokhulupirika. Kodi mumacheza nawo nthaŵi zonse ndi kuphunzira kwa iwo pamisonkhano ya mpingo?—Ahebri 10:24, 25.
Mukakumana ndi mavuto othetsa nzeru, dziŵani kuti Yehova amakusamalani ndipo adzakuthandizani. (1 Petro 5:6-10) Limbikirani kuti musalole mavuto anu kulamulira moyo wanu. Tengerani chitsanzo cha Yosefe, Davide, ndi ena mwa kusasunga chakukhosi, mwa kuchita zimene mungathe ngakhale muli pamavuto, ndi mwa kudikira Yehova kuti apereke njira yabwino yothetsera mavutowo. Yandikirani kwa iye mwa kupemphera ndi kuchita zinthu zauzimu. Mukatero, mudzakhalabe osangalala ngakhale nthaŵi zovuta.—Salmo 34:8.
[Chithunzi pamasamba 20, 21]
Yosefe anayesetsa kuchita zimene akanatha ngakhale anali pamavuto
[Chithunzi patsamba 23]
Davide anadikira Yehova kuti athetse mavuto ake