Kodi Muli ndi Chifukwa Chomveka Choyembekezera Paradaiso?
‘Ndidziŵa munthu wa mwa Kristu . . . amene anakwatulidwa kumka ku Paradaiso.’—2 AKORINTO 12:2-4.
1. Kodi ndi malonjezo ati a m’Baibulo amene anthu ambiri amasangalala nawo?
PARADAISO. Kodi mukukumbukira mmene munamvera mutangodziŵa kumene za lonjezo la Mulungu la paradaiso wa padziko lapansi? Mwina mukukumbukira nthaŵi imene munamva kuti ‘maso a akhungu adzatsegulidwa, makutu a ogontha adzatsegulidwa, ndiponso kuti chipululu chidzatulutsa’ zinthu zokongola. Nanga munamva bwanji mutauzidwa za ulosi wakuti mmbulu udzakhala pamodzi ndi mwana wa nkhosa ndipo mwana wa mbuzi adzakhala pamodzi ndi nyalugwe? Kodi simunasangalale kuŵerenga kuti anthu amene munali kuwakonda omwe anamwalira adzaukitsidwa kuti akhale m’Paradaiso ameneyo?—Yesaya 11:6; 35:5, 6; Yohane 5:28, 29.
2, 3. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti pali zifukwa zomveka zoti muziyembekezera zimene Baibulo limalonjeza? (b) Kodi tili ndi chifukwa chinanso chiti chokhalira ndi chiyembekezo?
2 Chiyembekezo muli nachochi n’chomveka. Muli ndi zifukwa zomveka zokhulupirira malonjezo a Baibulo okhudza Paradaiso ameneyu. Mwachitsanzo, mumakhulupirira zimene Yesu anauza munthu wochita zoipa amene anapachikidwa uja, zoti: “Udzakhala ndi ine m’Paradaiso.” (Luka 23:43) Mumakhulupirira lonjezo lakuti: “Monga mwa lonjezano lake tiyembekezera miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano mmenemo mukhalitsa chilungamo.” Mumakhulupiriranso lonjezo lakuti Mulungu adzapukuta misozi yonse; sikudzakhalanso imfa, chisoni, kulira, ndi zowawa. Izi zikutanthauza kuti padziko lapansi pano padzakhalanso paradaiso.—2 Petro 3:13; Chivumbulutso 21:4.
3 Koma pali chifukwa chinanso choyembekezera Paradaiso ameneyu. Chifukwa chake n’chakuti Akristu padziko lonse ali mbali ya chinthu chinachake. Kodi chinthu chake n’chiyani? Mulungu wakonza paradaiso wauzimu amene waloŵetsamo anthu ake. Mawu akuti “paradaiso wauzimu” angaoneke ngati ovuta kuwamvetsa, koma paradaiso ameneyu anatchulidwa kalekale muulosi, ndipo ndi weniwenidi.
Masomphenya a Paradaiso
4. Kodi 2 Akorinto 12:2-4 amafotokoza za masomphenya otani, ndipo n’zachionekere kuti ndani anaona zimenezi?
4 Pankhani yokhudza paradaiso wauzimuyu, onani zimene mtumwi Paulo analemba: ‘Ndidziŵa munthu wa mwa Kristu . . . amene anakwatulidwa wotereyo kumka naye Kumwamba kwachitatu. Ndipo ndidziŵa munthu wotereyo (ngati m’thupi, ngati wopanda thupi, sindidziŵa; adziŵa Mulungu), kuti anakwatulidwa kumka ku Paradaiso, namva maneno osatheka kuneneka, amene saloleka kwa munthu kulankhula.’ (2 Akorinto 12:2-4) Paulo analemba izi atangotha kufotokoza mfundo zosonyeza kuti iyeyo ndi woyeneretsedwa kukhala mtumwi. Chinanso, Baibulo silinena za munthu winanso amene anaonapo zoterezi, ndipo ndi Paulo amene akutiuza za zinthu zimenezi. Motero, n’zachionekere kuti ndi Paulo yemweyo amene anaona masomphenya ameneŵa. Kodi, panthaŵi imene Yehova ankamuonetsa masomphenyaŵa, Paulo analoŵa ‘m’Paradaiso’ wotani?—2 Akorinto 11:5, 23-31.
5. Kodi Paulo sanaone chiyani, motero ndi “Paradaiso” wotani amene anaona?
5 Nkhani yomwe mukupezeka lembali sisonyeza kuti “Kumwamba kwachitatu” komwe anatchulaku ndi dziko lina osati dziko lapansi lino kapena kuti ndi malo enaake m’mlengalengamu. Nthaŵi zambiri Baibulo likatchula zinthu zitatu limakhala likusonyeza kugogomezera. (Mlaliki 4:12; Yesaya 6:3; Mateyu 26:34, 75; Chivumbulutso 4:8) Motero, zimene Paulo anaona m’masomphenyaŵa ndi zinthu zinazake zauzimu zokwezeka kapena kuti zapamwamba kwambiri.
6. Kodi ndi zinthu ziti zomwe zinachitika m’mbiri, zimene zikutithandiza kumvetsa bwino zimene Paulo anaona?
6 Maulosi amene Baibulo linafotokoza Paulo asanaone masomphenyaŵa amatithandiza kuimvetsetsa bwino nkhaniyi. Mtundu wakale wa Mulungu utalephera kukhala wokhulupirika kwa iye, Mulunguyo analola kuti Ababulo amenye nkhondo ndi Yuda ndiponso Yerusalemu. Mapeto ake, mbiri ya Baibulo imasonyeza kuti mtundu wa Yuda ndiponso mzinda wa Yerusalemu zinawonongedwa m’chaka cha 607 Kristu Asanabwere. Ulosi unanena kuti dzikoli lidzakhala labwinja zaka 70; kenako Mulungu adzalola Ayuda olapa kuti abwerere kwawo ndi kukayambiranso kulambira koona. Izi zinachitika kuyambira m’chaka cha 537 Kristu Asanabwere. (Deuteronomo 28:15, 62-68; 2 Mafumu 21:10-15; 24:12-16; 25:1-4; Yeremiya 29:10-14) Komano, kodi n’chiyani chimene chinachitikira dziko lenilenilo? M’zaka 70 zimenezo, dzikolo linamera thengo, madera ena n’kukhala ouma ndipo kunayamba kukhala nkhandwe. (Yeremiya 4:26; 10:22) Komabe panali lonjezo ili lakuti: “Yehova watonthoza mtima wa Ziyoni, watonthoza mtima wa malo ake onse abwinja; ndipo wasandutsa chipululu chake ngati Edene, ndi nkhwangwara yake ngati munda [kapena kuti Paradaiso] wa Yehova.”—Yesaya 51:3.
7. Kodi n’chiyani chinadzachitika zitatha zaka 70 zija zomwe dziko linakhala bwinja?
7 Izi zinachitika zaka 70 zija zitatha. Zinthu zinayamba kukhala bwino chifukwa cha madalitso a Mulungu. Tapangani chithunzithunzi cha zinthu izi m’maganizo mwanu: “Chipululu ndi malo ouma adzakondwa; ndipo dziko loti se lidzasangalala ndi kuphuka ngati duŵa. Lidzaphuka mochuluka ndi kusangalala, ngakhale kukondwa ndi kuyimba; . . . wopunduka adzatumpha ngati nswala, ndi lilime la wosalankhula lidzayimba; pakuti m’chipululu madzi adzatuluka, ndi mitsinje m’dziko loti se. Ndipo mchenga wong’azimira udzasanduka thamanda, ndi nthaka yopanda madzi idzasanduka zitsime zamadzi; m’malo a ankhandwe mmene iwo anagona, mudzakhala udzu ndi mabango ndi milulu.”—Yesaya 35:1-7.
Anthu Obwezeretsedwa ndi Osinthidwa
8. Kodi tikudziŵa bwanji kuti chaputala 35 cha Yesaya chimanena za anthu?
8 Apatu dziko linasintha kwambiri. Linachoka pa bwinja n’kusanduka paradaiso. Komatu, ulosi umenewu ndiponso maulosi ena odalirika ankasonyeza kuti anthunso adzasintha, mofanana ndi kusintha kwa dziko labwinja kukhala dziko lachonde. N’chifukwa chiyani tinganene choncho? Yesaya anali kunena za “owomboledwa a Yehova,” amene anabwerera kudziko lawo “alikuyimba,” n’kukhala ‘osekerera ndi okondwa.’ (Yesaya 35:10) Izi zinachitikira anthu, osati dziko lenilenilo ayi. Komanso, panthaŵi ina Yesaya ananeneratu za kubwezeretsedwa kwa anthu ku Ziyoni. Anati: “Iwo atchedwe mitengo ya chilungamo yakuioka Yehova . . . Pakuti monga dziko liphukitsa mphundu zake . . . Yehova adzaphukitsa chilungamo ndi matamando pamaso pa amitundu onse.” Yesaya ananenanso izi zokhudza anthu a Mulungu: “Yehova adzakutsogolera posalekayi . . . , ndi kulimbitsa mafupa ako; ndipo udzafanana ndi munda wothirira madzi.” (Yesaya 58:11; 61:3, 11; Yeremiya 31:10-12) Motero, mofanana ndi kusintha kwa dziko lenilenilo, nawonso Ayuda obwezeretsedwa anasintha.
9. Kodi Paulo anaona “Paradaiso” wotani, ndipo kodi anakwaniritsidwa liti?
9 Zimene zinachitika kalekalezi zikutithandiza kumvetsa zimene Paulo anaona m’masomphenya aja. Zimene anaonazo zinali zokhudza mpingo wachikristu, umene anautcha kuti “chilimo cha Mulungu” ndipo munda umenewu unadzakhala wachonde kwambiri. (1 Akorinto 3:9) Kodi masomphenyaŵa anadzakwaniritsidwa liti? Paulo ananena kuti zimene anaonazo zinali ‘vumbulutso,’ kutanthauza kuti zinali zinthu zodzachitika m’tsogolo. Iye ankadziŵa kuti akadzamwalira kudzakhala mpatuko waukulu kwambiri. (2 Akorinto 12:1; Machitidwe 20:29, 30; 2 Atesalonika 2:3, 7) Panthaŵi imene anthu ampatukowo anali ndi mphamvu kwambiri kuposa Akristu oona kunali kosatheka kuyerekezera Akristu oonawo ndi munda wachonde. Komabe, nthaŵi yoti kulambira koona kudzayambenso inali m’tsogolo. Anthu a Mulungu anadzabwezeretsedwa kuti ‘olungama aŵale monga dzuŵa, mu Ufumu wa Atate wawo.’ (Mateyu 13:24-30, 36-43) Izi zinachitika patatha zaka zochepa Ufumu wa Mulungu utakhazikitsidwa kumwamba. Ndipo chikhazikitsidwire Ufumuwo, zakhala zoonekeratu kuti anthu a Mulungu akukhala m’paradaiso wauzimu amene Paulo anaona m’masomphenya aja.
10, 11. N’chifukwa chiyani tinganene kuti tili m’paradaiso wauzimu ngakhale kuti ndife opanda ungwiro?
10 Inde, tikudziŵa kuti ifeyo patokhapatokha ndife opanda ungwiro, motero sitidabwa kuti timakhala ndi mavuto, monganso mmene zinkachitikira ndi Akristu a m’nthaŵi ya Paulo. (1 Akorinto 1:10-13; Afilipi 4:2, 3; 2 Atesalonika 3:6-14) Komabe taganizirani za paradaiso wauzimu amene tilimo panopa. Tikayerekezera mmene tinalili, panopa tinachiritsidwa mwauzimu. Ndipo tasiyanitsani njala yomwe tinali nayo kale ndi mmene tikudyera bwino mwauzimu tsopano. M’malo mokhala mozunzika ngati kuti ali m’dziko louma mwauzimu, anthu a Mulungu ndi oyanjidwa naye ndipo amalandira madalitso ake ankhaninkhani. (Yesaya 35:1, 7) M’malo mokhala akhungu mumdima wandiweyani wauzimu, timaona kuŵala komwe kumatipatsa mtendere ndiponso kumatithandiza kuti tiyanjane ndi Mulungu. Anthu ambiri amene kale anali asanawamvetsepo bwinobwino maulosi a m’Baibulo, tsopano akumva bwinobwino zimene Malemba amanena. (Yesaya 35:5) Mwachitsanzo, Mboni za Yehova zambirimbiri padziko lonse zinaphunzira vesi lililonse la ulosi wa Danieli. Kenako zinaphunzira mwakuya chaputala chilichonse cha buku la m’Baibulo la Yesaya. Kodi chakudya chotsitsimutsa chauzimu chimenechi sichitipatsa umboni woti tikukhala m’paradaiso wauzimu?
11 Taganiziraninso za kusintha kwa makhalidwe a anthu osiyanasiyana oona mitima amene ayesetsa kumvetsa ndi kutsatira Mawu a Mulungu pamoyo wawo. Kwenikweni, anthu ameneŵa ayesetsa kuvula makhalidwe auchinyama amene anali nawo poyamba. Mwina inu mwachita zimenezi ndipo mwasintha kwambiri, ndipotu nawonso abale ndi alongo anu auzimu achita chimodzimodzi. (Akolose 3:8-14) Motero, mukamasonkhana ndi mpingo wa Mboni za Yehova, ndiye kuti mumakhala ndi anthu amene tsopano amakonda mtendere ndiponso ndi anthu osangalatsa kukhala nawo. Sikuti anthu ameneŵa ndi angwiro, koma sitinganene kuti iwo ali ngati mikango yoopsa kapena zilombo zolusa zakuthengo. (Yesaya 35:9) Kodi kukhala pamodzi mwabata ndi mwamtendere kumeneku kukusonyeza chiyani? N’zoonekeratu kuti tili m’malo auzimu amene sitingalakwitse titanena kuti ndi paradaiso wauzimu. Ndipo paradaiso wathu wauzimu akusonyeza mmene zinthu zidzakhalire m’paradaiso wa padziko lapansi pano amene tidzakhalemo tikapitiriza kukhala okhulupirika kwa Mulungu.
12, 13. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tipitirize kukhala m’paradaiso wathu wauzimu?
12 Komabe pali chinthu china chimene sitiyenera kuchinyalanyaza. Mulungu anauza Aisrayeli kuti: “Muzisunga malamulo onseŵa ndikuuzani lerolino, kuti mukhale amphamvu, ndi kuloŵa ndi kulandira dziko.” (Deuteronomo 11:8) Dziko lomweli linatchulidwanso pa Levitiko 20:22, 24, kuti: “Muzisunga malemba anga onse, ndi maweruzo anga onse, kuwachita; lingakusanzeni inu dziko limene ndipita nanuko, kuti mukhale m’mwemo. Koma ndanena nanu, Mudzalandira dziko lawo inu, ndipo ine ndilipereka kwa inu likhale lanu, ndilo dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi.” Inde, kuti alandire Dziko Lolonjezedwa panafunika kuti Aisrayeli akhale paunansi wabwino ndi Yehova Mulungu. Mulungu analola Ababulo kumenyana ndi Aisrayeli ndi kuwachotsa m’dziko lawo chifukwa chakuti sanamumvere.
13 N’kutheka kuti tikusangalala ndi zinthu zambiri m’paradaiso wathu wauzimuyu. Ndi malo osangalatsa komanso otsitsimutsa kwambiri. Tikukhala mwamtendere ndi Akristu amene achita khama n’kusiya makhalidwe awo auchinyama. Akuyesetsa kuti akhale anthu okoma mtima ndiponso othandiza anzawo. Komabe, kungokhala paunansi wabwino ndi anthu ameneŵa sikokwanira kuti tipitirize kukhala m’paradaiso wathu wauzimuyu. Pakufunikanso kuti tikhale paunansi wabwino ndi Yehova ndi kuchita zofuna zake. (Mika 6:8) Tinafuna tokha kuloŵa m’paradaiso wauzimu ameneyu, koma n’zotheka kutulukamo kapena kuthamangitsidwamo, ngati sitikuchita khama kuti tipitirize kukhala paunansi wabwino ndi Mulungu.
14. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tikhale m’paradaiso wauzimu?
14 Mfundo yofunika kwambiri yomwe ingatithandize ndiyo kupitiriza kupeza mphamvu m’Mawu a Mulungu. Taonani mawu ophiphiritsa a pa Salmo 1:1-3: “Wodala munthuyo wosayenda mu uphungu wa oipa . . . Komatu m’chilamulo cha Yehova muli chikondwerero chake; ndipo m’chilamulo chake amalingirira usana ndi usiku. Ndiye akunga mtengo wooka pa mitsinje ya madzi; wakupatsa chipatso chake pa nyengo yake, tsamba lake lomwe losafota; ndipo zonse azichita apindula nazo.” Kuwonjezera apo, m’paradaiso wauzimuyu timalandira chakudya chauzimu kudzera m’mabuku ofotokoza za m’Baibulo ofalitsidwa ndi kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.—Mateyu 24:45-47.
Kulimbikitsa Chiyembekezo Chanu cha Paradaiso
15. N’chifukwa chiyani Mose sanathe kuloŵetsa Aisrayeli m’Dziko Lolonjezedwa, koma kodi anaona chiyani?
15 Taonaninso chinthu china chotithandiza kuona zomwe zidzachitike m’Paradaiso. Aisrayeli atayenda m’chipululu zaka 40, Mose anawatsogolera ku zigwa za Moabu, zomwe zili kum’maŵa kwa mtsinje wa Yordano. Chifukwa cha zinthu zina zolakwika zimene Mose anali atachita m’mbuyomo, Yehova sanafune kuti Mose awolotse Aisrayeliwo mtsinje wa Yordano. (Numeri 20:7-12; 27:12, 13) Mose anapempha Mulungu kuti: “Ndiwoloketu, ndilione dziko lokomali lili tsidya la Yordano.” Ngakhale kuti Mose sanakaloŵemo, atakwera paphiri la Pisiga ndi kuona zigawo zosiyanasiyana za dzikoli, iye mwachionekere anazindikira kuti linali ‘dziko lokoma.’ Kodi inuyo mukuganiza kuti dziko limeneli linali lotani?—Deuteronomo 3:25-27.
16, 17. (a) Kodi masiku ano Dziko Lolonjezedwa n’losiyana motani ndi mmene linalili kale? (b) Kodi n’chifukwa chiyani tingakhulupirire kuti panthaŵi ina Dziko Lolonjezedwa linali ngati paradaiso?
16 Ngati mungaganizire za derali malinga ndi mmene lilili panopa, mungaganize kuti linali dera louma la mchenga, la chipululu cha miyala, ndiponso lotentha kwambiri. Koma pali zifukwa zokhulupirira kuti derali m’nthaŵi za m’Baibulo linali losiyana kwambiri ndi mmene lilili panopa. M’magazini yakuti Scientific American, katswiri wa za madzi ndi nthaka, Dr. Walter C. Lowdermilk anafotokoza kuti dera la kumeneko “lawonongeka chifukwa choligwiritsa ntchito molakwika kwa zaka 1,000.” Katswiriyu analemba kuti: “Zochita za anthu, osati chilengedwe, n’zimene zapangitsa kuti dera lomwe linali lachondeli likhale ‘chipululu.’” Ndipotu, kufufuza kwake kunasonyeza kuti “dera limeneli kale linali ngati paradaiso wodyetserako ziŵeto.” Ndiye zikuonekeratu kuti anthu ndi amene awononga derali, limene kale linali “ngati paradaiso wodyetserako ziŵeto.”a
17 Mukaganizira zimene mwakhala mukuŵerenga m’Baibulo, mukhoza kuona kuti mfundo imeneyi ndi yomveka kwambiri. Kumbukirani zimene Yehova anatsimikizira anthu kudzera mwa Mose, kuti: “Dziko limene mumukako kulilandira ndilo dziko la mapiri ndi zigwa; limamwa madzi a mvula ya kumwamba; ndilo dziko loti Yehova Mulungu wanu alisamalira.”—Deuteronomo 11:8-12.
18. Kodi lemba la Yesaya 35:2 liyenera kuti linawapatsa motani Aisrayeli chithunzithunzi cha mmene Dziko Lolonjezedwa lidzakhalire?
18 Dziko Lolonjezedwali linali lobiriŵira ndi lokongola kwambiri, komanso lachonde, moti kungotchulapo madera ena a dzikoli kunkakumbutsa anthu za malo onga paradaiso. Tikuona bwino zimenezi kuchokera pa ulosi wa mu chaputala 35 cha Yesaya. Ulosiwu unakwaniritsidwa koyamba pamene Aisrayeli anabwerera kuchoka ku Babulo. Yesaya analosera kuti: “Lidzaphuka mochuluka ndi kusangalala, ngakhale kukondwa ndi kuyimba; lidzapatsidwa ulemerero wa Lebano, ndi ukulu wa Karimeli ndi Saroni; anthuwo adzaona ulemerero wa Yehova, ukulu wake wa Mulungu wathu.” (Yesaya 35:2) Kutchula Lebano, Karimeli, ndi Saroni kuyenera kuti kunapatsa Aisrayeli chithunzithunzi chosangalatsa kwambiri.
19, 20. (a) Fotokozani mmene dera la Saroni wakale linalili. (b) Kodi njira imodzi imene ingatithandize kuti tikhale ndi chiyembekezo champhamvu choti dzikoli lidzakhalanso Paradaiso ndi iti?
19 Tiyeni tiganizire za Saroni, chigwa chomwe chinkathera m’nyanja ndipo chinali pakati pa mapiri a Samariya ndi Nyanja Yaikulu, kapena kuti ya Mediterranean. (Onani chithunzi patsamba 10.) Chigwachi chinali chokongola kwambiri komanso chachonde. Popeza kuti chinkakhala ndi madzi okwanira bwino, chigwachi chinali chabwino kudyetserako ziŵeto, koma kumpoto kwa chigwachi kunali nkhalango zamitengo ikuluikulu kwambiri. (1 Mbiri 27:29; Nyimbo ya Solomo 2:1; Yesaya 65:10) Motero, Yesaya 35:2 anali kulosera za kubwezeretsedwa kwa zinthu ndiponso dziko labwino kwambiri, lokhala ngati ndi paradaiso. Ulosiwu unali kunenanso za paradaiso wauzimu wosangalatsa kwambiri, mogwirizana ndi zimene Paulo anadzaona m’masomphenya. Pomaliza, ulosi umenewu, ndiponso maulosi ena, amalimbikitsa chiyembekezo chathu cha paradaiso wa padziko lapansi mmene anthu adzakhalamo.
20 Pamene tili m’paradaiso wathu wauzimu, tingathe kuchita zinthu zoti zitithandize kuti tiziyamikira kwambiri paradaisoyu ndiponso zoti zitithandize kuti chiyembekezo chathu choti dziko lapansi lidzakhalanso Paradaiso chikhale champhamvu. Kodi tingachite zimenezi motani? Tingatero mwa kumvetsa bwino zinthu zimene timaŵerenga m’Baibulo. Zimene Baibulo limafotokoza ndiponso maulosi amene lili nawo nthaŵi zambiri amatchula malo enaake. Kodi mukufuna kumvetsa kumene kunali malo ameneŵa ndiponso kuti anali kugwirizana motani ndi malo enanso? M’nkhani yotsatirayi, tiona mmene mungachitire zimenezi m’njira yopindulitsa.
[Mawu a M’munsi]
a Denis Baly, m’buku lina lofotokoza za madera otchulidwa m’Baibulo lakuti The Geography of the Bible, anati: “Chilengedwe chiyenera kuti chasintha kwambiri kusiyana ndi mmene chinalili m’nthaŵi za m’Baibulo.” Kodi chachititsa zimenezi n’chiyani? “Anthu ankafuna mitengo ya nkhuni ndiponso milimo motero . . . anayamba kugwetsa mitengo, zimene zinachititsa kuti deralo likhale pambalambanda ndipo liyambe kuwonongeka chifukwa cha nyengo yoipa. Kuloŵerera chilengedwe kwamtunduwu kwachititsa kuti . . . derali liwonongeke pang’ono ndi pang’ono chifukwa cha nyengo yake.”
Kodi Mukukumbukira?
• Kodi mtumwi Paulo anaona “Paradaiso” uti m’masomphenya?
• Kodi zimene zinafotokozedwa mu Yesaya chaputala 35 zinakwaniritsidwa liti koyamba, ndipo kodi zikugwirizana motani ndi zimene Paulo anaona m’masomphenya?
• Kodi tingatani kuti tiziyamikira kwambiri paradaiso wathu wauzimu ndiponso kuti chiyembekezo chathu cha paradaiso wa padziko lapansi chikhale cholimba?
[Chithunzi patsamba 10]
Chigwa cha Saroni, dera limene linali lachonde kwambiri m’Dziko Lolonjezedwa
[Mawu a Chithunzi]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.
[Chithunzi patsamba 12]
Mose anazindikira kuti linali ‘dziko lokoma’