Phunzirani Kuchokera ku Choonadi cha M’chilamulo
“[Ndinu omvetsa] zinthu zofunika kuzidziwa ndi choonadi zopezeka m’Chila mulo.”—AROMA 2:20.
1. N’chifukwa chiyani tifunika kumvetsa zimene Paulo ananena zokhudza Chilamulo cha Mose?
ZIMENE Paulo analemba m’Baibulo zimatithandiza kumvetsa kufunika kwa mbali zosiyanasiyana za Chilamulo cha Mose. Mwachitsanzo, m’kalata yake yopita kwa Aheberi iye ananena kuti Yesu ndi ‘mkulu wa ansembe wokhulupirika’ amene anapereka “nsembe yophimba machimo” kamodzi kokha. Anthu amene amakhulupirira nsembeyi akhoza kukhala pa mtendere ndi Mulungu ndiponso akhoza ‘kulanditsidwa kwamuyaya.’ (Aheb. 2:17; 9:11, 12) Paulo ananena kuti chihema chinali “mthunzi wa zinthu zakumwamba” ndiponso kuti Yesu anali Mkhalapakati wa “pangano labwino koposa” losiyana ndi limene Mose anali Mkhalapakati wake. (Aheb. 7:22; 8:1-5) M’nthawi ya Paulo, nkhani zokhudza Chilamulo zinali zofunika kwambiri kwa Akhristu ndipo ndi zofunikabe masiku ano. Zimatithandiza kumvetsa bwino kufunika kwa zimene Mulungu watipatsa.
2. Kodi Akhristu achiyuda anali ndi mwayi wotani kusiyana ndi anthu a mitundu ina?
2 Zina zimene Paulo ananena polembera kalata Akhristu a ku Roma, kwenikweni zinali zokhudza Akhristu a mumpingowo amene anali Ayuda. Akhristu amenewa ankadziwa bwino Chilamulo cha Mose. Iye ananena kuti iwo ‘amamvetsa zinthu zofunika kuzidziwa ndi choonadi’ chonena za Yehova ndiponso mfundo zake zolungama chifukwa chakuti ankadziwa Chilamulo chimene Mulungu anapereka. Iwo ankamvetsa choonadi cha m’Chilamulo ndipo ankachikonda. Choncho mofanana ndi Ayuda amene anakhalapo kalelo, iwo akanatha kuphunzitsa anthu ena mfundo za choonadi chokhudza Yehova.—Werengani Aroma 2:17-20.
ZIMENE ZINKACHITIRA CHITHUNZI NSEMBE YA YESU
3. Kodi kuphunzira za nsembe zimene Ayuda ankapereka kungatithandize bwanji?
3 Mfundo za choonadi za m’Chilamulo zimene Paulo anatchula ndi zofunikanso kwa ife kuti timvetse zolinga za Yehova. Mfundo zazikulu zimene zili m’Chilamulo cha Mose n’zofunikabe masiku ano. Choncho tiyeni tione mbali imodzi ya Chilamulocho. Tione mmene zopereka zosiyanasiyana zinathandizira Ayuda odzichepetsa kumvetsa chifukwa chake ankafunika Khristu ndiponso zimene Mulungu ankafuna kuti iwo azichita. Ndiye popeza kuti zinthu zikuluzikulu zimene Yehova amafuna kwa atumiki ake sizisintha, malamulo amene Mulungu anapereka kwa Aisiraeli onena za nsembe ndi zopereka angatithandize kuona mmene tingachitire utumiki wathu wopatulika.—Mal. 3:6.
4, 5. (a) Kodi Chilamulo cha Mose chinkawakumbutsa chiyani anthu a Mulungu? (b) Kodi nsembe zimene Aisiraeli ankapereka zinkaimira chiyani?
4 Mfundo zambiri za m’Chilamulo cha Mose zinkakumbutsa Ayuda kuti ndi ochimwa. Mwachitsanzo, ngati wina wakhudza mtembo wa munthu ankafunika kuchita mwambo woti adziyeretse. Pa mwambowu, ng’ombe yaikazi yofiira imene inali yathanzi inkaphedwa n’kuitentha. Ndiye phulusa lakelo ankalithira “m’madzi oyeretsera” amene ankamuwaza munthu wofunika kuyeretsedwayo pa tsiku lachitatu ndi la 7 kuchokera pamene anadetsedwa. (Num. 19:1-13) Ndiponso kuti azikumbukira za uchimo umene anthu amabadwa nawo, mzimayi amene wabereka mwana ankakhala wodetsedwa kwa kanthawi kenako ankafunika kupereka nsembe yophimba machimo.—Lev. 12:1-8.
5 Nsembe za nyama zinali zofunika pa zochitika zosiyanasiyana kuti aphimbe machimo awo. Kaya iwo ankadziwa kapena ayi, nsembe zimenezi kuphatikizapo nsembe zonse zimene zinkaperekedwa kukachisi, zinali “mthunzi” chabe wa nsembe yangwiro imene Yesu anapereka.—Aheb. 10:1-10.
ZOLINGA ZABWINO N’ZOFUNIKA POPEREKA NSEMBE
6, 7. (a) Kodi n’chiyani chinkathandiza Aisiraeli posankha zinthu zoyenera kupereka nsembe ndipo kodi zimenezi zinkaimira chiyani? (b) Kodi tiyenera kudzifunsa mafunso ati?
6 Nyama iliyonse imene inkaperekedwa nsembe inkafunika kukhala “yopanda chilema.” Apa ankatanthauza kuti isakhale yakhungu, yovulala, yolemala kapena yodwala. (Lev. 22:20-22) Popereka nsembe ya zipatso kapena ya mbewu, ankayenera kuonetsetsa kuti zikhale “zipatso zoyambirira,” kapena kuti “zabwino koposa.” (Num. 18:12, 29) Zinthu zosaoneka bwino sizinali zoyenera kuperekedwa kwa Yehova. Nsembe zanyama zabwino kwambiri zimene Aisiraeli ankayenera kupereka, zinkaimira nsembe ya Yesu yomwe inali yopanda mawanga kapena chilema. Lamuloli linkasonyezanso kuti Yehova adzapereka nsembe yabwino koposa ndiponso yamtengo wapatali kwambiri pofuna kupulumutsa anthu ku uchimo ndi imfa.—1 Pet. 1:18, 19.
7 Posonyeza kuyamikira pa zabwino zonse zimene Yehova akumuchitira, munthu wopereka nsembeyo ankasankha kupereka nsembe yabwino koposa. Unali udindo wa aliyense kusankha nyama kapena mbewu zimene ankafuna kupereka nsembe. Komabe ankadziwa kuti Mulungu sangasangalale ndi nsembe yolemala. Kupereka nsembe zotero kukanangosonyeza kuti munthuyo akuchita zinthu mwamwambo chabe ndiponso akuona kuti lamulo lopereka nsembe ndi lolemetsa. (Werengani Malaki 1:6-8, 13.) Zimenezi ziyenera kutithandiza kuona mmene tikuchitira utumiki wathu. Tiyenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimatumikira Yehova ndi mtima wotani komanso zolinga zotani? Kodi ndiyenera kusintha zinthu zina? Kodi ndikumupatsa zinthu zamtengo wapatali?’
8, 9. N’chifukwa chiyani tiyenera kuganizira mtima umene Aisiraeli ankakhala nawo popereka nsembe?
8 Nthawi zina munthu wachiisiraeli ankasankha kupereka nsembe yaufulu posonyeza kuyamikira Yehova. Kapena ankasankha kupereka nsembe yopsereza imene inali yaufulu pofuna kuti asangalatse Yehova. Pa zochitika zimenezi iye sakanavutika kusankha nyama yabwino kwambiri. Masiku ano, Akhristu sapereka nsembe za nyama zimene zinatchulidwa m’Chilamulo cha Mose. Komabe iwo amapereka nsembe pogwiritsa ntchito nthawi, mphamvu ndiponso chuma chawo kuti atumikire Yehova. Mtumwi Paulo ananena kuti pamene ‘tikulengeza’ chikhulupiriro chathu ndiponso “kuchita zabwino ndi kugawana zinthu ndi ena” timakhala tikupereka nsembe zimene Mulungu amakondwera nazo. (Aheb. 13:15, 16) Mtima umene anthu a Yehova amakhala nawo pochita zinthu zimenezi umasonyeza ngati amayamikira kwambiri zinthu zonse zimene Mulungu wawapatsa. Choncho mofanana ndi Aisiraeli, tiyenera kuonanso mtima umene tili nawo potumikira Mulungu ndiponso zolinga zimene timakhala nazo.
9 Pa nthawi ina, Chilamulo cha Mose chinkanena kuti Mwisiraeli amene wachimwa apereke nsembe yamachimo kapena nsembe ya kupalamula. Popeza nsembezi zinkafunika, kodi mukuganiza kuti Mwisiraeli ankapereka monyinyirika? (Lev. 4:27, 28) Ayi. Sakanatero ngati ankafunadi kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova.
10. Kodi Akhristu ayenera kuchita chiyani kuti akonze ubwenzi umene wasokonezeka?
10 Masiku anonso mukhoza kuzindikira kuti mwina mosadziwa kapena mosaganiza bwino mwalakwira m’bale wanu. Chikumbumtima chanu chikhoza kukuuzani kuti mwalakwa. Izi zikachitika, munthu aliyense amene amaona kuti kutumikira Yehova n’kofunika adzayesetsa kukonza zinthu. Mwina angapepese munthuyo kuchokera pansi pa mtima ndipo ngati ndi tchimo lalikulu, akhoza kupempha thandizo kwa oyang’anira achikhristu. (Mat. 5:23, 24; Yak. 5:14, 15) Choncho munthu ayenera kuchitapo kanthu ngati walakwira m’bale wake kapena Mulungu ndipo zimene angachitezo zili ngati kupereka nsembe. Tikamapereka nsembe zoterezi timakonza ubwenzi wathu ndi Yehova komanso ndi abale athu komanso timakhala ndi chikumbumtima chabwino. Tikatero, timadziwa kuti kutsatira njira za Yehova n’kwabwino kwambiri.
11, 12. (a) Kodi nsembe zachiyanjano zinali chiyani? (b) Kodi tikuphunzira chiyani pa nsembe zachiyanjano?
11 Chilamulo cha Mose chinkanenanso kuti Aisiraeli azipereka nsembe zachiyanjano. Nsembezi zinkasonyeza kuti woperekayo anali pa mtendere ndi Yehova. Munthu wopereka nsembe imeneyi limodzi ndi banja lake ankadya nyama ya nsembeyo mwina m’chipinda china chodyera m’kachisi. Wansembe yemwe ankatsogolera popereka nsembe komanso ansembe ena amene anali kutumikira kukachisi ankapatsidwa mbali ina ya nyamayo. (Lev. 3:1; 7:31, 33) Munthu ankapereka nsembeyi n’cholinga choti akhale pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu. Zinali ngati kuti munthuyo, banja lake, ansembe ndiponso Yehova akudyera pamodzi mwamtendere.
12 Choncho kupereka nsembe yachiyanjano kunali ngati kuitana Yehova kuti adzadye nawo chakudya. Yehova akavomera, unkakhala mwayi waukulu kwambiri kwa Mwisiraeli amene wakonza chakudyacho. N’zosachita kufunsa kuti mlendo wolemekezeka ngati ameneyu ankamukonzera chakudya chabwino kwambiri. Nsembe zachiyanjano zinali mbali ya zinthu zofunika za choonadi cha m’Chilamulo. Zinkasonyeza kuti nsembe ya Yesu, yomwe ndi yaikulu koposa, idzapereka mwayi woti anthu onse akhale pa mtendere ndiponso ubwenzi wabwino ndi Mlengi wawo. Masiku anonso, tikhoza kukhala mabwenzi a Yehova ngati tipereka mofunitsitsa zinthu zathu ndiponso mphamvu zathu pomutumikira.
ZITSANZO ZA NSEMBE ZIMENE MULUNGU SANALANDIRE
13, 14. N’chifukwa chiyani Yehova sanasangalale ndi nsembe imene Mfumu Sauli inkafuna kupereka?
13 Kuti Yehova alandire nsembe, munthu woperekayo anayenera kukhala ndi mtima komanso zolinga zoyenera. Koma Baibulo limatiuzanso za nsembe zimene Mulungu sanalandire. N’chifukwa chiyani Mulungu anakana nsembezo? Tiyeni tione zitsanzo ziwiri.
14 Mneneri Samueli anauza Mfumu Sauli kuti nthawi yoti Yehova awononge Aamaleki yakwana. Choncho Sauli anafunika kuwononga adaniwo limodzi ndi ziweto zawo. Koma atawagonjetsa, Sauli anauza asilikali ake kuti asaphe Agagi yemwe anali mfumu ya Aamaleki. Iye sanaphenso nyama zabwino n’kumaganiza kuti akazipereke nsembe kwa Yehova. (1 Sam. 15:2, 3, 21) Kodi Yehova anatani? Iye anakana Sauli chifukwa chakuti sanamvere. (Werengani 1 Samueli 15:22, 23.) Kodi tikuphunzira chiyani pamenepa? Kuti Mulungu alandire nsembe, munthu woperekayo ayenera kumvera malamulo ake.
15. Kodi khalidwe loipa la Aisiraeli ena amene ankapereka nsembe nthawi ya Yesaya linasonyeza chiyani?
15 M’buku la Yesaya mulinso chitsanzo chofanana ndi chimenechi. Pa nthawiyo, Aisiraeli ankapereka nsembe kwa Yehova. Koma khalidwe lawo loipa linachititsa kuti nsembezo zikhale zosayenera. Yehova anawafunsa kuti: “Kodi nsembe zanu zambirimbirizo zili ndi phindu lanji kwa ine? Nsembe zopsereza zathunthu za nkhosa zamphongo ndiponso mafuta a nyama zodyetsedwa bwino zandikwana. Ine sindikusangalalanso ndi magazi a ana a ng’ombe amphongo, ana a nkhosa amphongo ndiponso a mbuzi zamphongo. . . . Musabweretsenso nsembe zina zaufa zopanda phindu. Zofukiza zanu ndikunyansidwa nazo.” Kodi vuto linali chiyani? Mulungu anawauza kuti: “Ngakhale mupereke mapemphero ambiri, ine sindimvetsera. Manja anu adzaza magazi amene mwakhetsa. Sambani, dziyeretseni. Chotsani zochita zanu zoipa pamaso panga. Lekani kuchita zoipa.”—Yes. 1:11-16.
16. N’chiyani chimachititsa kuti nsembe ikhale yovomerezeka kwa Mulungu?
16 Yehova sankasangalala ndi nsembe za anthu ochimwa amene sankalapa. Koma Mulungu ankayankha mapemphero a anthu amene ankayesetsa kutsatira malamulo ake ndipo iye ankalandira nsembe zawo. Mfundo za m’Chilamulo zinkawaphunzitsa kuti iwo ndi ochimwa ndipo afunika kukhululukidwa. (Agal. 3:19) Kuzindikira zimenezi kunawathandiza kuti azimva chisoni chifukwa cha machimo awo n’kumafuna kuti awakhululukire. Masiku anonso, tiyenera kuzindikira kuti tifunika nsembe ya Khristu imene ikhoza kuphimbadi machimo athu. Tikamazindikira zimenezi n’kumayamikira zimene Yehova watichitira, iye adzakondwera ndi zimene timapereka pomutumikira.—Werengani Salimo 51:17, 19.
KHULUPIRIRANI NSEMBE YA YESU
17-19. (a) Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira Yehova chifukwa chopereka Mwana wake nsembe? (b) Kodi tidzakambirana chiyani m’nkhani yotsatira?
17 Aisiraeli ankangoona “mthunzi” wa zolinga za Yehova. Koma ife tikuona zenizeni. (Aheb. 10:1) Malamulo okhudza nsembe ankaphunzitsa Aisiraeli zinthu zimene zinkafunika kuti akhale pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu. Iwo ankafunika kukhala oyamikira, ofunitsitsa kumupatsa zinthu zabwino kwambiri ndiponso kuzindikira kuti akufunika kukhululukidwa. Masiku ano, Malemba Achigiriki amatithandiza kudziwa kuti Yehova adzagwiritsa ntchito nsembe ya dipo imene Yesu anapereka kuti achotseretu uchimo ndi imfa. Chifukwa cha nsembe imeneyi, Mulungu akhoza kutikhululukira machimo n’cholinga choti tikhale ndi chikumbumtima chabwino ngakhale panopa. Nsembe ya dipo imene Yesu anapereka ndi mphatso yamtengo wapatali yochokera kwa Yehova.—Agal. 3:13; Aheb. 9:9, 14.
18 Koma pali zinthu zinanso zimene tiyenera kuchita kuti tipindule ndi nsembe ya dipo. Paulo analemba kuti: “Chilamulo chakhala mtsogoleri wotifikitsa kwa Khristu, kuti tiyesedwe olungama chifukwa cha chikhulupiriro.” (Agal. 3:24) Ndipo zochita zathu n’zimene zimasonyeza kuti tili ndi chikhulupiriro. (Yak. 2:26) M’nthawi ya atumwi, Akhristu achiyuda ankadziwa choonadi chifukwa chakuti ankadziwa Chilamulo cha Mose. Ndiyeno Paulo anawalimbikitsa kuti azichita zinthu mogwirizana ndi zimene ankadziwazo. Zimenezi zikanathandiza kuti khalidwe lawo lizigwirizana ndi mfundo za choonadi zimene ankaphunzitsa.—Werengani Aroma 2:21-23.
19 Ngakhale kuti masiku ano Akhristu satsatira Chilamulo cha Mose, iwo amafunika kupereka nsembe zovomerezeka kwa Yehova. M’nkhani yotsatira tidzakambirana mmene tingachitire zimenezi.
[Mawu Otsindika patsamba 17]
Zinthu zikuluzikulu zimene Yehova amafuna kwa atumiki ake sizisintha
[Chithunzi patsamba 18]
Kodi ndi nyama iti imene inuyo mukanapereka nsembe kwa Yehova?
[Chithunzi patsamba 19]
Yehova amasangalala ndi anthu amene amapereka nsembe zovomerezeka