Numeri
18 Kenako Yehova anauza Aroni kuti: “Iwe ndi ana ako, ndi nyumba yonse ya bambo ako, mudzayankha mlandu wa zolakwa zanu pa malamulo okhudza malo opatulika.+ Iweyo ndi ana ako mudzayankha mlandu wa zolakwa zanu pa malamulo okhudza unsembe wanu.+ 2 Utengenso abale ako a fuko la Levi, omwe ndi a mtundu wa bambo ako, kuti azikuthandiza. Azitumikira iweyo+ limodzi ndi ana ako pachihema cha Umboni.+ 3 Azichita utumiki umene mwawapatsa komanso azigwira ntchito zawo zonse zapachihema.+ Koma asamayandikire zipangizo zamʼmalo oyera, kapena kuyandikira guwa lansembe kuti iwowo kapena inuyo musafe.+ 4 Azikuthandizani komanso azigwira ntchito zawo zonse zapachihema chokumanako, ndipo munthu wamba* aliyense asamayandikire kwa inu.+ 5 Inu nokha ndi amene muzigwira ntchito za ansembe mʼmalo opatulika+ ndi paguwa lansembe,+ kuti ndisadzakwiyirenso+ Aisiraeli. 6 Ine ndatenga Alevi omwe ndi abale anu pakati pa Aisiraeli ndipo ndawapereka kwa inu kuti akhale mphatso yanu.+ Iwo aperekedwa kwa Yehova kuti azitumikira pachihema chokumanako.+ 7 Iweyo ndi ana ako, udindo wanu ndi kugwira ntchito zaunsembe paguwa lansembe komanso pa zinthu zamkati ndi kuseri kwa katani.+ Umenewu ndi utumiki wanu.+ Ndakupatsani utumiki waunsembe kuti ukhale mphatso kwa inu, ndipo munthu wamba* aliyense akayandikira pafupi aziphedwa.”+
8 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Aroni kuti: “Ine ndakupatsa udindo woyangʼanira zinthu zonse zimene anthu azipereka kwa ine.+ Pa zinthu zonse zopatulika zimene Aisiraeli azipereka, ndakupatsa gawo iweyo ndi ana ako, kuti likhale lanu mpaka kalekale.+ 9 Gawo limene muzilandira lizichokera pa nsembe zonse zopatulika koposa zowotcha pamoto. Nsembe zake ndi izi: nsembe zilizonse zimene angapereke kwa ine, kuphatikizapo nsembe zawo zambewu,+ nsembe zawo zamachimo+ komanso nsembe zawo zakupalamula.+ Gawolo lizikhala chinthu chopatulika koposa kwa iwe ndi ana ako. 10 Uzilidyera mʼmalo oyera koposa,+ ndipo mwamuna aliyense wa fuko lanu angathe kudya nawo. Gawo limenelo lizikhala chinthu chopatulika kwa iwe.+ 11 Zinthu izinso zizikhala zako: mphatso zonse za Aisiraeli,+ limodzi ndi nsembe zawo zonse zoyendetsa uku ndi uku+ zimene azipereka. Ndazipereka kwa iwe ndi kwa ana ako aamuna komanso ana ako aakazi kuti zikhale gawo lanu mpaka kalekale.+ Aliyense wamʼnyumba yako amene si wodetsedwa angathe kudya nawo.+
12 Ndakupatsa+ mafuta onse abwino koposa, vinyo yense watsopano wabwino koposa ndi mbewu zabwino koposa, zimenezi ndi zipatso zawo zoyambirira+ zimene azipereka kwa Yehova. 13 Zipatso zonse zoyamba kupsa mʼminda yawo, zimene azizipereka kwa Yehova zizikhala zako.+ Aliyense wamʼnyumba yako amene si wodetsedwa angathe kudya nawo.
14 Chinthu chilichonse chimene anthu achipereka kwa Mulungu* mu Isiraeli chizikhala chako.+
15 Chamoyo chilichonse choyamba kubadwa+ chimene azipereka kwa Yehova, kaya ndi munthu kapena nyama, chizikhala chako. Komabe uzionetsetsa kuti wawombola mwana woyamba kubadwa wa munthu+ komanso mwana woyamba kubadwa wa nyama yodetsedwa.+ 16 Mwanayo akakwanitsa mwezi umodzi kapena kuposerapo uzimuwombola ndi mtengo wowombolera. Uzimuwombola pa mtengo umene anaikiratu wa masekeli asiliva 5,*+ mogwirizana ndi sekeli lakumalo oyera* lomwe ndi lokwana magera 20.* 17 Koma usawombole ngʼombe yamphongo yoyamba kubadwa, mwana wa nkhosa wamphongo woyamba kubadwa, kapena mbuzi yoyamba kubadwa.+ Zimenezi ndi zopatulika. Magazi ake uziwawaza paguwa lansembe,+ ndipo mafuta ake uziwawotcha pamoto kuti akhale nsembe yakafungo kosangalatsa* kwa Yehova.+ 18 Uzitenga nyama yake kuti ikhale yako. Ngati mmene umachitira ndi chidale cha nsembe yoyendetsa uku ndi uku komanso mwendo wamʼmbuyo wakumanja, nyamayi izikhala yako.+ 19 Zopereka zonse zopatulika zimene Aisiraeli azipereka kwa Yehova,+ ndakupatsa iwe ndi ana ako aamuna ndi aakazi, kuti likhale gawo lanu mpaka kalekale.+ Limeneli ndi pangano lamuyaya lamchere* limene Yehova akupanga ndi iwe komanso mbadwa zako.”
20 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Aroni kuti: “Iwe udzakhala wopanda cholowa mʼdziko mwawo, ndipo sudzapatsidwa malo pakati pawo kuti akhale cholowa chako.+ Ine ndine gawo lako ndi cholowa chako pakati pa Aisiraeli.+
21 Ine ndapereka kwa ana a Levi chakhumi chilichonse+ mu Isiraeli kuti chikhale cholowa chawo chifukwa cha utumiki umene akuchita, utumiki wapachihema chokumanako. 22 Aisiraeli asadzayandikirenso chihema chokumanako, chifukwa akadzatero adzachimwa nʼkufa. 23 Aleviwo azichita utumiki wawo pachihema chokumanako, ndipo ndi amene aziyankha mlandu wa zolakwa za anthuwo.+ Iwo asakhale ndi cholowa pakati pa Aisiraeli.+ Limeneli ndi lamulo mpaka kalekale mʼmibadwo yanu yonse. 24 Chakhumi chimene Aisiraeli azipereka kwa Yehova, ndapereka kwa Alevi kuti chikhale cholowa chawo. Nʼchifukwa chake ndinawauza kuti, ‘Asalandire cholowa pakati pa Aisiraeli.’”+
25 Kenako Yehova anauza Mose kuti: 26 “Uza Alevi kuti, ‘Muzilandira kwa Aisiraeli chakhumi chimene ndakupatsani kuti chikhale cholowa chanu.+ Ndipo pa chakhumi chimene muzilandiracho, muzipereka chakhumi kwa Yehova.+ 27 Chakhumicho Mulungu azichiona kuti ndi chopereka chanu mofanana ndi tirigu wochokera pamalo opunthira,+ vinyo wochuluka wochokera mopondera mphesa kapena mafuta ochuluka ochokera mʼchofinyira mafuta. 28 Mukamachita zimenezi inunso muzikhala kuti mwapereka chopereka chanu kwa Yehova, kuchokera pa zakhumi zonse zimene muzilandira kuchokera kwa Aisiraeli. Kuchokera pa zakhumizo, muzipereka chopereka chanu kwa Yehova popereka kwa Aroni wansembe. 29 Pa mphatso zonse zabwino koposa zimene mwalandira monga chinthu chopatulika, muzipereka kwa Yehova zopereka zosiyanasiyana.’+
30 Ndipo uwauze kuti, ‘Mukapereka zabwino koposa za zoperekazo, Mulungu aziona kuti Alevinu mwapereka tirigu wochokera pamalo opunthira, vinyo wochokera mopondera mphesa kapena mafuta ochokera mʼchofinyira mafuta. 31 Inuyo ndi amʼnyumba mwanu muzidya zimenezo pamalo alionse, chifukwa amenewo ndi malipiro anu pa utumiki umene muzichita pachihema chokumanako.+ 32 Mukapereka zinthu zabwino koposa kuchokera pa zinthu zimenezi, simudzachimwa ngati mutadya, komanso musaipitse zinthu zopatulika za Aisiraeli, kuti musafe.’”+