Anadzipereka ndi Mtima Wonse ku New York
ZAKA zingapo zapitazo, Cesar ndi mkazi wake Rocio ankakhala mosangalala ku California. Cesar ankagwira ntchito yokonza makina otenthetsa ndi kuziziritsa m’nyumba pomwe Rocio ankagwira mu ofesi ya dokotala. Iwo anali ndi nyumba yabwino ndipo analibe ana. Ndiyeno panachitika chinthu china chimene chinawachititsa kusintha moyo wawo.
Mu October 2009, ofesi ya nthambi ku United States inatumiza makalata m’mipingo yopempha kuti anthu amene ali ndi luso linalake afunsire mwayi wokagwira nawo ntchito yomanga nyumba zina ku Wallkill ku New York. Iwo anati: “Popeza ndife okulirapo, tinkaona kuti umenewu ndi mwayi womwe sungabwere kawiri. Tinaona kuti tisauphonye.” Nthawi yomweyo analemba mafomu n’kupereka.
Ndiyeno chaka chinadutsa osaitanidwa ku Beteli. Koma anapitiriza kusintha zinthu kuti akhale ndi moyo wosalira zambiri n’cholinga choti akwaniritse cholinga chawocho. Anati: “Tinakonza galaja yathu n’kukhala kanyumba koti tizikhalamo n’cholinga choti munthu wina azichita lendi nyumba yathu yaikulu. Tinasamuka m’chinyumba chathucho n’kukalowa m’kanyumba kakang’onoko. Cesar anati: “Zimene tinachitazi zinathandiza kuti tikonzekere moyo wa ku Beteli ngati titaitanidwa.” Rocio anati: “Patangopita mwezi umodzi kuchokera pamene tinasamukira m’kanyumbako, tinalandira kalata yotiuza kuti tikathandize nawo kwakanthawi pa ntchito ya ku Wallkill. Apa tinaona kuti kukhala ndi moyo wosalira zambiri kwachititsa kuti Yehova atidalitse.”
AKUDALITSIDWA CHIFUKWA CHA MTIMA WODZIPEREKA
Palinso abale ndi alongo ambiri amene adzimana zinthu zambiri n’cholinga choti athandize pa ntchito ya zomangamanga ku New York. Ena akugwira ku Wallkill pomwe ena akumanga nawo likulu lathu ku Warwick.a Ambiri asiya nyumba zawo zabwino, ntchito zapamwamba komanso zinthu zina n’cholinga choti atumikire Yehova ndipo adalitsidwa kwambiri.
Mwachitsanzo, Way ndi mkazi wake Debra ankakhala ku Kansas ndipo anagulitsa nyumba ndi katundu wawo wambiri. Kenako anasamukira pafupi ndi ku Wallkill kuti azikayendera potumikira kumeneko.b M’baleyu amagwira ntchito zamagetsi ndipo iye ndi mlongoyu ndi azaka pafupifupi 60. Iwo anafunika kusintha zambiri kuti akwanitse kuchita utumikiwu ndipo akuona kuti adalitsidwa kwambiri. Pofotokoza za utumiki wawo ku Beteli, Debra anati: “Nthawi zina ndimamva ngati tikuchita zimene timaona m’zithunzi za m’mabuku athu zija. Ndimaona ngati ndili m’Paradaiso ndipo ndikugwira nawo ntchito yomanga.”
Nayenso Melvin ndi mkazi wake Sharon anagulitsa nyumba ndi katundu wawo ku South Carolina n’cholinga choti akathandize pa ntchito ya ku Warwick. Kuchita zimenezi sikunali kophweka koma amaona kuti ndi mwayi waukulu kugwira nawo ntchito yofunika kwambiriyi. Iwo anati: “Timamva bwino kwambiri tikaganizira zoti ntchito imene tikugwira ithandiza gulu la padziko lonse.”
Kenneth ndi mkazi wake Maureen anasamuka ku California n’kupita kukagwiranso ntchito ku Warwick. Iwo ndi azaka za m’ma 50 ndipo mwamunayu ankagwira ntchito ya zomangamanga. Asanasamuke anapempha mlongo wina kuti aziyang’anira nyumba yawo. Anapemphanso achibale kuti azisamalira bambo a Kenneth chifukwa choti ndi okalamba. Iwo sanong’oneza bondo chifukwa cha zimene anasankha. Kenneth anati: “Zinthu zikutiyendera bwino kwambiri. N’zoona kuti pali mavuto ena koma pali madalitso ambiri ndipo tikulimbikitsa anzathu kuti agwire nawo ntchitoyi.”
MAVUTO AMENE ANAKUMANA NAWO
Anthu ambiri amene adziperekawa anakumana ndi mavuto ena. Mwachitsanzo, William ndi mkazi wake Sandra ankakhala mosangalala ku Pennsylvania. Iwo ali ndi zaka za m’ma 60 ndipo anali ndi kampani komanso antchito okwana 17. Anazolowera kwambiri mpingo wawo chifukwa ankasonkhana kumeneko kuyambira ali ana ndipo achibale awo ambiri amakhala kumeneko. Iwo anapatsidwa mwayi woti asamukire ku Wallkill kuti azikayendera n’kumatumikira ku Beteli. Koma ankadziwa kuti ayenera kusiya achibale, anzawo ndiponso zinthu zambiri zimene anazizolowera. William anati: “Sizinali zapafupi kusiyana ndi zinthu zonse zimene tinazolowera.” Koma atapemphera kwambiri anasankha zosamuka ndipo sakunong’oneza bondo. Iye ananenanso kuti: “Mwayi wogwira ntchitoyi komanso wotumikira limodzi ndi banja la Beteli ndi wamtengo wapatali. Ine ndi Sandra tikusangalala kwambiri panopa.”
M’bale wina, dzina lake Ricky, anali bwana pa kampani ya zomangamanga ku Hawaii ndipo anapemphedwa kuti asamukire cha ku Warwick kuti azikatumikira kumeneko. Mkazi wake dzina lake Kendra ankafuna kuti apite. Koma ankadera nkhawa za mwana wawo wazaka 11 dzina lake Jacob. Ankaopa kuti akasamuka mwina mwana wawo adzavutika kuzolowera moyo wa ku New York.
Ricky anati: “Tinkafunitsitsa kupeza mpingo umene unali ndi achinyamata abwino kuti azilimbikitsa Jacob.” Mumpingo umene anasamukira muli achinyamata ochepa koma muli anthu ambiri otumikira ku Beteli. Ricky ananenanso kuti: “Titapita ku misonkhano yoyamba ndinafunsa Jacob mmene akuonera mpingo watsopanowu popeza mulibe ana amsinkhu wake. Iye anandiuza kuti, ‘Adadi, musadandaule. Anzanga akhala abale achinyamata amene akutumikira ku Beteli.’”
Zimenezi zachitikadi. Abale otumikira ku Beteli aja ayamba kucheza naye ndipo izi zikuthandiza kwambiri Jacob. Ricky anati: “Tsiku lina usiku ndinaona kuti magetsi akuyakabe m’chipinda cha mwana wathuyu. Ndinkaganiza kuti akuchita masewera apakompyuta koma ayi ankawerenga Baibulo. Nditamufunsa zimene ankachita, anati: ‘Ndikuchita zimene a ku Beteli amachita. Ndikufuna kuwerenga Baibulo lonse m’chaka chimodzi.’” Ricky ndi Kendra akusangalala kwambiri chifukwa chakuti Ricky ali ndi mwayi wotumikira ku Warwick komanso kuti kusamukaku kwathandiza mwana wawo kuti azikonda kwambiri Yehova.—Miy. 22:6.
SADERA NKHAWA ZA M’TSOGOLO
Anthu amene tikukambiranawa amadziwa kuti ntchito imene akugwira ku Wallkill ndi ku Warwick idzatha, choncho adzangotumikira ku Beteli kwakanthawi. Koma sadera nkhawa zimene azidzachita m’tsogolo. Mwachitsanzo, pali mabanja awiri ochokera ku Florida azaka za m’ma 50 amene akutumikira ku New York. Banja loyamba ndi la John ndi mkazi wake Carmen. M’baleyu anali bwana pa kampani ya zomangamanga ndipo akutumikira limodzi ndi mkazi wake ku Warwick. Iye anati: “Yehova wakhala akutisamalira mpaka pano. Sangatibweretse kuno kenako n’kungotitaya.” (Sal. 119:116) Banja lachiwiri ndi la Luis ndi Quenia. M’baleyu amagwira ntchito yopanga zipangizo zozimitsira moto ndipo akutumikira ku Wallkill limodzi ndi mkazi wake. Iwo anati: “Taona kuti Yehova ndi wowolowa manja ndipo amatipatsa zofunika pa moyo wathu. Tikudziwa kuti iye sadzasiya kutisamalira zivute zitani.”—Sal. 34:10; 37:25.
“MADALITSO OTI MUDZASOWA POWALANDIRIRA”
Anthu amene anadziperekawa anali ndi zifukwa zowalepheretsa kukatumikira. Koma iwo anamuyesa Yehova potsatira mawu ake akuti: “Ndiyeseni chonde pa nkhani imeneyi, kuti muone ngati sindidzakutsegulirani zipata za kumwamba ndi kukukhuthulirani madalitso oti mudzasowa powalandirira.”—Mal. 3:10.
Kodi nanunso mudzamuyesa Yehova kuti muone mmene angakudalitsireni? Ndi bwino kuiganizira nkhaniyi ndiponso kuipempherera n’kuona ngati mungathandize pa ntchito yomanga ku New York kapena kwina kulikonse. Mukatero, Yehova adzakudalitsani kwambiri.—Maliko 10:29, 30.
M’bale wina dzina lake Dale ndi mkazi wake dzina lake Cathy amalimbikitsanso anthu kugwira nawo ntchitoyi. Iwo ndi ochokera ku Alabama ndipo m’baleyu amagwira ntchito ya zomangamanga. Banjali linadzipereka kukatumikira ku Wallkill ndipo linati: “Munthu akalolera kusiya moyo umene anazolowera, amakhala ndi mwayi woona mzimu wa Yehova ukumuthandiza.” Kodi n’chiyani chimafunika kuti munthu adzipereke? Dale anati: “Chofunika n’kuchita zonse zimene mungathe kuti muyambe moyo wosalira zambiri. Simudzanong’oneza bondo ngakhale pang’ono.” M’bale wina wa ku North Carolina, dzina lake Gary, wakhala akuyang’anira ntchito ya zomangamanga kwa zaka 30. Iye ndi mkazi wake Maureen amasangalala kwambiri kutumikira ku Warwick. Ananena kuti: “Timagwira ntchito limodzi ndi abale ndi alongo abwino kwambiri amene akhala akutumikira Yehova ku Beteli kwa zaka zambirimbiri.” Gary anati: “Kuti munthu atumikire ku Beteli amafunika kukhala moyo wosalira zambiri. Moyo umenewu ndi wabwino kwambiri m’dzikoli.” M’bale wina dzina lake Jason anasamuka ku Illinois, limodzi ndi mkazi wake Jennifer ndipo akutumikira ku Wallkill. M’baleyu amagwira ntchito zamagetsi ndipo banjali linati: “Utumiki umenewu umachititsa munthu kukhala ngati akulawa moyo wa m’dziko latsopano.” Jennifer ananenanso kuti: “Zimasangalatsa kwambiri kudziwa kuti Yehova amayamikira ntchito imene tikugwira naye limodzi pokonzekera zimene zili m’tsogolo. Yehova amadalitsa kwambiri anthu amene adzipereka chonchi.”
b Ambiri mwa anthuwa amapeza okha nyumba komanso zinthu zofunika pa moyo ndipo ku Beteliko amangogwira ntchito tsiku limodzi kapena angapo pa mlungu.