Zimene Zachitika M’chaka Chapitachi
NGAKHALE kuti zinthu m’dziko la Satanali zikuipiraipira, atumiki a Yehova ali ndi ‘zochita zambiri mu ntchito ya Ambuye.’ (1 Akor. 15:58) Malipoti otsatirawa akusonyeza zimene a Mboni za Yehova akhala akuchita posonyeza kuti ‘amakhulupirira Yehova, amachita zabwino komanso amayesetsa kukhala okhulupirika m’zochita zawo zonse.’—Sal. 37:3.
Ntchito Yosamutsa Likulu la Mboni za Yehova Komanso Ofesi ya Nthambi
Ntchito yomanga maofesi atsopano mumzinda wa Wallkill ku New York inatha pa 1 February, 2016. Choncho Komiti ya Nthambi ya ku United States, Dipatimenti ya Utumiki komanso madipatimenti ena anasamukira kumalowa. Ntchito yomanga likulu la Mboni za Yehova lapadziko lonse inatha ku Warwick moti anthu a m’banja la Beteli ya ku Brooklyn ayamba kusamukira kumalo atsopanowa.
Kuyambira Lolemba pa 3 April, 2017, anthu azidzatha kupita kukaona malo atsopanowa. Poona mbali zitatu, anthu azidzayenda okha, koma poona mbali ina ya 4, azidzayenda ndi munthu wowasonyeza malo.
Mbali ya “Dzina la Mulungu M’Baibulo” ili ndi Mabaibulo akale kwambiri omwe sapezeka masiku ano. Mbaliyi ilinso ndi umboni wosonyeza kuti dzina la Mulungu liyenera kupezeka m’Baibulo.
Mbali ya “Anthu Odziwika ndi Dzina la Yehova” ili ndi zithunzi zosonyeza mbiri ya Mboni za Yehova. Mbaliyi ikusonyezanso kuti Yehova wakhala akutsogolera, kuphunzitsa komanso kuthandiza anthu ake kuti azichita chifuniro chake mwadongosolo.
Mbali ya “Likulu Lapadziko Lonse—Anasonyeza Chikhulupiriro” ili ndi mavidiyo osonyeza mmene makomiti a Bungwe Lolamulira amathandizira kuti atumiki a Yehova azisonkhana, azilalikira, aziphunzira Mawu a Mulungu komanso azikondana.
Mbali zimenezi zizidzakhala zotsegula kuchokera Lolemba mpaka Lachisanu, kuyambira 8:00 koloko m’mawa mpaka 4:00 koloko madzulo. Mbali yomwe anthu azidzayenda ndi munthu wowasonyeza malo ija, izidzakhala ya maminitsi 20. Anthu azidzaona maofesi komanso panja pa Beteli. Azidzaona malo amenewa kuchokera Lolemba mpaka Lachisanu, kuyambira 8:00 koloko m’mawa mpaka 11:00 koloko komanso 1:00 koloko masana mpaka 4:00 koloko madzulo.
Musanapite kukaona malo, pitani pa jw.org. Onani pamene palembedwa kuti ZOKHUDZA IFEYO > MAOFESI NDI KUONA MALO > United States.