KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBULO
Kodi Tsiku la Chiweruzo n’chiyani?
Kale, Mulungu ankagwiritsa ntchito oweruza ndipo ankapulumutsa anthu ake ku zinthu zopanda chilungamo zomwe zinkachitika. (Oweruza 2:18) Baibulo limanenanso za Tsiku la Chiweruzo lomwe likubwera kutsogoloku. Limati nthawi imeneyi idzakhala yosangalatsa chifukwa Yehova, yemwe ndi Woweruza wa dziko lapansi, adzapulumutsa anthu ku zinthu zopanda chilungamo zomwe zikuchitika m’dzikoli.—Werengani Salimo 96:12, 13; Yesaya 26:9.
Mulungu wasankha Yesu kuti adzaweruze anthu amoyo ndi amene anamwalira. (Machitidwe 10:42; 17:31) Pali anthu ambiri omwe anamwalira asanaphunzire za Mulungu. Pa Tsiku la Chiweruzo, Yesu adzaukitsa anthu amenewa kuti aphunzire za Mulungu ndi kumudziwa.—Werengani Machitidwe 24:15.
N’chifukwa chiyani Tsiku la Chiweruzo lidzakhale la zaka 1,000?
Akufa adzaukitsidwa mkati mwa zaka 1,000 zimenezi. (Chivumbulutso 20:4, 12) Anthu amenewa adzafunika kuphunzira za Mulungu kuti amudziwe n’kuyamba kumumvera. Mosiyana ndi zimene anthu ambiri amaganiza, Baibulo limasonyeza kuti anthu oukitsidwa adzaweruzidwa potengera zimene adzachite akadzaphunzitsidwa za Mulungu.—Werengani Aroma 6:7.
Baibulo limanenanso za tsiku lina lachiweruzo lomwe lidzabwere modzidzimutsa, zaka 1,000 zisanayambe. Monga tafotokozera m’nkhani zoyambirira m’magaziniyi, tsiku limeneli limadziwikanso kuti nthawi ya mapeto. Pa tsiku limeneli, Mulungu adzawononga anthu onse oipa. (2 Petulo 3:7) Choncho, ngati tikufuna kudzapulumuka pa tsikuli, tiyenera kuchita zimene Mulungu amafuna.—Werengani 2 Petulo 3:9, 13.