Kodi Yehova Amasonyeza Bwanji Kuti Amatikonda?
“Taganizirani za chikondi chachikulu chimene Atate watisonyeza.”—1 YOH. 3:1.
1. Kodi mtumwi Yohane analimbikitsa Akhristu kuchita chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani anatero?
PALEMBA la 1 Yohane 3:1, mtumwi Yohane anati: “Taganizirani za chikondi chachikulu chimene Atate watisonyeza.” Apa iye analimbikitsa Akhristu kuti aziganizira mmene Yehova amawakondera. Tikamachita zimenezi timayamba kukonda kwambiri Mulungu ndiponso kukhala naye pa ubwenzi wolimba.
2. N’chifukwa chiyani anthu ena amaona kuti Mulungu sawakonda?
2 Anthu ena amaona kuti Mulungu sangawakonde. Mwina amaona kuti Mulungu amangopereka malamulo ndi kulanga anthu amene samvera malamulowo. Ena amaphunzitsidwa mabodza osonyeza kuti Mulungu ndi wankhanza ndipo n’zosatheka kumukonda. Pomwe anthu enanso amakhulupirira kuti Mulungu sangasiye kuwakonda ngakhale iwo atachita zinthu zoipa. Pamene munkaphunzira Baibulo munamva kuti khalidwe lalikulu la Mulungu ndi chikondi. Munaphunziranso kuti chifukwa cha chikondicho, Yehova anapereka Mwana wake kuti atiwombole. (Yoh. 3:16; 1 Yoh. 4:8) Ngakhale zili choncho, zinthu zoipa zimene munthu wakumana nazo pa moyo wake zingamulepheretsenso kukhulupirira kuti Mulungu amamukonda.
3. Kodi tiyenera kumvetsa mfundo iti kuti tidziwe mmene Mulungu amatikondera?
3 Kodi Yehova amasonyeza bwanji kuti amatikonda? Kuti tiyankhe funsoli, tiyenera kumvetsa kaye mfundo yoti iye ndi amene anatilenga. (Werengani Salimo 100:3-5.) N’chifukwa chake Baibulo limanena kuti Adamu anali “mwana wa Mulungu.” (Luka 3:38) Nayenso Yesu anaphunzitsa kuti tizitchula Mulungu kuti “Atate wathu wakumwamba.” (Mat. 6:9) Popeza Yehova ndi amene anatilenga, ifeyo tili ngati ana ake. Choncho Yehova amatikonda ngati mmene bambo wabwino amakondera ana ake.
4. (a) Kodi Yehova amasiyana bwanji ndi anthu pa nkhani yosamalira ana? (b) Kodi tikambirana chiyani m’nkhaniyi ndiponso yotsatira?
4 Koma ngakhale bambo wabwino atayesetsa kwambiri kusonyeza chikondi, sangafanane ndi Yehova. Ndipo pali abambo ena amene amazunza ana awo moti anawo saiwala nkhanza zimene anachitiridwa. Izitu n’zopweteka komanso zomvetsa chisoni. Koma Yehova sachita zimenezi. (Sal. 27:10) Iye amatikonda komanso kutisamalira bwino. Kudziwa zimenezi kungatithandize kumukondanso kwambiri. (Yak. 4:8) M’nkhaniyi tikambirana zinthu 4 zimene Yehova amachita posonyeza kuti amatikonda. Ndiyeno m’nkhani yotsatira tidzakambirana zinthu 4 zimene tingachite posonyeza kuti timakonda Yehova.
YEHOVA AMATISAMALIRA MWACHIKONDI
5. Kodi mtumwi Paulo ananena kuti Mulungu amatipatsa zinthu ziti?
5 Pamene mtumwi Paulo anali mumzinda wa Atene ku Girisi, anaona mafano ambiri a milungu imene anthu ankakhulupirira kuti inkawapatsa moyo komanso chilichonse chofunika. Ndiyeno Paulo anati: “Mulungu amene anapanga dzikoli ndi zinthu zonse zili mmenemu, . . . amapatsa anthu onse moyo, mpweya, ndi zinthu zonse. . . . Chifukwa cha iye tili ndi moyo, timayenda ndipo tilipo.” (Mac. 17:24, 25, 28) Choncho Yehova amatipatsa “zinthu zonse” zofunika pa moyo chifukwa chotikonda. Koma kodi ndi zinthu zina ziti zimene Yehova watipatsa?
6. Kodi dziko lapansi limasonyeza bwanji kuti Mulungu amatikonda? (Onani chithunzi patsamba 18.)
6 Mulungu ‘anapereka dziko lapansi kwa ana a anthu.’ (Sal. 115:15, 16) Ndiye taganizirani zinthu zimene zimapezeka m’dzikoli. Asayansi awononga ndalama zambiri kuti afufuze ngati pali pulaneti lina lofanana ndi dziko lapansi. Iwo anatulukira mapulaneti ambirimbiri koma mapulaneti ena onsewo alibe zinthu zothandiza kuti anthu akhale ndi moyo. Zikuoneka kuti dziko lapansi lokhali ndi limene Mulungu analilenga kuti likhale ndi zinthu zonse zofunika pa moyo. Iye anaonetsetsanso kuti likhale lokongola, losangalatsa ndi lotetezeka. (Yes. 45:18) Umenewutu ndi umboni wakuti Yehova amatikonda kwambiri.—Werengani Yobu 38:4, 7; Salimo 8:3-5.
7. Kodi Yehova anasonyeza bwanji chikondi potilenga?
7 Koma Yehova amadziwanso kuti anthufe timafunikira zinthu zina kuti tizikhala osangalala. Mwana amamva bwino akaona kuti makolo ake amamukonda ndiponso kumusamalira. Ndiyeno Yehova analenga anthu m’chifanizo chake. (Gen. 1:27) Choncho timatha kuzindikira kuti iye amatikonda ndiponso ifeyo tikhoza kumukonda. Paja Yesu ananenanso kuti timakhala osangalala tikakhala pa ubwenzi ndi Yehova. (Mat. 5:3) Iye ndi Atate wathu wachikondi ndipo “amatipatsa mowolowa manja zinthu zonse kuti tisangalale.”—1 Tim. 6:17; Sal. 145:16.
YEHOVA AMATIPHUNZITSA MWACHIKONDI
8. Kodi Yehova wasonyeza bwanji kuti ndi bambo wabwino?
8 Abambo amakonda kwambiri ana awo ndipo amafunitsitsa kuwateteza kuti asasocheretsedwe. Koma makolo ambiri satsatira mfundo za Mulungu ndipo amalephera kutsogolera bwino ana awo. Izi zimasokoneza kwambiri anawo. (Miy. 14:12) Koma Yehova ndi “Mulungu wachoonadi” ndipo amatsogolera bwino ana ake. (Sal. 31:5) Iye amatikonda kwambiri ndipo amasangalala kutitsogolera pomulambira ndiponso pa moyo wathu wonse. (Werengani Salimo 43:3.) Kodi Yehova wasonyeza kuti amatikonda potiphunzitsa zinthu zotani?
9, 10. Kodi Yehova amasonyeza bwanji kuti amatikonda potiphunzitsa mfundo zoona zokhudza (a) iyeyo? (b) ifeyo?
9 Choyamba, Yehova watithandiza kuti timudziwe bwino. Mwachitsanzo, watiuza dzina lake lomwe limapezeka m’Baibulo m’malo ambiri kuposa dzina lina lililonse. Izi zimasonyeza kuti akufunitsitsa kukhala nafe pa ubwenzi. (Yak. 4:8) Iye amatithandizanso kudziwa makhalidwe ake. Mwachitsanzo, tikamayang’ana chilengedwe timaona kuti Yehova ndi wamphamvu komanso wanzeru. (Aroma 1:20) Baibulo limasonyezanso kuti iye ndi wachilungamo ndiponso wachikondi. Mulungu ali ngati bambo wamphamvu, wanzeru, wachilungamo ndiponso wachikondi. Choncho n’zosavuta kukhala naye pa ubwenzi.
10 Yehova watiuzanso cholinga chake. Iye watiphunzitsa kuti ife ndi angelo tili ngati banja lake. Baibulo limatiuzanso kuti Mulungu sanalenge anthufe m’njira yoti tizisankha tokha zabwino ndi zoipa. Munthu akanyalanyaza mfundo imeneyi amakumana ndi mavuto aakulu. (Yer. 10:23) Choncho tiyenera kutsogoleredwa ndi Mulungu kuti tizikhala mwamtendere ndiponso mosangalala. Yehova watiphunzitsa mfundo yofunika imeneyi chifukwa choti amatikonda.
11. Kodi Yehova watilonjeza chiyani?
11 Bambo wachikondi amafunitsitsa kuti zinthu ziziyenda bwino pa moyo wa ana ake. Koma chomvetsa chisoni n’chakuti anthu ambiri sadziwa zam’tsogolo ndipo amatanganidwa ndi zinthu zosakhalitsa. (Sal. 90:10) Ifeyo tili ndi mwayi chifukwa Atate wathu wakumwamba watilonjeza tsogolo labwino kwambiri. Izi zimathandiza kuti tizikhala anthu osangalala.
YEHOVA AMATILANGIZA
12. Kodi Yehova anasonyeza bwanji chikondi polangiza Kaini komanso Baruki?
12 Yehova ataona kuti Kaini wakwiya kwambiri anamufunsa kuti: “N’chifukwa chiyani wapsa mtima choncho, ndipo nkhope yako yagweranji? Ukasintha n’kuchita chabwino, sindikuyanja kodi? . . . Kodi iweyo suugonjetsa [uchimowo]?” (Gen. 4:6, 7) Apatu Yehova anapereka malangizo othandiza kwambiri. Iye anachita zimenezi ataona kuti Kaini watsala pang’ono kuchita zoipa. Koma Kaini sanamvere malangizowo ndipo zotsatira zake zinali zoipa kwambiri. (Gen. 4:11-13) Pa nthawi ina, mlembi wa Yeremiya dzina lake Baruki, anakhumudwa kwambiri ndipo Yehova anamuthandiza kuzindikira vuto lake lenileni. Koma mosiyana ndi Kaini, Baruki anamvera malangizo a Yehova ndipo anapulumuka.—Yer. 45:2-5.
13. N’chifukwa chiyani Yehova analola kuti atumiki ake ena akumane ndi mavuto?
13 Mtumwi Paulo analemba kuti: “Yehova amalanga aliyense amene iye amamukonda, ndipo amakwapula aliyense amene iye amamulandira monga mwana wake.” (Aheb. 12:6) Palembali, mawu akuti ‘kulanga’ amatanthauzanso kuphunzitsa m’njira zosiyanasiyana. M’Baibulo muli zitsanzo zosonyeza kuti Yehova ankalola kuti atumiki ake ena akumane ndi mavuto pofuna kuwathandiza kukhala anthu abwino. Mwachitsanzo, Yosefe, Mose ndiponso Davide anakumana ndi mavuto aakulu kwambiri. Koma Yehova sanawasiye ndipo zimene anaphunzira pa nthawi ya mavutowo zinawathandiza kuti iye adzawagwiritse ntchito pa maudindo aakulu. Tikamawerenga nkhani ngati zimenezi timaoneratu kuti Yehova amatikonda kwambiri.—Werengani Miyambo 3:11, 12.
14. Kodi Yehova amatisonyeza bwanji chikondi tikalakwitsa zinazake?
14 Yehova amatisonyezanso chikondi tikalakwitsa zinthu. Iye amatilangiza ndipo tikamvera malangizo akewo n’kulapa, ‘amatikhululukira ndi mtima wonse.’ (Yes. 55:7) Zimene Davide ananena zimasonyeza kuti Yehova ndi wachifundo kwambiri. Iye anati: ‘Akukukhululukira zolakwa zako zonse ndipo akukuchiritsa matenda ako onse. Akuwombola moyo wako kudzenje, akukuveka kukoma mtima kosatha ndi chifundo ngati chisoti chachifumu, monga mmene kum’mawa kwatalikirana ndi kumadzulo, momwemonso, watiikira kutali zolakwa zathu.’ (Sal. 103:3, 4, 12) Choncho tiyenera kumvera malangizo a Yehova podziwa kuti iye amatilangiza chifukwa chotikonda.—Sal. 30:5.
YEHOVA AMATITETEZA
15. Kodi Yehova amachitanso chiyani posonyeza kuti amatikonda?
15 Bambo wachikondi amaona kuti kuteteza ana ake n’kofunika kwambiri. Atate wathu wakumwamba amachitanso zimenezi. Wolemba masalimo wina ananena kuti Yehova “amateteza moyo wa anthu ake okhulupirika. Amawalanditsa m’manja mwa anthu oipa.” (Sal. 97:10) Anthufe timaona kuti maso athu ndi ofunika ndipo timawateteza kwambiri. Nayenso Yehova amatiteteza chifukwa choona kuti ndife ofunika.—Werengani Zekariya 2:8.
16, 17. Kodi Yehova anateteza bwanji atumiki ake akale, nanga amachita bwanji zimenezi masiku ano?
16 Nthawi zina Yehova amagwiritsa ntchito angelo poteteza anthu ake. (Sal. 91:11) Mwachitsanzo, mngelo mmodzi anapulumutsa mzinda wa Yerusalemu pamene Asuri ankafuna kuuwononga. Iye anapha asilikali 185,000 usiku umodzi. (2 Maf. 19:35) Petulo ndi Paulo anapulumutsidwanso pamene angelo anawatulutsa m’ndende. (Mac. 5:18-20; 12:6-11) Masiku ano Yehova amatetezanso anthu ake. M’bale wina woimira likulu lathu anapita m’dziko lina ku Africa. Iye ananena kuti m’dzikolo munali chipwirikiti ndipo anthu ankamenyana, kuba, kugwirira akazi ndiponso kupha anzawo. Koma palibe abale ndi alongo amene anaphedwa ngakhale kuti ena anaberedwa katundu wawo. Pamene m’baleyo anawafunsa mmene zinthu zilili, onse anamwetulira n’kuyankha kuti: “Zonse zili bwino ndipo timangothokoza Yehova.” Iwo ankadziwa kuti Mulungu amawakonda.
17 Koma nthawi zina, Yehova amalola kuti adani ake aphe anthu okhulupirika. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Sitefano. Ngakhale zili choncho, Yehova amateteza anthu ake powapatsa malangizo kuti asakodwe m’misampha ya Satana. (Aef. 6:10-12) Malangizo a m’Baibulo komanso m’mabuku athu amatithandiza kuti tipewe mtima wokonda chuma, chiwerewere, zosangalatsa zachiwawa komanso kugwiritsa ntchito Intaneti molakwika. Apa tingati Yehova ndi Bambo wachikondi amene amateteza ana ake.
TILI NDI MWAYI WAUKULU KWAMBIRI
18. Kodi inuyo mumamva bwanji mukaganizira mmene Yehova amakukonderani?
18 M’nkhaniyi taona kuti Yehova amatisonyeza chikondi m’njira zambiri. Izi zimatichititsa kukhala ndi maganizo amene Mose anali nawo. Paja iye atatumikira Yehova kwa nthawi yaitali, ananena kuti: “M’mawa mutikhutiritse ndi kukoma mtima kwanu kosatha, kuti tifuule mokondwera ndi kuti tikhale osangalala masiku onse a moyo wathu.” (Sal. 90:14) Kunena zoona, tili ndi mwayi waukulu kwambiri chifukwa chakuti timadziwa kuti Yehova amatikonda komanso amatisonyeza chikondicho m’njira zambiri. M’pake kuti mtumwi Yohane ananena kuti: “Taganizirani za chikondi chachikulu chimene Atate watisonyeza.”—1 Yoh. 3:1.