MAFUNSO OCHOKERA KWA OWERENGA
Kodi odzozedwa amalandira bwanji “chikole” nanga amadindidwa bwanji “chidindo”?—2 Akor. 1:21, 22.
Chikole: Buku lina limanena kuti mawu achigiriki amene anawamasulira kuti “chikole” pa 2 Akorinto 1:22, “ankawagwiritsa ntchito pa zinthu zokhudza malamulo komanso malonda.” Mawuwa amatanthauza “ndalama zochepa zimene munthu amapereka choyamba, pogula chinthu. Ndalamazi zimatsimikizira kuti mwagwirizanadi kuti mudzagulitsana chinthucho ndipo malipiro onse adzaperekedwa.” Mkhristu akadzozedwa amakhala kuti walandira chikole, koma malipiro onse amene adzalandire afotokozedwa pa 2 Akorinto 5:1-5. Odzozedwa adzapita kumwamba ndipo adzakhala ndi moyo wosafa.—1 Akor. 15:48-54.
M’Chigiriki cha masiku ano, mawu ofanana ndi akuti chikole amawagwiritsanso ntchito ponena za mphete ya ukwati. Zimenezi n’zomveka tikaganizira mfundo yoti odzozedwa adzakhala ngati mkazi wa Khristu.—2 Akor. 11:2; Chiv. 21:2, 9.
Chidindo: Kale chidindo ankachigwiritsa ntchito ngati siginecha posonyeza mwini wa chinthu, potsimikizira kuti chinthucho n’chenicheni komanso posonyeza kuti anthu anagwirizana zinazake. Tingati Akhristu odzozedwa ‘anadindidwa’ ndi mzimu woyera posonyeza kuti ndi a Mulungu. (Aef. 1:13, 14) Komabe kutsimikizira kwenikweni kumachitika Mkhristu wodzozedwa akatsala pang’ono kumwalira ali wokhulupirika kapena kudzachitika chisautso chachikulu chitatsala pang’ono kuyamba.—Aef. 4:30; Chiv. 7:2-4.