Gwiritsani Chilengezo Chapoyera cha Chiyembekezo Chanu Mosagwedera
1 Phunziro la Nsanja ya Olonda ndiyo njira yaikulu mwa imene “zakudya [zauzimu] panthaŵi yake” zimaperekedwera kwa anthu a Mulungu. (Mat. 24:45) Timapezeka pamsonkhano wofunika umenewu pazifukwa ziŵiri—kulimbikitsidwa mwauzimu ndi kulengeza poyera chiyembekezo chathu kwa ena.—Aheb. 10:23-25.
2 Kuphindula Ife Enife: Munomo m’Malaŵi, nzachisoni kudziŵa kuti m’mipingo yochuluka oŵerengeka okha opezeka pamsonkhanowo ndiwo amakhala ndi makope awoawo a Nsanja ya Olonda ndipo pafupifupi chiŵerengero chimenecho ndiwo amayankhapo. Zimenezi zimasonyeza kuti oŵerengeka kwambiri mwa omvetserawo ndiwo amakonzekera phunzirolo pasadakhale. Chakudya chauzimu chotafuna chopezeka m’Phunziro la Nsanja ya Olonda sichingamvetsetsedwe kwenikweni pamsonkhano pokhapo. Mufunikira kupatula nthaŵi ya kuphunzira nkhaniyo pasadakhale.
3 Pokonzekera phunzirolo, kungakhale kothandiza choyamba kuŵerenga ndi kusinkhasinkha mafunso m’bokosi limene lili chakumapeto kwa nkhaniyo. Kuchita motero kungakuthandizeni kusumika maganizo anu pamfundo zazikulu zimene zidzapendedwa m’phunzirolo.
4 Mkati mwa phunziro mvetserani mosamalitsa zimene zikunenedwa. Mvetserani ndemanga zotsegulira za wochititsa; ndemanga zimenezi zimapereka maziko a phunzirolo. Iye angadzutse mafunso atatu kapena anayi amene adzayankhidwa, kapena angabwereze mfundo zina zazikulu za phunziro la mlungu wathawo ngati phunziro la mlunguwo likupitiriza ndi nkhani imodzimodziyo. Ngati pali kusintha m’kumvetsetsa kwathu ulosi wa Baibulo kapena lamulo la mkhalidwe la Malemba, adzasumika maganizo athu pa zimenezi. Indetu, ndemanga za wochititsa ziyenera kukhala zachidule, popeza kuti chimodzi cha zifuno za phunzirolo ndicho kupatsa mpingo mpata wa kulengeza chiyembekezo chawo. Mvetserani mosamalitsa pamene ena akupereka ndemanga pa zimene aphunzira; zimenezi zingakuthandizeni kulimbitsa chikhulupiriro chanu.
5 Lengezani Chiyembekezo Chanu: Kodi inu nthaŵi zonse mumayankha paphunziro? Mayankho achindunji ndi achidule ndiwo afunika. (Yerekezerani ndi Luka 21:1-4.) Onse amayamikira yankho losavuta lochokera mumtima. Kaŵirikaŵiri yankho loyamba la funso liyenera kukhala lachidule ndi lachindunji. Zimenezo zimalola ena kutchula lemba kapena kusumika maganizo pamfundo yochirikiza m’ndimemo. Mwanjirayi ambiri angalengeze poyera chiyembekezo chawo. Nthaŵi zonse mayankho ayenera kukhala abwino ndi omangirira.
6 Ngati mwangoyamba kumene kupezeka paphunziro kapena ngati ndinu wamanyazi kuyankha, mungapemphe chithandizo kwa wochititsa. Mpempheni kuona dzanja lanu pamene ndime yakutiyakuti ikupendedwa. Mwinamwake mungadzipereke kuŵerenga lemba losonyezedwa ndi kufotokoza mwachidule tanthauzo lake. Mukhoza kulemba timawu tingapo mphepete tokuthandizani kukumbukira zimene mufuna kunena poyankha. Ngati ndinu mwana wamng’ono, kumbukirani kuti mayankho anu ngofunika ndipo amayamikiridwa.—Mat. 21:16.
7 Nkofunika kwa ife kufotokoza chikhulupiriro chathu, ndipo Phunziro la Nsanja ya Olonda limapereka mpata wabwino wa kuchita zimenezo. Ngati mumazengereza kuyankha, yesani kuchita zomwe mungathe kulaka vutolo, ndipo dzikakamizeni kuyankhapo ngakhale kamodzi kokha. Mudzakhala mutachirikiza msonkhanowo, ndipo mudzapeza bwino. Chotero bwanji osalinganiza kuti mukayankhepo ngakhale kamodzi kokha pa Phunziro la Nsanja ya Olonda lotsatira lenilenilo?—Miy. 15:23.