Kodi Sitinazimvepo Zimenezi?
1 Ndithudi tinazimvapo! Yehova amabwerezabwereza zinthu zambiri m’Mawu ake kuti anthu ake apindule. Yesu nthaŵi zambiri anali kubwereza ziphunzitso zake zokhudza mbali zosiyanasiyana za Ufumu. Atumwi ake nthaŵi zonse anali kubwereza nkhani zauzimu ndi awo amene anali okhazikika m’choonadi.—Aroma 15:15; 2 Pet. 1:12, 13; 3:1, 2.
2 M’nthaŵi yathu gulu la Yehova lakonza nkhani zofunika kwambiri kuti zizibwerezedwa nthaŵi ndi nthaŵi pamisonkhano yampingo. Mabuku ena aphunziridwa mobwerezabwereza. Inde, n’kofunikadi kumva zinthu zimene tinazimvapo kale!
3 Kubwereza Kumakwaniritsa Chinthu Chofunika Kwambiri: Zikumbutso za Yehova zimawonjezera kamvedwe kathu, kukhwimitsa malingaliro athu, ndiponso kulimbikitsa chidaliro chathu kuti tikhalebe panjira yauzimu. (Sal. 119:129) Kubwereza miyezo ya Mulungu ndi malangizo ake kuli ngati kuyang’ana pagalasi. Kumatithandiza kuti tidzipende ndi kuthetsa chizoloŵezi chokhala “wakumva wakuiwala.”—Yak. 1:22-25.
4 Ngati sitidzikumbutsa za choonadi, mitima yathu idzakopeka ndi zinthu zina. Zikumbutso za Mulungu zimatilimbikitsa kukana zisonkhezero zoipa za dziko la Satana. (Sal. 119:2, 3, 99, 133; Afil. 3:1) Zikumbutso zimene timalandira nthaŵi zonse zokhudza kukwaniritsidwa kwa zifuno za Mulungu zimatilimbikitsa kukhala ‘odikira.’ (Marko 13:32-37) Kubwerezedwa kwa choonadi cha m’Malemba kumatithandiza kukhalabe panjira ya kumoyo wosatha. —Sal. 119:144.
5 Mmene Aliyense Angapindulire: Tiyenera ‘kulingitsa mitima yathu ku mboni za Mulungu.’ (Sal. 119:36) Pamene nkhani yodziŵika ikukaphunziridwa pamsonkhano wampingo, tiyenera kukonzekereratu, ŵerengani malemba omwe asonyezedwa, ndipo lingalirani mmene tingagwiritsire ntchito chidziŵitsocho. Tisaphonye kukonzekera kubwereramo kolemba kwa m’Sukulu ya Utumiki wa Teokalase, tikumaganiza kuti n’kosafunika. (Luka 8:18) Tisayese kukhala wosamvetsera chifukwa chakuti ziphunzitso za choonadi zimabwerezedwa kaŵirikaŵiri pamisonkhano yathu.—Aheb. 5:11.
6 Tikhaletu ndi maganizo onga a wamasalmo akuti: “Ndinakondwera m’njira ya mboni zanu, koposa ndi chuma chonse.” (Sal. 119:14) Inde, chuma chamtengo wapatali chimenechi tinachimvapo kale, ndipo mosakayikira tidzachimvanso. Chifukwa chiyani? Yehova akudziŵa kuti tifunika kuchimva!