Chisonkhezero cha Mabwenzi ndi Mwayi Wanu Wolalikira
1 Chisonkhezero cha mabwenzi n’champhamvu. Amatisonkhezera kuchita zabwino kapena zoipa. Atumiki a Yehova anzathu amatisonkhezera kuchita zinthu zabwino zimene zimatifulumiza kuntchito zabwino zachikristu. (Aheb. 10:24) Komabe, am’banja lathu, anzathu akuntchito, anzathu akusukulu, anansi athu, ndi ena odziŵana nawo amene si Mboni angatilimbikitse kuyenda m’njira yosemphana ndi mfundo zachikhalidwe zachikristu. Angamalankhule ‘zosinjirira mayendedwe [athu] abwino pamene tikutsata Khristu.’ (1 Pet. 3:16, Buku Loyera) Ndi motani mmene tingakhalirebe otsimikiza mtima kupitiriza kulalikira ngakhale tikumane ndi chisonkhezero choipa cha mabwenzi?
2 Am’banja Lathu: Nthaŵi zina, mwamuna komanso bambo amene sali wa Mboni za Yehova sangafune kuti mkazi wake ndi ana ake azilalikira. Zinachitikapo m’banja lina ku Mexico. Mkazi ndi ana asanu ndi aŵiri a mwamuna wina analoŵa choonadi. Poyamba mwamunayo ankatsutsa chifukwa sankafuna kuti banja lake lizilalikira n’kumagaŵira mabuku ofotokoza Baibulo kunyumba ndi nyumba. Ankati zimenezi n’zosapatsa ulemu. Komabe, mkazi wake ndi ana akewo, analimbikira chosankha chawo chotumikira Yehova ndi kumaloŵa mu utumiki nthaŵi zonse. M’kupita kwa nthaŵi, mwamuna uja anayamba kuona kufunika komvera makonzedwe a Mulungu pantchito yolalikira, ndipo iyenso anadzipatulira kwa Yehova. Zinam’tengera zaka 15 kuti alandire choonadi, koma kodi mwamunayo akanatero chikhala kuti banja lake silinaumirire mwayi wawo wolalikira?—Luka 1:74; 1 Akor. 7:16.
3 Anzathu Akuntchito: Kuyesetsa kwanu kulalikira anzanu akuntchito sikungawasangalatse ena. Mlongo wina akuti atayamba kukambirana nkhani ya kutha kwa dziko muofesi, anam’seka chifukwa chakuti anawapempha kuti akaŵerenge Mateyu chaputala 24. Komabe, patatha masiku angapo, mmodzi wa anzake aja kuntchito anamuuza kuti anaŵerenga chaputala chija ndipo anachita chidwi. Anam’gaŵira buku, ndipo anakonza zakuti aziphunzira naye Baibulo ndi mwamuna wake yemwe. Tsiku loyamba anaphunzira mpaka 2 koloko ya m’maŵa. Ataphunzira katatu, anayamba kupita ku misonkhano, ndipo posakhalitsa analeka kusuta fodya ndipo anayamba kuloŵa mu utumiki. Kodi izi zikanachitika chikhala kuti mlongo wathuyo sanayesetse kuuza ena chiyembekezo chake?
4 Anzathu Akusukulu: Si zachilendo Mboni zachinyamata kusonkhezeredwa ndi mabwenzi akusukulu ndiponso kuopa kunyozedwa ndi achinyamata anzawo chifukwa cholalikira. Ku United States, Mkristu wina wachinyamata anati: “Ndinkaopa kulalikira achinyamata anzanga chifukwa ndinkaopa kusekedwa.” Choncho ankapeŵa kulalikira achinyamata anzake kusukulu komanso m’gawo. Kodi mungazipeze kuti mphamvu zogonjetsera chisonkhezero cha mabwenzi? Khulupirirani Yehova, funani chiyanjo chake. (Miy. 29:25) Nyadirani chifukwa chodziŵa kugwiritsa ntchito Mawu a Mulungu mu utumiki wanu. (2 Tim. 2:15) Wachinyamata amene wagwidwa mawuyo anapemphera kwa Yehova, kum’pempha kuti am’thandize kukhala n’chilakolako cholankhula kwa anzake akusukulu. Anayamba kuchitira umboni wamwamwayi kusukulu, panatsatira zabwino, ndipo mosakhalitsa anayamba kulankhula kwa aliyense amene amam’dziŵa. Ananena kuti: “Achinyamata amenewo amasoŵa komanso amafuna chiyembekezo cha m’tsogolo, ndipo Yehova akutigwiritsa ntchito ifeyo kuti tiwathandize.”
5 Anansi: Mwina tili ndi anansi kapena ena odziŵana nawo amene sasangalala nafe chifukwa cha amene tili ndiponso chifukwa cha zikhulupiriro zathu. Ngati mumaopa zimene amaganiza, dzifunseni kuti: ‘Kodi amadziŵa choonadi chotsogolera ku moyo wosatha? Kodi ndingatani kuti ndiwafike pamtima?’ Woyang’anira dera wina ananena kuti pamakhala zotsatira zabwino ngati tichitira umboni kwa anansi athu pang’onopang’ono. Pemphani kwa Yehova mphamvu ndi nzeru zofunikira kuti mupitirize kufunafuna oona mtima.—Afil. 4:13.
6 Kugonjera zisonkhezero zoipa za mabwenzi kumasangalatsa otsutsa, koma kodi zimenezo zidzawathandiza iwowo kapena kutithandiza ifeyo? Yesu anatsutsidwa ndi anthu a m’dera lake lomwe. Anapirira ngakhale mawu opweteketsa mtima a abale ake. Koma anadziŵa kuti angawathandize kokha ngati akhalabe wokhulupirika panjira imene Mulungu anamuikira. N’chifukwa chake Yesu “adapirira ndi ochimwa otsutsana naye.” (Aheb. 12:2, 3) Tiyenera kuchita chimodzimodzi. Tsimikizani mtima kugwiritsa ntchito mwayi wanu wonse wolalikira uthenga wabwino wa Ufumu. Potero, ‘mudzadzipulumutsa inu eni ndi iwo akumva inu.’—1 Tim. 4:16.