CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | LEVITIKO 12-13
Zimene Tingaphunzire pa Malamulo Okhudza Khate
Kodi mfundo za m’malamulo okhudza khate zingatiphunzitse chiyani pa nkhani ya kuteteza moyo wathu wauzimu?
Yehova anaphunzitsa ansembe zimene angachite kuti azindikire khate likangoyamba. Masiku anonso, abusa a Chikhristu amathandiza mwachangu munthu amene wayamba kudwala mwauzimu.—Yak 5:14, 15
Aisiraeli ankafunika kuwononga chinthu chilichonse chodetsedwa ndi khate kuti matendawo asafalikire. Akhristu nawonso ayenera kusiya chilichonse, ngakhale chimene amachikonda kwambiri, chomwe chingawachititse kuchimwa. (Mt 18:8, 9) Zimenezi zingaphatikizepo zinthu monga makhalidwe awo, anzawo komanso zosangalatsa
Kodi Mkhristu angasonyeze bwanji kuti akufuna kuthandizidwa ndi Yehova?