Kodi Zinthu Zopanda Chilungamo Zidzatha Padzikoli?
Zikuoneka kuti anthu padziko lonse akukumana ndi zinthu zopanda chilungamo. Tiyeni tione zitsanzo ziwiri za anthu amene anamangidwa popanda zifukwa zomveka:
Mu January 2018, woweruza milandu m’khoti la ku United States, analamula kuti bambo wina yemwe anakhala m’ndende kwa zaka pafupifupi 38 atulutsidwe. Zinadziwika kuti bamboyu sanapalamule mlandu womwe anamumangirawo pambuyo poyeza DNA yake.
Mu September 1994, anyamata atatu a m’dziko lina la ku Africa anamangidwa atakana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira. Pofika mu September 2020, anyamatawa anali atagwira ukaidi kwa zaka 26. Komabe, ndondomeko yowazengera mlandu sinatsatidwe ndiponso sanapatsidwe mwayi wokaonekera kukhoti.
Ngati anthu akukuchitirani zinthu zopanda chilungamo, mwina mungamve ngati mmene anamvera Yobu yemwe anati: “Ndakhala ndikufuula popempha thandizo, koma chilungamo sichikupezeka.” (Yobu 19:7) Ngakhale kuti zingaoneke ngati zosatheka kukhala m’dziko lachilungamo, koma Baibulo limatilonjeza kuti m’tsogolomu padzikoli padzakhala chilungamo chenicheni. Komanso mfundo za m’Baibulo zingakuthandizeni kudziwa zoyenera kuchita ngati mukukumana ndi zinthu zopanda chilungamo panopa.
Ndi Ndani Amene Amachititsa Zinthu Zopanda Chilungamo?
Anthu amene safuna kutsatira malangizo a Mulungu ndi amene amayambitsa zinthu zopanda chilungamo. Baibulo limasonyeza kuti chilungamo chenicheni chimachokera kwa Mulungu. (Yesaya 51:4) M’Baibulo, mawu amene anawamasulira kuti “chiweruzo” ndi akuti “chilungamo,” amayendera limodzi. (Salimo 33:5) Zinthu zomwe ndi zolungama, zolondola kapena zoyenera mogwirizana ndi mfundo za Mulungu, zimachititsa kuti pakhale chilungamo. Mosiyana ndi zimenezi, zinthu zopanda chilungamo zimachitika chifukwa cha uchimo, zomwe ndi zosemphana ndi mfundo zolungama za Mulungu. Tiyeni tione zitsanzo zotsatirazi:
Kudzikonda. Kudzikonda kumayendera limodzi ndi uchimo. (Yakobo 1:14, 15) Anthu odzikonda amachitira ena zinthu zopanda chilungamo n’cholinga choti apeze zomwe akufuna. Mosiyana ndi zimenezi, Mulungu amafuna kuti tiziika zofuna za ena patsogolo pa zofuna zathu.—1 Akorinto 10:24.
Kuchita zinthu mosazindikira. Anthu ena angachitire ena zinthu zopanda chilungamo chifukwa chosazindikira. Komabe Mulungu amaona kuti kuchita zimenezi ndi tchimo. (Aroma 10:3) Chifukwa chosazindikira, anthu ena m’mbuyomu anapha Yesu Khristu. Ndipotu zimene anachitazi kunali kupanda chilungamo kwakukulu kwambiri.—Machitidwe 3:15, 17.
Mabungwe ndiponso mfundo za anthu zomwe n’zosathandiza. Andale, amalonda komanso magulu azipembedzo amanena kuti angathetse zinthu zopanda chilungamo zomwe zikuchitika padzikoli. Koma m’malomwake, anthu amenewa ndi amene amayambitsa mavuto monga katangale, tsankho, dyera, kudyerana masuku pamutu pa nkhani za chuma ndiponso kusagwirizana. Zinthu zimenezi n’zimene zingayambitse zinthu zopanda chilungamo. Koma zotsatirapo zake n’zakuti zoyesayesa za anthu onse amene satsatira malangizo a Mulungu siziphula kanthu.—Mlaliki 8:9; Yeremiya 10:23.
Kodi Mulungu zimamukhudza anthu akamachita zinthu zopanda chilungamo?
Inde, iye amadana ndi zinthu zopanda chilungamo ndiponso chilichonse chimene chimayambitsa zimenezi. (Miyambo 6:16-18) Mulungu anauzira mneneri Yesaya kuti alembe mawu akuti: “Pakuti ine Yehovaa ndimakonda chilungamo. Ndimadana ndi zauchifwamba ndi kupanda chilungamo.”—Yesaya 61:8.
Lamulo limene Mulungu anapereka kwa Aisiraeli m’mbuyomu limasonyeza kuti iye ankafuna kuti anthuwo azichita zinthu mwachilungamo. Iye analamula oweruza awo kuti azikana kulandira ziphuphu komanso kuchita zinthu zomwe zingapotoze chilungamo. (Deuteronomo 16:18-20) Mulungu anadzudzula Aisiraeli omwe sankamumvera podyera masuku pamutu anthu osauka ndi onyozeka ndipo pamapeto pake anawasiya chifukwa choti analephera kutsatira mfundo zake.—Yesaya 10:1-3.
Kodi Mulungu adzathetsa zinthu zopanda chilungamo?
Inde. Mulungu adzagwiritsa ntchito Yesu Khristu kuti adzachotse uchimo womwe umachititsa kuti anthu azichita zinthu zopanda chilungamo n’kuwathandiza kuti akhalenso angwiro ngati mmene ankafunira poyamba. (Yohane 1:29; Aroma 6:23) Iye wakhazikitsanso Ufumu womwe udzabweretsa dziko latsopano lolungama ndipo anthu onse azidzachita zinthu mwachilungamo. (Yesaya 32:1; 2 Petulo 3:13) Kuti mudziwe zambiri zokhudza Ufumu womwe uli kumwambawu, onerani vidiyo yakuti Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?
Kodi moyo udzakhala wotani m’dziko latsopano lolungama?
Padzikoli pakadzakhala mtendere wokhawokha anthu onse azidzakhala mwamtendere komanso motetezeka. (Yesaya 32:16-18) Mulungu amaona kuti moyo wa munthu aliyense ndi wofunika, choncho adzachitira anthu onse zinthu mwachilungamo. Iye adzachotseratu mavuto amene amayamba chifukwa cha zinthu zopanda chilungamo monga chisoni, kulira ndiponso kupweteka ndipo m’kupita kwa nthawi, sitidzamvanso ululu kapena kukumbukira chilichonse chokhudza zinthu zopanda chilungamo. (Yesaya 65:17; Chivumbulutso 21:3, 4) Kuti mumve zambiri werengani nkhani yakuti “Kodi Ufumu wa Mulungu Udzachita Chiyani?”
Kodi muyenera kukhulupiriradi zomwe Mulungu analonjeza kuti adzathetsa zinthu zopanda chilungamo?
Inde. Baibulo lili maulosi odalirika, limafotokoza molondola mbiri yakale komanso nkhani zokhudza sayansi ndiponso mfundo zake zonse n’zogwirizana. Zimenezi zikusonyeza kuti muyenera kukhulupirira zimene Baibulo limalonjeza. Mungaone mfundo zina m’nkhani zotsatirazi:
Kodi n’zotheka kuthetsa zinthu zopanda chilungamo panopa?
Baibulo limanena za anthu ena okhulupirika akale amene anachita zomwe akanatha kuti zinthu zopanda chilungamo zisawachitikire. Mwachitsanzo, Ayuda ananamizira mtumwi Paulo kuti wapalamula mlandu womwe ukanachititsa kuti aphedwe. Podziwa kuti sanalakwe, iye sanalole kuti zinthu zopanda chilungamozo zimuchitikire koma anagwiritsa ntchito malamulo a pa nthawiyo ndipo anapempha kuti mlandu wake ukaweruzidwe ndi Kaisara.—Machitidwe 25:8-12.
Komabe, anthu sangathetse zinthu zopanda chilungamo padzikoli ngakhale atayesetsa bwanji. (Mlaliki 1:15) Ngakhale zili choncho, anthu ambiri aona kuti kukhulupirira kwambiri zimene Mulungu analonjeza zokhudza dziko latsopano lolungama, kwawathandiza kuti akhale ndi mtendere wamumtima zinthu zopanda chilungamo zikamawachitikira.
a Yehova ndi dzina la Mulungu.—Salimo 83:18.