7 “Yehova Mulungu wanu akadzakulowetsani mʼdziko limene mwatsala pangʼono kulitenga kuti likhale lanu,+ adzakuchotseraninso mitundu ikuluikulu.+ Adzakuchotserani Ahiti, Agirigasi, Aamori,+ Akanani, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi,+ mitundu 7 ikuluikulu komanso yamphamvu kuposa inu.+