11 Pamapeto pake Samueli anafunsa Jese kuti: “Kodi anyamata ako onse ndi omwewa basi?” Iye anayankha kuti: “Wamng’ono kwambiri sanabwerebe,+ pakuti akuweta nkhosa.”+ Chotero Samueli anauza Jese kuti: “Tumiza munthu akam’tenge, chifukwa sitikhala pansi kuti tidye kufikira iye atabwera pano.”