1 Samueli
16 Patapita nthawi, Yehova anauza Samueli kuti: “Kodi ulirira Sauli+ mpaka liti, pamene ine ndamukana kuti alamulire monga mfumu ya Isiraeli?+ Thira mafuta m’nyanga yako+ ndipo unyamuke. Ndikutumiza kwa Jese+ wa ku Betelehemu, chifukwa ndapeza munthu pakati pa ana ake aamuna woti akhale mfumu yanga.”+ 2 Koma Samueli anati: “Ndipita bwanji? Sauli akangomva andipha ndithu.”+ Atatero, Yehova anamuuza kuti: “Popita utenge ng’ombe yaikazi yaing’ono pakati pa ng’ombe zako, ndipo ukanene kuti, ‘Ndabwera kudzapereka nsembe kwa Yehova.’+ 3 Ukakatero ukaitanire Jese kopereka nsembeko, ndipo ine ndidzakuuza zochita.+ Kumeneko ukandidzozere+ munthu amene ndidzakusonyeza.”
4 Samueli anachita zimene Yehova anamuuza. Atafika ku Betelehemu,+ akulu a mzindawo anayamba kunjenjemera+ atakumana naye. Ndiyeno iwo anati: “Kodi n’kwabwino?”+ 5 Iye anayankha kuti: “Inde, n’kwabwino. Ndabwera kudzapereka nsembe kwa Yehova. Dziyeretseni,+ ndipo mupite nane kopereka nsembe.” Chotero iye anayeretsa Jese ndi ana ake, kenako anawaitanira kopereka nsembe. 6 Tsopano zimene zinachitika n’zakuti, pamene iwo anali kulowa, ndipo Samueli ataona Eliyabu,+ nthawi yomweyo anati: “Mosakayikira wodzozedwa wake waonekera pamaso pa Yehova.” 7 Koma Yehova anauza Samueli kuti: “Usaone maonekedwe ake ndi kutalika kwa msinkhu wake,+ pakuti ine ndamukana ameneyu. Chifukwa mmene munthu amaonera si mmene Mulungu amaonera.+ Munthu amaona zooneka ndi maso,+ koma Yehova amaona mmene mtima ulili.”+ 8 Pamenepo, Jese anaitana Abinadabu+ kuti adutse pamaso pa Samueli, koma Samueli anati: “Yehova sanasankhenso ameneyu.” 9 Kenako Jese anaitana Shama+ kuti adutse, koma Samueli anati: “Yehova sanasankhenso ameneyu.” 10 Choncho Jese anadutsitsa ana ake 7 pamaso pa Samueli. Koma Samueli anauza Jese kuti: “Yehova sanasankhe aliyense mwa amenewa.”
11 Pamapeto pake Samueli anafunsa Jese kuti: “Kodi anyamata ako onse ndi omwewa basi?” Iye anayankha kuti: “Wamng’ono kwambiri sanabwerebe,+ pakuti akuweta nkhosa.”+ Chotero Samueli anauza Jese kuti: “Tumiza munthu akam’tenge, chifukwa sitikhala pansi kuti tidye kufikira iye atabwera pano.” 12 Iye anatumadi munthu kukam’tenga. Mnyamatayo anali wamaonekedwe ofiirira,+ mnyamata wa maso okongola, ndiponso wooneka bwino. Pamenepo Yehova anati: “Ndi ameneyu! Nyamuka umudzoze.”+ 13 Choncho Samueli anatenga nyanga ya mafuta+ ndi kum’dzoza pakati pa abale ake. Zitatero, mzimu wa Yehova unayamba kugwira ntchito pa Davide kuyambira tsiku limenelo mpaka m’tsogolo.+ Kenako Samueli ananyamuka kupita ku Rama.+
14 Tsopano mzimu wa Yehova unachoka+ pa Sauli, ndipo Yehova analola maganizo oipa*+ kum’vutitsa Sauli. 15 Zitatero, atumiki a Sauli anayamba kumuuza kuti: “Taonani tsopano, mzimu woipa wa Mulungu ukukuvutitsani. 16 Mbuye wathu, chonde, lamulani kuti atumiki anu amene ali pamaso panu akufunireni katswiri+ woimba zeze.+ Ndiyeno mzimu woipa wa Mulungu ukabwera pa inu, iye azikuimbirani zezeyo, ndipo inu muzipeza bwino.” 17 Chotero Sauli anauza atumiki ake kuti: “Chonde, ndipezereni munthu wodziwa kuimba, ndipo mubwere naye kuno.”+
18 Mmodzi mwa atumikiwo anayankha, kuti: “Inetu ndinaona luso loimba+ la mwana wa Jese wa ku Betelehemu. Iye ndi mwamuna wolimba mtima ndiponso wamphamvu,+ mwamuna wankhondo,+ wolankhula mwanzeru+ ndi wooneka bwino,+ komanso Yehova ali naye.”+ 19 Atamva zimenezi, Sauli anatuma mithenga kwa Jese, kuti: “Nditumizire mwana wako Davide amene akuweta nkhosa.”+ 20 Pamenepo Jese anatenga bulu, mkate, thumba lachikopa+ la vinyo ndi mwana wa mbuzi, ndipo anazitumiza kwa Sauli kudzera mwa Davide mwana wake.+ 21 Choncho Davide anapita kwa Sauli ndipo anali kum’tumikira.+ Sauli anam’konda kwambiri Davide, moti anakhala womunyamulira zida zake.+ 22 Zitatero, Sauli anatumiza uthenga kwa Jese, kuti: “Chonde, lola kuti Davide apitirize kunditumikira, chifukwa ndam’konda.” 23 Ndiyeno mzimu woipa wa Mulungu ukafika pa Sauli, Davide anali kutenga zeze ndi kumuimbira. Akatero, Sauli anali kupeza bwino, ndipo mzimu woipawo unali kum’chokera.+