22 Matanthauzo a Mawu Ena
A B C D G H K L M N P S T U W Y Z
A
Afarisi.
Gulu lotchuka lachipembedzo chachiyuda limene linalipo m’nthawi ya Yesu. Anthu ena a m’gulu limeneli analinso akuluakulu a m’Khoti Lalikulu la Ayuda.
Alefa ndi Omega.
Alembi.
Amenewa anali anthu okopera Malemba Achiheberi. Pofika nthawi ya Yesu, mawu akuti “alembi” ankanena za gulu la anthu amene anaphunzira Chilamulo.
Aloye.
Mtengo umene unali kutulutsa utomoni ndi zinthu zina zafungo lonunkhira zimene kale anali kupangira mafuta odzola onunkhira bwino.
Asaduki.
Gulu lotchuka lachipembedzo chachiyuda limene linali kugwirizana ndi ansembe. Anthu ena a m’gulu limeneli analinso akuluakulu a m’Khoti Lalikulu la Ayuda.
Aserafi.
Angelo amene amaima pafupi ndi mpando wachifumu wa Yehova kumwamba.
Azazeli.
Mawu amene anali kuwagwiritsa ntchito ponena za mbuzi imene anali kuitumiza kuchipululu. Malinga ndi malemba akale achiheberi, zikuoneka kuti mawuwa anapangidwa pophatikiza mawu awiri otanthauza “mbuzi” ndi “kuzimiririka.” Choncho mawuwa amatanthauza “Mbuzi Imene Imazimiririka.” Mawu achigiriki amene anawagwiritsa ntchito m’Baibulo la Septuagint amatanthauza “wonyamula (kupewa) zoipa.”
B
Basamu.
Zomera, zitsamba ndi mitengo yosiyanasiyana imene inali kutulutsa utomoni wonunkhira ndi wamafuta. Basamu anali wamtengo wapatali kwambiri kwa anthu a Kum’mawa.
C
Chaka cha Ufulu.
Chimenechi chinali chaka chilichonse cha nambala 7 kuyambira pamene Aisiraeli analowa m’Dziko Lolonjezedwa. Chaka chonse cha ufulu chinali chaka cha chikondwerero kapena kuti chaka chomasuka.
Chihema Chokumanako.
Mawu amenewa akunena za hema la Mose komanso chihema chopatulika chimene Aisiraeli anapanga m’chipululu. Zikuoneka kuti chinali kutchedwa chihema chokumanako chifukwa chakuti anthu ankapita kumeneko kukafunsira kwa Yehova, choncho anali kukumana ndi Yehova kumeneko.
Chihema chopatulika.
Chinali nyumba ya Aisiraeli yopembedzeramo Mulungu yopangidwa ndi tenti. Chihema chimenechi anali kuyenda nacho, ndipo nthawi zina chimatchedwanso kuti “chihema chokumanako.”
Chikole.
Chinthu chopatsa munthu wina pomutsimikizira kuti lonjezo limene walonjezedwa lidzakwaniritsidwadi, kapena pomutsimikizira kuti munthu amene wamupatsa ngongole adzabweza ngongoleyo.
Chikwere.
Ndi chinthu chonyamuliramo mbalame kapena nkhuku.
Chilimwe.
Nyengo yotentha pamene sikugwa mvula.
Chinganga.
Choimbira chachitsulo chooneka ngati chimbale chimene amachimenyanitsa ndi chinzake poimba.
Chisanu.
Nyengo yozizira kwambiri.
Chishango.
Chida chachikulu chodzitetezera pa nkhondo chimene kale mitundu yonse ya anthu inali kugwiritsa ntchito. Chinkakhala ndi chogwirira mkati mwake ndipo msilikali ankachinyamula ndi dzanja lamanzere.
Chithaphwi.
Dzenje losazama kwambiri pamene madzi aimapo.
Chitsime.
Panali zitsime zina zosiyana ndi zitsime zimene ndi zodziwika kwambiri. Zitsime zimenezi sizinkatulutsa madzi pazokha, koma ankazikumba kuti muzifikira madzi a mvula kapena madzi ochokera pakasupe.
Chiunda chomenyerapo nkhondo.
Chiunda chomenyerapo nkhondo chinali chimulu cha dothi kapena chimulu cha miyala chimene gulu la nkhondo linali kuunjika pafupi ndi mpanda wolimba kwambiri wa mzinda wa adani. Anali kumanga chiunda chimenechi kuti chikhale malo okwera oti azifika pa mpandawo ndi zida zawo zankhondo zowonongera mzindawo, komanso zida zina zogwiritsa ntchito poukira adaniwo.
Chivundikiro chophimba machimo.
Chimenechi chinali chivundikiro cha likasa la pangano. Mkulu wa ansembe anali kudontheza magazi a nsembe yamachimo kutsogolo kwa likasalo pa Tsiku la Mwambo Wophimba Machimo.
D
Dilili.
Mbewu imene inali kubzalidwa ku Palesitina ndipo njere zake ndi zonunkhira. Njerezo anali kuzigwiritsa ntchito popanga zokometsera chakudya komanso mankhwala a m’mimba.
Dinari.
Imeneyi inali ndalama yasiliva ya Aroma. Ndalama imeneyi anaipanga kuti izioneka ngati mutu wa Kaisara. M’masiku a utumiki wa Yesu padziko lapansi, anthu ogwira ntchito yolima ankalandira dinari imodzi akagwira ntchito ya maola 12.
Dipo.
Malipiro owombolera munthu kapena chinthu kuti chimasulidwe ku mlandu kapena pa mavuto ena ake. Mawuwa amatanthauzanso kusinthanitsa kapena kubweza chinthu chofanana ndendende.
G
Galeta.
Ngolo yokokedwa ndi mahatchi imene nthawi zambiri anali kuigwiritsa ntchito pomenya nkhondo.
Gumbwa.
Chomera chachikulu cha mtundu wa mlulu kapena mantchedza. Gumbwa amamera m’mphepete mwa madzi ndipo anali kumugwiritsa ntchito popanga zinthu zosiyanasiyana monga zolembapo, mphasa kapena mabasiketi.
H
Haramagedo.
Kutanthauza “Phiri la Megido.” Nkhondo ya Haramagedo idzachitika padziko lonse lapansi m’tsogolo muno. Pa nkhondo imeneyi Yesu Khristu amene ndi Mfumu yodzozedwa ndi Yehova adzawononga adani a Mulungu.
K
Kalamasi.
Kamtengo kamene anali kukagwiritsa ntchito popanga mafuta onunkhira.
Kalonga.
M’Baibulo dzina laulemu lakuti “kalonga” limatanthauza atsogoleri osiyanasiyana a m’mafuko a Isiraeli, akuluakulu a boma ngakhalenso mkulu wa asilikali. (Ge 12:15; 1Mb 27:22; Es 3:12; Yer 38:17, 18, 22) Yehova amatchedwa kuti “Kalonga wa khamu” ndiponso “Kalonga wa akalonga.” (Da 8:11, 25) Mikayeli mkulu wa angelo amatchedwa kuti “kalonga wamkulu.” (Da 12:1) Ziwanda zimene zinali kutsogolera maulamuliro amphamvu kwambiri padziko lonse, a Perisiya ndi Girisi, zimatchedwanso kuti akalonga m’Baibulo.—Da 10:13, 20.
Kasiya.
Mtengo wa m’gulu la Sinamoni umene khungwa lake anali kuligwiritsa ntchito popanga mafuta onunkhira.
Kerubi.
Mngelo wapamwamba wokhala ndi maudindo apadera.
Khalidwe lotayirira.
Khalidwe limeneli si kungochita zolakwa zing’onozing’ono ayi. Limatanthauza kuchita machimo akuluakulu amene amaphwanya malamulo a Mulungu. Munthu wakhalidwe limeneli amachita zinthu zoipa mopanda mantha zimene zimasonyeza kuti ali ndi mtima wonyoza komanso salemekeza olamulira ndi malamulo.
Khristu.
Kutanthauza “Wodzozedwa.” Limeneli si dzina longofuna kusiyanitsira Ambuye Yesu ndi anthu ena amene ali ndi dzina lakuti Yesu, koma ndi dzina laudindo wake.
Kufunkha.
Kutenga katundu wa anthu amene agonjetsedwa pa nkhondo.
Kukhulupirira mizimu.
Buku lina lomasulira mawu a m’Baibulo limanena kuti mawu amenewa amatanthauza kugwiritsa ntchito mankhwala ndi kuchita zamatsenga. Pochita zamatsengazo anthu amagwiritsa ntchito mankhwala ndipo amanena mawu kapena kuimba nyimbo yopempha mphamvu kwa mizimu. Iwo amagwiritsanso ntchito zithumwa ndi zinthu zina zimene amakhulupirira kuti zimachotsa mphamvu ya ziwanda.
Kukoma mtima kwakukulu.
Mfundo yaikulu ya mawuwa ndi chinthu chosangalatsa ndi chokopa. Mawuwa angatanthauzenso mphatso imene munthu wapereka mokoma mtima kapena khalidwe labwino lokonda kupatsa ena mphatso. Komanso angatanthauze kuyamikira kapena kuthokoza chifukwa chochitiridwa zinthu mokoma mtima, kapena kukomera mtima munthu amene sakuyenera kumukomera mtima.
Kuphimba machimo.
Mfundo yaikulu ya mawuwa ndi “kuphimba” kapena “kusinthanitsa,” kapenanso chinthu chimene chimaperekedwa posinthanitsa ndi chinthu china kapena kuphimba chinthu chinachake. Chinthu chimene akuphimbacho kapena chimene akusinthanitsacho chiyenera kukhala chofanana ndendende ndi chinthu chinacho.
Kuusa moyo.
Kupuma kokoka mpweya wambiri kusonyeza kukhumudwa kapena kutopa.
L
Likasa la pangano.
Bokosi lopatulika limene linali kukhala m’Malo Oyera Koposa a m’chihema chopatulika. Pambuyo pake linali kukhala m’kachisi amene Solomo anamanga. Yehova ndiye analamula kuti bokosi limeneli lipangidwe ndipo anapereka malangizo a mmene angalipangire. M’bokosili anali kusunga miyala iwiri yosema pamene analembapo Malamulo 10.
Lipenga.
Chipangizo choimbira mochita kuuzira mpweya cha kukamwa kwakukulu.
Lubani.
Zinthu zonunkhira zimene amachita kuzitentha kuti zitulutse fungo lonunkhira.
Luwe.
Chomera chonunkhira kwambiri chimene mwina chinali kulimidwa ku Palesitina, ndipo anali kuchigwiritsa ntchito popanga mankhwala ndi zokometsera chakudya.
M
Malo okwezeka.
Anali kungotanthauza malo okwera, zitunda ndi mapiri, koma kawirikawiri anali kunena za nyumba kapena akachisi kumene anali kulambirirako mafano. Choncho kawirikawiri “Malo okwezeka” amagwirizana ndi kulambira konyenga.
Malo Oyera Koposa.
Chipinda chamkati kwambiri cha chihema chopatulika. Kachisi atamangidwa analinso ndi chipinda chotero. Chipindachi chimatchedwanso Malo Opatulikitsa.
Malo Oyera.
Chipinda chachikulu choyambirira cha chihema chopatulika. Kachisi atamangidwa analinso ndi chipinda chotero. Chipinda chimenechi chinali chosiyana ndi chipinda chachiwiri chamkati mwenimweni chimene chinali kutchedwa Malo Oyera Koposa.
Manda achikumbutso.
Mawu achigiriki amene tawamasulira kuti “manda achikumbutso” amatanthauza kuti chilichonse chokhudza munthu amene wamwalira chikukumbukiridwabe. Mawu amenewa amatsindika mfundo yakuti munthu womwalirayo akukumbukiridwabe.
Matangadza.
Chipangizo chakale cholangira munthu komanso kumumangira kuti asathawe. Chinali chopangidwa ndi matabwa ndipo anali kumangiriramo mapazi a munthu, ndiponso nthawi zina manja ndi mutu womwe, iye atakhala pansi.
Mdyerekezi.
Kutanthauza “wonenera ena zoipa.” Satana anapatsidwa dzina limeneli chifukwa ndiye mtsogoleri wonenera ena zoipa komanso wonenera Yehova zabodza.
Mdzakazi.
Wantchito wamkazi amene nthawi zina mbuye wake anali kumutenga ngati mkazi wake. Panali adzakazi a mitundu itatu: (1) Mtsikana wachiheberi amatha kugulitsidwa ndi bambo ake kuti akakhale kapolo. (2) Munthu amatha kugula kapolo wamkazi kudziko lina. (3) Mtsikana amatha kugwidwa kunkhondo n’kutengedwa kukhala kapolo.
Mesiya.
Amenewa ndi mawu achiheberi otanthauza kuti “wodzozedwa.” Pa Chigiriki amati Khristu.
Minti.
Kuyambira kale chomera chimenechi chakhala chikugwiritsidwa ntchito monga mankhwala ndi zokometsera chakudya, chifukwa chakuti masamba ake ndi mtengo wake zili ndi mafuta onunkhira bwino.
Mkate wachionetsero.
Mikate 12 imene anali kuiika patebulo m’Malo Oyera muchihema chopatulika kapena m’kachisi. Mikate imeneyi anali kuichotsa pa tsiku lililonse la Sabata ndi kuikapo ina yatsopano.
Mnaziri.
Kutanthauza “Wosankhidwa Kuchokera Pakati pa Anzake,” “Wodzipereka,” “Wopatulidwa.” Panali magulu awiri a Anaziri: Amene anali kufuna okha kuti akhale Anaziri ndi amene anachita kusankhidwa ndi Mulungu kuti akhale Anaziri.
Mpaka kalekale.
Mawuwa angathenso kunena za zinthu zimene zidzakhalapo kwamuyaya. Koma kawirikawiri amanena za zinthu zimene zili ndi pothera. Timanena kuti zinthuzo zidzakhala ‘mpaka kalekale’ chifukwa chakuti nthawi imene zidzathe sikudziwika.
Mpukutu.
Mtundu wa zolembapo zimene zinali kugwiritsidwa ntchito pa nthawi imene Baibulo linalembedwa. Nthawi zambiri zinali zopangidwa ndi zikopa kapena gumbwa. Malemba anali kulembedwa ndi kukopedwa pa zinthu zimenezi. Kuti apange mpukutu ankamata zinthu zimenezi zingapo n’kupanga cholembapo chachitali chimene anali kuchikulunga kumtengo.
Mtima wosagawanika.
Mawu akuti “mtima wosagawanika” ali ndi tanthauzo la kukhala wowongoka, wopanda cholakwa, wolungama ndi wopanda chifukwa. Komabe kukhala ndi mtima wosagawanika kumafuna zambiri osati kungochita zinthu zabwino zokha. Kumafuna kukhala ndi makhalidwe abwino komanso kudzipereka kwa Mulungu ndi mtima wonse.
Mule.
Utomoni wonunkhira wolimbirapo wochokera kuzitsamba zaminga zosiyanasiyana ndi mitengo ing’onoing’ono. Mitengoyi ndi makungwa ake zimakhala ndi fungo lamphamvu. Utomoniwu anali kuugwiritsa ntchito zosiyanasiyana, monga kupangira mafuta onunkhira, zinthu zokometsera chakudya ndi mankhwala osiyanasiyana.
Mwana wa munthu.
M’Mauthenga Abwino, mawu amenewa akupezeka maulendo pafupifupi 80 ndipo nthawi zonse amanena za Yesu Khristu. Mawu amenewa amasonyeza kuti Mwana wa Mulungu pa nthawiyo analidi munthu. Amasonyezanso kuti Yesu adzakwaniritsa ulosi wopezeka pa Da 7:13, 14.
Mzimu woyera.
Mphamvu imene Mulungu amagwiritsa ntchito kapena kutumiza kuti akwaniritse zilizonse zimene akufuna. Pogwiritsa ntchito mphamvu imeneyi, Mulungu analenga zinthu zakumwamba, dziko lapansi ndi zamoyo zonse.
N
Nduwira (ya mkulu wa ansembe).
Nsalu imene wansembe anali kuikulunga kumutu kwake ngati duku. Patsogolo pake ankamangirirapo kachitsulo kagolide ndi chingwe cha buluu. N’kuthekanso kuti nsalu imeneyi ankaisoka kuti ikhale ngati chipewa.
Ngale.
Mwala wamtengo wapatali wolimba ndi wosalala umene umanyezimira ndipo umaoneka kuti uli ndi mitundu yosiyanasiyana.
Nisani.
Dzina la mwezi woyamba pakalendala yopatulika yachiyuda imene Ayuda anali kugwiritsa ntchito atabwerera kwawo kuchokera ku ukapolo. Mwezi umenewu unali kuyambira kumapeto kwa mwezi wa March mpaka kumayambiriro kwa mwezi wa April. Poyamba mwezi umenewu ankautcha kuti Abibu.
Nsembe yachakumwa.
Nsembe imeneyi inali kuperekedwa pamodzi ndi nsembe zina. Chakumwa chake chinali vinyo kapena kuti “chakumwa choledzeretsa,” ndipo anali kuchithira paguwa la nsembe.
Nsembe yoweyula.
Zikuoneka kuti munthu akabwera kudzapereka nsembe imeneyi, amanyamula nsembeyo m’manja mwake. Ndiyeno wansembe ankaika manja ake kunsi kwa manja a munthuyo n’kumayendetsa nsembeyo uku ndi uku. Kapena wansembeyo anali kuyendetsa yekha chinthu chimene chikuperekedwa nsembecho uku ndi uku. N’kutheka kuti poyendetsa nsembeyo, wansembe anali kuilozetsa kuguwa lansembe.
Nthawi.
Mawu amene tawamasulira kuti “nthawi” (chigiriki, ai·onʹ) angatanthauze makamaka mmene zinthu zikukhalira nthawi zambiri, mmene zinthu zilili, kapena zochitika zimene zachititsa nthawi inayake yaitali, kapena nyengo inayake, kukhala yosiyana ndi ina. Mawuwa sakunena za nthawi wamba.
Nthungo.
Mkondo waung’ono wopepukirapo.
P
Pasika.
Pasika ndi mwambo wokumbukira kupulumutsidwa kwa Aisiraeli ku Iguputo ndi kupulumuka kwa ana awo oyamba kubadwa pamene mngelo wa Yehova anali kupha ana oyamba kubadwa a Aiguputo. Mwambo umenewu unayambika usiku woti mawa lake ana a Isiraeli achoka ku Iguputo.
Pentekosite.
Dzina limene Malemba Achigiriki amatchulira Chikondwerero cha Zokolola (Eks 23:16), kapena Chikondwerero cha Masabata (Eks 34:22). Chikondwerero chimenechi chimatchedwanso “tsiku la zipatso zoyamba kucha” (Nu 28:26). Chikondwererochi chinali kuchitika pa tsiku la 50 kuchokera pa tsiku la Nisani 16. Mawu akuti Pentekosite amatanthauza “Tsiku la 50.”
Phula.
Zinthu zofewa zachikasu zimene njuchi zimapanga. Nthawi zambiri zimakhala polowera njuchizo ndipo zimasungunuka zikatentha.
S
Sabata.
Tsiku limene Mulungu analipatula kuti likhale lopuma pa ntchito ya nthawi zonse. Yehova anapereka Sabata monga chizindikiro pakati pa iyeyo ndi ana a Isiraeli. Chilamulo cha Mose chimanenanso za Masabata a zaka.
Satana.
Kutanthauza “Wotsutsa.” Limeneli ndi dzina la Mdani Wamkulu wa Mulungu.
Sinamoni.
Mtengo umene khungwa lake anali kuligwiritsa ntchito popanga mafuta onunkhira.
Sulufule.
Miyala imene imayaka mosavuta. Moto wake umakhala wotentha kwambiri ndiponso wonunkha.
Sunagoge.
Mawuwa amatanthauza “msonkhano,” koma m’malemba ambiri akunena za malo kumene Ayuda anali kusonkhana kuti apemphere ndi kuwerenga Malemba.
T
Tsiku la Chiweruzo.
Limeneli ndi “tsiku” kapena kuti nyengo inayake, pamene magulu a anthu, mitundu ya anthu ndi anthu onse adzaweruzidwe ndi Mulungu. Ingakhalenso nthawi imene anthu amene anaweruzidwa kale kuti sayenera kukhala ndi moyo adzaphedwe. Pa nthawi imeneyi anthu ena adzapulumutsidwa ndi kulandira moyo wosatha.
U
Urimu ndi Tumimu.
Zinthu zimene anali kuzigwiritsa ntchito kuti adziwe zimene Mulungu akufuna pa nkhani zokhudza mtundu wonse wa Isiraeli zimene zimafunika kuti Yehova ayankhepo.
W
Wokana Khristu.
Mawu ake enieni, “kutsutsana ndi (kapena m’malo mwa) Khristu.” Mawuwa akunena za anthu onse amene amatsutsa kapena kunamizira kuti iwowo ndi Khristu. Akunenanso za anthu onse amene amanamizira kuti ndi oimira Khristuyo komanso amene amatsutsa zimene Mawu a Mulungu amanena zokhudza Khristu.
Y
Yehova wa makamu.
Mawu akuti “Yehova wa makamu” amasonyeza mphamvu zimene Wolamulira wa chilengedwe chonse, amene amalamulira makamu a zolengedwa zauzimu, ali nazo.
Z
Zeze.
Chipangizo choimbira chooneka ngati uta chokhala ndi zingwe.
Zigamulo.
Yehova Mulungu, monga Woweruza, Wopereka Malamulo komanso Mfumu anapatsa mtundu wa Isiraeli malamulo ambiri. Zigamulo zake pa nkhani zokhudza milandu zinali ngati mfundo zothandiza popereka chigamulo kwa munthu ndiponso pa nkhani zokhudza mtundu wonsewo.
Ziwanda.
Mizimu yoipa yosaoneka imene ili ndi mphamvu kuposa za anthu. Mizimu imeneyi ndi angelo amene sanamvere Mulungu m’masiku a Nowa ndipo anagwirizana ndi Satana popandukira Yehova.