Kodi Ukwati Unayamba Bwanji Nanga Cholinga Chake N’chiyani?
“Yehova Mulungu anati: ‘Si bwino kuti munthu akhale yekha. Ndimupangira womuthandiza, monga mnzake womuyenerera.’”—GEN. 2:18.
1, 2. (a) Kodi ukwati unayamba bwanji? (b) Kodi Yehova ankafuna kuti mwamuna ndi mkazi oyamba adziwe zotani zokhudza ukwati? (Onani chithunzi pamwambapa.)
UKWATI ndi nkhani yaikulu kwambiri kwa anthufe. Choncho tiyeni tikambirane mmene unayambira komanso cholinga chake. Izi zitithandiza kukhala ndi maganizo oyenera pa nkhaniyi komanso kuti tizisangalala m’banja. Yehova atalenga Adamu, anamubweretsera nyama zonse kuti azitchule mayina. Koma Adamuyo “analibe womuthandiza, monga mnzake womuyenerera.” Ndiyeno Mulungu anamugonetsa tulo tofa nato n’kumuchotsa nthiti. Kenako anamupangira mkazi pogwiritsa ntchito nthitiyo n’kumubweretsera. (Werengani Genesis 2:20-24.) Choncho Mulungu ndi amene anayambitsa ukwati.
2 Yesu anasonyeza kuti Yehova ndi amene ananena kuti: “Pa chifukwa chimenechi mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake n’kudziphatika kwa mkazi wake, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi.” (Mat. 19:4, 5) Zimene Yehova anachita pogwiritsa ntchito nthiti ya mwamuna n’kupanga mkazi, zinasonyeza kuti ankafuna kuti anthuwo azikondana komanso kugwirizana kwambiri. Sanafune kuti iwo adzalekane kapena kuchita mitala.
UKWATI UMAKWANIRITSA CHOLINGA CHA YEHOVA
3. Kodi cholinga cha Yehova poyambitsa ukwati chinali chiyani?
3 Adamu ataona mkazi wakeyo, anasangalala kwambiri ndipo anamupatsa dzina loti Hava. Iye analidi mnzake womuyenerera ndipo ankasangalala naye tsiku lililonse chifukwa choti ankathandizana zinthu zambiri. (Gen. 2:18) Cholinga cha Yehova chinali choti banjali likhale ndi ana n’kudzaza dziko lapansi. (Gen. 1:28) Ngakhale kuti ana amakonda makolo awo, Yehova ankafuna kuti akakula azisiya makolowo, n’kukayamba banja lawo. Izi zikanachititsa kuti anthu adzaze bwinobwino padzikoli n’kulisintha lonse kukhala Paradaiso.
4. Fotokozani zimene zinachitika m’banja loyambirira.
4 Koma Adamu ndi Hava analephera kumvera Yehova ndipo banja lawo linayamba kukumana ndi mavuto. Zomwe zinachitika n’zakuti Satana Mdyerekezi, yemwe amatchedwanso “njoka yakale ija,” anapusitsa Hava pomuuza kuti adye chipatso cha “mtengo wodziwitsa chabwino ndi choipa.” Anamuuza kuti akadya, akhala ndi nzeru zapadera moti azitha kusiyanitsa yekha chabwino ndi choipa. Hava anachita zinthu mopanda ulemu chifukwa sanafunse kaye mwamuna wake za nkhaniyo. Nayenso Adamu m’malo momvera Mulungu anangolandira chipatso chimene Hava anamupatsa, n’kudya.—Chiv. 12:9; Gen. 2:9, 16, 17; 3:1-6.
5. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Adamu ndi Hava anayankha atafunsidwa ndi Yehova?
5 Mulungu atafunsa za nkhaniyi, Adamu anaimba mlandu mkazi wake. Iye anati: “Mkazi amene munandipatsayu ndi amene wandipatsa chipatso cha mtengowo, ndipo ine ndadya.” Nayenso Hava ananena kuti njoka ndi imene inamulakwitsa. (Gen. 3:12, 13) Zifukwa zimene ankaperekazi zinali zosamveka. Kusamvera kwawoku kunasonyeza kuti akuderera Yehova ndipo sankafuna kuti aziwalamulira. Kodi tikuphunzirapo chiyani? Kuti banja likhale losangalala, aliyense ayenera kumvera Yehova komanso kuvomereza zimene walakwitsa.
6. Kodi mawu a pa Genesis 3:15 amatanthauza chiyani?
6 Satana atayambitsa mavuto m’munda wa Edeni, Yehova ananena ulosi woyamba m’Baibulo wonena za tsogolo labwino la anthu. (Werengani Genesis 3:15.) Iye ananena kuti Satanayo adzaphwanyidwa ndi ‘mbewu ya mkazi.’ Ponena kuti mkazi ankatanthauza gulu lakumwamba la angelo ake. Apatu Yehova anathandiza anthu kudziwa mgwirizano umene ulipo pakati pa iyeyo ndi gulu la angelo kumwambako. Kenako, Malemba anayamba kusonyeza kuti Mulungu adzatumiza winawake kuchokera m’gulu lakumwambali kuti adzaphwanye Mdyerekezi. Zimenezi zidzathandiza kuti anthu omvera apeze moyo wosatha mogwirizana ndi cholinga cha Mulungu choyambirira.—Yoh. 3:16.
7. (a) Kodi zimene Adamu ndi Hava anachita zakhudza bwanji mabanja? (b) Kodi Baibulo limalimbikitsa mwamuna ndi mkazi kuti azichita chiyani?
7 Zimene Adamu ndi Hava anachita zinayambitsa mavuto m’banja lawo komanso mabanja onse. Mwachitsanzo, zinachititsa kuti Hava ndiponso akazi onse azivutika akakhala oyembekezera komanso akamabereka. Zinachititsanso kuti akazi azikhumba amuna awo koma amunawo aziwapondereza ndi kuwachitira nkhanza ngati mmene zilili m’mabanja ambiri masiku ano. (Gen. 3:16) Koma Baibulo limalimbikitsa amuna kuti azikonda akazi awo. Limanenanso kuti akazi ayenera kugonjera amuna awo. (Aef. 5:33) Mwamuna ndi mkazi akakhala oopa Mulungu komanso ogwirizana, mavuto amachepa m’banja mwinanso kutheratu.
KUCHOKERA NTHAWI YA ADAMU KUDZAFIKA NTHAWI YA CHIGUMULA
8. Kodi zinthu zinali bwanji pa nkhani ya ukwati kuchokera nthawi ya Adamu kufika nthawi ya Chigumula?
8 Adamu ndi Hava asanafe, anabereka ana aamuna ndi aakazi. (Gen. 5:4) Mwana wawo woyamba anali Kaini, ndipo anakwatira mmodzi mwa achibale ake. Munthu woyamba kutchulidwa m’Baibulo kuti anali ndi akazi awiri anali Lameki ndipo anali wochokera ku banja la Kaini. (Gen. 4:17, 19) Pa anthu amene anakhalako kuchokera nthawi ya Nowa kufika nthawi ya Chigumula, ndi anthu ochepa okha amene ankalambira Yehova. Ena mwa anthuwa anali Abele, Inoki komanso Nowa ndi banja lake. M’nthawi ya Nowa “ana a Mulungu woona anayamba kuona kuti ana aakazi a anthu anali okongola. Chotero, anayamba kudzitengera okha akazi alionse amene anawasankha.” Ndiyeno angelowa ndi akaziwo anabereka ziphona zankhanza zotchedwa Anefili. Komanso ‘kuipa kwa anthu kunachuluka padziko lapansi, ndipo malingaliro onse a m’mitima ya anthu anali oipa okhaokha.’—Gen. 6:1-5.
9. Kodi anthu oipa a m’nthawi ya Nowa zinawathera bwanji, nanga ifeyo tikuphunzirapo chiyani?
9 Yehova anabweretsa Chigumula m’nthawi ya Nowa ndipo chinawononga anthu onse oipa. Pa nthawiyo anthu ankangotanganidwa ndi zinthu za tsiku ndi tsiku monga kukwatira ndi kukwatiwa. Iwo sankamvetsera uthenga woti Mulungu awononga dziko umene Nowa, yemwe anali “mlaliki wa chilungamo,” ankalalikira. (2 Pet. 2:5) Yesu ananeneratu kuti zimene zinkachitikazo zidzachitikanso masiku otsiriza ano. (Werengani Mateyu 24:37-39.) Masiku ano anthu ambiri samvetsera uthenga wa Ufumu. Uthengawu ukulalikidwa padziko lonse kuti ukhale umboni ku mitundu yonse ndipo kenako mapeto afika. Koma ifeyo tisalole kuti zinthu ngati banja komanso kulera ana zitilepheretse kukhala maso podziwa kuti tsiku la Yehova lili pafupi.
KUCHOKERA NTHAWI YA CHIGUMULA KUFIKA NTHAWI YA YESU
10.(a) Pa nthawi ya Nowa, kodi anthu ambiri ankachita zotani? (b) N’chifukwa chiyani tingati banja la Abulahamu ndi Sara linali chitsanzo chabwino?
10 Nowa anali ndi mkazi mmodzi. N’chimodzimodzinso ana ake atatu aja. Koma anthu ena pa nthawiyo ankakwatira mitala. M’zikhalidwe zambiri kuchita chiwerewere sinali nkhani ndipo ena ankaona kuti ndi mbali ya chipembedzo chawo. Pa nthawi imene Abulahamu ndi Sara ankafika ku Kanani, anthu ambiri m’dzikolo anali ndi makhalidwe oipa osalemekeza ukwati. Choncho Yehova analamula kuti mizinda ya Sodomu ndi Gomora iwonongedwe chifukwa anthu a m’mizindayi ankachita komanso kulekerera zinthu zachiwerewere zoipa kwambiri. Koma Abulahamu ankatsogolera bwino banja lake ndipo Sara ankapereka chitsanzo chabwino pogonjera mwamuna wakeyo. (Werengani 1 Petulo 3:3-6.) Abulahamu anaonetsetsanso kuti mwana wake Isaki akwatire mkazi wolambira Yehova. Nayenso Yakobo ankachita zinthu zogwirizana ndi kulambira koona. Yakobo ndi amene anadzakhala kholo la mafuko 12 a Isiraeli.
11. Kodi Chilamulo cha Mose chinkateteza bwanji Aisiraeli?
11 Patapita nthawi, Yehova anachita pangano ndi Aisiraeli ndipo anawapatsa Chilamulo cha Mose. M’chilamulochi munalinso malamulo onena za zinthu zimene anthu ankachita pa nthawiyo, monga kukwatira mitala. Chilamulo chinkateteza Aisiraeli kuti asasiye kulambira koona chifukwa chinkawaletsa kukwatirana ndi anthu osalambira Yehova. (Werengani Deuteronomo 7:3, 4.) Panali akuluakulu amene ankathandiza, m’banja mukakhala mavuto aakulu. Panalinso zoyenera kuchita ngati pali kusakhulupirika, nsanje komanso kukayikirana m’banja. Chilamulo chinkalola munthu kuthetsa banja, koma panalinso malamulo onena za nkhaniyi. Mwachitsanzo, munthu ankaloledwa kusiya mkazi wake ngati “wam’peza ndi vuto linalake.” (Deut. 24:1) Baibulo silinena kuti mawu akuti “vuto linalake” akunena za chiyani. Koma n’zodziwikiratu kuti sakunena za timavuto ting’onoting’ono.—Lev. 19:18.
MUSAMACHITIRE CHINYENGO MKAZI KAPENA MWAMUNA WANU
12, 13. (a) M’nthawi ya Malaki, kodi amuna ena ankachitira zotani akazi awo? (b) Ngati Mkhristu wasiya mwamuna kapena mkazi wake n’kukwatira wina, kodi zotsatira zake zingakhale zotani?
12 M’masiku a mneneri Malaki, Ayuda ambiri ankachitira akazi awo zachinyengo powasiya popanda zifukwa zomveka. Akatero ankakwatira atsikana kapena akazi osalambira Yehova. Zoterezi zinkachitikabe mpaka m’nthawi ya Yesu moti amuna ena ankasiya akazi awo “pa chifukwa chilichonse.” (Mat. 19:3) Koma Yehova amadana kwambiri ndi zimenezi.—Werengani Malaki 2:13-16.
13 Mpingo wachikhristu sulekerera munthu aliyense wochita chinyengo m’banja. Koma tiyerekeze kuti Mkhristu wina wapabanja wayamba chibwenzi ndi mwamuna kapena mkazi wa munthu wina. Kenako akuthetsa banja lake n’kukwatirana ndi chibwenzicho. N’zoona kuti zoterezi sizichitikachitika pakati pa Akhristu. Koma ngati Mkhristu wotereyu atapanda kulapa, angachotsedwe mumpingo n’cholinga choti mpingowo ukhalebe woyera. (1 Akor. 5:11-13) Kuti abwezeretsedwe, ayenera kuonetsa ‘zipatso zosonyeza kuti walapa.’ (Luka 3:8; 2 Akor. 2:5-10) N’zoona kuti palibe lamulo loti payenera kupita nthawi yakutiyakuti kuti munthuyo abwezeretsedwe. Komabe asanabwezeretsedwe, pamafunika kuiganizira bwino nkhaniyo ndiponso zimene anachitazo. Mwina pangatenge chaka kapena kuposa, kuti munthuyo asonyeze kuti walapadi. Koma ngakhale munthu wotereyu atabwezeretsedwa, ayenera kudziwa kuti adzayankhabe mlandu “pa mpando woweruzira milandu wa Mulungu.”—Aroma 14:10-12; onani Nsanja ya Olonda yachingelezi ya November 15, 1979, tsamba 31-32.
ZIMENE AKHRISTU AYENERA KUCHITA
14. Kodi Chilamulo chinathandiza bwanji Aisiraeli?
14 Aisiraeli anatsatira Chilamulo cha Mose kwa zaka zoposa 1,500. Chilamulochi chinathandiza anthu a Mulungu kutsatira mfundo za makhalidwe abwino zokhudza banja komanso nkhani zina. Chinawathandizanso kukonzekera kubwera kwa Mesiya. (Agal. 3:23, 24) Koma imfa ya Yesu inachititsa kuti Chilamulochi chisiye kugwira ntchito ndipo Mulungu anayamba kugwiritsa ntchito njira ina potsogolera anthu ake. (Aheb. 8:6) Zinthu zina zimene zinkaloledwa m’Chilamulo cha Mose zinali zosalolekanso.
15. (a) Kodi mpingo wachikhristu umatsatira mfundo ziti pa nkhani ya ukwati? (b) Kodi Mkhristu ayenera kuganizira mfundo ziti asanathetse banja?
15 Pa nthawi ina Afarisi anafunsa Yesu zokhudza banja. Powayankha, iye ananena kuti zimene Mose analola pa nkhani yothetsa banja, si zimene Mulungu ankafuna “kuyambira pa chiyambi.” (Mat. 19:6-8) Apa anasonyeza kuti mpingo wachikhristu uyenera kutsatira zimene Mulungu anayambitsa mu Edeni zokhudza ukwati. (1 Tim. 3:2, 12) Popeza anthu akakwatirana amakhala “thupi limodzi,” kuti banja lawo likhale lolimba ayenera kukondana kwambiri komanso kukonda Mulungu. Mkhristu angathetse banja ngati mnzakeyo wachita chigololo. Koma ngati angathetse pa zifukwa zina, sakhala womasuka kuti angakwatiranenso ndi wina. (Mat. 19:9) Mkhristu angasankhe kukhululukira mnzake amene wachita chigololo n’kulapa ngati mmene Hoseya anakhululukira Gomeri. Nayenso Yehova anakhululukira mtundu wa Isiraeli umene tingati unachita chigololo. (Hos. 3:1-5) Mfundo ina yoyenera kuikumbukira ndi yakuti, ngati mwamuna kapena mkazi wachita chigololo ndiyeno mnzakeyo wavomera kugona naye, ndiye kuti wamukhululukira ndipo palibe chifukwa cha m’Malemba chothetsera banjalo.
16. Kodi Yesu ananena zotani pa nkhani ya kusakhala pa banja?
16 Yesu atanena zoti banja siliyenera kutha pa zifukwa zina kupatula chigololo, ananenanso za anthu amene “ali ndi mphatso” yosakhala pa banja. Ndiyeno ananena kuti: “Amene angathe kuchita zimenezi achite.” (Mat. 19:10-12) Pali anthu ambiri amene asankha kusakhala pa banja n’cholinga choti azitumikira Yehova popanda zododometsa. Anthu oterewa amafunika kuwayamikira kwambiri.
17. Kodi Mkhristu angadziwe bwanji nthawi yoyenera kulowa m’banja?
17 Kodi n’chiyani chingathandize munthu kudziwa ngati ayenera kukhala pa banja kapena ayi? Munthu amafunika kuganizira nkhaniyi mofatsa n’kuona ngati angakwanitse kusakhala pa banja. Mtumwi Paulo ananena kuti kusakhala pa banja n’kwabwino. Komabe iye ananenanso kuti: “Koma chifukwa cha kuwanda kwa dama, mwamuna aliyense akhale ndi mkazi wakewake ndipo mkazi aliyense akhale ndi mwamuna wakewake.” Ndiye anapitiriza kuti: “Ngati sangathe kudziletsa, akwatire, pakuti ndi bwino kukwatira kusiyana ndi kuvutika ndi chilakolako.” Komabe munthu asanaganize zolowa m’banja, ayenera kuganiziranso za zaka zake popeza Paulo anati: “Ngati wina akuona kuti zikumuvuta kukhalabe yekha, ngati wapitirira pachimake pa unyamata, ndipo ngati ziyenera kutero, achite mmene akufunira, sachimwa. Akwatire.” (1 Akor. 7:2, 9, 36) N’zoona kuti kukhala pa banja kungathandize munthu kupewa chiwerewere kapena chizolowezi choseweretsa maliseche. Komabe munthu sayenera kusankha kukwatira kapena kukwatiwa chifukwa cha chilakolako chogonana chimene chimakhala champhamvu pa zaka zaunyamata. Chifukwa pa nthawiyi angakhale adakali wamng’ono moti sangathe kusamalira banja.—1 Tim. 4:1-3.
18, 19. (a) Kodi banja lachikhristu liyenera kuyamba bwanji? (b) Kodi tidzakambirana chiyani m’nkhani yotsatira?
18 Banja lachikhristu liyenera kuyamba ndi mwamuna komanso mkazi amene anadzipereka kwa Yehova ndipo amamukonda ndi mtima wonse. Komanso anthu amene akufuna kukwatiranawo akhale oti amakondana kwambiri ndipo akufuna kukhala limodzi moyo wawo wonse. Banja lotere limadalitsidwa chifukwa choti anthuwo anatsatira malangizo akuti akwatire kapena kukwatiwa “mwa Ambuye.” (1 Akor. 7:39) Iwo amaona kuti malangizo a m’Baibulo amawathandiza kukhala ndi banja losangalala.
19 Masiku ano amuna ndi akazi ambiri ali ndi makhalidwe amene amasokoneza mabanja awo. M’nkhani yotsatira tidzakambirana mfundo za m’Malemba zimene zingathandize Akhristu apabanja kuthana ndi mavuto amene tikukumana nawo “masiku otsiriza” ano. (2 Tim. 3:1-5) Tikuthokoza kwambiri Yehova chifukwa amagwiritsa ntchito Mawu ake potithandiza kudziwa zoyenera kuchita kuti tikhale ndi banja labwino komanso losangalala. Izi zimatithandiza kuti tipitirizebe kuyenda limodzi ndi anthu ake pamsewu wopita kumoyo wosatha.—Mat. 7:13, 14.