NKHANI YOPHUNZIRA 3
Yehova Amatithandiza Kuti Zinthu Zizitiyendera Bwino
“Yehova anakhalabe ndi Yosefe . . . , chilichonse chimene anali kuchita, Yehova anali kuchidalitsa.”—GEN. 39:2, 3.
NYIMBO NA. 30 Atate Wanga, Mulungu Wanga Ndiponso Bwenzi Langa
ZIMENE TIPHUNZIREa
1-2. (a) N’chifukwa chiyani sitimadabwa kuti timakumana ndi mayesero? (b) Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?
MONGA atumiki a Yehova sitimadabwa tikamakumana ndi mayesero. Timazindikira kuti monga mmene Baibulo limanenera, “tiyenera kukumana ndi masautso ambiri kuti tikalowe mu ufumu wa Mulungu.” (Mac. 14:22) Timadziwanso kuti mavuto athu ena sangatheretu mpaka nthawi imene tidzakhale m’dziko latsopano la Mulungu pamene “imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.”—Chiv. 21:4.
2 Yehova samatiteteza kuti tisakumane ndi mayesero. Koma amatithandiza kuti tiziwapirira. Taonani zomwe mtumwi Paulo anauza Akhristu a ku Roma. Choyamba anatchula mayesero amene iye ndi abale ndi alongo ake ankakumana nawo. Kenako analemba kuti: “Tikugonjetsa zinthu zonsezi kudzera mwa iye amene anatikonda.” (Aroma 8:35-37) Zimenezi zikutanthauza kuti Yehova angatithandize kuti zinthu zizitiyendera bwino ngakhale pa nthawi imene tikukumana ndi mayesero. Tiyeni tione mmene Yehova anathandizira Yosefe komanso mmene angatithandizire ifeyo.
ZINTHU ZIKASINTHA MOSAYEMBEKEZEREKA
3. Kodi zinthu zinasintha bwanji mosayembekezereka pa moyo wa Yosefe?
3 Yakobo anasonyeza kuti ankakonda kwambiri Yosefe. (Gen. 37:3, 4) Zimenezi zinachititsa kuti azichimwene ake azimuchitira nsanje. Pamene mpata unapezeka iwo anamugulitsa kwa amalonda a ku Midiyani. Amalondawa anamutengera kutali kwambiri ku Igupto kumene anakagulitsidwanso kwa Potifara, yemwe anali mkulu wa asilikali olondera Farao. Pamenepatu moyo wa Yosefe unasintha mofulumira kwambiri kuchoka pokhala mwana wokondedwa wa Bambo ake, n’kukhala kapolo ku Iguputo.—Gen. 39:1.
4. Kodi ifenso tingakumane bwanji ndi mavuto ofanana ndi amene Yosefe anakumana nawo?
4 Mogwirizana ndi zimene Baibulo lina limanena, “zinthu zoipa zimagwera aliyense.” (Mlal. 9:11) Nthawi zina timakumana ndi mavuto kapena mayesero omwe ‘amagweranso anthu ena.’ (1 Akor. 10:13) Kapenanso tingavutike chifukwa choti ndife ophunzira a Yesu. Mwachitsanzo, tikhoza kumanyozedwa, kutsutsidwa ngakhalenso kuzunzidwa chifukwa cha chikhulupiriro chathu. (2 Tim. 3:12) Kaya mukukumana ndi mayesero otani, Yehova angakuthandizeni kuti zinthu zikuyendereni bwino. Kodi iye anathandiza bwanji Yosefe?
5. Kodi Potifara anazindikira chiyani poona kuti zinthu zikumuyendera bwino Yosefe? (Genesis 39:2-6)
5 Werengani Genesis 39:2-6. Potifara anaona kuti Yosefe anali wachinyamata wanzeru komanso wolimbikira ntchito. Iye ankadziwanso chifukwa chake zinali choncho. Anaona kuti “chilichonse chimene [Yosefe] anali kuchita, Yehova anali kuchidalitsa.”b M’kupita kwa nthawi Mwiguputoyu anaika Yosefe kukhala wantchito wake komanso woyang’anira nyumba yake yonse. Kodi zotsatira zake zinali zotani? Zinthu zinkamuyendera bwino Potifara.
6. Kodi Yosefe ayenera kuti ankamva bwanji chifukwa cha mmene zinthu zinalili pa moyo wake?
6 Tayesani kuona nkhaniyi mmene Yosefe ankaionera. Kodi n’kutheka kuti iye ankafunitsitsa chiyani? Kodi iye ankafuna kuti Potifara aone zimene akuchita komanso kumupatsa mphoto? N’zoonekeratu kuti Yosefe ankafuna kumasulidwa kuti abwererenso kwa bambo ake. Ndipotu ngakhale kuti iye anali ndi mwayi woyang’anira nyumba yonse ya Potifara, anali kapolo wa munthu yemwe sankalambira Yehova. Yehova sanachititse kuti Potifara amasule Yosefe pa ukapolo. Ndipo zinthu zinali zitatsala pang’ono kuipa kwambiri pa moyo wa Yosefe.
NGATI ZINTHU ZAIPA KWAMBIRI
7. Kodi chinachitika n’chiyani kuti zinthu pa moyo wa Yosefe ziipireipire? (Genesis 39:14, 15)
7 Monga mmene timawerengera pa Genesis 39, mkazi wa Potifara anakopeka ndi Yosefe ndipo mobwerezabwereza ankamunyengerera kuti agone naye. Nthawi zonse Yosefe ankakana zimenezo. Pamapeto pake mkaziyo anamukwiyira ndipo anamunamizira kuti amafuna kumugwiririra. (Werengani Genesis 39:14, 15.) Potifara atamva izi anaika Yosefe m’ndende momwe anakhalamo kwa zaka zambiri. (Gen. 39:19, 20) Kodi ndende yake inali yotani? Mawu a Chiheberi omwe Yosefe anagwiritsa ntchito ponena za “ndende” angatanthauze “chitsime” kapena “dzenje,” zomwe zikutanthauza kuti munali mdima komanso ankaona kuti alibe chiyembekezo. (Gen. 40:15) Baibulo limasonyeza kuti kwa kanthawi mapazi ake anali m’matangadza komanso khosi lake linamangidwa ndi unyolo. (Sal. 105:17, 18) Zinthu zinkangoipiraipira pa moyo wake. Anachoka pokhala kapolo wodalirika n’kufika pokhala mkaidi wamba.
8. Ngakhale mayesero atakula bwanji, kodi tingakhale otsimikiza mtima za chiyani?
8 Kodi munakumanapo ndi mavuto omwe ankaipiraipira ngakhale kuti munapemphera mochokera pansi pa mtima? Zimenezi zingachitike. Yehova satiteteza kuti tisakumane ndi mavuto m’dziko lolamulidwa ndi Satanali. (1 Yoh. 5:19) Komabe mungakhale otsimikiza kuti Yehova akudziwa zimene mukukumana nazo ndipo amakuderani nkhawa. (Mat. 10:29-31; 1 Pet. 5:6, 7) Ndipotu iye amalonjeza kuti: “Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.” (Aheb. 13:5) Yehova angakuthandizeni kupirira ngakhale pamene zikuoneka kuti mwasowa mtengo wogwira. Tiyeni tione mmene anathandizira Yosefe.
9. Kodi n’chiyani chimene chikusonyeza kuti Yehova anali ndi Yosefe pamene anali m’ndende? (Genesis 39:21-23)
9 Werengani Genesis 39:21-23. Ngakhale pa nthawi yovuta yomwe anali m’ndende, Yehova anachititsa kuti zinthu zimuyendere bwino Yosefe. Motani? Patapita nthawi mkulu wandende anayamba kudalira komanso kulemekeza Yosefe ngati mmene Potifara anachitira. Posakhalitsa iye anamuika kuti akhale woyang’anira akaidi ena. Ndipotu Baibulo limati “mkulu wandendeyo sanali kuyang’aniranso chilichonse chimene chinali m’manja [mwa Yosefe].” Tsopano Yosefe anayamba kukhala wotanganidwa ndi ntchito yake. Apatu zinthu zinasintha mosayembekezereka. Kodi zinatheka bwanji kuti mkaidi yemwe ankaimbidwa mlandu wofuna kugwiririra mkazi wa nduna ya panyumba ya mfumu apatsidwe udindo waukuluwu? Ndi chinthu chimodzi chokha chomwe chikanachititsa. Monga mmene lemba la Genesis 39:23 limanenera, “Yehova anali ndi Yosefe, ndipo chilichonse chimene iye anali kuchita Yehova anali kuchidalitsa.”
10. Fotokozani chifukwa chake Yosefe sakanaona kuti chilichonse chinkamuyendera bwino.
10 Yesaninso kuona nkhaniyi mmene Yosefe ankaionera. Pambuyo poimbidwa mlandu wabodza komanso kutsekeredwa m’ndende, kodi iye ankaona kuti chilichonse chikumuyendera bwino? Kodi ankafunitsitsa chiyani? Kodi iye ankafuna kuti mkulu wandendeyo azimukonda? N’zoonekeratu kuti Yosefe ankafuna mlandu wakewu utatha n’kutulutsidwa m’ndende. Ndipotu iye anauza kapolo wina yemwe anali atatsala pang’ono kutulutsidwa kuti akapemphe Farao kuti amutulutse m’ndende yoopsayo. (Gen. 40:14) Koma munthuyo sanauze Farao nthawi yomweyo ndipo Yosefe anakhalabe m’ndendemo kwa zaka zina ziwiri. (Gen. 40:23; 41:1, 14) Komabe Yehova anapitiriza kumuthandiza kuti zinthu zizimuyendera bwino. Motani?
11. Kodi Yehova anapatsa Yosefe luso lapadera lotani, nanga zinathandiza bwanji kukwaniritsa zolinga zake?
11 Yosefe adakali m’ndende, Yehova anachititsa mfumu ya Iguputo kulota maloto awiri osautsa. Farao ankafunitsitsa kudziwa zimene malotowo ankatanthauza. Atamva kuti Yosefe amatha kumasulira maloto, iye anamuitanitsa. Mothandizidwa ndi Yehova, Yosefe anamasulira malotowo ndipo Farao anakhutira ndi malangizo othandiza omwe iye anamupatsa. Poona kuti Yehova anali ndi mnyamatayu, Farao anamuika kukhala woyang’anira chakudya m’dziko lonse la Iguputo. (Gen. 41:38, 41-44) Kenako kunagwa njala yoopsa yomwe inakhudza ku Iguputo komanso ku Kanani komwe kunkakhala abale ake a Yosefe. Apa Yosefe anali ndi mwayi wopulumutsa banja lakwawo lomwe linali mzere wodzabadwira Mesiya.
12. Kodi Yehova anachititsa kuti zinthu zimuyendere bwino Yosefe m’njira ziti?
12 Taganizirani zinthu zosayembekezereka zomwe zinachitikira Yosefe. Ndani anachititsa kuti Potifara achite chidwi ndi Yosefe yemwe anali kapolo wamba? Ndi ndani anachititsa mkulu wandende kuti amukonde ngakhale kuti anali mkaidi wotsika? Ndi ndani analotetsa Farao maloto osautsa komanso kupatsa Yosefe luso lotha kuwamasulira? Ndi ndani anachititsa kuti Yosefe apatsidwe udindo woyang’anira chakudya ku Iguputo? (Gen. 45:5) N’zodziwikiratu kuti Yehova ndi amene ankachititsa kuti zonse zimene Yosefe ankachita zizimuyendera bwino. Pamapeto pake Yehova anagwiritsa ntchito chiwembu chimene abale ake a Yosefe anamuchitira kukhala ngati njira yokwaniritsira chifuniro chake.
MMENE YEHOVA AMATITHANDIZIRA KUTI ZINTHU ZITIYENDERE BWINO
13. Kodi Yehova amalowererapo pa chilichonse chomwe chimatichitikira? Fotokozani.
13 Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani ya Yosefe? Kodi Yehova amalowererapo pa zilizonse zimene zimatichitikira? Kodi ndi amene amachititsa zilizonse zomwe zimachitika pa moyo wathu, moti zoipa zonse zimatichitikira pachifukwa chabwino? Ayi, Baibulo silifotokoza zimenezo. (Mlal. 8:9; 9:11) Komabe timadziwa kuti tikamakumana ndi mayesero, Yehova amadziwa ndipo amamvetsera kufuula kwathu kopempha thandizo. (Sal. 34:15; 55:22; Yes. 59:1) Kuwonjezera pamenepo, Yehova amatithandiza kuti tipirire mavuto alionse. Motani?
14. Kodi Yehova amatithandiza bwanji tikakhala pamavuto?
14 Njira imodzi imene Yehova amatithandizira ndi kutitonthoza komanso kutilimbikitsa, ndipo nthawi zambiri amachita zimenezo pa nthawi yoyenera. (2 Akor. 1:3, 4) Izi ndi zimene zinachitikira m’bale wina wa ku Turkmenistan dzina lake Eziz, yemwe anagamulidwa kuti akhale m’ndende kwa zaka ziwiri chifukwa cha chikhulupiriro chake. Iye anati: “M’mawa wa tsiku la mlandu wanga, m’bale wina anandisonyeza lemba la Yesaya 30:15, lomwe limati: ‘Mudzakhala amphamvu mukakhala osatekeseka ndi achikhulupiriro.’ Vesili linkandithandiza kuti mtima wanga uzikhala m’malo ndiponso ndizidalira Yehova pa chilichonse. Kuliganizira kunandithandiza pa nthawi yonse yomwe ndinali m’ndende.” Kodi mukukumbukira nthawi yomwe Yehova anakuthandizani pokutonthozani komanso kukulimbikitsani pamene munkafunikira kwambiri zimenezi?
15-16. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene zinachitikira Tori?
15 Nthawi zambiri timazindikira mmene Yehova watithandizira kupirira mayesero enaake pambuyo poti mayeserowo atha. Mlongo wina dzina lake Tori anavomereza mfundo imeneyi. Mwana wake Mason anadwala khansa kwa zaka 6, mpaka pamene anamwalira. Tori anali ndi chisoni chachikulu ndipo zimenezi n’zomveka. Iye anati, “Ndimaona kuti chimenechi chinali chinthu chopweteka kwambiri kwa ine monga mayi.” Anawonjezeranso kuti, “Ndikukhulupirira kuti makolo ambiri angavomereze kuti kuona mwana wako akuvutika n’kowawa kwambiri kusiyana n’kuti uzivutika iweyo.”
16 Ngakhale kuti mayeserowo anali opweteka kwambiri, Tori pambuyo pake anaganizira mmene Yehova anamuthandizira kupirira. Iye anati: “Ndikaganizira zimene zinkachitika, ndimaona kuti Yehova ankandithandiza mwachikondi pa nthawi yonse imene mwana wanga ankadwala. Mwachitsanzo, ngakhale pamene Mason wadwala kwambiri moti sakutha kuzindikira omwe abwera kudzamuona, abale ndi alongo ankayenda pagalimoto kwa maola awiri kubwera kuchipatala komwe tinali. Nthawi zonse pankakhala munthu yemwe wabwera mofunitsitsa kuti adzatithandize. Komanso tinkapatsidwa zinthu zomwe tinkafunikira. Ngakhale pa nthawi yovuta kwambiri sitinasowepo kanthu.” Yehova anapatsa Tori ndi Mason zomwe ankafunikira kuti athe kupirira. Onani bokosi lakuti, “Yehova Ankatipatsa Zenizeni Zomwe Tinkafunikira.”
MUZIGANIZIRA MADALITSO ANU
17-18. N’chiyani chingatithandize kuti tizizindikira komanso kuyamikira mmene Yehova amatithandizira pa nthawi ya mayesero? (Salimo 40:5)
17 Werengani Salimo 40:5. Munthu amene akukwera phiri cholinga chake chimakhala kukafika pamwamba penipeni pa phirilo. Komabe akafika pamalo ena amaima n’kusangalala ndi zomwe akuona. Mofanana ndi zimenezi nthawi zina muziima kaye n’kuganizira mmene Yehova akukuthandizirani kuti zinthu zikuyendereni bwino ngakhale pamene mukukumana ndi mavuto. Kumapeto kwa tsiku lililonse muzidzifunsa kuti: ‘Kodi Yehova wandipatsa madalitso ati lero? Ngakhale kuti ndikukumanabe ndi mayesero, kodi Yehova akundithandiza bwanji kuwapirira?’ Muzipeza ngakhale dalitso limodzi lochokera kwa Yehova lomwe lakuthandizani kuti zinthu zikuyendereni bwino.
18 N’zoona kuti mungapemphere kuti mayeserowo athe. Zimenezo n’zomveka ndiponso ndi zoyenera. (Afil. 4:6) Koma tiyeneranso kumaganizira madalitso amene tikupeza panopa. Ndipotu Yehova akulonjeza kuti adzatilimbitsa komanso kutithandiza kuti tipirire. Choncho nthawi zonse muziyamikira kuti Yehova akukuthandizani. Mukatero mudzaona mmene akukuthandizirani kuti zinthu zizikuyenderani bwino ngati mmene anathandizira Yosefe ngakhale pa nthawi ya mayesero.—Gen. 41:51, 52.
NYIMBO NA. 32 Khalani Okhulupirika kwa Yehova
a Tikamakumana ndi mayesero ovuta tisamaganize kuti Yehova sakutithandiza. Nthawi zina tingamaone ngati zinthu zatiyendera bwino mayeserowo akatha. Komabe zimene zinachitikira Yosefe zikutiphunzitsa mfundo yofunika kwambiri yakuti Yehova angatithandize kuti zinthu zizitiyenderabe bwino ngakhale pa nthawi imene tikukumana ndi mayesero. Munkhaniyi tiona mmene iye amachitira zimenezi.
b Baibulo limafotokoza m’mavesi ochepa chabe mmene zinthu zinasinthira pa moyo waukapolo wa Yosefe, koma n’kutheka kuti zimenezi zinachitika kwa zaka zingapo.