Mutu 15
‘Ndani Ali Woyenera Kutsegula Mpukutu?’
1. Kodi kenako Yohane anaona chiyani m’masomphenyawa?
MASOMPHENYA amene Yohane anaona anali aulemerero komanso ochititsa chidwi kwambiri. Iye anaona mpando wachifumu wa Yehova umene unali pakati pa nyale zamoto, akerubi, akulu 24 ndiponso nyanja yoyera mbee! ngati galasi. Kodi kenako Yohane anaona chiyani? Iye akutifotokozera zimene zinkachitika pakatikati pa zonsezi, kuti: “Kenako, ndinaona mpukutu wolembedwa mkati ndi kunja komwe, uli m’dzanja lamanja la Iye wokhala pampando wachifumu. Unali womatidwa mwamphamvu ndi zidindo 7 zomatira. Ndipo ndinaona mngelo wamphamvu akulengeza ndi mawu okweza kuti: ‘Ndani ali woyenera kumatula zidindo zimene amatira mpukutuwu ndi kuutsegula?’ Koma sipanapezeke ndi mmodzi yemwe, kaya kumwamba, padziko lapansi, kapena pansi pa nthaka, wotha kutsegula mpukutuwo kapena kuyang’anamo ndi kuuwerenga. Choncho ine ndinalira kwambiri chifukwa sipanapezeke wina aliyense woyenera kutsegula mpukutuwo, kapena kuyang’anamo ndi kuuwerenga.”—Chivumbulutso 5:1-4.
2, 3. (a) N’chifukwa chiyani Yohane ankafunitsitsa kuti papezeke winawake wotsegula mpukutuwo, koma kodi zinthu zinali bwanji? (b) Kodi m’nthawi yathu ino, atumiki odzozedwa a Mulungu akhala akuyembekezera chiyani mwachidwi?
2 Yehova, yemwe ndi Ambuye Wamkulu Koposa, ndi amene wanyamula mpukutuwu. Mpukutuwo walembedwa mkati ndi kunja komwe, choncho uyenera kuti uli ndi mfundo zochuluka zofunika kwambiri. Zimenezi zikutichititsa kufuna kudziwa zimene zili mumpukutuwo. Komanso, tikukumbukira mawu amene Yehova anauza Yohane pomuitana kuti: “Kwera kumwamba kuno, ndikuonetse zinthu zimene ziyenera kuchitika.” (Chivumbulutso 4:1) Choncho, tili ndi chidwi chachikulu chofuna kudziwa zinthu zimenezi. Koma pali vuto limodzi. Mpukutuwo ndi wotseka ndipo wamatidwa mwamphamvu ndi zidindo 7 zomatira.
3 Kodi mngelo wamphamvuyo akanapeza aliyense woyenera kutsegula mpukutuwo? Malinga ndi Baibulo linalake (Kingdom Interlinear), mpukutuwo unali “padzanja lamanja” la Yehova. Mfundo imeneyi ingasonyeze kuti iye waugwira m’dzanja lake lotambasula. Koma zikuoneka kuti kumwamba konse komanso padziko lapansi, palibe aliyense amene ali woyenera kulandira mpukutuwo ndi kuutsegula. Ngakhale pansi pa nthaka, pagulu la atumiki a Mulungu okhulupirika amene anamwalira, palibe aliyense amene ali woyenera kuchita utumiki wapamwamba umenewu. Choncho, n’zosadabwitsa kuti Yohane anayamba kulira. Mwina iye ankaganiza kuti sathanso kudziwa “zinthu zimene ziyenera kuchitika.” M’nthawi yathu inonso, atumiki odzozedwa a Mulungu akhala akudikira mwachidwi kuti Yehova awaunikire ndiponso awadziwitse choonadi chokhudza mfundo za m’buku la Chivumbulutso. Ndipo Yehova amachita zimenezi pang’onopang’ono pa nthawi yake yoyenera pamene masomphenyawo akukwaniritsidwa. Iye amachita zimenezi pofuna kutsogolera anthu ake ku ‘chipulumutso chachikulu.’—Salimo 43:3, 5.
Amene Ali Woyenera
4. (a) Kodi ndani amene anapezeka kuti ndi woyenera kutsegula mpukutuwo ndi kumatula zidindo zake? (b) Kodi Akhristu odzozedwa komanso anzawo ali ndi mwayi ndiponso madalitso otani masiku ano?
4 Koma panapezeka winawake amene akanatha kutsegula mpukutuwo. Yohane akutiuza kuti: “Koma mmodzi wa akulu aja anandiuza kuti: ‘Tonthola. Taona! Mkango wa fuko la Yuda, muzu wa Davide, anapambana pa nkhondo moti iye ndiye woyenera kumatula zidindo 7 zimene amatira mpukutuwo ndi kuutsegula.’” (Chivumbulutso 5:5) Choncho, Yohane anasiya kulira. Akhristu odzozedwa ndi anzawo okhulupirika masiku ano nawonso apirira kwa zaka zambiri pozunzidwa mwankhanza, uku akudikira moleza mtima kuti aunikiridwe mwauzimu. Tsopano tadalitsidwa kwambiri chifukwa tikumvetsa tanthauzo la masomphenyawo, ndiponso tili ndi mwayi waukulu chifukwa tikukwaniritsa nawo masomphenyawo polengeza uthenga wake kwa anthu ena.
5. (a) Kodi Yakobo ananena ulosi wotani wokhudza Yuda, ndipo mbadwa za Yuda zinkalamulira kuti? (b) Kodi Silo ndani?
5 Mngeloyo anatchula za “Mkango wa fuko la Yuda.” Yohane ankadziwa bwino ulosi umene Yakobo, kholo la mtundu wa Ayuda, ananena wokhudza Yuda, amene anali mwana wake wamwamuna wachinayi. Yakobo anati: “Yuda ndi mwana wa mkango. Umapha nyama n’kubwerako ndithu, mwana wanga. Iye amapinda mawondo ake n’kudziwongola ngati mkango utagona pansi. Ndipo monga mkango, ndani angamudzutse? Ndodo yachifumu sidzachoka kwa Yuda, ndiponso chibonga cha wolamulira sichidzachoka pakati pa mapazi ake, kufikira Silo atabwera. Ndipo mitundu ya anthu idzamumvera.” (Genesis 49:9, 10) M’fuko la Yuda ndi mmene munkachokera mafumu omwe ankalamulira anthu a Mulungu. Kuyambira ndi Davide, mafumu onse amene ankalamulira ku Yerusalemu mpaka nthawi imene Ababulo anawononga mzindawo, anali mbadwa za Yuda. Koma pa mafumu amenewa panalibe Silo, yemwe analoseredwa ndi Yakobo. Dzina lakuti Silo limatanthauza “Mwiniwake [Woyenerera].” Malinga ndi ulosi, dzina limeneli limanena za Yesu, amene tsopano ndiye mwiniwake wa Ufumu wa Davide mpaka kalekale.—Ezekieli 21:25-27; Luka 1:32, 33; Chivumbulutso 19:16.
6. Kodi Yesu anakhala bwanji “nthambi” ya Jese ndiponso “muzu wa Davide”?
6 Yohane anazindikira mwamsanga amene ankaimiridwa ndi “muzu wa Davide.” M’maulosi, Mesiya wolonjezedwa amatchedwa ‘nthambi yotuluka pachitsa cha Jese [amene anali bambo a Mfumu Davide], . . . mphukira’ ndiponso “muzu wa Jese womwe udzaimirire ngati chizindikiro kwa anthu.” (Yesaya 11:1, 10) Yesu anali nthambi ya Jese chifukwa anabadwira m’banja lachifumu la Davide, mwana wa Jese. Komanso, monga muzu wa Jese, iye anachititsa kuti ufumu wa Davide uphukirenso, poupatsa moyo ndi zinthu zonse zofunikira kuti ukhalebe moyo mpaka kalekale.—2 Samueli 7:16.
7. N’chifukwa chiyani Yesu ali woyenera kulandira mpukutu uja m’dzanja la wokhala pampando wachifumu?
7 Kuposa wina aliyense, Yesu ndi amene anatumikira Yehova ndi mtima wosagawanika pamene ankakumana ndi mayesero oopsa kwambiri ali munthu wangwiro. Iye anapereka yankho lamphamvu pa bodza limene Satana ananena. (Miyambo 27:11) Choncho, pa usiku woti mawa lake afa imfa yansembe, iye ananena kuti: “Ndaligonjetsa dziko ine.” (Yohane 16:33) Pa chifukwa chimenechi, Yesu ataukitsidwa, Yehova anam’patsa “ulamuliro wonse . . . kumwamba ndi padziko lapansi.” Pa atumiki onse a Mulungu, ndi iye yekha amene ali woyenera kulandira mpukutu uja n’cholinga choti adziwitse ena uthenga wofunika kwambiri umene uli mumpukutuwo.—Mateyu 28:18.
8. (a) Pa nkhani ya Ufumu, n’chiyani chikusonyeza kuti Yesu ndi woyenera? (b) N’chifukwa chiyani zinali zoyenera kuti mmodzi wa akulu 24 auze Yohane za munthu woyenera kutsegula mpukutu?
8 N’zoyeneradi kuti Yesu atsegule mpukutu uja. Iye anaikidwa pampando wachifumu mu 1914 monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu wa Mesiya. Ndipo mumpukutuwu muli mauthenga ambiri onena za Ufumu umenewu ndiponso zimene udzachite. Pamene anali padziko lapansi, Yesu ankalalikira mokhulupirika za choonadi cha Ufumuwu. (Yohane 18:36, 37) Iye anaphunzitsa otsatira ake kuti azipemphera kuti Ufumuwo ubwere. (Mateyu 6:9, 10) Anayambitsanso ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu chakumayambiriro kwa nthawi yathu ino ndipo analosera kuti ntchito yolalikirayi idzafika pachimake m’nthawi yamapeto. (Mateyu 4:23; Maliko 13:10) Motero, zinali zoyeneranso kuti mmodzi wa akulu 24 aja auze Yohane kuti Yesu ndi amene ali woyenera kumatula zidindo za mpukutuwo. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti akulu amenewa akhala m’mipando yachifumu ndiponso avala zisoti zachifumu, ndipo ndi olandira cholowa anzake a Khristu mu Ufumu wake.—Aroma 8:17; Chivumbulutso 4:4.
‘Mwana wa Nkhosa Amene Anaphedwa’
9. M’malo moona mkango, kodi Yohane anaona chiyani chitaimirira “pafupi ndi mpando wachifumu,” ndipo iye anachifotokoza bwanji?
9 Yohane anayang’anitsitsa kuti aone “Mkango wa fuko la Yuda” umenewu. Koma anadabwa kwambiri kuona kuti pabweranso chinthu china chosiyaniratu ndi zimenezi. Iye anati: “Kenako ndinaona mwana wa nkhosa wooneka ngati wophedwa, ataimirira pafupi ndi mpando wachifumu uja ndi zamoyo zinayi, ndi pakati pa akulu aja. Iye anali ndi nyanga 7, ndi maso 7. Maso amenewo akuimira mizimu 7 ya Mulungu, imene yatumizidwa m’dziko lonse lapansi.”—Chivumbulutso 5:6.
10. Kodi “mwana wa nkhosa” amene Yohane anaona akuimira ndani, ndipo n’chifukwa chiyani zimenezi zili zoyenerera?
10 Patsogolo pa mpando wachifumu, pakatikati pa bwalo la akulu 24 komanso pafupi ndi zamoyo zinayi zija, panali mwana wa nkhosa. N’zosakayikitsa kuti Yohane anazindikira mofulumira kuti mwana wa nkhosa ameneyu ndi “Mkango wa fuko la Yuda” ndiponso “muzu wa Davide.” Iye ankadziwa kuti zaka zoposa 60 m’mbuyomo, Yohane M’batizi anauza Ayuda anzake kuti Yesu ndi “Mwanawankhosa wa Mulungu amene akuchotsa uchimo wa dziko!” (Yohane 1:29) Pa nthawi yonse imene Yesu anakhala ndi moyo padziko lapansi, sanadetsedwe ndi dzikoli, ndipo anakhala ngati mwana wa nkhosa wopanda chilema. Choncho, iye anatha kupereka moyo wake wosalakwa monga nsembe yopulumutsa anthu.—1 Akorinto 5:7; Aheberi 7:26.
11. N’chifukwa chiyani sitinganene kuti n’kupanda ulemu kuyerekezera Yesu amene ali mu ulemerero wake ndi “mwana wa nkhosa wooneka ngati wophedwa”?
11 Kodi tinganene kuti n’kupanda ulemu kapena kunyoza kuyerekezera Yesu amene ali mu ulemerero wake ndi “mwana wa nkhosa wooneka ngati wophedwa”? Ayi. Zimene Yesu anachita pokhalabe wokhulupirika mpaka imfa yake zinasonyeza kuti Satana wagonjetsedwa kotheratu ndipo Yehova Mulungu wapambana kwambiri. Kuyerekezera Yesu mwa njira imeneyi kukusonyeza bwino kuti iye anagonjetsa dziko la Satanali ndiponso zikutikumbutsa kuti Yesu ndi Yehova amakonda kwambiri anthu. (Yohane 3:16; 15:13; yerekezerani ndi Akolose 2:15.) Choncho, zimenezi zikusonyeza kuti Yesu ndi Mbewu yolonjezedwa, ndipo ndi woyenerera bwino kutsegula mpukutu uja.—Genesis 3:15.
12. Kodi nyanga 7 za Mwanawankhosa zikuimira chiyani?
12 Kodi n’chiyaninso chimene chikutichititsa kuyamikira kwambiri “mwana wa nkhosa” ameneyu? Mwana wa nkhosayo ali ndi nyanga 7. Nthawi zambiri Baibulo limagwiritsa ntchito nyanga ngati chizindikiro choimira mphamvu kapena udindo, ndipo 7 akuimira kukwanira. (Yerekezerani ndi 1 Samueli 2:1, 10; Salimo 112:9; 148:14.) Motero, nyanga 7 za Mwanawankhosa zikuimira mphamvu zokwanira zimene Yehova wapereka kwa Yesu. Iye ali “pamwambamwamba kuposa boma lililonse, ulamuliro uliwonse, amphamvu onse, ambuye onse, ndi dzina lililonse loperekedwa kwa wina aliyense, osati mu nthawi ino yokha, komanso imene ikubwerayo.” (Aefeso 1:20-23; 1 Petulo 3:22) Yesu wakhala akusonyeza mphamvu za ulamuliro, makamaka kuyambira mu 1914 pamene Yehova anamuika pampando wachifumu kumwamba monga Mfumu.—Salimo 2:6.
13. (a) Kodi maso 7 a Mwanawankhosa akuimira chiyani? (b) Kodi Mwanawankhosayo anachita chiyani?
13 Komanso, Yesu ndi wodzazidwa mokwanira ndi mzimu woyera, monga mmene maso 7 a Mwanawankhosa akusonyezera. Izi zili choncho chifukwa “maso amenewo akuimira mizimu 7 ya Mulungu.” Kudzera mwa Yesu, Yehova amapereka mphamvu yake yokwanira yogwira ntchito kwa atumiki ake okhulupirika padziko lapansi. (Tito 3:6) N’zodziwikiratu kuti mzimu umenewu ndi umene umathandiza Yesu kumwamba kuti azitha kuona zimene zikuchitika padziko lapansili. Mofanana ndi Atate wake, iye ndi wozindikira kwambiri ndipo amaona chilichonse. (Yerekezerani ndi Salimo 11:4; Zekariya 4:10.) Choncho, n’zoonekeratu kuti Mwana ameneyu ndi woyenerera bwino kwambiri kulandira mpukutu m’dzanja la Yehova. Izi zili choncho chifukwa iye anatumikira Mulungu ndi mtima wosagawanika ndipo anagonjetsa dziko lapansi. Komanso iye ndi Mkango wa fuko la Yuda ndiponso muzu wa Davide ndipo anapereka moyo wake kuti awombole anthu. Iye ndi woyenereranso chifukwa ali ndi ulamuliro wokwanira bwino, ali ndi mzimu woyera wokwanira bwino ndiponso amathandizidwa ndi Yehova Mulungu kukhala wozindikira bwino kwambiri. Kodi iye anazengereza kulandira udindo umenewu, wotumikira m’gulu lokwezeka la Yehova? Ayi. M’malomwake, “Iye anapita, ndipo nthawi yomweyo anatenga mpukutu umene unali kudzanja lamanja la Iye wokhala pampando wachifumu.” (Chivumbulutso 5:7) Chimenechi ndi chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani yotumikira Mulungu mofunitsitsa.
Nyimbo Zotamanda
14. (a) Kodi zamoyo zinayi pamodzi ndi akulu 24 anachita chiyani Yesu atalandira mpukutu? (b) Kodi zimene Yohane anaona zokhudza akulu 24 aja zikutithandiza bwanji kuwazindikira bwino komanso kuzindikira udindo wawo?
14 Kodi zamoyo zinayi pamodzi ndi akulu 24 amene anazungulira mpando wachifumu wa Yehova, anachita chiyani? “Atatenga mpukutuwo, zamoyo zinayi ndi akulu 24 aja anagwada ndi kuwerama pamaso pa Mwanawankhosa. Aliyense wa iwo anali ndi zeze woimbira ndi mbale yagolide yodzaza ndi zofukiza. Zofukizazo zikuimira mapemphero a oyera.” (Chivumbulutso 5:8) Mofanana ndi zamoyo zinayi zomwe zinazungulira mpando wachifumu wa Mulungu, zomwe ndi akerubi, akulu 24 anagwada ndi kuweramira Yesu. Iwo anachita zimenezi posonyeza kuti akuzindikira udindo wake. Koma akulu okhawa ndi amene anali ndi azeze oimbira ndiponso mbale za zofukiza.a Ndipo iwo okha ndi amene ankaimba nyimbo yatsopano. (Chivumbulutso 5:9) Choncho, iwo akufanana ndi a 144,000 amene ndi “Isiraeli [wopatulika] wa Mulungu,” amenenso ali ndi azeze oimbira ndipo akuimba nyimbo yatsopano. (Agalatiya 6:16; Akolose 1:12; Chivumbulutso 7:3-8; 14:1-4) Komanso, akulu 24 akuoneka m’masomphenyawa akukwaniritsa udindo wawo wokhala ansembe kumwamba, umene unkachitiridwa chithunzi ndi ansembe akale ku Isiraeli omwe ankapereka nsembe ya zofukiza kwa Yehova kuchihema. Nsembe zimenezi zinatha padziko lapansi pamene Mulungu anachotsa Chilamulo cha Mose pochikhoma pamtengo wozunzikirapo wa Yesu. (Akolose 2:14) Kodi tikupezapo mfundo yotani pa zonsezi? Tikupeza mfundo yakuti masomphenya amenewa akusonyeza Akhristu odzozedwa opambana pa nkhondo akuchita utumiki wawo monga ‘ansembe a Mulungu ndi a Khristu, ndipo akulamulira monga mafumu limodzi naye zaka 1,000.’—Chivumbulutso 20:6.
15. (a) Ku Isiraeli, ndani yekha amene anali ndi mwayi wolowa ku Malo Oyera Koposa a chihema? (b) N’chifukwa chiyani kuwotcha zofukiza asanalowe ku Malo Oyera Koposa inali nkhani ya moyo kapena imfa kwa mkulu wa ansembe?
15 Kale ku Isiraeli, mkulu wa ansembe yekha ndi amene ankalowa ku Malo Oyera Koposa, kumene kunkakhala Yehova mophiphiritsira. Kwa mkulu wa ansembe, kunyamula zofukiza inali nkhani ya moyo kapena imfa. Yehova analamula kuti: “[Aroni] azitenga chofukizira chodzaza ndi makala amoto ochokera paguwa lansembe limene lili pamaso pa Yehova. Azitenganso zofukiza zonunkhira zabwino kwambiri zokwana manja awiri odzaza, ndi kulowa nazo kuchipinda, kuseri kwa nsalu yotchinga. Akatero, aziika zofukizazo pamoto umene uli pamaso pa Yehova, ndipo utsi wa zofukizazo uzikuta chivundikiro cha Likasa, chimene chili pa Umboni, kuopera kuti angafe.” (Levitiko 16:12, 13) Zinali zosatheka kuti mkulu wa ansembe alowe bwinobwino ku Malo Oyera Koposa popanda kuwotcha zofukiza.
16. (a) Mumpingo wachikhristu, ndani amalowa ku Malo Oyera Koposa akumwamba? (b) N’chifukwa chiyani Akhristu odzozedwa amafunikira ‘kuwotcha zofukiza’?
16 Mumpingo wachikhristu, si Yesu Khristu yekha, amene ndi Mkulu wa Ansembe, yemwe adzalowe ku Malo Oyera Koposa akumwamba, kumene Yehova amakhala. Ansembe aang’ono a 144,000 nawonso pamapeto pake adzalowa kumalo amenewa. (Aheberi 10:19-23) N’zosatheka kuti ansembe amenewa, amene akuimiridwa ndi akulu 24, alowe ku Malo Oyera Koposa popanda ‘kuwotcha zofukiza,’ zimene zikutanthauza kupereka kwa Yehova nthawi zonse mapemphero opempha ndi opembedzera.—Aheberi 5:7; Yuda 20, 21; yerekezerani ndi Salimo 141:2.
Nyimbo Yatsopano
17. (a) Kodi akulu 24 ankaimba nyimbo yatsopano yotani? (b) Kodi kawirikawiri mawu akuti “nyimbo yatsopano” amagwiritsidwa ntchito bwanji m’Baibulo?
17 Tsopano kunamveka nyimbo yokoma. Nyimboyi ankaimbira Mwanawankhosa ndipo amene ankaimba ndi ansembe anzake, omwe ndi akulu 24 aja. “Iwo anali kuimba nyimbo yatsopano, yakuti: ‘Inu ndinu woyenera kutenga mpukutuwo ndi kumatula zidindo zake zomatira, chifukwa munaphedwa, ndipo ndi magazi anu, munagula anthu kuti atumikire Mulungu. Anthu ochokera mu fuko lililonse, chinenero chilichonse, mtundu uliwonse, ndi dziko lililonse.’” (Chivumbulutso 5:9) Mawu akuti “nyimbo yatsopano” amapezeka nthawi zingapo m’Baibulo ndipo kawirikawiri amatanthauza nyimbo yotamanda Yehova chifukwa cha mphamvu zimene wasonyeza populumutsa anthu. (Salimo 96:1; 98:1; 144:9) Choncho nyimboyo imakhala yatsopano chifukwa chakuti woimbayo ali ndi zifukwa zatsopano zotamandira Yehova poona ntchito zake zina zodabwitsa ndiponso chifukwa chakuti ali ndi zifukwa zina zotamandira dzina la Yehova laulemerero.
18. Kodi n’chifukwa chiyani akulu 24 aja ankatamanda Yesu ndi nyimbo yawo yatsopano?
18 Koma apa akulu 24 ankaimbira Yesu nyimbo yatsopano, osati Yehova. Komabe mfundo yake ndi yofanana. Iwo ankatamanda Yesu chifukwa cha zinthu zatsopano zimene iye, monga Mwana wa Mulungu, anawachitira. Kudzera m’magazi ake, iye anakhala mkhalapakati wa pangano latsopano, limene linathandiza kuti pakhale mtundu watsopano, umene ndi chuma chapadera cha Yehova. (Aroma 2:28, 29; 1 Akorinto 11:25; Aheberi 7:18-25) Anthu a mumtundu watsopano wauzimu umenewu anachokera m’mitundu yosiyanasiyana, koma Yesu anawagwirizanitsa kuti akhale mumpingo umodzi ngati mtundu umodzi.—Yesaya 26:2; 1 Petulo 2:9, 10.
19. (a) Kodi mtundu wa Isiraeli unalephera kulandira madalitso otani chifukwa cha kusakhulupirika kwake? (b) Kodi mtundu watsopano wa Yehova udzasangalala ndi madalitso otani?
19 Pamene Yehova ankathandiza Aisiraeli kuti akhale mtundu m’masiku a Mose, anachita nawo pangano ndipo anawalonjeza kuti ngati iwo angakhalebe okhulupirika ku panganolo, adzakhala ufumu wake wa ansembe. (Ekisodo 19:5, 6) Koma Aisiraeli anakhala osakhulupirika ndipo sanalandire madalitso amene Yehova anawalonjeza. Koma mtundu watsopano wakhalabe wokhulupirika. Mtunduwu unakhazikitsidwa chifukwa cha pangano latsopano limene mkhalapakati wake ndi Yesu. Choncho, anthu a mumtundu watsopanowu adzalamulira dziko lapansi monga mafumu ndiponso adzagwira ntchito ngati ansembe, pothandiza anthu olungama kuti agwirizanenso ndi Yehova. (Akolose 1:20) Zimenezi zikugwirizana ndi mawu a m’nyimbo yatsopanoyo, akuti: “Ndipo munawasandutsa mafumu ndi ansembe a Mulungu wathu, moti adzakhala mafumu olamulira dziko lapansi.” (Chivumbulutso 5:10) Akulu 24 amenewa amasangalala kwambiri akamaimba nyimbo yatsopano imeneyi, yotamanda Yesu amene ali mu ulemerero wake.
Nyimbo Yakumwamba
20. Kodi Yohane anamva nyimbo yotani yotamanda Mwanawankhosa?
20 Kodi zolengedwa zina zambirimbiri zomwe zili mbali yakumwamba ya gulu la Yehova, zinatani zitamva nyimbo yatsopanoyo? Yohane anasangalala atamva zolengedwazo zikuvomereza nyimboyo. Iye anati: “Kenako, ndinaona ndi kumva mawu a angelo ambiri atazungulira mpando wachifumu limodzi ndi zamoyo zija ndi akulu aja. Chiwerengero chawo chinali miyanda kuchulukitsa ndi miyanda ndiponso masauzande kuchulukitsa ndi masauzande. Iwo anali kunena mofuula kuti: ‘Mwanawankhosa amene anaphedwa ndiye woyenera kulandira mphamvu, chuma, nzeru, nyonga, ulemu, ulemerero, ndi madalitso.’” (Chivumbulutso 5:11, 12) Imeneyitu ndi nyimbo yotamanda Mwanawankhosa yochititsa chidwi kwambiri.
21. Kodi kutamandidwa kwa Mwanawankhosa kukuchepetsa ulamuliro wa Yehova kapena udindo wake? Fotokozani.
21 Kodi zimenezi zikutanthauza kuti Yesu watenga malo a Yehova Mulungu ndipo zolengedwa zonse zayamba kutamanda iyeyo m’malo motamanda Atate wake? Ayi ndithu. M’malomwake, nyimbo yotamanda imeneyi ikugwirizana ndi zimene mtumwi Paulo analemba. Iye anati: “Mulungu anamukweza [Yesu] n’kumuika pamalo apamwamba. Ndipo anamukomera mtima n’kumupatsa dzina loposa lina lililonse. Anachita zimenezi kuti m’dzina la Yesu, onse akumwamba, apadziko lapansi, ndi apansi pa nthaka apinde mawondo awo. Kutinso aliyense avomereze poyera ndi lilime lake kuti Yesu Khristu ndiye Ambuye, polemekeza Mulungu Atate.” (Afilipi 2:9-11) Apa Yesu akutamandidwa chifukwa cha zimene anachita pothetsa nkhani yofunika kwambiri yokhudza zolengedwa zonse. Nkhaniyi ndi yosonyeza kuti Yehova ndiye woyenera kulamulira chilengedwe chonse. Zimenezi zinabweretsadi ulemerero waukulu kwa Atate wake.
Nyimbo Yoimbidwa ndi Zamoyo Zonse
22. Kodi anthu a padziko lapansi akuimba nawo nyimbo yotani?
22 M’masomphenya amene Yohane anafotokozawa, zolengedwa zambirimbiri zakumwamba zinkaimba nyimbo yokoma yotamanda Yesu chifukwa cha kukhulupirika kwake ndiponso chifukwa cha udindo umene ali nawo kumwamba. Zolengedwa zakumwambazi zikugwirizana ndi anthu a padziko lapansi amenenso akuimba nawo nyimbo yotamanda Atate ndi Mwana. Monga mmene zochita zabwino za mwana zingabweretsere ulemu waukulu kwa makolo ake, kukhulupirika kwa Yesu kunachititsa kuti chilengedwe chonse ‘chilemekeze Mulungu Atate.’ Choncho Yohane anapitiriza kulemba kuti: “Ndipo cholengedwa chilichonse chakumwamba, padziko lapansi, pansi pa nthaka, panyanja, ndi zinthu zonse za mmenemo, ndinazimva zikunena kuti: ‘Iye wokhala pampando wachifumu, ndi Mwanawankhosa, atamandidwe ndiponso alandire ulemu, ulemerero, ndi mphamvu, kwamuyaya.’”—Chivumbulutso 5:13.
23, 24. (a) Kodi n’chiyani chikusonyeza nthawi imene nyimboyi inayamba kuimbidwa kumwamba ndiponso padziko lapansi? (b) Kodi oimba nawo nyimboyi achuluka bwanji pamene zaka zakhala zikudutsa?
23 Kodi nyimbo yosangalatsayi inayamba kumveka liti? Inayamba kuimbidwa chakumayambiriro kwa tsiku la Ambuye. Satana ndi ziwanda zake atachotsedwa kumwamba, “cholengedwa chilichonse chakumwamba” chinayamba kuimba nawo nyimbo yotamandayi. Ndipo zimene zakhala zikuchitika zikusonyeza kuti kuyambira mu 1919, anthu ambiri padziko lapansi ayamba kuimba nawo nyimbo yotamanda Yehova. Iwo awonjezeka kuchokera pa masauzande ochepa kufika pa oposa 7 miliyoni m’chaka cha 2010.b Dziko la Satana likadzawonongedwa, “cholengedwa chilichonse . . . padziko lapansi” chizidzaimba nyimbo yotamanda Yehova ndi Mwana wake. Pa nthawi yoikidwa ndi Yehova, anthu mamiliyoni ambiri amene anafa adzayamba kuukitsidwa, ndipo “cholengedwa chilichonse . . . pansi pa nthaka,” kutanthauza anthu amene Mulungu akuwakumbukira, chidzakhala ndi mwayi woimba nawo nyimbo imeneyi.
24 Panopa, anthu mamiliyoni ambiri akuimba nyimbo yatsopano mogwirizana ndi gulu la Yehova lapadziko lonse, “kuchokera kumalekezero a dziko lapansi . . . nyanja ndi . . . zilumba.” (Yesaya 42:10; Salimo 150:1-6) Nyimbo yosangalatsayi idzafika pachimake kumapeto kwa Zaka 1,000, anthu onse akadzakhala angwiro. Kenako Satana, yemwe ndi wonyenga wamkulu komanso njoka yakale ija, adzawonongedwa pokwaniritsa ulosi wa pa Genesis 3:15. Ndiyeno nyimbo imene ikuimbidwa ndi zolengedwa zonse zamoyo, zauzimu ndiponso anthu, idzafika pachimake. Zolengedwazo zidzaimba mogwirizana kuti: “Iye wokhala pampando wachifumu, ndi Mwanawankhosa, atamandidwe ndiponso alandire ulemu, ulemerero, ndi mphamvu, kwamuyaya.” M’chilengedwe chonse simudzakhalanso wotsutsa aliyense.
25. (a) Kodi kuwerenga nkhani ya m’masomphenya a Yohane onena za nyimbo yoimbidwa ndi zamoyo zonse kukutilimbikitsa kuchita chiyani? (b) Kodi pamapeto pa masomphenyawa, zamoyo zinayi ndiponso akulu 24 aja akutipatsa chitsanzo chabwino kwambiri chiti?
25 Imeneyi idzakhala nthawi yosangalatsa kwambiri. Zimene Yohane wafotokozazi zikutichititsa kusangalala kwambiri komanso zikutilimbikitsa kugwirizana ndi zolengedwa zambirimbiri zakumwamba poimba kuchokera pansi pa mtima nyimbo zotamanda Yehova Mulungu ndi Yesu Khristu. Zikutilimbikitsanso kuti tipitirize kupirira kuposa kale pochita ntchito zabwino. Tikachita zimenezi, tingayembekezere kuti Yehova atithandiza kuti tidzakhalepo pa nthawi yosangalatsa kwambiriyo, n’kumaimba nawo nyimbo zotamanda Mulungu ndi Yesu mogwirizana ndi zolengedwa zonse m’chilengedwechi. Zikuonekeratu kuti zamoyo zinayi, zomwe ndi akerubi, n’zogwirizana kwambiri ndi Akhristu odzozedwa amene aukitsidwa, chifukwa masomphenyawa anatha ndi mawu akuti: “Ndiyeno zamoyo zinayi zija zinati: ‘Ame!’ Ndipo akulu aja anagwada n’kuwerama ndi kulambira.”—Chivumbulutso 5:14.
26. Kodi tiyenera kukhulupirira chiyani, ndipo Mwanawankhosa wakonzeka kutani?
26 Choncho tikukupemphani inuyo amene mukuwerenga bukuli kuti mukhulupirire nsembe ya Mwanawankhosa, yemwe ndi “woyenera.” Mukachita zimenezi, mudzadalitsidwa pamene mukuyesetsa modzichepetsa kulambira ndi kutumikira Yehova, “Iye wokhala pampando wachifumu.” Lolani kuti Akhristu odzozedwa akuthandizeni masiku ano pamene akupereka “chakudya [chauzimu] chokwanira pa nthawi yake,” chomwe ndi chofunika kwambiri. (Luka 12:42) Koma tsopano Mwanawankhosa akuoneka kuti wakonzeka kumatula zidindo 7 zomatira zija. Kodi mumpukutuwo timvamo uthenga wosangalatsa wotani?
[Mawu a M’munsi]
a Pavesili, mawu akuti “aliyense wa iwo anali ndi zeze woimbira ndi mbale yagolide yodzaza ndi zofukiza,” akhoza kutanthauza akulu aja pamodzi ndi zamoyo zinayi zija. Koma nkhaniyi ikusonyeza mooneka bwino kuti mawuwa akunena za akulu 24 okha aja basi.
b Onani tchati patsamba 64.
[Chithunzi chachikulu pasamba 86]