Mverani Mulungu Kuti Mupindule ndi Malumbiro Ake
“[Mulungu] analumbira pa dzina lake chifukwa panalibe wina wamkulu kwa iye amene akanamulumbirira.”—AHEB. 6:13.
1. Kodi zonena za Yehova zimasiyana bwanji ndi za anthu ochimwa?
YEHOVA ndi “Mulungu wachoonadi.” (Sal. 31:5) Anthu ochimwa sitingawakhulupirire nthawi zonse koma “n’zosatheka kuti Mulungu aname.” (Aheb. 6:18; werengani Numeri 23:19.) Zimene Mulungu amafuna kuchitira anthu zimatheka nthawi zonse. Mwachitsanzo, zonse zimene Mulungu ananena kuti zichitike pa tsiku lililonse lolenga zinthu, zinachitikadi. N’chifukwa chake pa mapeto pa tsiku la 6 lolenga zinthu, “Mulungu anaona kuti zonse zimene anapanga zinali zabwino kwambiri.”—Gen. 1:6, 7, 30, 31.
2. Kodi tsiku lopuma la Mulungu n’chiyani? N’chifukwa chiyani “analipatula”?
2 Ataona zonse zimene anapanga, Yehova Mulungu anafotokoza za tsiku la 7. Tsikuli si la maola 24 koma ndi nthawi yaitali imene Mulungu wakhala akupuma pa ntchito yolenga zinthu padziko lapansi. (Gen. 2:2) Tsiku lopuma la Mulungu limeneli likupitirirabe. (Aheb. 4:9, 10) Baibulo silinena nthawi yeniyeni imene tsikuli linayamba. Timangodziwa kuti linayamba pafupifupi zaka 6,000 zapitazo, pambuyo polenga Hava. M’tsogolomu tikuyembekezera Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Yesu Khristu. Mu ulamuliro umenewu, Mulungu adzakwaniritsa cholinga chimene analengera dziko lapansi chakuti likhale Paradaiso ndiponso lidzaze ndi anthu angwiro. (Gen. 1:27, 28; Chiv. 20:6) Kodi tikudziwa bwanji kuti tidzakhaladi ndi tsogolo losangalatsa limeneli? Tikudziwa chifukwa ‘Mulungu anadalitsa tsiku la 7 ndipo analipatula kuti likhale lopatulika.’ Zimenezi zinatsimikizira kuti palibe zimene zingalepheretse cholinga cha Mulungu kukwaniritsidwa pofika kumapeto kwa tsiku lake lopuma.—Gen. 2:3.
3. (a) N’chiyani chinachitika tsiku lopuma la Mulungu litayamba? (b) Kodi Yehova ananena mawu ati osonyeza kuti adzathetsa kupandukaku?
3 Koma tsiku lopuma la Mulungu litayamba, zinthu zinasokonekera. Satana, yemwe anali mngelo wa Mulungu, anafuna kuti anthu azimulambira. Iye ananena bodza loyamba n’kupusitsa Hava kuti asamvere Yehova. (1 Tim. 2:14) Kenako Hava anachititsa mwamuna wake kuti apandukirenso Mulungu. (Gen. 3:1-6) Pa nthawiyi, zinthu zinavuta kwambiri chifukwa Satana anachititsa kuti Mulungu azikayikiridwa. Ngakhale zinali choncho, Yehova sanaone kuti m’pofunika kulumbira kuti adzakwaniritsabe cholinga chake. M’malomwake, anangonena kuti: “Ndidzaika chidani pakati pa iwe [Satana] ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbewu yako ndi mbewu yake. Mbewu ya mkaziyo idzaphwanya mutu wako, ndipo iwe udzaivulaza chidendene.” Mawu amenewa anasonyeza kuti Mulungu adzathetsa kupandukaku. Ndipo pa nthawi yoyenera, iye anathandiza anthu kumvetsa tanthauzo lake.—Gen. 3:15; Chiv. 12:9.
KULUMBIRA KUNALI KOFUNIKA
4, 5. Kodi nthawi zina Abulahamu ankachita chiyani potsimikizira zinthu zofunika?
4 Zikuoneka kuti Adamu ndi Hava atangolengedwa kumene, kulumbira sikunali kofunika ndipo m’chilankhulo chimene Mulungu anawapatsa munalibe mawu olumbirira. Poyamba, onse anali angwiro ndipo ankakonda Mulungu ndi kumutsanzira. Choncho, sankafunika kulumbira chifukwa chakuti ankanena zoona zokhazokha ndipo ankakhulupirirana. Koma anthu atachimwa, zinthu zinasintha. Patapita nthawi, mabodza ndi chinyengo zinafala kwambiri moti munthu ankafunika kulumbira potsimikizira zinthu zofunika kwambiri.
5 Mwachitsanzo, Abulahamu anafunika kulumbira pofuna kutsimikizira nkhani zina. Tikudziwa maulendo atatu pamene iye anachita zimenezi. (Gen. 21:22-24; 24:2-4, 9) Pa nthawi ina, iye analumbira pochokera kokagonjetsa mfumu ya Elamu ndi anzake. Mfumu ya ku Salemu ndi mfumu ya ku Sodomu anapita kukakumana ndi Abulahamu. Mfumu ya ku Salemuyo inali Melekizedeki ndipo inalinso “wansembe wa Mulungu Wam’mwambamwamba.” Monga wansembe, iye anadalitsa Abulahamu ndiponso kutamanda Mulungu chifukwa chothandiza Abulahamu kugonjetsa adani ake. (Gen. 14:17-20) Ndiyeno mfumu ya ku Sodomu inafuna kuthokoza Abulahamu chifukwa chopulumutsa anthu ake ku magulu ankhondowo. Koma Abulahamu analumbira kuti: “Ndikukweza manja anga kulumbira kwa Yehova Mulungu Wam’mwambamwamba, Amene anapanga kumwamba ndi dziko lapansi. Ndikulumbira kuti pa zinthu zako sinditengapo kanthu n’kamodzi komwe, kaya kakhale kaulusi kapena kachingwe komangira nsapato. Ayi sinditero, kuti usadzati, ‘Ndine ndinamulemeretsa Abulamu.’”—Gen. 14:21-23.
YEHOVA ANALUMBIRA POLONJEZA ABULAHAMU
6. (a) Kodi Abulahamu anapereka chitsanzo chotani kwa ife? (b) Kodi tidzapindula bwanji chifukwa cha kumvera kwa Abulahamu?
6 Pofuna kutsimikizira anthu ochimwa, Yehova Mulungu ankalumbiranso pogwiritsa ntchito mawu monga akuti: “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Pali ine Mulungu wamoyo.’” (Ezek. 17:16) Baibulo limafotokoza maulendo oposa 40 pamene Yehova Mulungu analumbira. Chitsanzo chodziwika bwino ndi chokhudza Abulahamu. Kwa zaka zambiri, Yehova anachita mapangano ndi Abulahamu osonyeza kuti Mbewu yolonjezedwa idzachokera m’banja la Abulahamu ndiponso Isaki. (Gen. 12:1-3, 7; 13:14-17; 15:5, 18; 21:12) Kenako Yehova anauza Abulahamu kuti achite zinthu zovuta kwambiri. Anamuuza kuti apereke nsembe mwana wake wokondedwa. Nthawi yomweyo, Abulahamu anamvera ndipo atatsala pang’ono kupereka Isaki, mngelo wa Mulungu anamuletsa. Kenako Mulungu anati: “Ndikulumbira pali dzina langa, kuti chifukwa cha zimene wachitazi, posakana kupereka mwana wako yekhayo, ndidzakudalitsa ndithu. Ndiponso ndidzachulukitsadi mbewu yako ngati nyenyezi zakumwamba, monganso mchenga wa m’mphepete mwa nyanja. Komanso mbewu yako idzalanda chipata cha adani ake. Kudzera mwa mbewu yako, mitundu yonse ya padziko lapansi idzapeza madalitso ndithu chifukwa chakuti wamvera mawu anga.”—Gen. 22:1-3, 9-12, 15-18.
7, 8. (a) N’chifukwa chiyani Mulungu analumbira kwa Abulahamu? (b) Kodi “nkhosa zina” za Yesu zidzapindula bwanji ndi lumbiro la Mulungu?
7 N’chifukwa chiyani Mulungu analumbira kwa Abulahamu kuti zimene analonjeza zidzachitika? Iye ankafuna kutsimikizira anthu okalamulira ndi Khristu kumwamba za lonjezo lake ndiponso kulimbitsa chikhulupiriro chawo. Anthu amenewa ndi mbali yachiwiri ya “mbewu” yolonjezedwa. (Werengani Aheberi 6:13-18; Agal. 3:29) Malinga ndi zimene Paulo ananena, Yehova “anachita kulumbira pa zimene analonjezazo. Anachita zimenezo kuti mwa zinthu ziwiri zosasinthika [lonjezo ndiponso lumbiro lake], zimene chifukwa cha zinthu zimenezo n’zosatheka kuti Mulungu aname, ife . . . tilimbikitsidwe kwambiri, kuti tigwire mwamphamvu chiyembekezo chimene chaikidwa patsogolo pathu.”
8 Koma si Akhristu odzozedwa okha amene amapindula ndi lumbiro la Mulungu kwa Abulahamu. Yehova analumbira kuti “mitundu yonse ya padziko lapansi idzapeza madalitso” kudzera mwa “mbewu” ya Abulahamu. (Gen. 22:18) “Nkhosa zina” zokhulupirika zili m’gulu la anthu amene adzapeze madalitso ndipo zikuyembekezera moyo wosatha m’Paradaiso padziko lapansi. (Yoh. 10:16) Kaya tikuyembekezera kupita kumwamba kapena kukhala padziko lapansi, tiyeni “tigwire mwamphamvu” chiyembekezo chathu. Tingachite zimenezi pomvera Mulungu nthawi zonse.—Werengani Aheberi 6:11, 12.
MULUNGU ANALUMBIRANSO
9. Kodi Mulungu analumbira za chiyani pa nthawi imene ana a Abulahamu anali pa ukapolo ku Iguputo?
9 Patapita zaka zambiri, Yehova analumbiranso za lonjezo lake kwa Abulahamu. Anachita zimenezi pamene ankatuma Mose kukalankhula ndi ana a Abulahamu, amene anali pa ukapolo ku Iguputo. (Eks. 6:6-8) Ponena za nthawi imeneyi, Mulungu anati: “Pa tsiku limene ndinasankha Isiraeli, . . . ndinakweza dzanja langa powalumbirira kuti ndidzawatulutsa m’dziko la Iguputo kupita nawo kudziko limene ndinaliyendera kuti iwo akakhalemo, dziko loyenda mkaka ndi uchi.”—Ezek. 20:5, 6.
10. Kodi Mulungu atalanditsa Aisiraeli ku Iguputo, anawalonjeza chiyani?
10 Aisiraeli atalanditsidwa ku Iguputo, Yehova analumbiranso n’kuwalonjeza kuti: “Ngati mudzalabadiradi mawu anga ndi kusunga pangano langa, pamenepo mudzakhaladi chuma changa chapadera pakati pa anthu ena onse, chifukwa dziko lonse lapansi ndi langa. Inuyo mudzakhala ufumu wanga wa ansembe ndi mtundu wanga woyera.” (Eks. 19:5, 6) Apatu tingati Mulungu anapatsa Aisiraeli mwayi waukulu kwambiri. Aisiraeli omvera akanakhala ndi mwayi wokhala ufumu wa ansembe n’cholinga choti athandize mitundu yonse kupeza madalitso. Ndiyeno Yehova anafotokoza zimene anachitira Aisiraeli pa nthawiyo. Iye anati: “Ndinakulumbirira n’kuchita nawe pangano.”—Ezek. 16:8.
11. Kodi Aisiraeli anatani Mulungu atawapatsa mwayi wochita naye pangano loti akhale mtundu wake wosankhidwa?
11 Koma Yehova sanawauze Aisiraeli kuti nawonso alumbire potsimikiza kuti adzamvera. Sanawakakamizenso kuti akhale naye pa ubwenzi wapaderawu. M’malomwake, Aisiraeliwo ananena mwa kufuna kwawo kuti: “Zonse zimene Yehova wanena tidzachita zomwezo.” (Eks. 19:8) Patangopita masiku atatu, Yehova Mulungu anauza Aisiraeli zimene iye ankafuna kuti azichita monga mtundu wosankhidwa. Choyamba, iwo anamva Malamulo Khumi kenako Mose anawauza malamulo ena amene ali pa Ekisodo 20:22 mpaka 23:33. Kodi Aisiraeli anatani atamva? “Anthu onse anayankhira pamodzi kuti: ‘Mawu onse amene Yehova wanena tidzachita.’” (Eks. 24:3) Ndiyeno Mose analemba malamulowo ‘m’buku la pangano’ ndipo anawerenga mokweza kuti mtundu wonse umve kachiwiri. Atatero, anthuwo ananenanso kachitatu kuti: “Zonse zimene Yehova wanena tidzachita zomwezo ndipo tidzamumvera.”—Eks. 24:4, 7, 8.
12. Kodi pangano litakhazikitsidwa, Yehova anachita chiyani? Nanga Aisiraeli anachita chiyani?
12 Nthawi yomweyo, Yehova anayamba kukwaniritsa mbali yake yokhudza pangano la Chilamulo. Iye anauza anthu kukonza chihema kuti Aisiraeli azikamulambira kumeneko. Mulungu anakhazikitsanso ansembe kuti azigwirizanitsa anthu ochimwa ndi iye. Koma Aisiraeli sanachedwe kuiwala zoti anadzipereka kwa Mulungu. Iwo “anali kumvetsa chisoni Woyera wa Isiraeli.” (Sal. 78:41) Mwachitsanzo, pamene Mose anali kulandira malangizo ena kuphiri la Sinai, Aisiraeli anaona kuti iye akuchedwa ndipo chikhulupiriro chawo chinayamba kuchepa. Iwo anaganiza kuti Mose wawathawa. Choncho anapanga fano la mwana wa ng’ombe n’kuuza anthu onse kuti: “Uyu ndiye Mulungu wanu, Aisiraeli inu, amene anakutulutsani m’dziko la Iguputo.” (Eks. 32:1, 4) Kenako anachita chikondwerero chimene anachitchula kuti “chikondwerero cha Yehova” n’kuyamba kupereka nsembe ndi kugwadira fano lawolo. Yehova ataona zimenezi, anauza Mose kuti: “Apatuka mofulumira panjira imene ndawalamula kuyendamo.” (Eks. 32:5, 6, 8) Chomvetsa chisoni n’chakuti kuyambira nthawi imeneyo, Aisiraeli ankangolumbira koma osachita.—Num. 30:2.
MALUMBIRO ENA AWIRI
13. Kodi Mulungu analumbira kwa Mfumu Davide pomulonjeza chiyani? Nanga lumbiroli linatanthauza chiyani?
13 Nthawi imene Davide anali mfumu, Yehova analumbiranso kawiri. Anachita zimenezi n’cholinga choti athandize anthu onse omvera. Poyamba, analumbira kwa Davide kuti mpando wake wachifumu udzakhala mpaka kalekale. (Sal. 89:35, 36; 132:11, 12) Zimenezi zinatanthauza kuti Mbewu yolonjezedwayo idzatchedwa “Mwana wa Davide.” (Mat. 1:1; 21:9) Modzichepetsa, Davide ananena kuti mbadwa yakeyo ndi “Ambuye” wake. Anatero chifukwa chakuti udindo wa Khristu unali waukulu kwambiri kuposa wake.—Mat. 22:42-44.
14. Ponena za Mbewu yolonjezedwa, kodi Yehova analumbira kuti chiyani? Nanga timapindula bwanji ndi lumbiroli?
14 Kachiwiri, Yehova anauzira Davide kulosera kuti Mfumu yapadera imeneyi idzatumikiranso anthu monga Mkulu wa Ansembe. Mu Isiraeli munthu mmodzi sankakhala mfumu komanso wansembe. Ansembe ankachokera mu fuko la Levi pamene mafumu ankachokera mu fuko la Yuda. Koma Davide ananeneratu za mfumu yapamwambayi kuti: “Yehova wauza Ambuye wanga kuti: ‘Khala kudzanja langa lamanja kufikira nditaika adani ako monga chopondapo mapazi ako.’ Yehova walumbira (ndipo sadzasintha maganizo). Iye wati: ‘Iwe ndiwe wansembe mpaka kalekale, monga mwa unsembe wa Melekizedeki!’” (Sal. 110:1, 4) Panopa ulosiwu ukukwaniritsidwa chifukwa chakuti Yesu Khristu, yemwe ndi Mbewu yolonjezedwa, ali kumwamba ndipo akulamulira. Akutumikiranso monga Mkulu wa Ansembe pothandiza anthu olapa kuti agwirizanenso ndi Mulungu.—Werengani Aheberi 7:21, 25, 26.
ISIRAELI WATSOPANO WA MULUNGU
15, 16. (a) Kodi Baibulo limatchula mitundu iwiri iti ya Isiraeli? Kodi ndi mtundu uti umene Mulungu akudalitsa masiku ano? (b) Kodi Yesu anapereka lamulo liti kwa otsatira ake lokhudza malumbiro?
15 Chifukwa chokana Yesu Khristu, mtundu wa Aisiraeli unataya mwayi wokhala pa ubwenzi wapadera ndi Mulungu ndiponso wodzakhala ‘ufumu wa ansembe.’ Yesu anauza atsogoleri achiyuda kuti: “Ufumu wa Mulungu udzachotsedwa kwa inu n’kuperekedwa kwa mtundu wobala zipatso zake.” (Mat. 21:43) Mtundu watsopanowu unabadwa pa Pentekosite m’chaka cha 33 C.E. pamene mzimu wa Mulungu unatsanuliridwa pa ophunzira a Yesu okwana 120, omwe anasonkhana ku Yerusalemu. Iwo anatchedwa kuti “Isiraeli wa Mulungu.” Pasanapite nthawi, iwo anachuluka mpaka kukhala masauzande ambiri ndipo anali ochokera kumayiko onse amene ankadziwika pa nthawiyo.—Agal. 6:16.
16 Mosiyana ndi Aisiraeli, mtundu watsopano wa Mulungu umenewu wakhala ukubereka zipatso zabwino chifukwa chomvera Mulungu nthawi zonse. Lamulo lina limene anthu ake amamvera ndi lokhudza malumbiro. Pamene Yesu anali padziko, anthu anali kulumbira monama kapena kulumbirira zinthu zosafunika kwenikweni. (Mat. 23:16-22) Yesu anaphunzitsa otsatira ake kuti: “Usamalumbire n’komwe . . . Tangotsimikizani kuti mukati Inde akhaledi Inde, ndipo mukati Ayi akhaledi Ayi, pakuti mawu owonjezera pamenepa achokera kwa woipayo.”—Mat. 5:34, 37.
Malonjezo a Yehova amakwaniritsidwa nthawi zonse
17. Kodi tidzakambirana mafunso ati m’nkhani yotsatira?
17 Mwina tikhoza kudzifunsa kuti, Kodi zimenezi zikutanthauza kuti nthawi zonse kulumbira n’kulakwa? Koma funso lofunika kwambiri n’lakuti, Kodi mawu oti “Inde akhaledi Inde” akutanthauza chiyani? Mafunsowa adzayankhidwa m’nkhani yotsatira. Tiyeni tipitirize kusinkhasinkha Mawu a Mulungu kuti azitilimbikitsa kumvera Yehova nthawi zonse. Tikamatero, iye adzakhala wofunitsitsa kutidalitsa mpaka kalekale mogwirizana ndi malumbiro ake.