MUTU 12
“Kodi Mulungu Alibe Chilungamo?”
1. Kodi timamva bwanji tikaona zinthu zopanda chilungamo?
MAYI wamasiye yemwenso ndi wachikulire amubera ndalama zimene ankasunga. Kholo louma mtima lasiya mwana wake wakhanda. Bambo wina waikidwa m’ndende pa mlandu woti sanapalamule. Kodi mumamva bwanji mukaganizira zinthu ngati zimenezi? Ziyenera kuti zimakukhumudwitsani ndipo m’pake kumva choncho. Mwachibadwa, anthufe timasangalala ndi zinthu zabwino ndipo timakhumudwa ndi zinthu zoipa. Zinthu zopanda chilungamo zikachitika, zimatikwiyitsa. Timafuna kuti amene walakwiridwayo apatsidwe chipukuta misozi ndipo wolakwayo alangidwe. Ngati zimenezi sizikuchitika, timadzifunsa kuti: ‘Kodi Mulungu akuona zimenezi? N’chifukwa chiyani sakuchitapo kanthu?’
2. Kodi Habakuku anatani ataona zinthu zopanda chilungamo zomwe zinkachitika, nanga n’chifukwa chiyani Yehova sanamudzudzule?
2 Kuyambira kale, atumiki okhulupirika a Yehova akhala akufunsa mafunso ngati amenewa. Mwachitsanzo, mneneri Habakuku anapemphera kwa Mulungu kuti: “N’chifukwa chiyani mukundionetsa zinthu zopanda chilungamo zoopsa chonchi? N’chifukwa chiyani mukulola kuti chiwawa, kusamvera malamulo, uchigawenga ndiponso nkhanza zifalikire paliponse?” (Habakuku 1:3, Contemporary English Version) Yehova sanadzudzule Habakuku chifukwa chofunsa mafunso moona mtima, chifukwa iye ndi amene anatilenga m’njira yoti tizikonda chilungamo. Pang’ono pokha, timasonyeza mmene Yehova amamvera pa nkhani ya chilungamo.
Yehova Amadana ndi Zinthu Zopanda Chilungamo
3. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yehova amadziwa bwino kwambiri zinthu zopanda chilungamo zimene zikuchitika kuposa ifeyo?
3 Yehova amadziwa zinthu zopanda chilungamo zonse zomwe anthu amachita. Ponena za m’nthawi ya Nowa, Baibulo limati: “Yehova anaona kuti anthu aipa kwambiri padziko lapansi. Anaona kuti maganizo a anthu komanso zofuna za mtima wawo zinali zoipa zokhazokha nthawi zonse.” (Genesis 6:5) Kodi mawu amenewa akutanthauza chiyani? Nthawi zambiri anthufe timangodziwa zinthu zopanda chilungamo zimene zachitikira ifeyo kapena zimene tamva kuti zachitikira ena. Koma Yehova amadziwa zinthu zopanda chilungamo zomwe zikuchitika padziko lonse. Iye amaona chilichonse. Kuwonjezera pamenepo, amadziwanso maganizo olakwika amene munthu ali nawo, omwe amam’pangitsa kuti achite zinthu zopanda chilungamo.—Yeremiya 17:10.
4, 5. (a) Kodi Baibulo limasonyeza bwanji kuti Yehova amadera nkhawa anthu amene achitiridwa zinthu zopanda chilungamo? (b) Kodi Yehova wakumanapo ndi zinthu zopanda chilungamo ziti?
4 Koma sikuti Yehova amangodziwa zinthu zopanda chilungamo zimene anthu amachita. Amaderanso nkhawa anthu amene achitiridwa zinthu zopanda chilungamowo. Pamene anthu amitundu ina ankachitira nkhanza anthu ake, Yehova ankawamvera chisoni chifukwa ankamva “kulira kwawo chifukwa cha anthu omwe ankawapondereza komanso kuwachitira nkhanza.” (Oweruza 2:18) Mwina munaonapo kuti anthu ena akaona mobwerezabwereza zinthu zopanda chilungamo, amangofika pozizolowera ndipo samvanso chisoni. Koma Yehova sachita zimenezo. Ngakhale kuti waona zinthu zopanda chilungamo kwa zaka pafupipafupi 6,000, iye amadana nazobe. Ndipo Baibulo limatitsimikizira kuti Yehova amanyansidwa ndi zinthu monga “lilime lonama,” “manja amene amakhetsa magazi a anthu osalakwa” komanso “mboni yachinyengo imene nthawi zonse imanena mabodza.”—Miyambo 6:16-19.
5 Taganiziraninso mmene Yehova anadzudzulira mwamphamvu atsogoleri opanda chilungamo a ku Isiraeli. Iye anauza mneneri wake kuti awafunse kuti: “Kodi simukuyenera kudziwa chilungamo?” Yehova atafotokoza momveka bwino mmene anthu achinyengowa ankagwiritsira ntchito mphamvu zawo molakwika, ananeneratu zimene zidzawachitikire kuti: “Adzafuulira Yehova kuti awathandize, koma sadzawayankha. Adzawabisira nkhope yake pa nthawi imeneyo, chifukwa cha zochita zawo zoipa.” (Mika 3:1-4) Izitu zikusonyeza kuti Yehova amanyansidwa ndi zinthu zopanda chilungamo. Kumbukirani kuti iyenso zakhala zikumuchitikira. Kwa zaka zambirimbiri, Satana wakhala akumunyoza popanda chifukwa. (Miyambo 27:11) Ndiponso anthu anachitira Mwana wake zinthu zopanda chilungamo zoipa kwambiri. Ngakhale kuti Mwanayo “sanachite tchimo,” anaphedwa ngati chigawenga. (1 Petulo 2:22; Yesaya 53:9) N’zoonekeratu kuti Yehova amadziwa zinthu zopanda chilungamo zimene anthu akukumana nazo ndipo amawadera nkhawa.
6. Kodi timamva bwanji zinthu zopanda chilungamo zikatichitikira, nanga n’chifukwa chiyani?
6 Komabe, zinthu zopanda chilungamo zikatichitikira kapena zikachitikira ena, mwachibadwa timakhumudwa kwambiri. Tinalengedwa m’chifaniziro cha Mulungu ndipo kupanda chilungamo n’kosiyana kwambiri ndi makhalidwe a Yehova. (Genesis 1:27) Nanga n’chifukwa chiyani Mulungu amalola kuti zinthu zopanda chilungamo zizichitika?
Nkhani Yofunika Kwambiri
7. Kodi Satana ananena chiyani zokhudza Yehova m’munda wa Edeni?
7 Yankho la funsoli ndi logwirizana ndi nkhani ina yofunika kwambiri. Monga taonera, Mlengi ali ndi ufulu wolamulira dziko lapansi ndiponso anthu onse. (Salimo 24:1; Chivumbulutso 4:11) Komabe anthu atangolengedwa chakumene, mngelo wina ananena bodza lokhudza Yehova komanso kuti salamulira bwino. Kodi zimenezi zinachitika bwanji? Yehova analamula Adamu, yemwe anali munthu woyamba, kuti asadye zipatso za mtengo winawake wa m’munda wa Edeni. Mulungu anamuuza kuti akapanda kumvera lamuloli ‘adzafa.’ (Genesis 2:17) Lamulo la Mulunguli linali losavuta kuti Adamu komanso mkazi wake Hava alitsatire. Komabe Satana anachititsa Hava kukhulupirira kuti Mulungu sanachite bwino kuwapatsa lamulo limeneli. Kodi Satana ananena kuti chingachitike n’chiyani Hava akadya zipatso za mtengowo? Iye anauza Hava mosapita m’mbali kuti: “Si zoona zimenezo, simudzafa ayi. Mulungutu akudziwa kuti tsiku limene mudzadye chipatso cha mtengo umenewu, maso anu adzatseguka ndithu, ndipo mudzafanana ndi Mulungu. Mudzadziwa zabwino ndi zoipa.”—Genesis 3:1-5.
8. (a) Kodi Satana ankatanthauza chiyani pa zomwe anauza Hava? (b) Kodi Satana anatsutsa chiyani pa nkhani yokhudza ulamuliro wa Mulungu?
8 Ponena mawu amenewa, Satana sankangotanthauza kuti Yehova anabisira Hava zinthu zimene ankafunika kuzidziwa, koma ankatanthauzanso kuti Yehova ananamiza Havayo. Satana anachititsa kuti Hava ayambe kukayikira Mulungu. Pamenepa ananyoza kwambiri dzina la Yehova. Iye anasonyezanso kuti Mulungu salamulira bwino. Satana anasamala kwambiri kuti asatsutse mfundo yoti Mulungu ndi wolamulira wa zinthu zonse. Koma ananena kuti si woyenera kulamulira, alibe ufulu wolamulira komanso salamulira mwachilungamo ndiponso m’njira yothandiza amene amawalamulirawo.
9. (a) Kodi zotsatirapo za kusamvera kwa Adamu ndi Hava zinali zotani, nanga kunayambitsa mafunso ofunika ati? (b) N’chifukwa chiyani Yehova sanangopha oukirawo?
9 Zotsatira zake zinali zakuti onse awiri, Adamu ndi Hava, sanamvere Yehova ndipo anadya zipatso za mtengo woletsedwawo. Chifukwa cha kusamverako, anafunika kulandira chilango cha imfa ngati mmene Mulungu ananenera. Koma bodza limene Satana ananena linayambitsa mafunso ofunika kwambiri. Kodi Yehova alidi ndi ufulu wolamulira anthu, kapena anthu ayenera kumadzilamulira okha? Kodi Yehova amalamuliradi bwino kwambiri? Popeza Yehova ali ndi mphamvu zopanda malire, akanatha kuwononga oukirawo nthawi yomweyo. Komabe mafunsowa sankakhudza mphamvu za Mulungu koma dzina lake, zomwe zikuphatikizapo mmene amalamulirira. Choncho kupha Adamu, Hava ndiponso Satana sikukanathandiza kuti zitsimikizirike kuti Mulungu amalamulira mwachilungamo. M’malomwake, zikanangowonjezera vutolo. Njira yokha yotsimikizira kuti anthu sangathe kudzilamulira bwinobwino popanda Mulungu, inali kulola kuti papite nthawi anthuwo akudzilamulira.
10. Kodi zimene zakhala zikuchitika zasonyeza chiyani pa nkhani ya ulamuliro wa anthu?
10 Kwa zaka masauzande ambiri, anthu ayesapo maboma osiyanasiyana monga boma lolamulidwa ndi munthu mmodzi, boma la demokalase ndiponso mitundu ina ya maboma. Ndiye kodi zotsatira zake zimakhala zotani? Ndi zogwirizana ndi zimene Baibulo limanena kuti: “Munthu wapweteka munthu mnzake pomulamulira.” (Mlaliki 8:9) M’pake kuti mneneri Yeremiya ananena kuti: “Ine ndikudziwa bwino, inu Yehova, kuti munthu alibe ulamuliro wosankha yekha njira ya moyo wake. Munthu amene akuyenda alibe ulamuliro wowongolera mapazi ake.”—Yeremiya 10:23.
11. N’chifukwa chiyani Yehova analola kuti anthu akumane ndi mavuto?
11 Yehova anadziwa kuti anthu adzakumana ndi mavuto ambiri akamadzilamulira. Ndiye kodi iye anachita zinthu mopanda chilungamo polola kuti zimenezi zichitike? Ayi. Tiyerekeze kuti muli ndi mwana amene akufunika opaleshoni chifukwa ali ndi matenda oti akhoza kufa nawo. Mukudziwa kuti mwana wanuyo adzamva ululu chifukwa cha opaleshoniyo, ndipo zimenezi zikukumvetsani chisoni kwambiri. Koma mukudziwanso kuti opaleshoniyo imuthandiza kuti achire n’kumasangalala. Mofanana ndi zimenezi, Mulungu ankadziwa ndipo ananeneratu kuti anthu adzakumana ndi mavuto chifukwa chowalola kuti azidzilamulira. (Genesis 3:16-19) Koma anadziwanso kuti angathe kudzachotsa mavuto onse ngati atalola kuti onse aone mavuto omwe amakhalapo anthu akamayesa kudzilamulira okha. Kuchita zimenezi kungathandize kuti nkhani ya ulamuliro wa Mulungu ithetsedwe mpaka kalekale.
Nkhani Yokhudza Kukhulupirika kwa Anthu
12. Mogwirizana ndi zimene nkhani ya Yobu ikusonyeza, kodi Satana anawanenera bodza lotani anthu?
12 Pali mbali inanso yokhudza nkhaniyi. Ponena kuti Mulungu si woyenera kulamulira komanso salamulira mwachilungamo, sikuti Satana anangonena bodza lokhudza ulamuliro wa Yehova komanso dzina lake. Iye ananenanso bodza lokhudza kukhulupirika kwa atumiki a Mulungu. Mwachitsanzo, taonani zimene Satana anauza Yehova zokhudza munthu wolungama, Yobu. Iye anati: “Kodi inuyo simwamuteteza pomuikira mpanda? Mwatetezanso nyumba yake ndi zinthu zonse zimene ali nazo. Mwadalitsa ntchito ya manja ake ndipo ziweto zake zachuluka kwambiri m’dzikoli. Koma panopa mutambasule dzanja lanu n’kuwononga zinthu zonse zimene ali nazo, ndipo muona, akutukwanani m’maso muli gwa!”—Yobu 1:10, 11.
13. Kodi Satana ankatanthauza chiyani pa zomwe ananena zokhudza Yobu, nanga n’chifukwa chiyani tinganene kuti zimenezi zikukhudza anthu onse?
13 Satana ananena kuti Yehova ankagwiritsa ntchito mphamvu zake zoteteza pogula kukhulupirika kwa Yobu. Ponena zimenezi, Satana ankatanthauzanso kuti Yobu anali wokhulupirika mwachiphamaso ndipo ankalambira Mulungu chifukwa cha zimene ankamupatsa. Iye anati Yobu akanatha kutukwana Mlengi wake ngati akanapanda kumudalitsa. Satana ankadziwa kuti Yobu anali chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani yokhala “munthu wokhulupirika amene amachita zoyenera, amaopa Mulungu ndiponso amapewa zoipa.”a Ankaganiza kuti ngati akanachititsa kuti Yobu asiye kukhala wokhulupirika, ndiye kuti akanathanso kuchita zimenezi kwa anthu onse. Choncho kwenikweni Satana ankanena kuti anthu amatumikira Mulungu pofuna kupezapo kenakake. Ndipotu posonyeza kuti nkhaniyo ikukhudza anthu onse, Satana anauza Yehova kuti: “Munthu angapereke chilichonse chimene ali nacho kuti apulumutse moyo wake.”—Yobu 1:8; 2:4.
14. Kodi zomwe zakhala zikuchitika zasonyeza chiyani pa zimene Satana ananena zokhudza anthu?
14 Zimene zakhala zikuchitika zasonyeza kuti mofanana ndi Yobu, anthu ambiri akakumana ndi mayesero amakhalabe okhulupirika kwa Yehova. Zimenezi n’zosiyana kwambiri ndi zimene Satana ananena. Anthuwa amasangalatsa mtima wa Yehova ndipo zimenezi zimachititsa kuti Yehovayo aziyankha Satana, yemwe amamutonza n’kumanena kuti anthu akhoza kusiya kutumikira Mulungu akakumana ndi mavuto. (Aheberi 11:4-38) Anthu a mitima yabwino samasiya kutumikira Mulungu. Amakhalabe okhulupirika ngakhale pamene akumana ndi mavuto aakulu ndipo amadalira kwambiri Yehova kuti awapatse mphamvu kuti athe kupirira.—2 Akorinto 4:7-10.
15. Kodi pangakhale funso liti lokhudza mmene Yehova anaweruzira anthu m’mbuyomu komanso mmene adzaweruzire m’tsogolomu?
15 Koma sikuti chilungamo cha Yehova chimangokhudza nkhani ya ulamuliro wake, chimakhudzanso kukhulupirika kwa anthu. Baibulo limafotokoza mmene Yehova anaweruzira anthu ena paokha ndiponso mitundu ya anthu. Lilinso ndi maulosi onena kuti adzaweruza anthu m’tsogolomu. Kodi n’chiyani chingatithandize kukhulupirira kuti Yehova anaweruza mwachilungamo ndipo m’tsogolomu adzaweruzanso mwachilungamo?
Chilungamo cha Mulungu Chimaposa cha Aliyense
16, 17. Perekani zitsanzo zosonyeza kuti nthawi zina anthu amalephera kuweruza mwachilungamo.
16 Ponena za Yehova, Baibulo limanena zoona kuti: “Njira zake zonse ndi zolungama.” (Deuteronomo 32:4) Palibe munthu amene anganene kuti mmenemu ndi mmenenso iyeyo alili, chifukwa nthawi zambiri anthufe sitidziwa zonse ndipo zimenezi zimatilepheretsa kuzindikira kuti zoyenera ndi ziti. Mwachitsanzo taganizirani za Abulahamu. Anachonderera Yehova kuti asawononge mzinda wa Sodomu ngakhale kuti anthu amumzindawo anali oipa kwambiri. Iye anafunsa Yehova kuti: “Kodi zoona muwonongadi olungama pamodzi ndi oipa?” (Genesis 18:23-33) N’zodziwikiratu kuti yankho linali lakuti ayi. Yehova “anagwetsa sulufule ndi moto ngati mvula ku Sodomu” Loti ndi ana ake akazi atafika kale mumzinda wa Zowari. (Genesis 19:22-24) Mosiyana ndi zimenezi, Yona “anakwiya koopsa” pamene Mulungu anachitira chifundo anthu a ku Nineve. Popeza Yona anali atalengeza kale kuti iwo awonongedwa, akanasangalala kuwaona akuphedwa ngakhale kuti anthuwo anali atalapa mochokera pansi pa mtima.—Yona 3:10 mpaka 4:1.
17 Yehova anatsimikizira Abulahamu kuti sikuti amasonyeza chilungamo chake pongowononga oipa, koma populumutsanso anthu olungama. Pomwe Yona ankafunika kuphunzira mfundo yoti Yehova ndi wachifundo. Anthu akasiya kuchita zoipa, iye amakhala ‘wokonzeka kuwakhululukira.’ (Salimo 86:5) Mosiyana ndi anthu, Yehova sapereka chiweruzo chokhwima pongofuna kuti adziwike kuti ndi wamphamvu. Ndiponso salephera kuchitira anthu chifundo poopa kuti ena amuona ngati wofooka. Nthawi zonse amasonyeza chifundo pakakhala chifukwa chochitira zimenezo.—Yesaya 55:7; Ezekieli 18:23.
18. Perekani umboni wa m’Baibulo wosonyeza kuti Yehova salekerera zinthu zoipa chifukwa choti ndi wachifundo.
18 Komabe, Yehova salekerera zoipa chifukwa choti ndi wachifundo. Pamene anthu ake ankapitirizabe kulambira mafano, iye analankhula mwamphamvu kuti: “Ndidzakuweruza mogwirizana ndi njira zako ndiponso kukulanga chifukwa cha zinthu zonse zonyansa zimene umachita. Diso langa silidzakumvera chisoni ndipo sindidzakuchitira chifundo. Ndidzakulanga mogwirizana ndi njira zako.” (Ezekieli 7:3, 4) Choncho ngati anthu sakufuna kusintha, Yehova amawapatsa chilango. Koma sawaweruza pongotengera mphekesera. Moti atamva madandaulo ambiri okhudza Sodomu ndi Gomora, iye anati: “Ndipitako kuti ndikaone ngati akuchitadi zimene ndamvazo.” (Genesis 18:20, 21) Tikuthokoza kuti Yehova ndi wosiyana ndi anthu ambiri amene amangofulumira kuweruza asanamve mfundo zonse. M’pake kuti Baibulo limanena kuti Yehova ndi “Mulungu wokhulupirika, amene sachita zinthu zopanda chilungamo.”—Deuteronomo 32:4.
Musamakayikire Kuti Yehova Ndi Wachilungamo
19. Kodi tingatani ngati sitikumvetsa zimene Yehova anachita pa nkhani inayake?
19 Baibulo siliyankha mafunso onse okhudza zimene Yehova anachita m’mbuyomo. Silifotokozanso mwatsatanetsatane zinthu zonse zimene adzachite poweruza anthu ndi magulu a anthu m’tsogolomu. Choncho ngati sitikumvetsa nkhani zina kapena maulosi ena a m’Baibulo chifukwa choti sanafotokoze zinthu mwatsatanetsatane, tingasonyeze kukhulupirika ngati mneneri Mika, yemwe analemba kuti: “Ndidzayembekezera moleza mtima Mulungu wa chipulumutso changa.”—Mika 7:7.
20, 21. N’chifukwa chiyani sitiyenera kukayikira kuti nthawi zonse Yehova adzachita zinthu mwachilungamo?
20 Tisamakayikire kuti Yehova adzachita zinthu mwachilungamo pa chilichonse. Ngakhale zitaoneka kuti anthu akulekerera zinthu zopanda chilungamo, Yehova amalonjeza kuti: “Kubwezera ndi kwanga, ndidzawabwezera ndine.” (Aroma 12:19) Tikamayembekezera moleza mtima kuti Yehova achitepo kanthu, nafenso tinganene mawu ofanana ndi amene mtumwi Paulo ananena kuti: “Kodi Mulungu alibe chilungamo? Ayi ndithu.”—Aroma 9:14.
21 Panopa tikukhala mu “nthawi yapadera komanso yovuta.” (2 Timoteyo 3:1) Kupanda chilungamo ndiponso ‘kuponderezana’ kwachititsa kuti anthu azichitidwa nkhanza kwambiri. (Mlaliki 4:1) Komabe Yehova sanasinthe. Iye amadanabe ndi kupanda chilungamo ndipo amadera nkhawa anthu amene amachitiridwa zopanda chilungamozo. Tikakhalabe okhulupirika kwa Yehova ndi ulamuliro wake, iye adzatipatsa mphamvu kuti tithe kupirira mpaka nthawi imene adzachotse zinthu zonse zopanda chilungamo mu Ufumu wake.—1 Petulo 5:6, 7.