Mbewu ya Njoka—Yavumbulidwa Motani?
“Ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbewu yako ndi mbewu yake.”—GENESIS 3:15.
1. (a) Kodi nchifukwa ninji Yehova ali Mulungu wachimwemwe? (b) Kodi wachitanji kutheketsanso ife kukhala ndi chimwemwe chimene iye ali nacho?
YEHOVA ndi Mulungu wachimwemwe ndipo pachifukwa chabwino. Iye ndiye Mpatsi wamkulu koposa ndi wopambana wa zinthu zabwino, ndipo palibe chimene chingalepheretse zifuno zake. (Yesaya 55:10, 11; 1 Timoteo 1:11, NW; Yakobo 1:17) Amafunanso kuti atumiki ake akhale ndi chimwemwe chimene iye ali nacho, ndipo amapereka zifukwa zabwino zakuti iwo akhale otero. Chotero, panthaŵi yatsoka lalikulu koposa m’mbiri ya munthu—chipanduko mu Edene—anayala maziko akuti ife tikhale ndi chiyembekezo cha mtsogolo.—Aroma 8:19-21.
2. Popereka chiweruzo pa opandukawo mu Edene, kodi Yehova anayala motani maziko a chiyembekezo kaamba ka mbadwa za Adamu ndi Hava?
2 Mmodzi wa ana auzimu a Yehova, mwa kutsutsa ndi kuneneza Mulungu, anali atangodzipanga kukhala Satana Mdyerekezi. Anthu oyamba, Hava ndiyeno Adamu, anali atakhala pansi pa ulamuliro wake naswa lamulo lomveka la Yehova. Iwo anaweruzidwira ku imfa molungama. (Genesis 3:1-24) Komabe, popereka chiweruzo pa opanduka ameneŵa, Yehova anayala maziko a chiyembekezo kaamba ka mbadwa za Adamu ndi Hava. Motani? Malinga ndi zolembedwa pa Genesis 3:15, Yehova anati: “Ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbewu yako ndi mbewu yake; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira chitende chake.” Ulosiwo ndiwo mfungulo yomvetsetsera Baibulo lonse limodzi ndi zochitika zakale ndi zamakono zokhudza dziko ndi atumiki a Yehova.
Chimene Ulosiwo Umatanthauza
3. Malinga ndi zimene zili pa Genesis 3:15, tchulani (a) Njokayo, (b) “mkaziyo,” (c) “mbewu” ya Njoka, (d) “mbewu” ya mkaziyo.
3 Kuti muzindikire tanthauzo lake, talingalirani mbali zosiyanasiyana za ulosiwo. Amene akulankhula naye pa Genesis 3:15 ndi Njoka—osati njoka wambayo koma amene anaigwiritsira ntchito. (Chivumbulutso 12:9) “Mkaziyo” si Hava ayi koma ndi gulu lakumwamba la Yehova, mayi wa atumiki ake odzozedwa ndi mzimu padziko lapansi. (Agalatiya 4:26) “Mbewu” ya Njoka, ndiyo mbewu ya Satana, mbadwa zake—ziŵanda ndi anthu ndiponso magulu aumunthu amene amasonyeza mikhalidwe ya Satana ndi amenenso amasonyeza udani kwa “mbewu” ya mkazi. (Yohane 15:19; 17:15) Kwenikweni, “mbewu” ya mkazi ndiye Yesu Kristu, amene anadzozedwa ndi mzimu woyera mu 29 C.E. A 144,000, amene ‘abadwa mwatsopano . . . mwa madzi ndi mzimu’ amenenso ali oloŵa nyumba ndi Kristu mu Ufumu wakumwamba, ali mbali yachiŵiri ya mbewu yolonjezedwayo. Ameneŵa anayamba kuwonjezedwa pa mbewu ya mkazi kuyambira Pentekoste wa 33 C.E. ndi mtsogolo mwake.—Yohane 3:3, 5; Agalatiya 3:16, 29.
4. Kodi Genesis 3:15 akugwirizana motani ndi kukhala paradaiso kwa dziko lapansi, lodzala ndi anthu omasuka ku uchimo ndi imfa?
4 Njoka yeniyeniyo mu Edene inagwiritsiridwa ntchito monga cholankhulira ndi uja amene chinyengo chake chinatayitsa anthu Paradaiso. Genesis 3:15 anasonya kutsogolo ku nthaŵi pamene uja amene anagwiritsira ntchito njoka ija adzatswanyidwa. Ndiyeno njira idzatsegukira atumiki a Mulungu aumunthu kuti akakhale m’Paradaiso, womasuka ku uchimo ndi imfa. Imeneyo idzakhaladi nthaŵi yosangalatsa!—Chivumbulutso 20:1-3; 21:1-5.
5. Kodi ndi mikhalidwe yotani imene imadziŵikitsa mbadwa zauzimu za Mdyerekezi?
5 Pambuyo pa chipanduko mu Edene, panayamba kukhala anthu ndi magulu amene anasonyeza mikhalidwe yonga ija ya Satana Mdyerekezi—chipanduko, kunama, kuneneza, mbanda, limodzi ndi kutsutsa chifuniro cha Yehova ndi aja olambira Yehova. Mikhalidwe imeneyo inasonyeza mbadwa, ana auzimu, a Mdyerekezi. Mmodzi wa iwo anali Kaini, yemwe anapha Abele pamene Yehova anayanja kulambira kwa Abele osati kwa Kaini. (1 Yohane 3:10-12) Nimrode anali munthu amene dzina lake linamsonyeza kukhala wopanduka ndipo anakhala mpalu wamphamvu wotsutsa Yehova. (Genesis 10:9) Ndiponso panali kutsatizana kwa maufumu akale, kuphatikizapo Babulo, limodzi ndi zipembedzo zawo zochirikizidwa ndi boma zozikidwa pa mabodza, ndipo ameneŵa anapondereza mwankhanza olambira a Yehova.—Yeremiya 50:29.
“Udani Pakati pa Iwe ndi Mkaziyo”
6. Kodi Satana wasonyeza motani udani kwa mkazi wa Yehova?
6 Panthaŵi yonseyi, panali udani pakati pa Njoka ndi mkazi wa Yehova, pakati pa Satana Mdyerekezi ndi gulu lakumwamba la Yehova la zolengedwa zauzimu zokhulupirika. Udani wa Satana unasonyezedwa pamene iye anatonza Yehova nafuna kusokoneza gulu lakumwamba la Yehova, akumakopa angelo kusiya malo awo oyenera. (Miyambo 27:11; Yuda 6) Unasonyezedwa pamene Satana anagwiritsira ntchito ziŵanda zake kuyesa kutsekereza amithenga aungelo otumidwa ndi Yehova. (Danieli 10:13, 14, 20, 21) Unaonekera kwambiri m’zaka za zana lino la 20 pamene Satana anafuna kuwononga Ufumu Waumesiya pakubadwa kwake.—Chivumbulutso 12:1-4.
7. Kodi nchifukwa ninji angelo a Yehova okhulupirika anasonyeza udani kwa Njoka yophiphiritsirayo, koma ndi kudziletsa kotani kumene iwo asonyeza?
7 Mkazi wa Yehova, gulu la angelo okhulupirika, analinso ndi udani kulinga kwa Njoka yophiphiritsirayo. Satana ananeneza dzina labwino la Mulungu; anakayikitsanso umphumphu wa cholengedwa chaluntha chilichonse cha Mulungu, kuphatikizapo angelo onse, ndipo anali kuyesa mokangalika kuswa kukhulupirika kwawo kwa Mulungu. (Chivumbulutso 12:4a) Angelo okhulupirika, akerubi, ndi aserafi sakanachitira mwina kusiyapo kunyansidwa naye uja amene anadzipanga kukhala Mdyerekezi ndi Satana. Komabe, ayembekezera Yehova kusamalira nkhaniyo panthaŵi yake ndipo mwanjira yake.—Yerekezerani ndi Yuda 9.
Udani kwa Mbewu ya Mkazi wa Mulungu
8. Kodi Satana anali watcheru kuyembekezera kuona yani?
8 Mkati mwa zonsezo, Satana anali watcheru kuyembekezera kuona Mbewu ya mkazi yolonjezedwayo, imene Yehova anati idzanzunzunda Njokayo kumutu. Pamene mngelo wochokera kumwamba analengeza kuti Yesu, amene anali atabadwa ku Betelehemu, anali “Mpulumutsi, amene ali Kristu Ambuye,” umenewo unali umboni wamphamvu wakuti iye adzakhala Mbewu ya mkazi yolonjezedwayo.—Luka 2:10, 11.
9. Kodi Satana anasonyeza motani udani wanjiru Yesu atabadwa?
9 Udani wanjiru wa Satana unaonekera posapita nthaŵi pamene anakopa openda nyenyezi achikunja paulendo umene choyamba unawafikitsa kwa Mfumu Herode ku Yerusalemu ndiyeno kunyumba ina ku Betelehemu kumene anapeza mnyamata wamng’onoyo Yesu ndi amake, Mariya. Mwamsanga pambuyo pake Mfumu Herode inalamula kupha anyamata onse kuyambira azaka ziŵiri kupita pansi, m’Betelehemu ndi m’milaga yake. Motero, Herode anasonyeza udani wausatana pa Mbewuyo. Mwachionekere Herode anadziŵa bwino lomwe kuti anali kuyesa kupha amene adzakhala Mesiya. (Mateyu 2:1-6, 16) Mbiri imachitira umboni kuti Mfumu Herode anali ndi makhalidwe oipa, wachiŵembu, ndi wambanda—inde, mmodzi wa mbewu ya Njokayo.
10. (a) Pambuyo pa ubatizo wa Yesu, kodi Satana iye mwini anayesa motani kulepheretsa chifuno cha Yehova ponena za Mbewu yolonjezedwayo? (b) Kodi ndi motani mmene Satana anagwiritsira ntchito atsogoleri achipembedzo achiyuda kuchita zolinga zake?
10 Yesu atadzozedwa ndi mzimu woyera mu 29 C.E. ndipo Yehova atalankhula kuchokera kumwamba kuvomereza kuti Yesu ndi Mwana wake, Satana anayesa mobwerezabwereza kuchititsa Yesu kugonja pa chiyeso, motero akumafuna kulepheretsa chifuno cha Yehova ponena za Mwana wake. (Mateyu 4:1-10) Atalephera zimenezo, anayamba kugwiritsira ntchito oimira ake aumunthu kuti akwaniritse zolinga zake. Ena amene anagwiritsira ntchito poyesa kuwononga mbiri ya Yesu anali atsogoleri onyenga achipembedzo. Iwo anagwiritsira ntchito mabodza ndi kuneneza, mtundu wa machenjera ogwiritsiridwa ntchito ndi Satana iye mwini. Pamene Yesu anauza wamanjenje kuti, “Limba mtima, . . . machimo ako akhululukidwa,” alembi, popanda kuyembekezera kuti aone ngati mwamunayo wachiradi, anati Yesu ndi wamwano. (Mateyu 9:2-7) Pamene Yesu anachiritsa anthu pa Sabata, Afarisi anamtsutsa monga wakuswa lamulo la Sabata napangana kumuwononga. (Mateyu 12:9-14; Yohane 5:1-18) Pamene Yesu anatulutsa ziŵanda, Afarisi ananena kuti iye anali kumvana ndi “Beelzebule, mkulu wa ziŵanda.” (Mateyu 12:22-24) Lazaro ataukitsidwa kwa akufa, anthu ambiri anakhulupirira Yesu, koma ansembe aakulu ndi Afarisi anapangananso za kumupha.—Yohane 11:47-53.
11. Kutatsala masiku atatu kuti Yesu afe, kodi iye anasonyeza ndani kukhala mbali ya mbewu ya Njoka, ndipo chifukwa ninji?
11 Pa Nisani 11, 33 C.E., Yesu, ngakhale anadziŵa bwino lomwe zimene iwo anali kupangana, analoŵa popanda mantha m’kachisi ku Yerusalemu ndipo mmenemo analengeza poyera chiweruzo chawo. Monga gulu, alembi ndi Afarisi anali atasonyeza kosaleka mtundu wa anthu amene iwo anali; chotero Yesu anati: “Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! chifukwa mutsekera anthu ufumu wakumwamba pamaso pawo; pakuti inu nokha simuloŵamo, ndipo muwaletsa amene alikuloŵa, kuti asaloŵemo.” Yesu mosapita m’mbali analengeza kuti iwo anali mbali ya mbewu ya Njoka, akumati: “Njoka inu, obadwa inu a mamba, mudzatha bwanji kuthaŵa kulanga kwake kwa Gehena?” (Mateyu 23:13, 33) Mawu ake akukumbutsa za ulosi wa pa Genesis 3:15.
12, 13. (a) Kodi ansembe aakulu ndi alembi anapereka motani umboni winanso wosonyeza atate wawo wauzimu? (b) Ndani anagwirizana nawo? (c) Pakukwaniritsidwa kwa Genesis 3:15, kodi Mbewu ya mkazi anainzunzunda motani kuchitende?
12 Atamva mawu a Yesu, kodi iwo analaswa mtima, kwakuti anachonderera chifundo kwa Mulungu? Kodi analapa pa kuipa kwawo? Ayi! Marko 14:1 akusimba kuti mmaŵa mwake, pamsonkhano wochitikira m’bwalo la mkulu wa ansembe, “ansembe aakulu ndi alembi anafunafuna momchitira chiŵembu [Yesu], ndi kumupha.” Iwo anapitiriza kusonyeza mzimu wambanda wa Satana, amene poyamba Yesu anali atamtcha wambanda. (Yohane 8:44) Posakhalitsa Yudase Isikariote anagwirizana nawo, amene Satana anamkopa kukhala wampatuko. Yudase anasiya Mbewu yosalakwa ya mkazi wa Mulungu nagwirizana ndi mbewu ya Njoka.
13 Mmamaŵa pa Nisani 14, a bwalo la milandu lachipembedzo lachiyuda anatenga Yesu monga wandende kupita naye kwa bwanamkubwa wachiroma. Kumeneko ansembe aakulu ndiwo anatsogolera kufuula kuti iye apachikidwe. Pamene Pilato anafunsa kuti, “Ndipachike Mfumu yanu kodi?” ansembe aakulu ndiwo anayankha kuti, “Tilibe Mfumu koma Kaisara.” (Yohane 19:6, 15) Inde, iwo anasonyeza mwanjira iliyonse kuti anali mbali ya mbewu ya Njoka. Komatu sanali okha. Nkhani youziridwa yolembedwa pa Mateyu 27:24, 25 ikusimba kuti: “Pilato . . . anatenga madzi, nasamba manja pamaso pa khamulo.” Ndiyeno anthu onse anati: “Mwazi wake uli pa ife ndi pa ana athu.” Motero Ayuda ambiri a mbadwo umenewo anasonyeza okha kuti anali mbali ya mbewu ya Njoka. Tsikulo lisanathe, Yesu anafa. Mwa kugwiritsira ntchito mbewu yake yooneka, Satana ananzunzunda Mbewu ya mkazi wa Mulungu kuchitende.
14. Kodi nchifukwa ninji kunzunzunda chitende cha Mbewu ya mkazi sikunatanthauze kuti Satana walakika?
14 Kodi Satana anapambana? Kutalitali! Yesu Kristu analilaka dziko lapansi nagonjetsa wolamulira wake. (Yohane 14:30, 31; 16:33) Anakhala wokhulupirika kwa Yehova kufikira imfa. Imfa yake monga munthu wangwiro inapereka mtengo wa dipo wofunika kugulira kuyenera kwa kukhala ndi moyo kumene Adamu anataya. Motero anatsegula njira ya kumoyo wamuyaya kwa aja amene adzasonyeza chikhulupiriro m’makonzedwe amenewo ndi kumvera malamulo a Mulungu. (Mateyu 20:28; Yohane 3:16) Yehova anaukitsa Yesu kwa akufa nampatsa moyo wosafa kumwamba. Panthaŵi yoikika ya Yehova, Yesu adzatswanya Satana kumchotsapo. Pa Genesis 22:16-18, panalosera kuti Yehova adzayanja mabanja onse padziko lapansi amene akuchita zimene afunikira kuchita kudzidalitsa okha mwa Mbewu yokhulupirikayo.
15. (a) Pambuyo pa imfa ya Yesu, kodi atumwi ake anapitiriza motani kuvumbula mbewu ya Njokayo? (b) Kodi udani umene mbewu ya Njoka yapitiriza kuusonyeza kufikira tsiku lathu ngwotani?
15 Pambuyo pa imfa ya Yesu, Akristu odzozedwa ndi mzimu anapitiriza kuvumbula mbewu ya Njoka, monga momwe anachitira Ambuye wawo. Atasonkhezeredwa ndi mzimu woyera, mtumwi Paulo anachenjeza za “munthu wosayeruzika” amene kukhalapo kwake kudzakhala “monga mwa machitidwe a Satana.” (2 Atesalonika 2:3-10) “Munthu” ameneyu wachiungwe ndiye kagulu ka atsogoleri achipembedzo a Dziko Lachikristu. Mbewu ya Njoka inazunzanso kowopsa otsatira a Yesu Kristu. Mu ulosi wolembedwa pa Chivumbulutso 12:17, mtumwi Yohane analosera kuti Satana adzapitiriza kuchita nkhondo ndi otsalira a mbewu ya mkazi wa Mulungu kufikira tsiku lathu. Ndi zimene zachitika kumene. M’maiko ambiri, Mboni za Yehova zaletsedwa, kumenyedwa, kutsekeredwa m’ndende, kapena kuponyedwa m’misasa ya chibalo chifukwa cha kuchirikiza kwawo kolimba Ufumu wa Mulungu ndi njira zake zolungama.
Kuvumbula Mbewu ya Njoka Kwamakono
16. M’nthaŵi zathu, kodi ndani amene avumbulidwa kukhala mbali ya mbewu ya Njoka, ndipo motani?
16 Motsanzira Yesu Kristu, Akristu oona sanaleke kuvumbula kwawo Njoka ndi mbewu yake mopanda mantha. Mu 1917 Ophunzira Baibulo, dzina la Mboni za Yehova panthaŵiyo, anafalitsa buku lakuti The Finished Mystery, mmene anavumbula chinyengo cha atsogoleri achipembedzo a Dziko Lachikristu. Pambuyo pake mu 1924, panatsatira chigamulo chosindikizidwa chamutu wakuti Ecclesiastics Indicted. Makope ake mamiliyoni makumi asanu anagaŵiridwa padziko lonse. Mu 1937, J. F. Rutherford, pulezidenti wa Watch Tower Society panthaŵiyo, anapereka nkhani zamphamvu zovumbula mbewu ya Satana, za mitu yakuti “Yavumbulidwa” ndi “Chipembedzo ndi Chikristu.” Chaka chotsatira, pamene omvetsera pamisonkhano 50 m’maiko osiyanasiyana anali kutchera khutu, iye anapereka nkhani yakuti “Dziŵani Zoona” pawailesi yolunzanitsa ndi telefoni kuchokera ku London, England. Patapita mwezi umodzi, nyumba ya wailesi yaikulu ku United States inaulutsa nkhani yakuti “Chifasisti Kapena Ufulu.” Pa zimenezi panawonjezedwa kuvumbula kwamphamvu m’mabuku onga Enemies ndi Religion ndiponso m’kabuku kakuti Uncovered. Mogwirizana ndi zimene zinafalitsidwa kuyambira m’ma 1920, buku lakuti Revelation—Its Grand Climax At Hand!,a losindikizidwa tsopano m’zinenero 65, limasonyeza kuti olamulira andale achinyengo ndiponso amalonda opanda khalidwe ndi aumbombo ali pakati pa ziŵalo zapatsogolo za mbewu ya Njoka. Pamene atsogoleri andale akhala ndi chizoloŵezi cha kunama kuti azinyenga anthu awo, kusalemekeza mwazi monga chinthu chopatulika, ndi kupondereza atumiki a Yehova (motero kusonyeza udani kwa mbewu ya mkazi wa Mulungu), amadzisonyezadi okha kuti ali mbali ya mbewu ya Njoka. Ngakhalenso amalonda amatero amene, popanda kuvutika chikumbumtima, amanama kuti apeze phindu ndi amenenso amapanga ndi kugulitsa zinthu zodziŵika kuti zimachititsa matenda.
17. Kodi anthu otchuka amene angatuluke m’dongosolo la dzikoli adakali ndi mwaŵi wotani?
17 Sikuti munthu yense wodetsedwa ndi chipembedzo cha dziko, ndale, kapena malonda amakhaliratu mbali ya mbewu ya Njoka. Ena mwa amuna ndi akazi ameneŵa amafika pakuyamikira Mboni za Yehova. Amagwiritsira ntchito malo awo kuwathandiza ndipo m’kupita kwa nthaŵi amakhala olambira oona. (Yerekezerani ndi Machitidwe 13:7, 12; 17:32-34.) Kwa onsewo, chiitano ichi chaperekedwa: “Tsono, mafumu inu, chitani mwanzeru: langikani, oweruza inu a dziko lapansi. Tumikirani Yehova ndi mantha, ndipo kondwerani ndi chinthenthe. Mpsompsoneni mwanayo, kuti angakwiye, ndipo mungatayike m’njira, ukayaka pang’ono pokha mkwiyo wake. Odala onse akumkhulupirira iye.” (Salmo 2:10-12) Inde, nkofunika kuti onse amene akufuna chiyanjo cha Yehova achitepo kanthu tsopano, Woweruza wakumwamba asanakankhe chitseko kutseka khomo la mwaŵi!
18. Ngakhale kuti saali mbali ya mbewu ya mkazi, kodi ndani amene akulambirabe Yehova?
18 Aja amene adzapanga Ufumu wakumwamba ndiwo okha amene ali mbali ya mbewu ya mkazi. Iwo ali oŵerengeka. (Chivumbulutso 7:4, 9) Komabe, pali khamu lalikulu la ena, inde, mamiliyoni, amene pokhala olambira Yehova akuyembekezera moyo wamuyaya padziko lapansi laparadaiso. Mwa mawu ndi zochita, amati kwa odzozedwa a Yehova: “Tidzamuka nanu, pakuti tamva kuti Mulungu ali ndi inu.”—Zekariya 8:23.
19. (a) Kodi anthu onse afunika kupanga chosankha chotani? (b) Ndi kwayani makamaka kumene chiitano chochonderera cha kuchitapo kanthu mwanzeru chikuperekedwa pamene kudakali mwaŵi?
19 Ino ndiyo nthaŵi yakuti anthu onse apange chosankha. Kodi akufuna kulambira Yehova ndi kuchirikiza uchifumu wake, kapena kodi adzalola Satana kukhala wolamulira wawo mwa kuchita zinthu zomkondweretsa? Anthu ngati mamiliyoni asanu ochokera m’mitundu yonse aima kumbali ya Yehova mogwirizana ndi otsalira a mbewu ya mkazi, oloŵa nyumba a Ufumu. Enanso mamiliyoni asanu ndi atatu asonyeza chidwi cha kuphunzira nawo Baibulo kapena kupezeka pamisonkhano yawo. Mboni za Yehova zikuti kwa onsewa: Khomo la mwaŵi lidakali chitsegukire. Imani mosakayika kumbali ya Yehova. Vomerezani Yesu Kristu monga Mbewu yolonjezedwa. Gwirizanani mwachimwemwe ndi gulu looneka la Yehova. Mulandiretu madalitso amene Iye adzapereka kupyolera mwa ulamuliro wa Mfumuyo, Kristu Yesu.
Footnote]
a Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi Njokayo yotchulidwa pa Genesis 3:15 ndani? Nanga mkaziyo ndani?
◻ Kodi ndi mikhalidwe yotani imene imadziŵikitsa mbewu ya Njoka?
◻ Kodi Yesu anavumbula mbewu ya Njoka kukhala yani?
◻ Kodi ndani amene avumbulidwa kukhala mbali ya mbewu ya Njokayo m’nthaŵi zathu?
◻ Kodi anthu mwamsanga afunika kuchita chiyani kuti apeŵe kukhala mbali ya mbewu ya Njoka?
[Chithunzi patsamba 10]
Yesu anavumbula atsogoleri onyenga achipembedzo kukhala mbali ya mbewu ya Njoka