Mbali ya Mkazi m’Malemba
‘Adzatchedwa Mkazi, chifukwa anamtenga mwa mwamuna.’—GENESIS 2:23.
1, 2. (a) Kodi anthu ena amalingalira kuti Baibulo limawawona motani akazi? (b) Kuti tiweruze bwino, kodi nkuyerekezera kotani kumene kuyenera kupangidwa, ndipo kodi bukhu lina la zilozero likulongosola chiyani?
KODI ndimotani mmene Malemba Opatulika amawonera akazi? Malingaliro amasiyana pankhaniyi. Bukhu lina laposachedwapa lonena za nkhaniyi likulongosola kuti: “Lingaliro losungidwiratu laposachedwapa nlakuti Baibulo linachepsa akazi.” Anthu ena amanena kuti m’mbali zake zonse ziŵiri Yachihebri ndi Yachigiriki, Baibulo nlouma mtima kwa akazi. Kodi zimenezi nzowona?
2 Kuti tiweruze bwino, nkoyenerera choyamba kusanthula mmene akazi ankachitidwira m’nthaŵi za Baibulo pakati pa anthu amene sankalambira Yehova. M’zitaganya zina zamakedzana zimene zinkalondola kulambira mulungu mayi, akazi ankalemekezedwa monga zizindikiro za kubala. Iwo akuwoneka kuti ankalemekezedwa m’Babulo ndi Igupto. Koma kumalo ena sizinawayendere bwino kwenikweni. Mu Asuri wamakedzana mwamuna akanatha kuthamangitsa mkazi wake atafuna ndipo ngakhale kumupha ngati mkaziyo anali wosakhulupirika. Kunja kwa nyumba, iye anafunikira kuvala chophimba kumaso. Mu Girisi ndi Roma, akazi olemera okha, ambiri a iwo omwe anali adama, kapena akazi achigololo olemera, ndiwo ankaphunzira ndiponso anasangalala ndi ufulu wakutiwakuti. Chotero, nchodzetsa mpumulo kuŵerenga mu The New International Dictionary of New Testament Theologya kuti: “Mosiyana ndi dziko (lachipembedzo) lonse la kum’mawa, iye [mkazi m’Malemba Achihebri] akuzindikiridwa monga munthu ndiponso monga mnzake wa mwamuna.” Izi zamveketsedwa bwino m’bukhu lomalizira la Malemba Achihebri, kumene mneneri wa Yehova akulongosola mkazi wa mwamuna kukhala ‘mnzake,’ akumawonjezera kuti: ‘Asamchitire monyenga mkazi wa ubwana wake ndi mmodzi yense.’—Malaki 2:14, 15.
Analengedwa Monga Mnzake wa Mwamuna
3 ndi mawu a m’tsinde. (a) Pambuyo polenga Adamu, kodi ndi ntchito zotani zimene Yehova anampatsa? (b) Chinkana kuti panthaŵiyo adalibe mkazi, kodi nchiyani chimene chinali chowona ponena za Adamu asanalengedwe Hava, ndipo nchiyaninso chimene chinali chowona ponena za “Adamu wotsirizayo,” Yesu?
3 Mogwirizana ndi Baibulo, Yehova analenga Adamu “ndi dothi lapansi” namuika m’munda wa Edene, kuti aulime. Mulungu anabweretsa nyama zakuthengo ndi zolengedwa zouluka kwa Adamu kuti aziwone ndi kuzitcha maina. Mkati mwa nthaŵi yonse imene izi zinatengera Adamu, iye anali yekha. Kaamba ka ntchito zimene iye analandira kwa Yehova kufikira panthaŵiyo, iye anali wangwiro, wokwanira, wosasoŵa kanthu.b Iye “analibe womthandiza monga womkwaniritsa.”—Genesis 2:7, 15, 19, 20, NW.
4, 5. (a) Pamene sikunalinso kwabwino kwa Adamu kupitiriza kukhala yekha, kodi Yehova anachitanji? (b) Kodi ndi ntchito yotenga nyengo yaitali yotani imene Yehova anapatsa Adamu ndi Hava, ndipo kodi iyo ikafunikiranji kwa onse aŵiriwo?
4 Komabe, patapita nthaŵi yakutiyakuti, Yehova analengeza kuti “si kwabwino kuti munthu akhale yekha,” ndipo anapatsa Adamu tsamwali woti athandizane naye ntchito zomwe zinali kutsogolo. Iye anamgoneka Adamu, nachotsako imodzi ya nthiti zake, naiumba kukhala mkazi, ‘fupa la mafupa a Adamu ndi mnofu wa mnofu wake.’ Adamu tsopano akakhala ndi “womthandiza,” “womkwaniritsa,” kapena mnzake. ‘Mulungu ndipo anadalitsa iwo, ndipo adati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: Mulamulire pa nsomba za m’nyanja, ndi pa mbalame za m’mlengalenga, ndi pa zamoyo zonse zakukwawa pa dziko lapansi.’—Genesis 1:25, 28; 2:18, 21-23.
5 Onani kuti ntchito imeneyi inaperekedwa kwa “iwo,” kwa onse aŵiri mwamuna ndi mkazi. Kugwirizana kwawo sikukathera pa kudzaza dziko lapansi. Kukaphatikizapo kuligonjetsa dziko lapansi ndi kupereka ulamuliro woyenera pa zolengedwa zonse zotsika. Iyo ikafunikira mikhalidwe yaluntha ndi yauzimu, ndipo onse aŵiri mwamunayo ndi mkaziyo anali ndi kuthekera koyenerera kokulitsira mikhalidweyi m’chigwirizano ndi chifuniro cha Mulungu.
Mbali Yoyenera ya Mkazi
6. (a) Kodi Baibulo limasonyezanji ponena za nyonga yakuthupi yochepa ya mwamuna ndi ya mkazi? (b) Kodi akazi angachite bwino kulingalira motani kuti avomereze kakonzedwe ka zinthu ka Yehova?
6 Ndithudi, kuligonjetsa dziko lapansi kukafunikiranso nyonga yakuthupi. M’nzeru zake zopanda malire, Yehova analenga Adamu choyamba, pamenepo Hava. Iye analengedwa “wa kwa mwamuna,” ‘chifukwa cha mwamuna,’ ndipo mwachiwonekere wokhala ndi nyonga yakuthupi yocheperako kuposa mwamuna. (1 Timoteo 2:13; 1 Akorinto 11:8, 9; yerekezerani ndi 1 Petro 3:7.) Iyi ndi mfundo ya moyo imene ochilikiza zabwino za akazi ambiri, ndi akazi enanso, amawoneka kukhala ndi vuto kuivomereza. Iwo akanakhala achimwemwe koposa akanayesa kumvetsetsa chifukwa chimene Yehova anakonzera zinthu mwanjira imeneyi, mwakutero kuvomereza mbali yawo yopatsidwa ndi Mulungu. Anthu amene amadandaula ponena za makonzedwe a Mulungu angayerekezeredwe ndi kambalame kotchedwa nightingale kamene kamabisala m’chisa chake chifukwa chakuti sikamphamvu mofanana ndi mbalame yotchedwa sea gull, mmalo momaulukira ku nthambi zazitali ndikumaimba moyamikira kaamba ka mphatso zapadera zimene Mulungu anakapatsa.
7. Kodi nchifukwa ninji Adamu anali mmalo abwino akuchita umutu pa Hava ndi ana alionse amene akabadwa, koma kodi zimenezi zinali zachivulazo kwa Hava?
7 Hava asanalengedwe, mosakaikira Adamu anali ndi kuzoloŵera kwakukulu m’kakhalidwe. Mkati mwa nthaŵiyi, Yehova anampatsa iye malangizo akutiakuti. Adamu anafunikira kupereka malangizoŵa kwa mkazi wake, mwakutero kuchita monga wolankhulira wa Mulungu. Moyenerera, iye anayenera kutsogolera m’nkhani zonse za kulambira ndi machitachita aumulungu amene anayenera kuwachita ndi cholinga chokwaniritsa ntchito yawo. Pamene ana anabadwa, iye akakhala mutu wa banja. Komatu izi sakazichita ku chivulazo cha mkazi wake. Mmalomwake, zikachitidwa ku ubwino wake chifukwa chakuti mkaziyo akakhala ndi winawake womchilikiza pamene akachita udindo wake wopatsidwa ndi Mulungu pa ana ake.
8. Kodi nkakonzedwe kazinthu kaumulungu kotani kamene kandandalitsidwa m’Baibulo?
8 Mogwirizana ndi kakonzedwe kazinthu kaumulungu, Adamu anali woŵerengera kwa Yehova, Hava anali pansi pa umutu wa Adamu, ana alionse akakhala pansi pa chitsogozo cha makolo awo, ndipo nyama zinali zogonjera kwa anthu. Mwamuna ndi mkazi anali ndi mbali zawo zosiyana, ndipo aliyense akanakhala ndi moyo wachimwemwe ndi wopindulitsa. Chotero, ‘zinthu zonse zikachitika mwaulemu ndi mwadongosolo.’—1 Akorinto 11:3; 14:33, 40, NW, mawu a m’tsinde.
Uchimo Unasintha Mbali ya Mkazi
9, 10. Kodi nziti zomwe zinali zotulukapo za kugwera m’tchimo kwa mwamuna ndi mkazi, ndipo kodi zimenezi zatulukapo chiyani kwa akazi ambiri?
9 Mwachibadwa, kuloŵerera kwa uchimo ndi kupanda ungwiro m’Paradaiso woyambirira kunasokoneza kakonzedwe kadongosolo ka zinthu. (Aroma 7:14-20) Kunabweretsa zovuta kwa mwamuna wopandukayo ndi mkazi wake wosamverayo. (Genesis 3:16-19) Chiyambire nthaŵi imeneyo, amuna ambiri adyera agwiritsira ntchito molakwa umutu wawo woyenerera, akumabweretsa kuvutika kwakukulu kwa akazi m’mibadwomibadwo.
10 Powoneratu chotulukapo chapadera cha uchimo chimenechi, Yehova anati kwa Hava: “Udzakhumba mwamuna wako, ndipo iye adzakulamulira iwe.” (Genesis 3:16) Kulamulira kolakwa kumeneku sikunakhale kusonyeza umutu koyenerera. Iko kwasonyeza mkhalidwe wochimwa wa mwamuna ndiponso kupanda ungwiro kwa mkazi, popeza kuti nthaŵi zina akazi avutika chifukwa choyesayesa kulanda ulamuliro wa amuna awo.
11. Kodi nchiyani chimene chiri chowona ponena za akazi ambiri, ndipo kodi mkonzi wina analemba zotani ponena za akazi m’nthaŵi za makolo akale?
11 Koma kuukulu umene malamulo amakhalidwe abwino a Baibulo alabadiridwa, akazi ambiri apeza chikhutiro ndi chimwemwe. Izi zinali tero ngakhale m’nthaŵi za makolo akale. Polankhula za nyengo imeneyo m’bukhu lake lakuti La Bible au Féminin (Baibulo Mkhalidwe wa Mawu Onena za Akazi), mkonzi Laure Aynard akulemba kuti: “Chomwe chiri chapadera koposa m’zolembedwa zonsezi ndi mbali yofunika imene akazi anaichita, ulemu wawo pamaso pa makolowo, ndi kuchita kwawo zinthu molimba mtima, ndi mkhalidwe waufulu umene anakhalamo.”
Akazi Pansi pa Chilamulo cha Mose
12, 13. (a) Kodi akazi anali ndi malo otani pansi pa Chilamulo cha Mose? (b) Kodi akazi anachita motani mwauzimu pansi pa Chilamulocho?
12 Mogwirizana ndi malamulo a Yehova operekedwa kupyolera mwa Mose, akazi okwatiwa anayenera kuwonedwa kukhala ‘apamtima.’ (Deuteronomo 13:6) Ulemu wa akazi okwatiwa unayenera kulemekezedwa m’nkhani za kugonana, ndipo palibe mkazi amene anayenera kuchitiridwa nkhanza mwakugonana. (Levitiko 18:8-19) Amuna ndi akazi anali ofanana pamaso pa Chilamulo ngati iwo anapezedwa ndi liŵongo la chigololo, kugonana kwa pachibale, kapena kugonana ndi zinyama. (Levitiko 18:6, 23; 20:10-12) Lamulo lachisanu linafuna kuti ulemu wolingana uperekedwe kwa atate ndi amayi.—Eksodo 20:12.
13 Pamwamba pa zonse, Chilamulo chinapereka kwa akazi mwaŵi waukulu wakukulitsa uzimu wawo. Iwo anapindula ndi kuŵerengedwa kwa Chilamulo. (Yoswa 8:35; Nehemiya 8:2, 3) Iwo anafunikira kusunga mapwando achipembedzo. (Deuteronomo 12:12, 18; 16:11, 14) Iwo anakhala ndi phande m’Sabata ya mlungu ndi mlungu ndipo akanatenga chowinda cha Mnaziri. (Eksodo 20:8; Numeri 6:2) Iwo anali ndi unansi waumwini ndi Yehova ndipo anapemphera kwa iye aliyense payekha.—1 Samueli 1:10.
14. Kodi katswiri wa Baibulo Wachikatolika akunenanji ponena za akazi Achihebri, ndipo kodi tinganenenji ponena za mbali ya akazi pansi pa Chilamulo?
14 Pothirira ndemanga pa akazi Achihebri, katswiri wa Baibulo Wachikatolika, Roland de Vaux akulemba kuti: “Ntchito yonse yovuta yapanyumba inamgwera iye; iye ankasamalira ziŵeto, ankagwira ntchito m’munda, kuphika chakudya, kupota thonje, ndi zina zotero. Komabe, mmalo mompangitsa kukhala ndi malo otsika, ntchito yowoneka kukhala yothodwetsayi inampangitsa kukhala wolingaliridwa. . . . Ndipo ndime zosawonekawoneka zimene zimatipatsa chithunzi cha kugwirizana kwa moyo wabanja zimasonyeza kuti mkazi Wachiisrayeli ankakondedwa ndi kumveredwa ndi mwamuna wake, ndikuti ankamchitira monga wolingana naye. . . . Ndipo palibe chikaikiro chakuti aka kanali kachitidwe kachibadwa. Chinali chisonyezero chokhulupirika cha chiphunzitso chopatulika cha Genesis, kumene Mulungu akunenedwa kuti analenga mkazi monga mthandizi wa mwamuna, kwa amene anayenera kumamatira (Gn 2:18, 24); ndipo mutu womalizira wa Miyambo umatamanda mkazi wabwino, wodalitsidwa ndi ana ake, ndi kunyada kwa mwamuna wake (Miy 31:10-31).” (Ancient Israel—Its Life and Institutions) Mosakaikira, pamene Chilamulo chinatsatiridwa mu Israyeli, akazi sanachitiridwe moipa.
Akazi Otchuka
15. (a) Kodi mkhalidwe wa Sara umafotokoza motani mwafanizo unansi woyenera pakati pa mwamuna ndi mkazi wake? (b) Kodi nchifukwa ninji nkhani ya Rahabi iri yofunika?
15 Malemba Achihebri ali ndi zitsanzo zambiri za akazi amene anali atumiki otchuka a Yehova Mulungu. Sara amapereka chitsanzo chabwino cha mmene mkazi wopembedza angakhalire wogonjera kwa mwamuna wake ndipo panthaŵi imodzimodziyo kukhala womthandiza popanga zosankha. (Genesis 21:9-13; 1 Petro 3:5, 6) Nkhani ya Rahabi njofunikanso. Imasonyeza chinenezo chakuti Yehova amakondera mafuko ndikuti ngwankhalwe kwa akazi kukhala chabodza. Rahabi anali wadama yemwe sanali Mwiisrayeli. Yehova sanangomlandira iye monga mlambiri wake koma chifukwa cha chikhulupiriro chake chachikulu, chochilikizidwa ndi ntchito kuphatikizapo kusintha kwa njira ya moyo, anamulengeza kukhala wolungama. Kuwonjezerapo, anamfupa ndi mwaŵi wosayembekezereka wakukhala kholo lalikazi la Mesiya.—Mateyu 1:1, 5; Ahebri 11:31; Yakobo 2:25.
16. Kodi chitsanzo cha Abigayeli chikufotokoza chiyani mwafanizo, ndipo kodi nchifukwa ninji kachitidwe kake kanalungamitsidwa?
16 Yomwe ikuchitira fanizo mfundo yakuti Yehova samafuna kuti mkazi adzigonjera mwamuna wake mwakhungu ndi nkhani ya Abigayeli. Mwamuna wake anali wachuma, wokhala ndi magulu ambiri a nkhosa ndi mbuzi. Koma anali ‘waphunzo ndi woipa machitidwe ake.’ Abigayeli anakana kutsatira mwamuna wake m’njira yake yoipa. Posonyeza kuchenjera, kulingalira kwabwino, kudzichepetsa, ndi kufulumira kuganiza, iye analetsa mkhalidwe womwe ukanakhala wangozi kwa banja lake, ndipo anadalitsidwa molemera ndi Yehova.—1 Samueli 25:2-42.
17. (a) Kodi ndimwaŵi wapadera wotani umene akazi ena anali nawo m’Israyeli? (b) Kodi chitsanzo cha Miriamu chiri ndi phunziro lotani kwa akazi Achikristu amene angapatsidwe mwaŵi wina wautumiki?
17 Akazi angapo adali aneneri aakazi. Umo ndimo zinaliri kwa Debora, m’nthaŵi ya Oweruza. (Oweruza, mitu 4 ndi 5) Hulida anagwiritsiridwa ntchito monga mneneri wamkazi m’Yuda, mwamsanga chiwonongeko cha Yerusalemu chisanachitike. (2 Mafumu 22:14-20) Nkhani ya Miriamu njofunika. Ngakhale kuti akutchulidwa kukhala mneneri wamkazi, wotumidwa ndi Yehova, mwachiwonekere mwaŵi umenewu panthaŵi ina unampangitsa kukhala wodzikuza. Iye analephera kuzindikira ulamuliro umene Yehova anapatsa mchimwene wake wamng’ono Mose wakutsogolera Israyeli, ndipo analangidwa chifukwa cha chimenecho, chinkana kuti mwachiwonekere iye analapa ndipo anabwezeretsedwa.—Eksodo 15:20, 21; Numeri 12:1-15; Mika 6:4.
Akazi Pansi pa Chiyuda
18, 19. Kodi akazi anali ndi malo otani pansi pa Chiyuda, ndipo kodi zimenezi zinachitika motani?
18 Monga momwe tawonera, Chilamulo cha Mose chinachinjiriza zoyenera akazi ndipo, pamene chinalabadiridwa, chinalola akazi kukhala ndi moyo wokhutiritsa. Koma m’kupita kwanthaŵi, makamaka pambuyo pa chiwonongeko cha Yerusalemu mu 607 B.C.E., panabuka chipembedzo cha Chiyuda, chozikidwa pa miyambo yapakamwa mmalo mwa Chilamulo cholembedwa cha Yehova. Kuchokera m’zaka za zana lachinayi B.C.E. kumka mtsogolo, Chiyuda chinatengera nthanthi zambiri Zachigiriki. Kwakukulukulu anthanthi Achigiriki sanalabadire kwenikweni zoyenera za akazi, chotero panabuka kutsika kolinganako kwa malo a akazi mkati mwa Chiyuda. Kuyambira zaka za zana lachitatu B.C.E., akazi anayamba kupatulidwa kwa amuna m’masunagoge Achiyuda ndipo analetsedwa kuŵerenga Torah (Chilamulo cha Mose). Encyclopaedia Judaica ikuvomereza kuti: “Monga chotulukapo akazi ochepa kwenikweni ndiwo anali ophunzira.” Maphunziro anali kwakukulukulu a anyamata.
19 M’bukhu lake lakuti Jerusalem in the Time of Jesus, J. Jeremias akulemba kuti: “Polingalira zinthu zonse, malo a akazi m’malamulo achipembedzo akulongosoledwa bwino koposa m’mawu obwerezedwabwerezedwa awa: ‘Akazi, akapolo (Achikunja) ndi ana.’ . . . Tingawonjezere ku zonsezi kuti padali malingaliro oipidwa ambiri ofotokozedwa kwa akazi. . . . Chotero tiri ndi lingaliro lakuti Chiyuda m’nthaŵi ya Yesu chinkalingalira mochepa za akazi.”
Akazi Okhulupirika Omwe Ankadikirira Mesiya
20, 21. (a) Mosasamala kanthu za mkhalidwe wotonza wa atsogoleri achipembedzo Achiyuda kulinga kwa akazi, kodi ndani omwe anayenera kupezeka pakati pa awo amene ankadikirira pamene nthaŵi ya Mesiya inayandikira? (b) Kodi nchiyani chimene chikusonyeza kuti Elizabeti ndi Mariya anali ndi kudzipereka kwaumulungu kozama?
20 Mkhalidwe wachitonzo umenewu kulinga kwa akazi unali njira ina imene arabi Achiyuda ‘anapeputsira mawu a Mulungu ndi miyambo yawo.’ (Marko 7:13) Koma mosasamala kanthu za kuipidwa kumeneku, pamene nthaŵi ya kudza kwa Mesiya inayandikira, akazi ena opembedza ankadikirira mwamaso. Mmodzi wa ameneŵa anali Elizabeti, mkazi wa Zakariya, wansembe Wachilevi. Iye ndi mwamuna wake anali ‘olungama mtima pamaso pa Mulungu, namayendabe m’malamulo onse ndi zoikika za [Yehova, NW] osachimwa.’ (Luka 1:5, 6) Elizabeti anachitidwa chisomo ndi Yehova nchakuti, ngakhale kuti anali wouma ndiponso wokalamba, iye anakhala amayi a Yohane Mbatizi.—Luka 1:7, 13.
21 Posonkhezeredwa ndi mzimu woyera, Elizabeti anasonyeza chikondi chakuya kwa mkazi wina wopembedza wa m’tsiku lake, wachibale wotchedwa Mariya. Chakumapeto kwa 3 B.C.E., pamene mngelo Gabrieli anadziŵitsa Mariya kuti akakhala ndi pathupi pozizwitsa pa (Yesu), iye analankhula naye ndi mawu akuti, ‘Wochitidwa chisomo,’ nawonjezera kuti: “[Yehova, NW] ali ndi iwe.” Mwamsanga pambuyo pa zimenezo, Mariya anachezera Elizabeti, yemwe anamdalitsa iye ndi mwana anali m’mimbayo, akumamutcha Yesu “Ambuye” wake ngakhale kuti anali asanabadwe. Pakumva zimenezo, Mariya anayamba kupereka chitamando kwa Yehova chimene chimachitira umboni kudzipereka kwake kwaumulungu kozama.—Luka 1:28, 31, 36-55.
22. Pambuyo pa kubadwa kwa Yesu, kodi ndi mkazi wowopa Mulungu uti amene anasonyeza kuti anali pakati pa awo amene ankadikirira Mesiya?
22 Pamene Yesu anabadwa ndipo Mariya anamka naye kukachisi m’Yerusalemu kukampereka kwa Yehova, mkazi wina wowopa Mulungu, Ana, mneneri wamkazi wokalambayo, anasonyeza chimwemwe chake. Iye anathokoza Yehova nalankhula za Yesu kwa onse omwe ankadikirira Mesiya wolonjezedwayo.—Luka 2:36-38.
23. Kodi mtumwi Petro akulankhula motani ponena za akazi okhulupirika a nthaŵi ya Chikristu isanafike, ndipo kodi ndi mafunso otani amene adzasanthulidwa m’nkhani yotsatira?
23 Chotero, pamene nthaŵi ya uminisitala wapadziko lapansi wa Yesu inayandikira, padali “akazi oyera mtima akuyembekezera Mulungu.” (1 Petro 3:5) Ena a akazi ameneŵa anakhala ophunzira a Kristu. Kodi Yesu anawachitira motani? Ndipo kodi pali akazi lerolino amene amalandira mwachimwemwe mbali yawo yofotokozedwa m’Baibulo? Mafunso ameneŵa adzasanthulidwa m’nkhani yotsatira.
[Mawu a M’munsi]
a Volyumu 3, tsamba 1055.
b Mofananamo, “Adamu wotsirizayo,” Yesu Kristu, anali wangwiro, munthu wokwanira, chinkana kuti analibe mkazi waumunthu.—1 Akorinto 15:45.
Mafunso Obwereramo
◻ Kodi kuchitiridwa kwa akazi m’Israyeli kunasiyana motani ndi m’maiko ena?
◻ Kodi malo ochepa a Adamu ndi Hava anali otani, ndipo nchifukwa ninji?
◻ Kodi ndimalo otani amene akazi Achiisrayeli anali nawo pansi pa Chilamulo, ndipo kodi iwo anali pangozi mwauzimu?
◻ Kodi ndi maphunziro ena otani amene tingaphunzire ku miyoyo ya akazi ena otchuka a m’Malemba Achihebri?
◻ Kodi nzitsanzo zabwino zachikhulupiriro zotani zimene zingapezedwe mosasamala kanthu za malingaliro a Chiyuda?
[Bokosi patsamba 10]
“MKAZI WOOPA YEHOVA”
‘10 Mkazi wangwiro ndani angampeze? Pakuti mtengo wake uposa ngale. 11 Mtima wa mwamuna wake umkhulupirira, sadzasoŵa phindu. 12 Mkaziyo amchitira zabwino, sizoipa, masiku onse a moyo wake. 13 Afuna ubweya ndi thonje, nachita mofunitsa ndi manja ake. 14 Akunga zombo za malonda; nakatenga zakudya zake kutali. 15 Aukanso kusanache, napatsa banja lake zakudya, nagaŵira adzakazi ake ntchito. 16 Asinkhasinkha za munda, naugula; naoka mipesa ndi zipatso za manja ake. 17 Amanga m’chuuno mwake ndi mphamvu, nalimbitsa mikono yake. 18 Azindikira kuti malonda ake ampindulira; nyali yake sizima usiku. 19 Agwira njinga ya thonje ndi dzanja lake, nafumbata mtengo wake. 20 Aolowera chikhato chake osauka; natambasulira aumphawi manja ake. 21 Saopera banja lake chipale chofewa; pakuti banja lake lonse livala mlangali. 22 Adzipangira zimbwi zamaangamaanga; navala bafuta ndi guta woti biriŵiri. 23 Mwamuna wake adziŵika kubwalo, pokhala pakati pa akulu a dziko. 24 Asoka malaya abafuta, nawagulitsa; napereka mipango kwa wogulitsa malonda. 25 Avala mphamvu ndi ulemu; nangoseka nthaŵi ya mtsogolo. 26 Atsegula pakamwa pake ndi nzeru, ndipo chilangizo cha chifundo chiri pa lilime lake. 27 Ayang’anira mayendedwe a banja lake, sadya zakudya za ulesi. 28 Anake adzanyamuka, nadzamutcha wodala; mwamuna wake namtama, nati, 29 Ana aakazi ambiri anachita mwangwiro, koma iwe uposa onsewo. 30 Kukongola kungonyenga, maonekedwe okoma ndi chabe; koma mkazi woopa Yehova adzatamandidwa. 31 Mumpatse zipatso za manja ake; ndi ntchito zake zimtame kubwalo.’—Miyambo 31:10-31.
[Chithunzi pamasamba 8, 9]
Malo a mkazi m’banja anali olemekezeka