“Adalenga Iwo Mwamuna ndi Mkazi”
Mulungu ndipo adalenga munthu m’chifanizo chake, m’chifanizo cha Mulungu adamlenga iye; adalenga iwo mwamuna ndi mkazi.”—GENESIS 1:27.
1. Kodi choonadi chakhala motani dalitso kwa amuna ndi akazi achikristu?
NKWABWINO chotani nanga kukhala pakati pa anthu a Yehova ndi kuyanjana ndi amuna ndi akazi, pamodzi ndi anyamata ndi atsikana, amene chinthu chachikulu m’moyo wawo ndicho kukonda Mulungu ndi kumvera iye! Choonadi chimatimasulanso ku maganizo ndi makhalidwe amene Yehova Mulungu samakondwera nawo, ndipo chimatiphunzitsa kukhala mmene Akristu ayenera kukhalira. (Yohane 8:32; Akolose 3:8-10) Mwachitsanzo, anthu kulikonse ali ndi miyambo kapena malingaliro awo a mmene amuna ayenera kusonyezera umuna wawo ndi akazi ukazi wawo. Kodi zangokhala choncho kuti amuna anangobadwa achimuna ndipo akazi achikazi? Kapena kodi pali zinthu zina zoloŵetsedwamo zofunika kuzipenda?
2. (a) Kodi lingaliro lathu ponena za umuna ndi ukazi liyenera kudalira pa chiyani? (b) Kodi malingaliro a anthu akhala otani ponena za amuna ndi akazi?
2 Kwa ife Akristu, Mawu a Mulungu ndiwo ulamuliro umene timagonjera, mosasamala kanthu za malingaliro a munthu, chikhalidwe kapena mwambo umene tingakhale nawo. (Mateyu 15:1-9) Baibulo silimalongosola zonse pa umuna ndi ukazi. M’malo mwake, limasiya mpata wakulolera njira zosiyanasiyana, monga momwe timaonera m’malo osiyanasiyana. Kuti amuna ndi akazi akhale mmene Mulungu anawalengera, amuna ayenera kukhala ndi mkhalidwe wachimuna, ndi akazi wachikazi. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti pamene mwamuna ndi mkazi anapangidwa kuti athangatane mwakuthupi, anapangidwa kuti athangatane kupyolera m’mikhalidwe yachimuna ndi yachikazi. (Genesis 2:18, 23, 24; Mateyu 19:4, 5) Komabe, malingaliro a umuna ndi ukazi akhala oluluzika ndi opotoka. Ambiri amaganiza kuti umuna ndiwo kupondereza mwankhanza, liuma, kapena mangolomera. Kumalo ena, zimakhala zodabwitsa, ndipo zochititsa manyazi kuona mwamuna akulira poyera, kapena ngakhale mseri. Komabe, “Yesu analira” pakati pa anthu kunja kwa manda a Lazaro. (Yohane 11:35) Zimenezo zinali zoyenera kwa Yesu, amene umuna wake unali wangwiro. Anthu ambiri lero ali ndi lingaliro losayenera ponena za ukazi; amangouona kukhala mpangidwe wa thupi ndi kukongola kokopa mwamuna.
Umuna ndi Ukazi Weniweni
3. Kodi amuna ndi akazi amasiyana motani?
3 Kodi umuna weniweni nchiyani, ndipo ukazi weniweni nchiyani? The World Book Encyclopedia imanena kuti: “Amuna ndi akazi ambiri amasiyana, si m’kapangidwe ka thupi kokha, komanso m’makhalidwe ndi zokonda zawo. Zina za kusiyana kumeneku nzachibadwa. . . . Koma zosiyana zambiri zosakhala za kapangidwe ka thupi zimaoneka kukhala zodalira pa ntchito zachimuna ndi zachikazi zimene munthu aliyense amadzaphunzira. Anthu amabadwa amuna ndi akazi, koma amachita kuphunzira kukhala achimuna kapena achikazi.” Chibadwa chathu chingasonkhezere zinthu zambiri, koma kukhala ndi mkhalidwe woyenera wachimuna kapena wachikazi kumadalira pakuphunzira kwathu zimene Mulungu amafuna kwa ife ndi zimene ife patokha timasankha kuchita m’moyo.
4. Kodi Baibulo limasonyezanji ponena za ntchito za mwamuna ndi mkazi?
4 Mbiri ya Baibulo imasonyeza kuti ntchito ya Adamu inali kutsogoza monga mutu wa mkazi wake ndi ana. Anayeneranso kuchita mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu cha kudzaza dziko lapansi, kuligonjetsa, ndi kulamulira zamoyo zina zonse za padziko lapansi. (Genesis 1:28) Ntchito ya mkazi ya Hava m’banja inali kukhala ‘wothangata’ Adamu, wogonjera ku umutu wake, akumagwirizana naye pakukwaniritsa chifuno cholengezedwa ndi Mulungu kwa iwo.—Genesis 2:18; 1 Akorinto 11:3.
5. Kodi unansi pakati pa mwamuna ndi mkazi unawonongeka motani?
5 Koma Adamu analephera kukwaniritsa udindo wake, ndipo Hava anagwiritsira ntchito ukazi wake kunyengerera Adamu kuti agwirizane naye pakupandukira Mulungu. (Genesis 3:6) Mwa kudzilekerera kuchita chimene anadziŵa kuti chinali cholakwa, Adamu analephera kusonyeza umuna weniweni. Iye mofooka anasankha kutsatira mkazi wake wonyengedwayo m’malo momvera zimene Atate wake ndi Mlengi wake adanena. (Genesis 2:16, 17) Posapita nthaŵi, anthu aŵiri oyambawo anayamba kukumana ndi zimene Mulungu anali ataoneratu kuti zidzakhala zotulukapo za kusamvera. Adamu, amene poyamba analongosola mkazi wake ndi mawu okongola a ndakatulo, tsopano moipidwa anangomuti “mkazi amene munandipatsa ine.” Kupanda ungwiro kwake kunaipitsa ndi kupotoza maganizo ake ponena za umuna wake, zikumamchititsa ‘kulamulira’ mkazi wake. Hava nayenso ‘anakhumba’ mwamuna wake, mwachionekere mopambanitsa kapena mosayenera.—Genesis 3:12, 16.
6, 7. (a) Kodi ndi maganizo opotoka otani ponena za umuna amene anakhalapo Chigumula chisanachitike? (b) Kodi tingaphunzirenji pamkhalidwe womwe unaliko Chigumula chisanafike?
6 Kugwiritsira ntchito molakwa umuna ndi ukazi kunakhala koonekera kwambiri Chigumula chisanafike. Angelo amene anasiya malo awo kumwamba anavala matupi aumunthu kuti adzasangalale ndi kugonana ndi ana aakazi a anthu. (Genesis 6:1, 2) Malemba amatchula amuna okha kukhala atabadwa m’maukwati achilendo amenewo. Ndipo zikuoneka kuti ana awo onse anali osabala. Anatchedwa amphamvu, Anefili, kapena Ogwetsa, chifukwa anali kugwetsera pansi anthu ena. (Genesis 6:4, NW, mawu amtsinde) Mwachionekere, iwo anali achiwawa, andewu, opanda chifundo kwa ena.
7 Ndithudi, kukongola kwakuthupi, kaumbidwe ka thupi, ukulu wa thupi, kapena nyonga, mwa izo zokha sizimachititsa umuna kapena ukazi wa munthu kukhala woyenera. Angelo amene anavala matupi aumunthu ayenera kuti anali ndi maonekedwe okongola. Ndipo Anefili anali aakulu matupi ndi amphamvu, koma maganizo awo anali opotoka. Angelo osamverawo ndi ana awo anadzaza dziko ndi chisembwere ndi chiwawa. Chifukwa chake, Yehova anawononga dzikolo. (Genesis 6:5-7) Komabe, Chigumulacho sichinachotse chisonkhezero cha ziŵanda, ndipo sichinachotse zotulukapo za uchimo wa Adamu. Malingaliro opotoka a umuna ndi ukazi anaonekeranso pambuyo pa Chigumula, ndipo Baibulo lili ndi zitsanzo, zabwino ndi zoipa, zimene tingaphunzirirepo.
8. Nchitsanzo chabwino chotani cha umuna woyenera chimene Yosefe anapereka?
8 Yosefe ndi mkazi wa Potifara akupereka chitsanzo champhamvu cha umuna woyenera wosiyana ndi ukazi wakudziko. Mkazi wa Potifara, potengeka mtima ndi maonekedwe abwino a Yosefe, anayesa kumnyengerera. Panthaŵiyo panalibe lamulo la Mulungu lolembedwa loletsa dama kapena chigololo. Komabe, Yosefe anathaŵa mkazi wachisembwere ameneyo nasonyeza kuti anali mwamuna weniweni woopa Mulungu, wosonyeza umuna umene Mulungu amafuna.—Genesis 39:7-9, 12.
9, 10. (a) Kodi Mfumukazi Vasiti anagwiritsira ntchito molakwa motani ukazi wake? (b) Kodi ndi chitsanzo chabwino chotani cha mkhalidwe wa akazi chimene Estere anapereka kwa ife?
9 Estere ndi Mfumukazi Vasiti anapereka kwa akazi zitsanzo ziŵiri zosiyana kwambiri. Zikuoneka kuti Vasiti anaganiza kuti anali wokongola kwambiri kwakuti Mfumu Ahaswero nthaŵi zonse adzagonja pa zokhumba zake. Koma kukongola kwakeko kunali kwachiphamaso chabe. Mwa iye munalibiretu kudzichepetsa ndi ukazi chifukwa chakuti analephera kusonyeza kugonjera mwamuna wake amene analinso mfumu. Mfumuyo inamkana iye ndi kusankha mkazi wa mkhalidwe weniweni wa ukazi amene, kwenikweni anaopa Yehova, kukhala mfumukazi yake.—Estere 1:10-12; 2:15-17.
10 Estere ali chitsanzo chabwino kwambiri kwa akazi achikristu. Anali “wa maonekedwe okoma, ndi wokongola,” komanso anasonyeza kukongola kwa “munthu wobisika wa mtima, m’chovala chosaola cha mzimu wofatsa ndi wachete.” (Estere 2:7; 1 Petro 3:4) Sanaone kukongola kwa maonekedwe akunja kukhala chinthu chofunika kwambiri. Estere anasonyezanso kuchenjera ndi kudziletsa. Anali wogonjera kwa mwamuna wake, Ahaswero, ngakhale pamene moyo wake ndi miyoyo ya anthu ake inali pangozi. Estere anakhala chete pamene kunali kwanzeru kutero koma analankhula molimba mtima pamene kunali kofunika ndi panthaŵi yake yoyenera. (Estere 2:10; 7:3-6) Analandira uphungu kwa msuwani wake wachidziŵitso, Moredekai. (Estere 4:12-16) Anasonyeza chikondi chake ndi kukhulupirika kwake kwa anthu ake.
Maonekedwe Akunja
11. Kodi tiyenera kukumbukiranji ponena za maonekedwe akunja?
11 Kodi nchiyani chingathandize munthu kukhala ndi ukazi woyenera? Mayi wina anati: “Kukongola kungonyenga, maonekedwe okoma ndi chabe; koma mkazi woopa Yehova adzatamandidwa.” (Miyambo 31:30) Choncho, kuopa Mulungu koyenera nkofunika, ndipo chifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, ndi chifatso pogwiritsira ntchito lilime kumathandiza kwambiri kukhala ndi ukazi wabwino kuposa kukongola kwa thupi.—Miyambo 31:26.
12, 13. (a) Mwachisoni, kodi ambiri amakonda kulankhula mawu otani? (b) Kodi Miyambo 11:22 imatanthauzanji?
12 Nzachisoni kuti amuna ndi akazi ambiri samatsegula pakamwa pawo mwanzeru, ndipo alibenso chifundo pa lilime lawo. Mawu awo amakhala onyoza, amwano, otukwana, osalingalira ena. Amuna ena amaganiza kuti mawu otukwana ndiwo umuna, ndipo akazi ena mopusa amawatsanzira. Ndipo ngati mkazi ali wokongola koma alibe nzeru ndipo ali wamakani, wamwano, kapena waliuma, kodi angakhaledi wokongola m’lingaliro lenileni la liwulo, ukazi weniweni? “Monga chipini chagolidi m’mphuno ya nkhumba, momwemo mkazi wokongola wosasinkhasinkha bwino.”—Miyambo 11:22.
13 Kukongola kwa mkazi wa malankhulidwe onyansa, amwano, kapena opanda nzeru kuli kosagwirizana ndi ukazi uliwonse umene munthu angasonyeze. Ndipo mkhalidwe wopanda umulungu umenewo ungachititse ngakhale munthu wokongola kuoneka woipa. Tikhoza kuona kuti maonekedwe akunja a mwamuna kapena mkazi mwa iwo okha sangalungamitse kusonyeza mkwiyo, kuzaza, kapena malankhulidwe onyoza. Akristu onse akhoza ndipo ayenera kukhala okongola kwa Mulungu ndi kwa anthu anzawo mwa malankhulidwe ndi makhalidwe awo ozikidwa pa Baibulo.—Aefeso 4:31.
14. Kodi ndi mavalidwe otani amene 1 Petro 3:3-5 amalimbikitsa, ndipo mukulingalira motani za iwo?
14 Pamene kuli kwakuti umuna ndi ukazi weniweni umadalira pamikhalidwe yauzimu, tiyenera kuzindikira kuti makhalidwe akuthupi ndi maonekedwe, kuphatikizapo malaya amene timavala ndi mmene timawavalira, zimanena za ife. Mtumwi Petro mosakayikira anaganiza za mavalidwe ena ndi mapesedwe a m’zaka za zana loyamba pamene anapatsa uphungu akazi achikristu kuti: “Kukometsera kwanu kusakhale kwa kunja, kuluka tsitsi ndi kuvala zagolidi, kapena kuvala chovala; koma kukhale munthu wobisika wa mtima, m’chovala chosaola cha mzimu wofatsa ndi wachete, ndiwo wa mtengo wake wapatali pamaso pa Mulungu. Pakuti koteronso kale akazi oyera mtima, akuyembekezera Mulungu, anadzikometsera okha, namvera amuna awo a iwo okha.”—1 Petro 3:3-5.
15. Kodi akazi achikristu ayenera kusonyezanji m’mavalidwe awo?
15 Pa 1 Timoteo 2:9, 10, timapezapo mawu a Paulo onena za mavalidwe a akazi: “Akazi adziveke okha ndi chovala choyenera, ndi manyazi, ndi chidziletso . . . (umo mokomera akazi akuvomereza kulemekeza Mulungu), mwa ntchito zabwino.” Panopa anagogomezera kufunika kwa kudekha ndi chovala chokonzedwa bwino chimene chimasonyeza kulama maganizo.
16, 17. (a) Kodi amuna ndi akazi ambiri agwiritsira ntchito bwanji molakwa zovala lero? (b) Kodi tinganenenji za uphungu woperekedwa pa Deuteronomo 22:5?
16 Ngati mwamuna kapena mkazi, mnyamata kapena mtsikana, achita zinthu kapena kuvala mwa njira yodzutsa chilakolako chakugonana amanyozera umuna kapena ukazi weniweni, ndipo samalemekeza konse Mulungu. Anthu ambiri m’dziko amachita mopambanitsa kusonyeza umuna kapena ukazi wawo mwa mavalidwe ndi makhalidwe awo. Ena amabisa ukazi kapena umuna ndi zolinga za chisembwere. Tili oyamikira chotani nanga ife Akristu kuti Baibulo limatiuza malingaliro a Mulungu! Yehova analengeza kwa Israyeli wakale kuti: “Mkazi asavale chovala cha mwamuna, kapena mwamuna asavale chovala cha mkazi; pakuti aliyense wakuchita izi Yehova Mulungu wanu anyansidwa naye.”—Deuteronomo 22:5.
17 Pankhaniyi, mudzakondwa kuŵerenganso Nsanja ya Olonda ya August 15, 1988, tsamba 17: “Nkhani sili yakuti kaya sitaelo ili yatsopano mopambanitsa koma, kuti kodi ili yoyenerera kwa mmodzi wodzinenera kukhala mtumiki wa Mulungu? (Aroma 12:2; 2 Akorinto 6:3) Zovala zosasamala kwambiri kapena zothina zingaletse uthenga wathu kumveka. Masitaelo amene mwadala amachititsa amuna kuoneka akazi kapena akazi kuoneka amuna sali konse oyenera. (Yerekezerani ndi Deuteronomo 22:5.) Ndithudi, mikhalidwe m’malo ena imasiyana, zikumadalira pa kachedwe kakunja, zofunikira pogwira ntchito, ndi zina zotero, choncho mpingo wachikristu sumapanga malamulo osasintha ogwira ntchito kuzungulira dziko lonse.”
18. Kodi tiyenera kuchitanji kuti tigwiritsire ntchito uphungu wa Baibulo pamavalidwe ndi kapesedwe?
18 Ha, ndi uphungu wabwino ndi woyenera chotani nanga! Mwachisoni, Akristu ena, amuna ndi akazi, amangotsatira mwaumbuli zilizonse zimene dziko limathokoza m’mavalidwe ndi mapesedwe popanda kulingalira za chithunzi chimene zingapereke pa Yehova ndi mpingo wachikristu. Aliyense wa ife ayenera kudzipenda kuona ngati kuti watengera kalingaliridwe ka dzikoli. Kapena tikhoza kufikira mbale kapena mlongo wolemekezeka ndi wachidziŵitso ndi kumfunsira malingaliro ake ponena za masinthidwe amene tiyenera kupanga m’kavalidwe kathu ndiyeno kupenda malingalirowo mosamalitsa.
Amuna ndi Akazi Achikristu—Ndiwo Amuna ndi Akazi Enieni
19. Kodi tiyenera kukaniza chisonkhezero choipa chotani?
19 Mulungu wa dzikoli ndi Satana, ndipo chisonkhezero chake chimaonekera m’chisokonezo chimene wachititsa ponena za ukazi ndi umuna, ndipo zimenezo zimaloŵetsamo zoposa zovala chabe. (2 Akorinto 4:4) M’maiko ena akazi ambiri amalimbirana umutu ndi amuna, akumanyalanyaza mapulinsipulo a Baibulo. Kumbali ina, amuna ochuluka amangonyalanyaza udindo wawo wa umutu, monga momwe anachitira Adamu. Pali awo amene amayesa ngakhale kusintha ukazi kapena umuna. (Aroma 1:26, 27) Baibulo silimapereka njira zina zamoyo zovomerezedwa ndi Mulungu. Ndipo aliyense amene, asanakhale Mkristu, sanadziŵe bwino mmene ayenera kukhalira kapena zoyenera akazi kapena amuna, ayenera kudziŵa kuti zidzamkhalira bwino kosatha ngati akhala ndi moyo wogwirizana ndi njira ya Mulungu, njira imene onse adzayamikira omwe adzafikira ungwiro wa munthu.
20. Kodi Agalatiya 5:22, 23 ayenera kutithandiza kukhala ndi lingaliro lotani la umuna ndi ukazi?
20 Malemba amasonyeza kuti amuna ndi akazi achikristu amafunikira kukulitsa ndi kusonyeza zipatso za mzimu wa Mulungu—chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, ndi chiletso. (Agalatiya 5:22, 23) Mwa nzeru yake yopambana, Mulungu anakhozetsa amuna kukongoletsa umuna wawo ndi akazi ukazi wawo mwa kukulitsa mikhalidwe imeneyo. Mwamuna amene amasonyeza zipatso za mzimu samavuta kulemekeza, ndipo mkazi amene amachita zimenezo samavuta kukonda.
21, 22. (a) Kodi Yesu anapereka chitsanzo chotani cha njira ya moyo? (b) Kodi Yesu anasonyeza motani umuna wake?
21 Munthu wamkulu woposa onse amene anakhalako anali Yesu Kristu, ndipo ili njira ya moyo wake imene Akristu onse ayenera kutsanzira. (1 Petro 2:21-23) Mofanana ndi Yesu, amuna ndi akazi omwe ayenera kusonyeza kuti ali okhulupirika kwa Mulungu ndi kumvera Mawu Ake. Yesu anasonyeza mikhalidwe yabwino koposa ya chikondi, kukoma mtima, ndi chifundo. Pokhala Akristu oona, tiyenera kumtsanzira iye kusonyeza kuti tilidi ophunzira ake.—Yohane 13:35.
22 Yesu Kristu anali mwamuna weniweni, ndipo mikhalidwe yake yachimuna tikhoza kuiona bwino lomwe pamene tiphunzira za mbiri ya moyo wake m’Malemba. Sanakwatirepo, koma Baibulo limasonyeza kuti anasangalala ndi mayanjano oyenera ndi akazi. (Luka 10:38, 39) Mayanjano ake ndi amuna ndi akazi nthaŵi zonse anali oyera ndi aulemu. Ali chitsanzo changwiro cha umuna. Sanalole aliyense—mwamuna, mkazi, kapena mngelo wopanduka—kumlanda umuna wake waumulungu ndi kukhulupirika kwake kwa Yehova. Sanazengereze kulandira maudindo ake, ndipo anatero mosaŵiringula.—Mateyu 26:39.
23. Ponena za ntchito ya mwamuna ndi mkazi, kodi Akristu oona ali odalitsidwa kwambiri motani?
23 Nkosangalatsa chotani nanga kukhala pakati pa anthu a Yehova ndi kuyanjana ndi amuna ndi akazi, limodzinso ndi anyamata ndi atsikana, amene chinthu chachikulu m’moyo wawo ndicho kukonda Yehova Mulungu ndi kumvera iye! Sitimakhala omangika m’goli pomvera Mawu a Mulungu. M’malo mwake, timakhala omasuka ku dzikoli ndi njira zake zimene zimaipitsa ubwino wake, chifuno chake, ndi mbali zake zosiyana za umuna ndi ukazi. Tikhoza kukhala ndi chimwemwe chenicheni cha kuchita mbali yathu yopatsidwa ndi Mulungu m’moyo, kaya tikhale amuna kapena akazi. Inde, tili oyamikira chotani nanga kwa Yehova Mulungu, Mlengiyo, pa zogaŵira zake zonse zachikondi kwa ife, ndi potilenga mwamuna ndi mkazi!
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi Baibulo limalongosola ntchito zotani zoyenera amuna ndi akazi?
◻ Kodi umuna unapotozedwa motani Chigumula chisanachitike, ndipo wapotozedwa motani lero limodzi ndi ukazi?
◻ Kodi ndi uphungu wa m’Baibulo wotani pamaonekedwe umene muyenera kugwiritsira ntchito?
◻ Kodi amuna ndi akazi achikristu angasonyeze motani kuti ali amuna ndi akazi enieni?
[Chithunzi patsamba 17]
Ngakhale kuti anali wokongola, timamkumbukira kwambiri Estere chifukwa cha kudzichepetsa kwake ndi mzimu wake wachete ndi wofatsa
[Chithunzi patsamba 18]
Perekani chisamaliro choyenera pamaonekedwe akunja, koma chisamaliro chachikulu chikhale pakukongola kwa mkati