Genesis
3 Tsopano njoka+ inali yochenjera kwambiri kuposa nyama zonse zakutchire zimene Yehova Mulungu anapanga. Ndipo njokayo inafunsa mkaziyo kuti: “Eti nʼzoona kuti Mulungu ananena kuti musadye zipatso za mtengo uliwonse wamʼmundamu?”+ 2 Mkaziyo anayankha njokayo kuti: “Anatiuza kuti tingathe kudya zipatso za mitengo yamʼmundamu.+ 3 Koma zipatso za mtengo umene uli pakati pa munda,+ Mulungu ananena kuti: ‘Musadye zipatso zake, ndipo musayerekeze kuukhudza, chifukwa mukatero mudzafa.’” 4 Kenako njokayo inauza mkaziyo kuti: “Si zoona zimenezo, simudzafa ayi.+ 5 Mulungutu akudziwa kuti tsiku limene mudzadye chipatso cha mtengo umenewu, maso anu adzatseguka ndithu, ndipo mudzafanana ndi Mulungu. Mudzadziwa zabwino ndi zoipa.”+
6 Mkaziyo atamva zimenezo, anayamba kuona kuti zipatso za mtengowo nʼzokoma kudya, zosiririka komanso zooneka bwino. Choncho anathyola chipatso cha mtengowo nʼkudya.+ Kenako anatenga zina nʼkukapatsa mwamuna wake pa nthawi imene anali limodzi, ndipo nayenso anadya.+ 7 Atatero onse maso awo anatseguka ndipo anazindikira kuti ali maliseche. Choncho anasoka masamba a mkuyu nʼkuwamangirira mʼchiuno mwawo.+
8 Pambuyo pake, iwo anamva mawu a Yehova Mulungu pamene iye ankayendayenda mʼmundamo pa nthawi imene kamphepo kayeziyezi kankaomba. Mwamuna ndi mkaziyo atamva, anabisala pakati pa mitengo ya mʼmundamo kuti Yehova Mulungu asawaone. 9 Koma Yehova Mulungu anapitiriza kuitana mwamunayo kuti: “Kodi uli kuti?” 10 Kenako mwamunayo anayankha kuti: “Ndinamva kuitana kwanu mʼmunda muno, koma ndinachita mantha poona kuti ndili maliseche. Choncho ndinabisala.” 11 Ndiyeno Mulungu anati: “Wakuuza ndi ndani kuti uli maliseche?+ Kodi wadya chipatso cha mtengo umene ndinakulamula kuti usadzadye uja?”+ 12 Mwamunayo anayankha kuti: “Mkazi amene munandipatsayu ndi amene wandipatsa chipatso cha mtengowo, ndipo ine ndadya.” 13 Ndiyeno Yehova Mulungu anafunsa mkaziyo kuti: “Ndiye chiyani wachitachi?” Mkaziyo anayankha kuti: “Njoka ndi imene yandipusitsa, ndipo ine ndadya.”+
14 Zitatero Yehova Mulungu anauza njokayo kuti:+ “Chifukwa cha zimene wachitazi, ukhala wotembereredwa pa nyama zonse zoweta ndi zakutchire. Udzakwawa ndi mimba yako ndipo udzadya fumbi masiku onse a moyo wako. 15 Ndidzaika chidani+ pakati pa iwe+ ndi mkaziyo,+ komanso pakati pa mbadwa* yako+ ndi mbadwa yake.+ Mbadwa ya mkaziyo idzaphwanya mutu wako,+ ndipo iwe udzaivulaza chidendene.”+
16 Ndiyeno Mulungu anauza mkaziyo kuti: “Ndidzawonjezera kwambiri kuvutika kwako pa nthawi imene uli woyembekezera. Ndipo pobereka ana udzamva ululu. Uzidzafunitsitsa kukhala ndi mwamuna wako, ndipo iye azidzakulamulira.”
17 Kenako Mulungu anauza Adamu* kuti: “Popeza wamvera mawu a mkazi wako, ndipo wadya chipatso cha mtengo umene ndinakulamula kuti,+ ‘Usadzadye zipatso zake,’ nthaka ikhale yotembereredwa chifukwa cha zimene wachitazi.+ Udzavutika kulima nthakayo masiku onse a moyo wako+ kuti upeze chakudya. 18 Minga ndi zitsamba zobaya zidzamera panthaka, ndipo chakudya chako chidzakhala zomera zamʼnthaka. 19 Udzadya chakudya kuchokera mʼthukuta la nkhope yako mpaka utabwerera kunthaka, chifukwa nʼkumene unatengedwa.+ Popeza ndiwe fumbi, kufumbiko udzabwerera.”+
20 Pambuyo pa zimenezi, Adamu anapatsa mkazi wake dzina lakuti Hava,* chifukwa anali woti adzakhala mayi wa anthu onse.+ 21 Kenako Yehova Mulungu anapangira Adamu ndi mkazi wake zovala zazitali zachikopa, nʼkuwaveka.+ 22 Ndiyeno Yehova Mulungu anati: “Tsopano munthu wakhala ngati ife chifukwa wadziwa zabwino ndi zoipa.+ Choncho kuti asathyolenso ndi kudya chipatso cha mtengo wa moyo,+ nʼkukhala ndi moyo mpaka kalekale,—”* 23 Atatero Yehova Mulungu anatulutsa munthuyo mʼmunda wa Edeni,+ kuti akalime nthaka imene anatengedwako.+ 24 Choncho anathamangitsa munthuyo mʼmundamo, nʼkuika akerubi+ kumʼmawa kwa munda wa Edeniwo. Anaikanso lupanga loyaka moto, limene linkazungulira nthawi zonse, kutchinga njira yopita kumtengo wa moyo.