Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Kodi Yehova anapangana naye pangano Abrahamu ali ku Uri kapena ku Harana?
Nkhani yoyambirira yosimba za pangano la Yehova ndi Abrahamu imapezeka pa Genesis 12:1-3. Lembali limanena kuti: “Yehova anati kwa Abramu, Tuluka iwe m’dziko lako, ndi kwa abale ako, ndi ku nyumba ya atate wako, kumka ku dziko limene ndidzakusonyeza iwe; ndipo ndidzakuyesa iwe mtundu waukulu, . . . ndipo mwa iwe adzadalitsidwa mabanja onse a dziko lapansi.”a Yehova ayenera kuti anapangana naye pangano limeneli Abrahamu ali ku Uri ndipo kenako analibwerezanso ali ku Harana.
M’zaka za zana loyamba, Stefano anatchula za lamulo lomwe Yehova anauza Abrahamu kuti apite ku Kanani. Polankhula m’bwalo la milandu la Sanihedirini, iye anati: ‘Mulungu wa ulemerero anaonekera kwa kholo lathu Abrahamu, pokhala iye m’Mesopotamiya, asanayambe kukhala m’Harana; nati kwa iye, Tuluka ku dziko lako ndi kwa abale ako, ndipo tiye ku dziko limene ndidzakusonyeza iwe.’ (Machitidwe 7:2, 3) Abrahamu kwawo kunali ku Uri ndipo monga Stefano ananenera, kumeneko n’kumene Abrahamu anali pamene anamva koyamba lamulo loti apite ku Kanani. (Genesis 15:7; Nehemiya 9:7) Stefano sanatchule pangano limene Mulungu anapangana ndi Abrahamu, koma pa Genesis 12:1-3, panganolo n’logwirizana ndi lamulo loti apite ku Kanani. Choncho n’kwanzeru kukhulupirira kuti Yehova anapangana naye panganolo Abrahamu ali ku Uri.
Komabe, kuŵerenga mosamalitsa nkhani ya mu Genesis kumasonyeza kuti Yehova anabwerezanso panganolo kwa Abrahamu ali ku Harana monga anachitira kangapo konse kutchula mwatsatanetsatane zinthu zina za m’panganolo ku Kanani. (Genesis 15:5; 17:1-5; 18:18; 22:16-18) Malinga ndi zomwe Genesis 11:31, 32, amanena, bambo ake a Abrahamu, a Tera, anachoka ku Uri kupita ku Kanani pamodzi ndi Abrahamu, Sara, ndi Loti. Anafika ku Harana ndipo anakhala komweko mpaka pamene Tera anamwalira. Abrahamu anakhala ku Harana nthaŵi yaitali moti mpaka anapeza chuma chochuluka ndithu. (Genesis 12:5) Ndipo pa nthaŵi ina, Nahori mbale wake wa Abrahamu anasamukiranso komweko.
Litanena za imfa ya Tera, Baibulo limanena za mawu a Yehova kwa Abrahamu ndipo limapitiriza kuti: “Ndipo anamuka Abramu monga Yehova ananena kwa iye.” (Genesis 12:4) Choncho, Genesis 11:31–12:4 amasonyeza kuti Yehova analankhula mawu omwe ali pa Genesis 12:1-3 Tera atamwalira kale. Ngati zimenezi zili zoona, ndiye kuti Abrahamu anachoka ku Harana ndi kupita ku dziko lomwe Yehova anamusonyeza pomvera lamulo lomwe analimva kumene komanso lomwe anali atalimvapo kale ku Uri.
Malinga ndi zomwe Genesis 12:1 amanena, Yehova analamula Abrahamu kuti: “Tuluka iwe m’dziko lako, ndi kwa abale ako, ndi ku nyumba ya atate wako.” Pa nthaŵi ina, ‘dziko’ la Abrahamu linali Uri ndipo “nyumba” ya atate wake inali komweko. Komabe, bambo a Abrahamu atasamutsa banja lawo kupita ku Harana, Abrahamu anayamba kutchula malowo dziko lake. Atakhala ku Kanani zaka zambiri, Abrahamu anatuma mnyamata wake kupita ku ‘dziko lake, kwa abale ake’ kuti akapeze mkazi wa mwana wake Isake. Mnyamatayo anapita ku “mudzi wa Nahori” (mwina unali Harana kapena chapafupi pomwepo). (Genesis 24:4, 10) Kumeneko mnyamatayo anapeza Rebeka pakati pa abale a Abrahamu, m’banja lalikulu la Nahori.—Genesis 22:20-24; 24:15, 24, 29; 27:42, 43.
Stefano polankhula za Abrahamu m’bwalo la milandu la Sanihedirini anati: “Atamwalira atate wake, Mulungu anam’suntha aloŵe m’dziko lino, mmene mukhalamo tsopano.” (Machitidwe 7:4) Zimenezi zikusonyeza kuti Yehova analakhula ndi Abrahamu ku Harana. N’kwanzeru kukhulupirira kuti panthaŵiyi m’pamene Yehova anabwereza pangano lake kwa Abrahamu monga lalembedwera pa Genesis 12:1-3, chifukwa chakuti panganolo linayamba kugwira ntchito Abrahamu atapita ku Kanani. Choncho, tikapenda mfundo zonse timaona kuti n’kutheka kuti Yehova anapangana naye panganolo Abrahamu ali ku Uri ndipo analibwerezanso ali ku Harana.
[Mawu a M’munsi]
a Yehova anasintha dzina la Abramu kukhala Abrahamu ku Kanani ali ndi zaka 99.—Genesis 17:1, 5.