Kodi Mukuphunzira kwa Mlangizi Wathu Wamkulu?
“NDINAPHUNZIRA zamalamulo kwa zaka zisanu pa imodzi ya mayunivesite otchuka koposa m’Spain,” Julio anafotokoza motero. “Koma zimene ndinadziŵa pamene ndinayamba kuphunzira Baibulo zinaposa zimenezo. Yunivesite inandiphunzitsa mmene ndingachitire phunziro; Baibulo linandiphunzitsa mmene ndingakhalire ndi moyo.”
Kupyolera m’Baibulo, timadziŵa malingaliro a Mulungu, malamulo ake a mkhalidwe, ndi malangizo ake. Malemba amafotokoza Yehova kukhala “Mlangizi Wamkulu” chifukwa chakuti iye ndiye mphunzitsi wabwino kopambana m’chilengedwe chonse. (Yesaya 30:20, NW) M’lingaliro lenileni, lemba Lachihebri limatcha Iye “alangizi”—liwu lochulukitsa losonyeza kupambana. Zimenezi ziyenera kutikumbutsa kuti kuphunzitsidwa ndi Yehova kupambana kwambiri kuphunzitsidwa ndi mphunzitsi wina aliyense.
Nzeru Yeniyeni Yochokera kwa Yehova
Kodi nchifukwa ninji chiphunzitso chaumulungu chili chopindulitsa? Choyamba, chifukwa cha zinthu zamtengo wake zophunzitsidwazo. Chiphunzitso cha Yehova chimatipatsa “nzeru yeniyeni.” Ndiponso, nzeru yopatsidwa ndi Mulungu “isunga moyo” wa awo amene amaigwiritsira ntchito.—Miyambo 3:21, 22; Mlaliki 7:12.
Wolemba Salmo 119 anazindikira kuti nzeru ya Yehova inali itamtetezera m’moyo wake wonse. Mwachitsanzo, iye anaimba kuti: “Chilamulo cha pakamwa panu chindikomera koposa golidi ndi siliva zikwizikwi. Chilamulo chanu chikadapanda kukhala chikondweretso changa, ndikadatayika m’kuzunzika kwanga. Malamulo anu andipatsa nzeru yakuposa adani anga; pakuti akhala nane chikhalire. Ndili nayo nzeru yakuposa aphunzitsi anga onse; pakuti ndilingalira mboni zanu.”—Salmo 119:72, 92, 98, 99.
Wamasalmoyo sindiye yekha amene ‘akanatayika m’kuzunzika kwake,’ pakadapanda chilamulo cha Yehova. Rosa, mtsikana wina wa ku Spain, ali wotsimikiza kuti moyo wake unapulumutsidwa chifukwa chakuti anagwiritsira ntchito malamulo a mkhalidwe aumulungu. “Pofika usinkhu wa zaka 26, ndinali nditayesapo kaŵiri kudzipha,” iye akumbukira motero.
Rosa anali kuchita uhule, limodzi ndi kugwiritsira ntchito molakwa zakumwa zoledzeretsa ndi anamgoneka. “Tsiku lina, pamene ndinali nditatayiratu mtima,” iye akutero, “banja lina la Mboni linalankhula nane za mmene Baibulo lingatithandizire kuthetsa mavuto athu. Ndinayamba kuphunzira Mawu a Mulungu, amene anandisangalatsa kwambiri. M’mwezi umodzi ndinali ndi nyonga ya kuyamba moyo woyera ndi watsopano kotheratu. Tsopano popeza kuti ndinali ndi chifuno m’moyo, sindinafunikirenso chichirikizo cha zoledzeretsa kapena anamgoneka. Ndipo popeza kuti ndinafunitsitsa kukhala bwenzi la Yehova, ndinali wotsimikiza kukhala ndi moyo mogwirizana ndi miyezo yake. Kukadapanda nzeru yeniyeni ya m’Mawu a Mulungu, ndili wotsimikizira kuti bwenzi nditadzipha kale.”
Zoonadi, nzeru yochokera kwa Yehova imapulumutsa moyo. Chotero, tingapindule osati chabe ndi zophunzitsidwa zamtengo wake za chiphunzitso chaumulungu komanso ndi njira imene Yehova akugwiritsira ntchito kulangizira atumiki ake. Popeza kuti Mwana wa Mulungu, Yesu Kristu, anatilamula kukhala aphunzitsi ndi opanga ophunzira, tikufuna kudziŵa njira zogwira mtima koposa zoperekera malangizo.—Mateyu 28:19, 20.
Kugwiritsira Ntchito Mafanizo kwa Yehova
Uthenga Wabwino wa Marko umanena kuti “[Yesu] sanalankhula nawo wopanda fanizo.” (Marko 4:34) Mbali yaikulu imeneyi ya kaphunzitsidwe ka Yesu siyodabwitsa. Iye anangotsanzira imodzi ya njira zimene mauthenga aulosi a Yehova anaperekedwera ku mtundu wa Israyeli. Ameneŵa ali ndi mafanizo ambiri ofotokozedwa bwino.—Yesaya 5:1-7; Yeremiya 18:1-11; Ezekieli 15:2-7; Hoseya 11:1-4.
Mwachitsanzo, taonani mmene Yehova akugwiritsirira ntchito fanizo lamphamvu kutiphunzitsa kuti mafano ngopanda pake. Yesaya 44:14-17 amati: “Iye adzidulira yekha mikungudza, natenga mtengo wambawa, ndi wathundu, . . . nawoka mtengo wamlombwa, . . . Ndipo udzakhala kuti munthu autenthe; iye natengako, nauwotha moto; inde auyatsa, nawotcha mkate; inde, apanga mulungu, naulambira, naupanga fano losema, naligwadira. Iye atenthako mbali ina pamoto; ndi mbali inayo adya nyama; akazinga zokazinga, nakhuta, . . . Ndipo chotsalacho apanga mulungu, ngakhale fano lake losema; iye aligwadira, nalipembedza, nalipemphera nati, Ndipulumutse ine, chifukwa kuti ndinu mulungu wanga.” Mafanizo onga ameneŵa ali zipangizo zamphamvu zothandizira oona mtima kukana kulambira mafano ndi ziphunzitso zonama.
Mafunso Ofufuzira Mtima
Baibulo lilinso ndi zitsanzo za mmene Yehova anasinthira kalingaliridwe ka atumiki ake ena mwa mafunso osonkhezera maganizo. Khololo Yobu linali mmodzi wa ameneŵa. Yehova anamthandiza moleza mtima kupenda kuchepa kwake poyerekezera ndi Mulungu. Zimenezi zinachitidwa mumpambo wa mafunso, amene Yobu analephera kotheratu kuyankha.
“Unali kuti muja ndinaika maziko a dziko lapansi?” Yehova anafunsa Yobu. “Anatseka nyanja ndani ndi zitseko? . . . Kodi ungamange gulu la Nsangwe? Kapena kumasula zomangira za Akamwiniatsatana? . . . Kodi uli nalo dzanja ngati Ine Mulungu?” Mafunso ochepetsa munthu ameneŵa anaphatikizapo funso lofunika kwambiri: “Udzanditsutsa [ine Yehova] kuti ndili woipa kodi, kuti ukhale wolungama ndiwe?”—Yobu 38:4, 8, 31; 40:8, 9.
Mafunso ofufuzira mtima ameneŵa anachititsa Yobu kuzindikira kuti adalankhula mopanda nzeru. Chifukwa chake, anadzinyansa nalapa. (Yobu 42:6) Mofanana ndi nkhaniyi, mafunso osankhidwa bwino angathandize kuwongolera kalingaliridwe kolakwa ka ana athu kapena ophunzira Baibulo athu.
Kukulitsa Chidaliro
Bwanji ngati tifuna kuthandiza wina amene akulingalira kuti ali wosayenerera kapena wosakhoza? Zimene zingathandize pamenepa ndizo kukambitsirana kwa Yehova ndi mneneri wake Mose. Pamene Mulungu anauza Mose kukhala womlankhulira kwa Farao ndi Aisrayeli, mneneriyo analingalira kuti anali wosakhoza kuchita ntchitoyo. “Ine ndine munthu wosoŵa ponena,” iye anatero. Komabe, Mulungu anayankha nati: “Anampangira munthu mkamwa ndani? . . . Sindine Yehova kodi? Ndipo tsopano muka, ndipo Ine ndidzakhala mkamwa mwako, ndi kukuphunzitsa chomwe ukalankhule.”—Eksodo 4:10-12.
Yehova anasankha mbale wa Mose, Aroni, kukhala womlankhulira, ndipo iwo anachita ntchito yawo m’Igupto. (Eksodo 4:14-16) Mboni za Yehova zambiri zakhala ndi lingaliro lofanana ndi la Mose la kusakhoza pochita utumiki wa kunyumba ndi nyumba kapena umboni wa m’khwalala kwa nthaŵi yoyamba. Monga momwe zinalili ndi Mose, kudziŵa kwathu kuti Yehova akutichirikiza ndi kuti tidzatsagana ndi mtumiki wachidziŵitso kungatikhozetse kulaka mantha athu. Monga momwedi Mose anakhozera kukulitsa chidaliro kumlingo wakuti anayamba kupereka nkhani zamphamvu zimene zimapezeka m’buku lonse la Baibulo la Deuteronomo, mothandizidwa ndi Yehova nafenso tingakulitse luso la kulankhula.
Phunziro la Chochitika
Chikhumbo choona cha kuthandiza ena chilinso chofunika kwambiri. Umenewo ndi mkhalidwe umene mneneri Yona anasoŵa. Yehova anatuma Yona kukachenjeza anthu ku Nineve za chiwonongeko cha mzindawo chimene chinali kuyandikira. Modabwitsa, Anineve analapa. (Yona 3:5) Chotero, Yehova sanadzetse tsokalo. Komabe, mmalo mosangalala ndi chipambano cha mkupiti wake wa kulalikira, Yona anakwiya kuti kunenera kwake sikukakwaniritsidwa. Kodi Yehova anamthandiza motani kukhala ndi lingaliro lolondola?
Yehova anagwiritsira ntchito msatsi kuphunzitsa Yona kufunika kwa kudera nkhaŵa ena. Chomeracho chinakula mozizwitsa usiku ndipo chinapereka mthunzi wabwino kwa Yona, amene anali atamanga thandala kunja kwa Nineve. Yona “anakondwera kwambiri” ndi chomera chimenecho. Komano Yehova anachititsa mphanzi kudya chomeracho kotero kuti chinafota. Potenthedwa ndi dzuŵa ndi mphepo yotentha, Yona anakwiya nati: “Kundikomera ine kufa, kukhala ndi moyo ayi.” (Yona 4:5-8) Kodi zonsezi zinali ndi phunziro lotani?
Yehova analankhula ndi Yona nati: “Unachitira chifundo msatsiwo umene sunagwirapo ntchito, kapena kuumeretsa, umene unamera usiku, nutha usiku; ndipo sindiyenera Ine kodi kuchitira chifundo Nineve mudzi waukulu uwu; mmene muli anthu oposa zikwi zana limodzi mphambu zikwi makumi aŵiri osadziŵa kusiyanitsa pakati pa dzanja lawo lamanja ndi lamanzere, ndi zoŵeta zambiri zomwe?”—Yona 4:9-11.
Limenelo linali phunziro la chochitika lamphamvu chotani nanga! Yona anakondwera kwambiri ndi msatsi kuposa anthu zikwizikwi. Ngakhale kuti kudera nkhaŵa mbali iliyonse ya chilengedwe cha Mulungu kuli koyamikirika, kuthandizira kupulumutsa miyoyo ya anthu ndiko ntchito yathu yofunika koposa.
Kuphunzitsa Moleza Mtima
Monga momwe Yona anapezera, kukwaniritsa utumiki wathu kumakhala kovuta nthaŵi zina. (2 Timoteo 4:5) Komabe, mkhalidwe woleza mtima kulinga kwa ena udzatithandiza.
Kodi mumachita motani pamene mmodzi wa ophunzira Baibulo anu amavutika kugwira zinthu kapena amazengereza? Mlangizi wathu Wamkulu amatiphunzitsa mmene tingachitire ndi vuto lotero. Iye anasonyeza kuleza mtima kwakukulu pamene Abrahamu anamfunsitsa mafunso ponena za chiweruzo chomayandikira pa Sodomu ndi Gomora. “Kodi mudzawononga olungama pamodzi ndi oipa?” Abrahamu anafunsa motero. “Kapena alipo olungama makumi asanu mkati mwa mudzi,” Abrahamu anachonderera. “Kodi mudzawononga, simudzasiya malowo chifukwa cha olungama makumi asanu ali momwemo?” Yankho la Yehova linasonkhezera Abrahamu kupitirizabe kuchonderera kufikira chiŵerengerocho chinafika pa khumi. Yehova anadziŵa kuti banja la Loti lokha ndilo linayenera kupulumutsidwa, ndipo makonzedwe a zimenezo anali atapangidwa kale. Koma Mulungu moleza mtima analola Abrahamu kupitirizabe kumfunsa kufikira atazindikira bwino lomwe ukulu wa chifundo cha Yehova.—Genesis 18:20-32.
Yehova analingalira za kuzindikira kochepa kwa Abrahamu ndi nkhaŵa yake. Ngati nafenso tizindikira zimene wophunzira wathu sakhoza kuchita, kudzatithandiza kusonyeza kuleza mtima pamene iye akuyesayesa kumvetsetsa chiphunzitso chakutichakuti kapena kulaka chizoloŵezi choumirira.
Pitirizanibe Kuphunzira kwa Yehova
Mosakayikira Yehova Mulungu ali Mlangizi Wamkulu. Kupyolera mwa zinthu zonga mafanizo, mafunso, ndi maphunziro a zochitika, iye moleza mtima amapatsa kuzindikira. Ngati titsanzira njira zake zophunzitsira kumlingo wokulira, ifeyo tidzakhala aphunzitsi abwino.
Popeza kuti awo amene amaphunzitsa ena sayenera kunyalanyaza kudziphunzitsa, tiyenera kupitiriza ‘kuphunzitsidwa ndi Yehova.’ (Yesaya 54:13) Yesaya analemba kuti: “[Maso anu adzakhala maso oona Mlangizi wanu Wamkulu, NW]; ndipo makutu ako adzamva mawu kumbuyo kwa iwe akuti, Njira ndi iyi, yendani inu mmenemo: potembenukira inu kulamanja, ndi potembenukira kulamanzere.” (Yesaya 30:20, 21) Mwa kupitirizabe kuyenda m’njira ya Yehova ndi kuthandiza ena kutero, tingakhale ndi mwaŵi wapadera wa kuphunzira kwa Mlangizi wathu Wamkulu kosatha.
[Chithunzi patsamba 28]
Yehova anafunsa Yobu kuti: “Kodi chiombankhanga chikwera m’mwamba pochilamulira iwe, nichimanga chisanja chake m’mwamba?”
[Chithunzi patsamba 28]
Kupyolera mwa msatsi, Yehova anaphunzitsa Yona kukhala wodera nkhaŵa anthu kwambiri