Konzekerani Kaamba ka Chipulumutso Kuloŵa M’dziko Latsopano
“Kumbukirani mkazi wa Loti.”—LUKA 17:32.
1. Kodi nchitsanzo chotani cha m’mbiri cha chipulumutso chaumulungu chimene phunziro lathu lalero likugogomezera, ndipo kodi lingatipindulitse motani?
PAMBUYO ponena za chipulumutso chozizwitsa chimene Yehova anachitira Nowa ndi banja lake, mtumwi Petro anasonya ku chitsanzo china cha m’mbiri. Anakokera chisamaliro ku kupulumutsidwa kwa Loti wolungama pamene Sodomu ndi Gomora anakhalitsidwa phulusa, monga mmene tikuŵerengera pa 2 Petro 2:6-8. Tsatanetsataneyo anasungidwa kaamba ka phindu lathu. (Aroma 15:4) Kusamalitsa kwathu zimene zinachitika m’chigwirizano ndi chipulumutso chimenecho kungatithandize kutiika pa mzera wa chipulumutso kuloŵa m’dziko latsopano la Mulungu.
Mmene Timachitira ku Njira Yamoyo ya Dziko
2. Kodi ndi mkhalidwe wotani wa mu Sodomu ndi Gomora umene unatsogolera ku chiwonongeko chawo chochitidwa ndi Mulungu?
2 Kodi nchifukwa ninji mizinda imeneyo ndi nzika zake zinawonongedwa? Mtumwi Petro akutchula kumwerekera “mu mkhalidwe wachisembwere.” (2 Petro 2:7, NW) Monga momwe zasonyezedwera mwakugwiritsira ntchito liwu Lachigriki ku limene mawu amenewo atembenuzidwa, anthu a mu Sodomu ndi Gomora anamwerekera m’machitachita oipa m’mkhalidwe umene unasonyeza kupanda ulemu kowonekera, kunyozadi lamulo ndi ulamuliro. Yuda 7 akuti ‘adadzipereka ku dama ndi kutsata zilakolako zachilendo.’ Kuipitsitsa kwa mkhalidwe wawo kunawonekera pamene anthu a mu Sodomu, “anyamata ndi okalamba, anthu onse a m’mbali zonse,” anazinga nyumba ya Loti ndi kulamula kuti atulutsire alendo ake kwa amuna a Sodomu kuti iwo akhutiritse zikhumbo zawo zoipa. Ndipo anafuula minyozo pa Loti chifukwa chakuti iye anatsutsa zikhumbo zawo zoipitsitsa.—Genesis 13:13; 19:4, 5, 9.
3. (a) Kodi Loti ndi banja lake anadzakhala motani m’malo oipa onga Sodomu? (b) Kodi Loti anachitanji ku mayendedwe onyansa a anthu a mu Sodomu?
3 Poyambirirapo Loti anasamukira kufupi ndi Sodomu chifukwa cha kuthekera kwake kwa chuma chakuthupi. M’kupita kwa nthaŵi, anakhala mu mzinda mwenimwenimo. (Genesis 13:8-12; 14:12; 19:1) Koma iye sanavomerezane ndi machitachita oipa a amuna a mu mzindawo, ndipo amunawo sanamuwone monga mmodzi wa iwo, mwachiwonekere chifukwa chakuti Loti ndi banja lake sanakhale ndi phande m’moyo wawo wamayanjano. Monga mmene 2 Petro 2:7, 8 akunenera kuti: “Loti . . . wolema mtima ndi mayendedwe onyansa a oipa aja—pakuti wolungamayo pokhala pakati pawo ndi kuwona ndi kumva zawo, anadzizunzira moyo wake wolungama tsiku ndi tsiku ndi ntchito zawo zosayeruzika.” Mikhalidwe imeneyo inapereka chiyeso chachikulu kwa Loti chifukwa chakuti, monga munthu wolungama, iye anada mkhalidwe woterowo.
4. (a) Kodi ndimwanjira zotani mmene mikhalidwe lerolino iri yofanana ndi ija ya mu Sodomu wakale? (b) Ngati ndife onga Loti wolungama, kodi timachita motani ku mikhalidwe yoipa imene iripoyi?
4 M’tsiku lathunso, mlingo wamakhalidwe wa chitaganya cha anthu wakhala woluluzika. M’maiko ambiri, owonjezerekawonjezereka amadziloŵetsa m’kugonana kwa osakwatirana kapena kwa kunja kwa ukwati. Ngakhale achichepere ambiri a ku sukulu adziloŵetsa mwakuya mu mkhalidwe umenewu wa moyo, ndipo amaseka awo amene sagwirizana nawo. Ogonana ofanana ziŵalo amadzidziŵikitsa mwapoyera ndipo amaguba m’makwalala a mizinda yaikulu kufuna kuzindikiridwa. Atsogoleri achipembedzo nawonso agwirizana mu mkhalidwewo. Mwalamulo, simatchalitchi ambiri amene amaika utumiki kwa odziŵika kukhala ogonana ofanana ziŵalo ndi adama. Komabe, m’chenicheni, monga mmene malipoti a nkhani asonyezera mobwerezabwereza, nzosavuta kupeza ogonana ofanana ziŵalo, adama, ndi achigololo m’mathayo a atsogoleri achipembedzo. Kwenikwenidi, atsogoleri ena achipembedzo asamutsidwira ku mizinda ina kapena kukakamizidwa kuleka ntchito chifukwa cha zolakwa za kugonana. Okonda chilungamo samamvera chifundo kuipa koteroko; iwo ‘amada choipa.’ (Aroma 12:9) Iwo amamvadi chisoni pamene mkhalidwe wa anthu amene amadzinenera kutumikira Mulungu ubweretsa chitonzo pa dzina lake ndi kupangitsa anthu osadziŵitsidwa kutembenuka kuchoka ku zipembedzo zonse chifukwa cha kuipidwa.—Aroma 2:24.
5. Kodi kuwononga Sodomu ndi Gomora kwa Yehova kumatiyankhira funso lotani?
5 Chaka ndi chaka mkhalidwewo umaipirako. Kodi padzakhala mapeto? Inde, adzakhalapo! Zimene Yehova anachita kwa Sodomu ndi Gomora wakale zimasonyeza mowonekera kuti, pa nthaŵi yake yoikika, iye adzapereka chiweruzo. Iye adzawononga kotheratu oipa, koma adzapulumutsa atumiki ake okhulupirika.
Kodi Ndani kapena Nchiyani Chimene Chimakhala Choyamba m’Moyo?
6. (a) Kodi ndi phunziro lapanthaŵi yake lotani limene liripo m’cholembera cha amuna achichepere amene ankafuna kukwatira ana aakazi a Loti? (b) Kodi ndimotani mmene mkhalidwe wa oyembekezeredwa kukhala anzawo a muukwati unayesera ana aakazi a Loti?
6 Kokha awo amene amasonyeza kudzipereka kwaumulungu kowona ndi amene adzapulumutsidwa. M’chigwirizano ndi chimenechi, lingalirani zimene angelo a Yehova ananena kwa Loti asanawononge Sodomu ndi Gomora. “Kodi muli nawo ena pano? Mkamwini, ndi ana ako aamuna, ndi ana ako aakazi, ndi onse ali nawo m’mudzi muno, utuluke nawo m’malo muno: popeza ife tidzawononga malo ano.” Chotero Loti analankhula ndi amuna achichepere amene ankafuna kukwatira ana ake aakazi. Anawafulumiza mobwerezabwereza kuti: “Tawukani, tulukani m’malo muno; popeza Yehova adzawononga mudziwu.” Unansi wawo ku banja la Loti unawapatsa mwaŵi wapadera kaamba ka chipulumutso, koma iwo mwaumwini anafunikira kuchitapo kanthu. Iwo anayenera kupereka umboni wowoneka wa chimvero kwa Yehova. M’malo mwake, m’maso mwawo Loti “anamuyesa wongoseka.” (Genesis 19:12-14) Mungalingalire mmene ana aakazi a Loti anamverera pamene anamva zimene zinachitika. Izo zinaika chikhulupiriro chawo mwa Mulungu ku chiyeso.
7, 8. (a) Pamene angelo anafulumiza Loti kutenga banja lake ndi kuthaŵa, kodi ndimotani mmene anachitira, ndipo kodi nchifukwa ninji kumeneku kunali kupanda nzeru? (b) Kuti apulumutsidwe, kodi nchiyani chimene chinali chofunika kwambiri kwa Loti ndi banja lake?
7 M’mawa wotsatira mbandakucha, angelowo anamfulumiza Loti. Iwo anati: “Uka, tenga mkazi wako, ndi ana ako aakazi aŵiri amene ali kunowa, kuti munganyeke m’mphulupulu ya mudzi.” Koma “anachedwa.” (Genesis 19:15, 16) Chifukwa ninji? Kodi nchiyani chimene chinamuletsa? Kodi kunali kukonda zinthu zakuthupi zimene anali nazo mu Sodomu—zenizenizo zimene zinamkopa kuloŵa m’derali poyambirirapo? Ngati iye akanamamatira ku zimenezi, akanawonongedwa ndi Sodomu.
8 Chifukwa cha chifundo, angelowo anagwira padzanja a m’banja lake ndi kuwafulumiza kutuluka mu mzinda. Ali kunja kwa mzinda, mngelo wa Yehova analamula kuti: “Tapulumuka ndi moyo wako; usacheuke, usakhale pachigwa pali ponse; thawira kuphiri, kuti unganyeke.” Loti anazengerezabe. Pomalizira pake, pamene anavomerezana kuti angapite ku malo amene sanali kutali kwambiri, iye ndi banja lake anathaŵa. (Genesis 19:17-22) Sipakadakhalanso kuchedwa kwina; chimvero chinali chofunika koposa.
9, 10. (a) Kodi nchifukwa ninji kukhala ndi mwamuna wake sikunali kokwanira kutsimikizira chipulumutso kwa mkazi wa Loti? (b) Pamene mkazi wa Loti anaphedwa, kodi ndi chiyeso chowonjezereka chotani chimene chinabwera pa Loti ndi ana ake aakazi?
9 Komabe, chipulumutso chinali chisadathebe pamene iwo anatuluka mu Sodomu. Genesis 19:23-25 akutiuza kuti: “Ndipo dzuŵa lidakwera pa dziko pamene Loti anafika ku Zoari. Ndipo Yehova anavumbitsa pa Sodomu ndi pa Gomora miyala ya sulfure ndi moto kutuluka kwa Mulungu kumwamba; ndipo anawononga midziyo, ndi chigwa chonse, ndi onse akukhala m’midzimo, ndi zimene zimera panthaka.” Koma kodi mkazi wa Loti anali kuti?
10 Iye adathaŵa ndi mwamuna wake. Komabe, kodi anali wogwirizana kotheratu ndi zimene mwamunayo ankachita? Palibe chirichonse chosonyeza kuti mwanjira iriyonse anavomereza mikhalidwe yachisembwere ya Sodomu. Koma kodi chikondi chake cha Mulungu chinali champhamvu kuposa kumamatira kwake ku nyumba yake ndi zinthu zakuthupi zimene anali nazo kumeneko? (Yerekezerani ndi Luka 17:31, 32.) Zimene zinali mu mtima mwake zinawonekera pansi pa chitsenderezo. Mwachiwonekere iwo anali kale pafupi ndi Zoari, mwinamwake ali pafupi kuloŵa mumzindawo, pamene iye mosamvera anatembenuka nayang’ana kumbuyo. Ndipo monga mmene cholembera cha Baibulo chikunenera, “nasanduka mwala wamchere.” (Genesis 19:26) Tsopano chiyeso chowonjezereka cha chikhulupiriro chinali pa Loti ndi ana ake aakazi. Kodi kumamatira kwa Loti kwa mkazi wake womwalira kapena malingaliro a asungwanawo kulinga kwa amayi awo omwalira anali amphamvu kuposa chikondi chawo cha Yehova, amene anabweretsa tsokalo? Kodi akapitiriza kumvera Mulungu ngakhale kuti winawake wapafupi kwenikweni anakhala wosakhulupirika? Ndi chikhulupiriro chotheratu mwa Yehova, iwo sanayang’ane m’mbuyo.
11. Kodi taphunziranji pano ponena za chipulumutso chimene Yehova akupereka?
11 Inde, Yehova amadziŵa kulanditsa anthu odzipereka mwaumulungu ku chiyeso. Iye amadziŵa kulanditsa mabanja onse amene ali ogwirizana m’kulambira kowona; amadziŵanso kupulumutsa munthu payekha. Pamene iwo mowonadi amkonda iye, amasonyeza kulingalira kwakukulu pochita nawo. “Popeza adziŵa mapangidwe athu; akumbukira kuti ife ndife fumbi.” (Salmo 103:13, 14) Koma chipulumutso chake chiri kokha kaamba ka awo amene ali anthu odzipereka mwaumulungu, awo amene kudzipereka kwawo kuli kwenikweni, awo amene kumvera kwawo kuli chisonyezero cha kukhulupirika.
Kukonzekera Kwachikondi kaamba ka Chipulumutso Chachikulu
12. Kodi ndi makonzedwe achikondi otani amene Yehova anapanga asanabweretse chipulumutso chimene tikuchiyembekezera mofunitsitsa chotero?
12 Yehova sanachotse oipa onse kosatha ndi zimene anachita m’masiku a Nowa ndi Loti. Monga mmene lemba likunenera, zinangokhazikitsa chitsanzo cha zinthu zirinkudza. Zinthu zimenezo zisanafike, Yehova anafuna kuchita zambiri kupindulitsa anthu amene amamkonda. Iye anafuna kutumiza Mwana wake wobadwa yekha, Yesu Kristu, ku dziko lapansi. Panopo, Yesu akachotsa chitonzo pa dzina la Mulungu mwakusonyeza mtundu wa kudzipereka umene Adamu monga munthu wangwiro anayenera ndipo umene akanapereka kwa Mulungu; koma Yesu akakuchita pansi pa mikhalidwe yovuta kwambiri. Yesu akapereka moyo wake waumunthu wangwiro monga nsembe kotero kuti mbadwa za Adamu zimene zikasonyeza chikhulupiriro zingakhale ndi chimene Adamu anataya. Pamenepo, “kagulu ka nkhosa” ka anthu okhulupirika kakasankhidwa ndi Mulungu kugwirizana ndi Kristu mu Ufumu wake wakumwamba, ndipo “khamu lalikulu” likasonkhanitsidwa kuchokera ku mitundu yonse kupanga maziko a chitaganya chatsopano cha anthu. (Luka 12:32; Chibvumbulutso 7:9) Zimenezo zitakwaniritsidwa, Mulungu akapanga chipulumutso chachikulu chophiphiritsidwa ndi zochitika zogwirizana ndi Chigumula ndi chiwonongeko cha Sodomu ndi Gomora.
Chifukwa Chake Kachitidwe Kosankha Kali Kofunika Tsopano
13, 14. Kodi tingaphunzirenji ku nsonga yakuti Petro anagwiritsira ntchito chiwonongeko cha anthu opanda umulungu m’masiku a Loti ndi Nowa monga zitsanzo?
13 Ophunzira a Mawu a Mulungu amadziŵa kuti Yehova wachita machitidwe a chipulumutso kwa atumiki ake pa zochitika zambiri. Komabe, m’zochitika zambiri Baibulo silinena kuti, ‘Monga mmene zinaliri pa nthaŵi imeneyo, kudzateronso kudza kwake kwa Mwana wa munthu.’ Kodi nchifukwa ninji mtumwi Petro, wouziridwa ndi mzimu woyera, akusankha zitsanzo ziŵiri zokha? Kodi ndi kusiyana kotani kumene kunalipo pakati pa zimene zinachitika m’masiku a Loti ndi a Nowa?
14 Chisonyezo chotsimikizirika chikupezeka pa Yuda 7, pamene tikuŵerenga kuti “Sodomu ndi Gomora, ndi midzi yakuizungulira, . . . iikidwa chitsanzo, pakuchitidwa chilango cha moto wosatha.” Inde, chiwonongeko cha ochimwa mopambanitsa m’mizinda imeneyo chinali chamuyaya, monga mmene chidzakhalira chiwonongeko pamapeto pa dongosolo loipa la zinthu. (Mateyu 25:46) Chigumula cha tsiku la Nowa mofananamo chikulozeredwa m’mawu ozungulira lembalo amene akulongosola ziweruzo zamuyaya. (2 Petro 2:4, 5, 9-12; 3:5-7) Chotero mwakuwononga anthu opanda umulungu m’masiku a Loti ndi Nowa, Yehova anasonyeza kuti adzapulumutsa atumiki ake mwakuwononga kosatha amene amachita chisalungamo.—2 Atesalonika 1:6-10.
15. (a) Kodi ndi chenjezo lamwamsanga lotani limene likuperekedwa kwa awo amene amadziloŵetsa m’machitachita oipa? (b) Kodi nchifukwa ninji chilungamo chidzaperekedwa kwa onse amene amaumirira m’chisalungamo?
15 Chiwonongeko cha oipa sichimakondweretsa Yehova, sichimakondweretsanso atumiki ake. Kupyolera mwa Mboni zake, Yehova akufulumiza anthu kuti: “Bwererani, bwererani, kuleka njira zanu zoipa, muferenji inu?” (Ezekieli 33:11) Mosasamala kanthu za izo, pamene anthu sasonyeza chikhumbo chirichonse cha kulabadira kuchonderera kwachikondi kumeneku koma aumirirabe m’njira yawo yamoyo yadyera, ulemu wa Yehova kaamba ka dzina lake loyera ndi chikondi chake kaamba ka atumiki ake okhulupirika amene amavutika ndi kuipsyidwa ndi anthu opanda umulungu zimafuna kuti iye achite chilungamo.
16. (a) Kodi nchifukwa ninji tingakhale ndi chidaliro kuti chipulumutso chonenedweratucho chiri pafupi kwambiri? (b) Kodi chipulumutso chidzapulumutsa ku chiyani ndi kupereka kuti?
16 Nthaŵi ya Mulungu yobweretsa chipulumutso iri pafupi kwambiri! Mikhalidwe ndi zochita zimene Yesu ananeneratu kukhala chizindikiro cha kukhalapo kwake ndi cha mathedwe a dongosolo la zinthu zikuwoneka poyera. Mbali za chizindikiro chimenecho zinayamba kuwoneka zaka zoposa 75 zapitazo, ndipo Yesu anati “mbadwo uno” sudzatha kuchoka Mulungu asanapereke chiweruzo pa dziko lopanda umulunguli. Pamene Yehova agamulapo kuti uthenga wa Ufumu walengezedwa ku ukulu wokwanira pa dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni kwa mitundu yonse, pamenepo mapeto a dziko loipali adzadza, ndipo ndi zimenezo kudzadzanso chipulumutso kwa anthu odzipereka mwaumulungu. (Mateyu 24:3-34; Luka 21:28-33) Kupulumutsidwa ku chiyani? Ku ziyeso zimene akhala akupyolamo zochokera kwa oipa, ndi ku mikhalidwe imene tsiku ndi tsiku yakhala magwero a chipsyinjo kwa iwo monga okonda chilungamo. Chidzakhalanso chipulumutso kuloŵa m’dziko latsopano kumene matenda ndi imfa zidzakhala zinthu zakale.
Thandizo Laumulungu Pokhala ndi Chipulumutso m’Chiyang’aniro
17. (a) Kodi ndi funso lodekha lotani limene tiyenera kudzifunsa? (b) Kodi ndimotani mmene tingaperekere umboni kuti, mofanana ndi Nowa, tikufulumizidwa ndi “mantha aumulungu”?
17 Funso limene tiyenera kulingalira aliyense payekha ndilakuti, ‘Kodi ndine wokonzekera kaamba ka kachitidwe ka Mulungu kameneko?’ Ngati tikukhulupirira mwa ife tokha kapena lingaliro la ife tokha la chilungamo, sindife okonzekera. Koma ngati, mofanana ndi Nowa, tafulumizidwa ndi “mantha aumulungu,” pamenepo tikuvomereza m’chikhulupiriro ku chitsogozo chimene Yehova akutipatsa, ndipo ichi chidzatsogoza ku chipulumutso chathu.—Ahebri 11:7, NW.
18. Kodi nchifukwa ninji kuphunzira ulemu weniweni kaamba ka ulamuliro wateokratiki kuli mbali yofunika koposa ya kukonzekera kwathu kaamba ka chipulumutso kuloŵa m’dziko latsopano?
18 Polongosola mokongola awo amene akusangalala ndi chitetezo chimene Yehova akuchipereka tsopano, Salmo 91:1, 2 likuti: “Iye amene akhala pansi m’ngaka yake ya Wam’mwambamwamba adzagonera mu mthunzi wa Wamphamvuyonse. Ndidzati kwa Yehova, Pothaŵirapo panga ndi linga langa; Mulungu wanga, amene ndimkhulupirira.” Pano pali gulu la anthu amene achinjirizidwa ndi Mulungu mofanana ndi anapiye pansi pa mapiko amphamvu a mbalame yomwe iri kholo. Chidaliro chawo chotheratu chiri mwa Yehova. Iwo amavomereza kuti iye ali Wam’mwambamwamba, Wamphamvuyonse. Monga chotulukapo, iwo amalemekeza ulamuliro wateokratiki ndi kudzigonjetsera ku iwo, kaya umachitidwa ndi makolo kapena “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyu 24:45-47) Kodi zimenezo nzowona kwa ife aliyense payekha? Mofanana ndi Nowa, kodi tikuphunzira kuchita ‘zonse zimene Yehova walamula’ kwa ife ndi kuchita zinthu m’njira yake? (Genesis 6:22) Ngati nditero, tikuvomereza ku kukonzekera kumene Yehova akutipatsa kaamba ka chipulumutso kuloŵa m’dziko lake latsopano lolungama.
19. (a) Kodi mtima wathu wophiphiritsira nchiyani, ndipo kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kuwupatsa chisamaliro? (Miyambo 4:23) (b) Kodi tingapindule motani ndi chitsanzo cha Loti ponena za kachitidwe kathu kulinga ku zokopa zakudziko?
19 Kukonzekera koteroko kumaloŵetsamonso kupereka chisamaliro ku mtima wathu wophiphiritsira. “Yehova ayesa mitima.” (Miyambo 17:3) Iye amatithandiza kuzindikira kuti sichiri kokha mmene timawonekera kunja chimene amawerengera, m’malomwake, ali munthu wamkati, mtima. Pamene kuli kwakuti sitimadzimwereketsa m’chiwawa kapena chisembwere mofanana ndi dziko lotizinga, nafenso tiyenera kukhala ochenjera kusadzilola ife eni kunyengedwa kapena kusangalatsidwa ndi zinthu zimenezi. Mofanana ndi Loti, tiyenera kuipidwa ndi kukhalapo kwenikweni kwa machitidwe osaweruzika oterowo. Awo amene amadana nacho choipa sadzafuna njira yodziloŵetseramo; komabe, anthu amene samachida angapeŵe mwakuthupi pamene mwamaganizo akukhumba kuti akanakhalako ndi phande. “Inu okonda Yehova, danani nacho choipa.”—Salmo 97:10.
20. (a) Kodi ndi m’njira zotani zimene Baibulo limatichenjezera ponena za njira yamoyo yokondetsa zakuthupi? (b) Kodi tingadziŵe motani kaya ngati maphunziro ofunika a Baibulo pa kukondetsa zakuthupi akhazikika mu mtima mwathu?
20 Mwachikondi Yehova akutiphunzitsa kupeŵa osati kokha mayendedwe achisembwere komanso njira yamoyo yokondetsa zinthu zakuthupi. Mawu ake akupereka uphungu wakuti, ‘Khalani okwanira ndi zakudya ndi zofunda.’ (1 Timoteo 6:8) Nowa ndi ana ake aamuna anayenera kusiya nyumba zawo pamene analoŵa m’chingalawa. Loti ndi banja lakenso, anayenera kusiya nyumba ndi katundu kotero kuti apulumutse miyoyo yawo. Kodi ndikuti kumene talunjikitsa chikondi chathu? “Kumbukirani mkazi wa Loti.” (Luka 17:32) Yesu anafulumiza kuti: “Koma muthange mwafuna ufumu wake ndi chilungamo chake.” (Mateyu 6:33) Kodi tikuchita zimenezo? Ngati miyezo yolungama ya Yehova imatitsogoza ndipo ngati kulengezedwa kwa mbiri yabwino ya Ufumu kuli chodera nkhaŵa choyamba m’miyoyo yathu, pamenepa ndithudi tikuvomereza ku kukonzekeretsa kwake anthu kaamba ka chipulumutso kuloŵa m’dziko latsopano.
21. Kodi nchifukwa ninji molondola tingayembekezere kuti lonjezo la Yehova la chipulumutso lidzakwaniritsidwa?
21 Kwa anthu odzipereka mwaumulungu amene akawona kukwaniritsidwa kwa chizindikiro cha kukhalapo kwake mu ulamuliro wa Ufumu, Yesu anati: “Weramukani, tukulani mitu yanu; chifukwa chiwomboledwe chanu chayandikira.” (Luka 21:28) Kodi mwachiwona chizindikiro chimenecho pamene chakulitsidwa m’tsatanetsatane wake yense? Chotero khalani ndi chidaliro chakuti kukwaniritsidwa kwa lonjezo la Yehova la chipulumutso kuli pafupi kwambiri! Khalani okhutiritsidwa mokwanira kuti “Yehova amadziŵa kulanditsa anthu odzipereka mwaumulungu ku chiyeso.”—2 Petro 2:9, NW.
Kodi Mwaphunziranji?
◻ Mofanana ndi Loti, kodi tiyenera kuchitanji ku mikhalidwe yamoyo ya dziko?
◻ Kodi ndi ziyeso zotani zimene Loti ndi banja lake anakumana nazo ngakhale pamene ankathaŵa kusiya Sodomu?
◻ Kodi ndimotani mmene zitsanzo zogwiritsiridwa ntchito ndi Petro zikugogomezera kufulumira kwa kukhala ndi kaimidwe kolimba ku mbali ya Yehova tsopano?
◻ Pokonzekeretsa anthu ake kaamba ka chipulumutso, kodi ndi maphunziro ofunika koposa otani amene Yehova akuphunzitsa?
[Chithunzi patsamba 18]
Anthu a Mulungu ngwochinjirizidwa ndi iye monga anapiye pansi pa mapiko amphamvu a kholo lawo