Abrahamu—Chitsanzo Kaamba ka Onse Ofunafuna Ubwenzi wa Mulungu
“Ndipo iye osafooka m’chikhulupiriro, . . . nakhazikikanso mumtima kuti, chimene [Mulungu] analonjeza, anali nayonso mphamvu yakuchichita.”—AROMA 4:19-21.
1. Nchifukwa ninji Satana wayesera kutsitsa cholembera chonena za Abrahamu?
MAWU aumulungu oikidwa m’Malemba ali “amoyo ndi ochitachita.” (Ahebri 4:12) Chotero, cholembera cha zochita za Yehova ndi Abrahamu, ngakhale kuti chinalembedwa zoposa zaka 3,500 zapitazo, chiri magwero a chilimbikitso kwa onse ofunafuna ubwenzi wa Mulungu. (Aroma 15:4) Mdani wamkulu, Satana, amadziŵa chimenechi ndipo wagwiritsira ntchito atsogoleri achipembedzo kuyesera kutsitsa cholembera chimenecho kukhala nthano.—2 Akorinto 11:14, 15.
2. Ndi kawonedwe kotani kamene ophunzira a Yesu anali nako ka Abrahamu?
2 Monga mbali ya “Lemba lirilonse . . . adaliwuzira Mulungu,” mbiri ya Abrahamu iri yowona ndi “yopindulitsa kaamba ka chiphunzitso [Chachikristu].” (2 Timoteo 3:16; Yohane 17:17) Ophunzira oyambirira a Yesu motsimikizirika anayamikira chimenechi, Abrahamu akumatchulidwa nthaŵi 74 m’Malemba Achikristu a Chigriki. Mu mutu 11 wopatsa chikhulupiriro wa Ahebri, malo aakulu aperekedwa kwa iye kuposa kwa mtumiki wina aliyense wa Mulungu wa nthaŵi ya Chikristu chisanakhale.
3. Ndimotani mmene Abrahamu analemekezedwera mokulira?
3 Abrahamu sanali “mneneri” wamba, popeza kuti Yehova anamgwiritsira ntchito iye kuchitira chithunzi “drama yophiphiritsira” (NW) yaikulu mu imene khololo linalemekezedwa mokulira m’kuchita monga mtundu wolosera wa Mulungu iyemwini. (Genesis 20:7; Agalatiya 4:21-26) Chotero, Yesu analankhula za “m’chifuwa cha Abrahamu” pamene anachitira fanizo malo achiyanjo ndi Mulungu.—Luka 16:22.
Kachitidwe Kake Koyambirira ka Chikhulupiriro
4. Mogwirizana ndi Baibulo, ndimotani mmene zochita za Mulungu ndi Abramu zinayambira?
4 Abramu, monga mmene iye poyambirira anatchedwera, analeredwa mu “Uri wa kwa Akaldayo.” Pamene iye anali kukhala kumeneko, Yehova Mulungu anawonekera kwa iye ndi kunena kuti: “Tuluka iwe m’dziko lako, ndi kwa abale ako, ndi ku nyumba ya atate wako, kunka ku dziko limene ndidzakusonyeza iwe; ndipo ndidzakuyesa iwe mtundu waukulu, ndipo ndidzakudalitsa iwe, ndi kubukitsa dzina lako; nukhale iwe mdalitso; ndipo ndidzadalitsa amene akudalitsa iwe; ndi kutemberera iye amene akutemberera iwe; ndipo mwa iwe adzadalitsidwa mabanja onse a dziko lapansi.”—Genesis 12:1-3; 15:7; Machitidwe 7:2, 3.
5. (a) Ndimotani mmene lonjezo la Mulungu linakhudzira mtima wa Abramu? (b) Ndimotani mmene Abramu anavomerezera ku lonjezolo?
5 Ndi chiitano chotokosa chotani nanga! Kwa Abramu, kumvera icho kunatanthauza kusiya malo ozungulira okhumbirika ndi achibale ake kaamba ka moyo kutali m’dziko lachilendo. Koma mtima wa Abramu unakhudzidwa mozama ndi lonjezo lachikondi la Mulungu. Monga mwamuna wokalamba wopanda mwana wokhala ndi mkazi wowuma, dzina lake linawoneka kukhala paulendo wonka ku kuiwalidwa posachedwapa. Lonjezo la Mulungu linatsimikizira chosiyanako: “Mtundu waukulu” ukatuluka kuchokera kwa iye. M’kuwonjezerapo, lonjezo la Mulungu linaphatikizapo chilengezo chozizwitsa cha mbiri yabwino kaamba ka mtundu wonse wa anthu, kuloza kutsogolo ku nthaŵi pamene mitundu yonse ikadalitsidwa. (Agalatiya 3:8) Abramu anasonyeza chikhulupiriro m’lonjezo la Yehova ndi kusiya malo apakati a kutsungula kopita patsogolo. “Anatuluka,” Baibulo likutiuza ife, “osadziŵa kumene akamukako.”—Ahebri 11:8.
6. (a) Nchifukwa ninji Genesis 11:31 imalemekeza Tera ndi kupanga ulendowo? (Machitidwe 7:2-4) (b) Kodi ndi m’njira zotani mmene Sara analiri chitsanzo kaamba ka akazi Achikristu lerolino?
6 Chikhulupiriro cha Abramu chinayambukira ena. Banja lake, limodzinso ndi Tera, atate wake, ndi Loti, mwana wa mphwake, anachoka limodzi naye. Ngakhale kuli tero, chifukwa chakuti Tera anali kholo la umutu la banjalo, iye akuyamikiridwa ndi kupanga ulendowo. (Genesis 11:31) Choyenera kuzindikiridwa chiri chichirikizo chimene Abramu analandira kuchokera kwa mkazi wake, Sarai, yemwe pambuyo pake anatchedwa Sara. Iye anapirira ndi muyezo wotsika wa kakhalidwe kwa moyo wake wonse. (Genesis 13:18; 24:67) Momvetsetseka, pa imfa yake, “Abrahamu anadza ku maliro a Sara, kuti amulire.” (Genesis 23:1, 2) Chifukwa cha chikhulupiriro chake cholimba ndi kugonjera kwa mtima wonse kwa ukazi, iye wakhazikitsidwa monga chitsanzo cha kukongola kowona kwauzimu kwa akazi Achikristu.—Ahebri 11:11, 13-15; 1 Petro 3:1-6.
7. Kodi ndi m’njira zotani mmene Akristu lerolino amasonyezera chikhulupiriro chonga chija cha Abrahamu ndi Sara?
7 Akristu ambiri lerolino asonyeza chikhulupiriro chofananacho mwa kudzipereka kufalitsa uthenga wa Mulungu m’malo amene ali ndi kusowa kokulira kaamba ka olalikira a Ufumu ndi kumanga ndi kugwiritsira ntchito kwa zinthu zatsopano zosindikizira ndi kutumiza mabukhu a Baibulo. (Mateyu 24:14) Akristu amenewa agawanamo m’kumvera lamulo lakuti, “Mukani phunzitsani anthu amitundu yonse.” M’kusamukira ku dziko lachilendo, iwo kaŵirikaŵiri afunikira kusinthira ku muyezo wosiyanako wa kakhalidwe. Ena apanga nsembe zozindikirika za zinthu zakuthupi ndi cholinga chofuna kupanga ophunzira m’gawo lawo.—Mateyu 28:19, 20.
Machitidwe Ena a Chikhulupiriro
8. Nchiyani chomwe chinatsogoza ku kuwoneka kwachiŵiri kwa Yehova kwa Abramu?
8 Abramu anaima mu mzinda wa Harana kufikira imfa ya atate wake, Tera. (Genesis 11:31, 32) Kenaka banja lake linawoloka Mtsinje wa Firate ndi kulinga kum’mwera. Potsirizira pake iwo anafika ku malo “a Sekemu” mkati mwa dziko la Kanani. Ndi malo osangalatsa chotani nanga mmene iwo anakhalira! Sekemu ali m’chigwa cha chonde pakati pa m’dadada wa mapiri aŵiri omwe amakwezeka pa Phiri la Ebala ndi Phiri la Gerizimu. Ilo lalongosoledwa kukhala “paradaiso la Dziko Lopatulika.” Moyenerera, Yehova pano anawonekanso kwa Abramu ndi kunena kuti: “Ndidzapatsa mbewu yako dziko lino.”—Genesis 12:5-7.
9. (a) Kodi ndi m’njira yowoneka yotani imene Abramu anapitirizira kusonyeza chikhulupiriro? (b) Kodi ndi phunziro lotani limene tikuphunzira kuchokera ku ichi?
9 Abramu anavomereza ndi kachitidwe kena ka chikhulupiriro. Monga mmene cholemberacho chikunenera: “Pamenepo anamangira Yehova guwa la nsembe.” (Genesis 12:7) Mwachidziŵikire, ichi chinaphatikizapo kupereka nsembe ya nyama, popeza kuti liwu la Chihebri lakuti “guwa la nsembe” limatanthauza “malo operekera nsembe.” Pambuyo pake, Abramu anabwereza machitidwe a chikhulupiriro amenewa m’mbali zina za dzikolo. M’kuwonjezerapo, iye ‘anaitanira pa dzina la Yehova.’ (Genesis 12:8; 13:18; 21:33) Mawu Achihebri akuti “kuitanira pa dzina” amatanthauzanso “kulengeza (kulalikira) dzinalo.” Banja la Abramu limodzinso ndi Akanani angakhale anamumva iye akulengeza molimba mtima dzina la Mulungu wake, Yehova. (Genesis 14:22-24) Mofananamo, onse ofuna ubwenzi ndi Mulungu lerolino ayenera kuitanira pa dzina lake m’chikhulupiriro. Ichi chikaphatikizapo kugawanamo m’kulalikira kwapoyera, “ku[ma]pereka chiperekere nsembe yakuyamika Mulungu, ndiyo chipatso cha milomo yovomereza dzina lake.”—Ahebri 13:15; Aroma 10:10.
10. (a) Ndi m’njira zina zotani mmene Abramu anasonyezera chikhulupiriro? (b) Ndi chitsanzo chotani chimene iye anakhazikitsa kaamba ka mitu ya banja Yachikristu? (1 Timoteo 3:12)
10 Chikhulupiriro cha Abramu mwa Yehova chinasonyezedwa m’njira zina zambiri. Iye anapereka nsembe kaamba ka mtendere ndipo komabe anachita ndi ngozizo molimba mtima. (Genesis 13:7-11; 14:1-16) Ngakhale kuti anali wolemera, iye sanali wokondetsa zinthu zakuthupi. (Genesis 14:21-24) M’malomwake, iye anali wochereza ndipo mowoloŵa manja anachirikiza kulambira kwa Yehova. (Genesis 14:18-20; 18:1-8) Chofunika koposa, iye anali mutu wa banja wopereka chitsanzo ndipo anatsatira chilangizo cha Yehova mwa kulamulira ana ake ndi banja lake pambuyo pake kotero kuti anasunga “njira ya Yehova, kuchita chilungamo.” (Genesis 18:19) Mu ichi, banja la Abramu linatenga njira yosiyana kotheratu ndi ija yomwerekera mu mkhalidwe wa kugonana ya Chikanani mu Sodomu ndi Gomora ya pafupipo. Abramu motsimikizirika sakanalekerera machimo okulira oterowo m’banja lake. Kunena kuti iye anayang’anira a banja lake mumkhalidwe wabwino kwawunikiridwa m’njira imene ziŵalo zake zinamutsanzira iye mwa kuitanira pa dzina la Yehova m’chikhulupiriro.—Genesis 16:5, 13; 24:26, 27; 25:21.
“Sanafooke m’Chikhulupiriro”
11. Ndimotani mmene Abramu analiri wokhoza kupirira monga “mlendo . . . [m’dziko] losati lake” kwa zaka zana limodzi?
11 Chikhulupiriro champhamvu cha Abramu chinamuthandiza iye kupirira zovuta pamene iye anakhala kwa zaka zana limodzi pakati pa anthu omwe anadzinenera kuti dzikolo linali lawo. (Genesis 12:4; 23:4; 25:7) Baibulo limanena kuti: “Anakhala mlendo ku dziko la lonjezano, losati lake, nakhalira m’mahema pamodzi ndi Isake ndi Yakobo, oloŵa nyumba pamodzi ndi iye a lonjezano lomwelo; pakuti analindirira mudzi [Ufumu wa Mulungu] wokhala nawo maziko, mmisiri wake ndi womanga wake ndiye Mulungu. Ndipotu [iye] adakakumbukira lijalo [iye] adatulukamo [iye] akadaona njira yakubwera nayo.”—Ahebri 11:9, 10, 15; yerekezani ndi Ahebri 12:22, 28.
12. Kodi ndi mwaŵi woyambirira wotani umene Abramu anali nawo wa kubwerera ku Uri, ndipo ndimotani mmene iye anachitira ndi vutolo?
12 Abramu sanakhale kwa nthaŵi yaitali mu Kanani pamene njala yowopsya inampatsa iye “njira yakubwera nayo.” Uri, akumakhala wopatsidwa madzi ochuluka a Mtsinje wa Firate, sanali wodalira pa kugwa kwa mvula kwachindunji. M’malo mobwerera kumeneko, ngakhale kuli tero, Abramu anaika chikhulupiriro mwa Yehova ndipo analunjika kupita ku malo osiyanako—Igupto. Kumeneko kunali kuika moyo pa chiswe. Pokhala ndi mkazi wokongola, mlendoyo, Abramu, anali pa ngozi ya moyo wake m’dziko lachilendo limenelo. Mosasamala kanthu za icho, iye anatenga chisamaliro mwa kufunsa Sarai kubisa unansi wawo waukwati. Yehova anadalitsa Abramu kaamba ka chikhulupiriro chake, ndipo mwamsanga anali wokhoza kubwerera ku Dziko Lolonjezedwa ndi chuma chambiri kuposa ndi kalelonse.—Genesis 12:10–13:2; 20:12.
13. Nchiyani chomwe chikuchitiridwa chithunzi ndi kuuma kwa Sarai ndi kubisa unansi wa ukwati kwa Abramu kwa mkaziyo?
13 Ichi kachiŵirinso chinapanga mbali ya drama ya ulosi imene Abramu mosadziŵa anaichita kaamba ka chilangizo chathu. Sarai, yemwe anali adakali wouma, anaimira gulu lakumwamba la Yehova longa mkazi la angelo okhulupirika. Mkazi wophiphiritsira wokongola ameneyu anayenera kudikira zaka zoposa 4,000 asanakhale wokhoza kupereka mbewu yowona ya Abrahamu Wamkulu, Yehova Mulungu. Chizunzo chapoyera cha atumiki okhulupirika a Mulungu mkati mwa zaka zimenezo za kudikira nthaŵi zina chinachipanga kuwoneka ngati kuti Yehova anabisa unansi wake wamwamuna kwa iye.—Genesis 3:15; Yesaya 54:1-8; Agalatiya 3:16, 27, 29; 4:26.
14. (a) Ndimotani mmene Sarai pomalizira anachitira ku kuuma kwake? (b) Nchiyani chomwe chinachitika m’chaka cha 99 cha Abramu, ndipo nchifukwa ninji?
14 Pambuyo popirira monga mlendo kwa zaka khumi, Abramu anali asadakhalebe ndi mwana wamwamuna monga wolowa m’malo. M’kusowa chochita, Sarai anamupempha iye kutulutsa mbadwa kuchokera kwa kapolo wake wamkazi, Hagara. Abramu anavomereza ndipo Ismayeli anabadwa. (Genesis 12:4; 16:1-4, 16) Koma mbewu yolonjezedwa ya dalitso inayenera kubwera kupyolera mwa winawake. M’chaka cha 99 cha Abramu, dzina lake linasinthidwa kukhala Abrahamu chifukwa chakuti, monga mmene Mulungu ananenera, “ndakuyesa iwe atate wa khamu lamitundu.” Dzina la Sarai linasinthidwa kukhala Sara ndi lonjezo lakuti iye akabala mwana wamwamuna.—Genesis 17:1, 5, 15-19.
15. (a) Nchifukwa ninji Abrahamu anaseka pa lingaliro lakuti Sara akamubalira iye mwana wamwamuna? (b) Ndi umboni wowonjezereka wotani umene Abrahamu anapereka wa chikhulupiriro chake cholimba?
15 Abrahamu (ndipo pambuyo pake Sara) anaseka pa lingaliro limenelo chifukwa onse aŵiri mphamvu za mwamunayo zakubala ndi za Sara zinali zitaleka. (Genesis 17:17; 18:9-15) Koma uku sikunali kuseka kwa kusakhulupirira kopanda chikhulupiriro. Monga mmene Baibulo likulongosolera: “Ndipo iye osafooka m’chikhulupiriro . . . Poyang’anira lonjezo la Mulungu sanagwedezeka, . . . analimbika m’chikhulupiriro, napatsa Mulungu ulemu, nakhazikikanso mu mtima kuti, chimene iye analonjeza, anali nayonso mphamvu yakuchichita.” (Aroma 4:18-21) Pa tsiku limodzimodzilo, Abrahamu anapereka umboni wa chikhulupiriro chake champhamvu. Monga chizindikiro cha pangano la Mulungu ndi iye, Yehova anawuza Abrahamu kudulidwa limodzi ndi mwamuna aliyense m’banja lake lalikulu. (Genesis 15:18-21; 17:7-12, 26) Ndimotani mmene iye anavomerezera ku lamulo lowawa limeneli? “Nadula khungu lawo tsiku lomwelo, monga Mulungu ananena naye.”—Genesis 17:22-27.
16. (a) Nchiyani chomwe chinachitika pa tsiku limene Isake anali kuletsedwa kuyamwa? (b) Kodi kuthamangitsidwa kwa Hagara ndi Ismayeli kunachitira chithunzi chiyani?
16 Isake, amene dzina lake limatanthauza “Kuseka,” anabadwa kwa Sara chaka chotsatira. (Genesis 21:5, 6) Mwamsanga nthaŵi inafika kaamba ka iye kuti aletsedwe kuyamwa. Mkati mwa phwandolo, Ismayeli wansanje anazunza Isake. Pa chimenechi, Sara mwamphamvu anafulumiza Abrahamu kuthamangitsa kapolo wamkaziyo, Hagara, ndi mwana wake kuchoka m’banjalo. Yehova Mulungu anachirikiza pempho la Sara. Ngakhale kuti anawawidwa mtima, Abrahamu anali wofulumira kumvera. (Genesis 21:8-14) Mogwirizana ndi Agalatiya 4:21-30, ichi chinachitira chithunzi mmene Abrahamu Wamkulu akathetsera unansi wake ndi mtundu wachibadwa wa Israyeli. Mofanana ndi mtundu wonse wa anthu, iwo anabadwa monga akapolo a chimo. (Aroma 5:12) Koma iwo anakananso Yesu Kristu, Mbewu yowona ya Abrahamu, yemwe anabwera kudzawamasula iwo. (Yohane 8:34-36; Agalatiya 3:16) Ndipo monga mmene Ismayeli anazunzira Isake, iwo anazunza mpingo Wachikristu wopangidwa chatsopano wa Israyeli wauzimu, omwe anali mbali yachiŵiri ya mbewu ya Abrahamu.—Mateyu 21:43; Luka 3:7-9; Aroma 2:28, 29; 8:14-17; 9:6-9; Agalatiya 3:29.
Chiyeso Chake Chachikulu Koposa cha Chikhulupiriro
17. Ndimotani mmene chikhulupiriro cha Abrahamu potsatira chinayesedwera mowopsya?
17 Sichanthaŵi zonse kuti tate aliyense waumunthu anakhalapo ndi chikondi choposerapo kaamba ka mwana kuposa chimene Abrahamu wokalamba anali nacho kaamba ka Isake. Nchozizwitsa chowopsya chotani nanga mmene icho chinaliri, chotero, pamene iye analandira lamulo iri: “Tengatu mwana wako, wamwamuna wayekhayo, Isake, amene ukondana naye, numuke ku dziko la Moriya, numpereke iye kumeneko nsembe yopsereza pa limodzi la mapiri lomwe ndidzakuuza iwe.”—Genesis 22:1, 2.
18. Ndimotani mmene Abrahamu anavomerezera ku lamulo la Yehova la kupereka nsembe Isake?
18 Chiyenera kukhala chinali chovuta kwa Abrahamu kumvetsetsa chifukwa cha lamulo lomvetsa chifundo limeneli. Komabe iye anasonyeza chimvero chake cha mwamsanga cha nthaŵi zonse. (Genesis 22:3) Chinamtengera iye masiku atatu otopetsa kukafika ku phiri losankhidwalo. Kumeneko iye anamanga guwa la nsembe ndi kuikapo nkhuni pamwamba pake. Pa nthaŵiyi, iye angakhale analongosola lamulo la Mulungu kwa Isake, yemwe akanathaŵa mopepuka. M’malomwake, Isake analola atate wake okalamba kumanga miyendo ndi mikono yake ndi kum’goneka iye pa guwa la nsembelo. (Genesis 22:4-9) Kodi nkuchiyani komwe tingapereke chimvero choterocho?
19. (a) Kodi nkuchiyani komwe tingapereke kugonjera kolimba mtima kwa Isake? (b) Ndimotani mmene unansi pakati pa Abrahamu ndi Isake uliri phunziro kaamba ka mabanja Achikristu lerolino?
19 Abrahamu anachita mathayo ake mokhulupirika m’chigwirizano ndi Isake, monga momwe zandandalitsidwira pa Genesis 18:19. Mosakaikira iye anatsimikiza pa Isake chifuno cha Yehova cha kuwukitsa akufa. (Genesis 12:3; Ahebri 11:17-19) Isake, kumbali yake, anali maziko a chikondi chozama cha Abrahamu ndipo akanafuna kukondweretsa atate wake m’chirichonse, makamaka pamene chinakhudza kuchita chifuniro cha Mulungu. Limeneli ndi phunziro labwino chotani nanga kaamba ka mabanja Achikristu lerolino!—Aefeso 6:1, 4.
20. Ndimotani mmene Abrahamu anamverera, ndipo ndi mphoto yotani?
20 Tsopano panafika pa kaindeinde pa chiyesocho. Abrahamu anatenga mpeni wophera. Koma pamene iye anali pafupi kupha mwana wake, Yehova anamletsa iye ndi kunena kuti: “Tsopano ndidziŵa kuti iwe umawopa Mulungu, pakuti sunandikanize ine mwana wako, mwana wako wayekha.” (Genesis 22:11, 12) Ndi molemerera chotani nanga mmene Abrahamu anafupidwira mwa kumva chilengezo chenicheni cha Mulungu cha chilungamo chake! Iye tsopano akanadzimva wotsimikizira kukhala atakwaniritsa chimene Mulungu amafuna kwa munthu wopanda ungwiro. Chofunika koposa, chiyerekezo cha poyambirirapo cha Yehova cha chikhulupiriro chake chinalemekezedwa. (Genesis 15:5, 6) Pambuyo pa ichi, Abrahamu anapereka nsembe nkhosa yamphongo yomwe inapatsidwa mozizwitsa kuloŵa m’malo Isake. Kenaka iye anamva Yehova akutsimikizira, mwa lumbiro, malonjezo a pangano. Pambuyo pake, iye anadziŵika monga bwenzi la Yehova.—Genesis 22:13-18; Yakobo 2:21-23.
21. Ndi fanizo laulosi lotani limene linaperekedwa pano, ndipo nchiyani chomwe liyenera kutilimbikitsa ife kufunafuna?
21 Nsembe ya Abrahamu inali “chiphiphiritso.” (Ahebri 11:19) Iyo inachitira chithunzi nsembe yoŵaŵa, ya mtengo wake imene Yehova Mulungu anapanga pamene anatumiza Mwana wake wokondedwa ku dziko lapansi kudzafa monga “Mwanawankhosa wa Mulungu amene achotsa chimo lake la dziko lapansi.” (Yohane 1:29) Ndipo kufunitsitsa kufa kwa Isake kumachitira fanizo mmene Isake Wamkulu, Yesu Kristu, mwachikondi anagonjera ku kuchita chifuniro cha Atate wake wa kumwamba. (Luka 22:41, 42; Yohane 8:28, 29) Pomalizira, monga mmene Abrahamu analandirira mwana wake wamoyo kuchokera ku guwa la nsembe, Yehova analandira Mwana wake wokondedwa kuchokera kwa akufa monga cholengedwa chauzimu chaulemerero. (Yohane 3:16; 1 Petro 3:18) Ncholimbikitsa chotani nanga mmene chonsechi chiriri kwa ofunafuna ubwenzi ndi Mulungu lerolino!
22. Ndimotani mmene gulu losankhidwa la anthu likupindulira kuchokera ku chikondi chosapambanika cha Mulungu?
22 Mwa kusonyeza chikhulupiriro m’kachitidwe kosapambanika ka chikondi kameneka ku mbali ya Abrahamu Wamkulu, Yehova Mulungu, gulu losankhidwa la anthu lalengezedwa lolungama monga ana a Mulungu. (Aroma 5:1; 8:15-17) Otengedwa choyamba kuchokera kwa Ayuda ndipo kenaka kuchokera kwa Akunja, awa adalitsidwadi kupyolera mwa Mbewu ya Abrahamu, Yesu Kristu. (Machitidwe 3:25, 26; Agalatiya 3:8, 16) Kenaka, iwo amapanga mbali yachiŵiri ya mbewu ya Abrahamu. (Agalatiya 3:29) Oterowo pomalizira amafika chiŵerengero cha 144,000 ndipo, mofanana ndi Yesu, akuwukitsidwa ku moyo wakumwamba pambuyo pa kudzitsimikizira iwo eni okhulupirika kufikira imfa.—Aroma 6:5; Chibvumbulutso 2:10; 14:1-3.
23. (a) Ndimotani mmene mamiliyoni akudalitsidwira kale kupyolera mu otsalira a mbewu ya Abrahamu? (2 Akorinto 5:20) (b) Ndi madalitso owonjezereka otani omwe ali kutsogolo kwa “khamu lalikulu”?
23 Pa nthaŵi ino, mamiliyoni kuchokera ku mitundu yonse ‘akudalitsidwa’ kupyolera mwa chivomerezo chawo ku utumiki wachikondi wa otsalira ochepera a mbewu ya Abrahamu. (Genesis 22:18) Iwo asangalatsidwa kuphunzira mmene anthu ochimwa angalengezedwere olungama monga mabwenzi a Mulungu. Monga chotulukapo chake, “khamu lalikulu . . . lochokera kwa mtundu uliwonse” akusangalala ndi chiyanjo cha Mulungu, pokhala “atatsuka zovala zawo naziyeretsa m’mwazi wa Mwanawankhosa.” Ndi otsalirawo akutenga chitsogozo, iwo nawonso akupereka kwa Mulungu “utumiki [wopatulika, NW] usana ndi usiku.” Choikidwa patsogolo pa khamu lalikulu limeneli chiri chiyembekezo chozizwitsa cha moyo wosatha m’Paradaiso monga “ana a Mulungu” a pa dziko lapansi. (Chibvumbulutso 7:9-17; 21:3-5; Aroma 8:21; Salmo 37:29) Ngakhale kuli tero, madalitso amenewo asanakhale enieni, zochitika za kufunika kokulira ziyenera kuchitika, monga mmene tidzaphunzirira m’nkhani yotsatira.
Mafunso Kaamba ka Kubwereramo
◻ Ndimotani mmene chikhulupiriro cha Abrahamu ndi cha abale ake chinayesedwera?
◻ Ndimotani mmene Akristu lerolino asonyezera chikhulupiriro chofananacho?
◻ Ndi m’njira zina zotani mmene Abrahamu anasonyezera chikhulupiriro?
◻ Ndimotani mmene Abrahamu, Sara, ndi Isake aliri zitsanzo kaamba ka mabanja Achikristu?
◻ Nchiyani chomwe chinachitiridwa fanizo ndi kachitidwe kakakulu koposa ka chikhulupiriro ka Abrahamu?