Genesis
14 Mʼmasiku a Amarafele mfumu ya ku Sinara,+ Arioki mfumu ya ku Elasara, Kedorelaomere+ mfumu ya ku Elamu+ ndi Tidala mfumu ya ku Goimu, 2 mafumuwa anachita nkhondo ndi mafumu otsatirawa: Bera mfumu ya ku Sodomu,+ Birisa mfumu ya ku Gomora,+ Sinabi mfumu ya ku Adima, Semebere mfumu ya ku Zeboyimu+ ndi mfumu ya ku Bela, kapena kuti ku Zowari. 3 Mafumu 5 onsewa anasonkhanitsa asilikali awo pamodzi ku chigwa cha Sidimu,+ kapena kuti Nyanja Yamchere.*+
4 Mafumuwa anatumikira Kedorelaomere kwa zaka 12, koma mʼchaka cha 13 anamupandukira. 5 Choncho mʼchaka cha 14, Kedorelaomere limodzi ndi mafumu omwe anali naye, anapita nʼkukagonjetsa Arefai ku Asiteroti-karanaimu, Azuzi ku Hamu, Aemi+ ku Save-kiriyataimu, 6 ndi Ahori+ kuphiri lawo la Seiri,+ mpaka kukafika ku Eli-parana, kuchipululu. 7 Kenako anabwerera nʼkulowera ku Eni-misipati, kumene ndi ku Kadesi,+ ndipo analanda dera lonse la Aamaleki,+ komanso anagonjetsa Aamori+ omwe ankakhala ku Hazazoni-tamara.+
8 Pa nthawi imeneyi, mfumu ya ku Sodomu, mfumu ya ku Gomora, mfumu ya ku Adima, mfumu ya ku Zeboyimu, ndi mfumu ya ku Bela, kapena kuti Zowari, ananyamuka nʼkupita ku chigwa cha Sidimu. Kumeneko, iwo anaima mwa dongosolo lomenyera nkhondo kuti amenyane ndi 9 Kedorelaomere mfumu ya ku Elamu, Tidala mfumu ya ku Goimu, Amarafele mfumu ya ku Sinara, ndi Arioki mfumu ya ku Elasara.+ Panali mafumu 4 amene anamenyana ndi mafumu 5. 10 Kenako mafumu a Sodomu ndi Gomora anayamba kuthawa. Koma chigwa cha Sidimu chinali ndi maenje aphula ambirimbiri, choncho iwo pothawa ankagwera mʼmaenje amenewo. Amene anatsala anathawira kudera lamapiri. 11 Ndiyeno amene anapambanawo anatenga katundu yense wa ku Sodomu ndi Gomora, limodzi ndi chakudya chawo chonse nʼkumapita.+ 12 Anatenganso Loti mwana wa mʼbale wake wa Abulamu, amene ankakhala ku Sodomu.+ Komanso anatenga katundu wake nʼkupitiriza ulendo wawo.
13 Kenako munthu wina amene anathawa anafika kwa Abulamu Mheberi. Pa nthawiyo nʼkuti Abulamu akukhala* pakati pa mitengo ikuluikulu imene mwiniwake anali Mamure, yemwe anali wa Chiamori.+ Ameneyu anali mʼbale wake wa Esikolo ndi Aneri.+ Iwowa anapanga ubale ndi Abulamu. 14 Choncho Abulamu anamva kuti mʼbale wake+ wagwidwa ndipo akupita naye kudziko lina. Atamva zimenezo iye anasonkhanitsa anyamata ake odziwa kumenya nkhondo. Anali atumiki ake okwanira 318, omwe anabadwira mʼnyumba yake. Iwo anatsatira adaniwo mpaka ku Dani.+ 15 Usiku iye anagawa mʼmagulu asilikali akewo, omwe anali atumiki ake, kuti amenyane ndi adaniwo. Ndipo anawagonjetsa, moti anawathamangitsa mpaka kukafika ku Hoba, kumpoto kwa Damasiko. 16 Ndipo anapulumutsa katundu yense. Anapulumutsanso Loti mʼbale wake, katundu wake, akazi ndi anthu ena.
17 Abulamu akubwera kuchokera kumene anagonjetsa Kedorelaomere limodzi ndi mafumu amene anali naye, mfumu ya ku Sodomu inapita kukakumana naye kuchigwa cha Save, kapena kuti chigwa cha Mfumu.+ 18 Ndipo Melekizedeki,+ mfumu ya mzinda wa Salemu,+ anabweretsa mkate ndi vinyo. Iyeyu anali wansembe wa Mulungu Wamʼmwambamwamba.+
19 Kenako anadalitsa Abulamu kuti:
“Mulungu Wamʼmwambamwamba,
Iye amene anapanga kumwamba ndi dziko lapansi, adalitse Abulamu.
20 Atamandike Mulungu Wamʼmwambamwamba,
Amene wapereka okupondereza mʼmanja mwako!”
Ndipo Abulamu anapatsa Melekizedeki chakhumi cha zinthu zonse+ zimene analanda adaniwo.
21 Kenako mfumu ya ku Sodomu inauza Abulamu kuti: “Mungondipatsa anthu okhawo, koma katunduyo mutenge.” 22 Koma Abulamu anauza mfumu ya ku Sodomuyo kuti: “Ndikukweza manja anga kulumbira kwa Yehova Mulungu Wamʼmwambamwamba, Amene anapanga kumwamba ndi dziko lapansi. 23 Ndikulumbira kuti pa zinthu zako sinditengapo kanthu nʼkamodzi komwe, ngakhale kaulusi kapena kachingwe komangira nsapato, kuti usadzati, ‘Ndine ndinamulemeretsa Abulamu.’ 24 Sinditengapo chilichonse kupatulapo zokhazo zimene anyamata adya kale. Koma amene anapita nane, amene ndi Aneri, Esikolo ndi Mamure,+ aliyense akhoza kutenga gawo lake.”