Kukongola kwa Chilengedwe cha Yehova
Chuma Chochuluka cha M’nyanja
DZUŴA likamaloŵa, panyanja pamakhala kamphepo kayeziyezi ndipo kamachititsa mafunde kuyenda mwabata n’kumakawomba kugombe. Kaphokoso ka mafundeŵa n’koiwalitsa mavuto ndipo kaphokosoka ndiko kamakopa anthu ambirimbiri amene amapita kunyanja pofuna kupuma ndiponso pofuna malo abata.a
Magombe ambirimbiri a nyanja za padziko pano n’ngotero. Nyanja zimakhala ndi malire ameneŵa amene madzi sayenera kupitirirapo ndipo malireŵa amasinthasintha. Umu ndi mmene Mlengi anakonzera zinthu. Mulungu ananena zimene anachitazi motere: “Ndinaika mchenga chilekaniro cha nyanja.” Ndipo anapitiriza kunena kuti: “Ngakhale mafunde ake achita gavigavi, alephera; ngakhale akokoma, sangathe kupitirirapo.”—Yeremiya 5:22; Yobu 38:8; Salmo 33:7.
Mbali yaikulu ya dziko lapansili ndi madzi okhaokha, koma sizili choncho ndi mayiko ena onse omwe amazungulira dzuŵa. Mmene Yehova ankakonza dzikoli kuti anthu azikhalamo ananena kuti: “Madzi a pansi pa kumwamba asonkhane pamodzi pa malo amodzi, uoneke mtunda.” Ndipo zimenezo ‘zinaterodi.’ Nkhaniyo imapitirira motere: “Ndipo Mulungu adautcha mtundawo Dziko lapansi; kusonkhana kwa madziko ndipo adatcha Nyanja: ndipo anaona Mulungu kuti kunali kwabwino.” (Genesis 1:9, 10) Koma kodi nyanja zimathandiza motani?
Madzi a m’nyanja anawapanga mwakuti azithandiza pa moyo m’njira zingapo zochititsa chidwi. Mwachitsanzo, madzi amatha kusunga chifundizi. Motero nyanja zimasunga chifundizi chochuluka n’kumathandiza kuti kunja kusamazizire kwambiri m’nyengo yachisanu.
Madzi amathandiza m’njira inanso. Madzi ndiwo amasungunula zinthu mosavuta kuposa chinthu china chilichonse chosungunulira zinthu. Kuti zamoyo zisafe, pamafunika kuti zinthu zosiyanasiyana zizisakanikirana m’matupi mwawo, motero zinthuzo zimafunika madzi kuti zisungunuke n’kusakanikirana bwinobwino. Zinthu zambiri zotere, zimene zimapezeka m’zinthu zamoyo, zimakhala ndi madzi. Buku lotchedwa The Sea linati: “Zamoyo zonse, kuphatikizapo zomera ndiponso zinyama zapamtunda, zimafunikira madzi omwe makamaka amachokera m’nyanja.”
Nyanja zimathandizanso kukonza mumlengalenga. Zomera za m’nyanja zimagwiritsira ntchito mpweya umene anthufe sitipuma ndipo zimatulutsa mpweya umene anthufe timapuma. Wofufuza wina anati: “Chaka chilichonse mpweya wambiri wam’mlengalengamu umene anthufe timapuma umachokera mu zomera za m’nyanja.”
Nyanja zingathenso kutipatsa mankhwala achilengedwe ochizira matenda. Kwa zaka zambiri, anthu akhala akupanga mankhwala kuchokera ku nsomba. Kwa nthaŵi yaitali, anthu akhala akugwiritsira ntchito mafuta a chiŵindi cha nsomba inayake ya m’nyanja zikuluzikulu. Chaposachedwapa ayamba kugwiritsira ntchito mankhwala otengedwa ku nsomba ndi zamoyo zina za m’nyanja pochizira matenda a chifuwa cha mphumu ndiponso matenda ena kuphatikizaponso khansa.
Anthu ena anayesapo kuŵerengera mtengo wa katundu ndiponso phindu limene anthu amapeza chifukwa cha nyanja. N’zosatheka kutchula ndendende phindu lakelo, komabe ofufuza akuti zinthu zambiri zimene timapindula nazo padziko pano ndi zam’nyanja. Izi zikugwirizana ndi mfundo yakuti nyanja anazipanga n’cholinga chinachake ndipo cholinga chake n’chakuti zizithandiza pa moyo. Cholinga chimenechi chikugwirizanadi kwambiri ndi mfundo ya m’Baibulo yakuti zimenezi ndi chuma chochuluka cha m’nyanja.—Deuteronomo 33:19.
Wokonza Zinthu Wamkulu ndiponso Wopanga chuma chonsechi ndi Yehova motero iyeyo ndiye amene tiyenera kumutamanda. Zimenezi zinam’chititsa Nehemiya kutamanda Yehova ponena kuti: “Inu ndinu Yehova, nokhanu; mwalenga thambo, . . . nyanja ndi zonse zili m’mwemo, ndi Inu muzisunga zamoyo zonsezi.”—Nehemiya 9:6.
[Mawu a M’munsi]
a Onani Kalendala ya 2004 ya Mboni za Yehova, pa mwezi wa September ndi October.
[Bokosi/Zithunzi patsamba 9]
Madzi, Mphepo, ndi Mafunde
Madzi ndi mphepo zimachititsa mafunde aakulu omwe amachita chimkokomo chogonthetsa m’kutu akamawombana m’magombe okhala ndi matanthwe ataliatali angati amene mukuwaona pachithunzipa, omwe ali ku California, m’dziko la United States. Nyanja zakhala ndi mafunde kuyambira kale, ndipo mafundeŵa amasonyeza kuti nyanja zili ndi mphamvu zosati n’kuseŵera nazo ayi. Komanso amatisonyeza mphamvu zodabwitsa zimene Mlengi ali nazo. Yehova ndiye ‘amaponda pa mafunde a panyanja.’ “Mwa mphamvu yake agwetsa nyanja bata; ndipo mwa luntha lake akantha kudzikuza kwake.” (Yobu 9:8; 26:12) Inde, “Wam’mwamba ndiye wamphamvu, Wakuposa mkokomo wa madzi ambiri, ndi mafunde olimba a nyanja.”—Salmo 93:4.
Zoumba za Mchenga
Gombe lanyanja nthaŵi zina limakhala ndi zoumba zochititsa kaso kwambiri za mchenga zofanana ndi milu ya mchenga imene mukuiona apayi, ya ku Namibia, kum’mwera kwa Africa. Mphepo ndiyo imawomba mchengawo kuti uzioneka ngati choumba. Ngakhale kuti milu ina ya mchengawu imakhala ing’onoing’ono kwambiri, ina imatalika mpaka mamita 400. Kuchuluka kwa mchengaku kumatithandiza kumvetsa zimene Baibulo limatanthauza ponena kuti “mchenga wa m’mphepete mwa nyanja.” Mawuŵa amasonyeza zinthu zochuluka kwambiri, zovuta kuziŵerenga. (Genesis 22:17) Timagoma naye kwambiri Mlengi pokonza mpanda woterewu womwe umateteza dziko ku mafunde nyanja ikakalipa.
[Chithunzi patsamba 9]
Dzuŵa likuloŵa pagombe, ku Bight of Biafra, ku Cameroon