Kusonyeza Chikondi Chachikristu kwa Okalamba
SAMUEL JOHNSON, mlembi wa m’zaka za zana la 18, ananena nkhani ya mwamuna wachichepere amene, pamene anali kuchezera mabwenzi, anaiŵala pamene anaika chipeŵa chake. Zimenezi sizinachititse zokambakamba. “Koma ngati kusasamala kumodzimodziko kupezedwa mwa mwamuna wachikulire,” anapitiriza motero Johnson, “anthu angayambe kung’ung’udza ndi kuti, ‘Iye akuyamba kutaya chikumbukiro chake.’”
Nkhani ya Johnson imasonyeza kuti okalamba, mwinamwake mofanana ndi magulu ena a anthu ochepa, amaikidwa mosayenera m’gulu la anthu amikhalidwe yofanana. Pamene kuli kwakuti kusamalira zosoŵa za okalamba kuli kovuta, pamakhala mapindu kwa onse oloŵetsedwamo. Kodi ndi ati amene ali mavuto ake ndi mphotho zake, ndipo kodi nchifukwa ninji nkhani imeneyi ikuyambukira anthu ochulukirachulukira?
Malinga ndi ziŵerengero, 6 peresenti ya anthu a m’dziko ili ndi zaka 65 zakubadwa kapena kuposapo, ndipo m’maiko otukuka peresentiyo njaikulu kuŵirikiza kaŵiri. Mgwirizano wa European Community, umene unatcha 1993 kukhala “Chaka cha ku Ulaya cha Anthu Okalamba ndi Chimvano Pakati pa Mibadwo,” munthu 1 mwa 3 ali ndi zaka zoposa 50. Kumeneko, mofanana ndi m’maiko ambiri a maindasitale otukuka, kutsika kwa chiŵerengero cha obadwa ndi kuwonjezeka kwa zaka za moyo kukuchititsa chiŵerengero cha achikulire kukwera kwambiri. Kusamalira a mvula zakale pansi pa mikhalidwe yotero kulidi ntchito yolemetsa. Zinthu zinali zosiyana chotani nanga m’nthaŵi zakale Kummaŵa!
“Nkhokwe za Chidziŵitso”
Handwörterbuch des Biblischen Altertums für gebildete Bibelleser (Handbook of Biblical Antiquity for Educated Readers of the Bible) imanena kuti m’nthaŵi zakale Kummaŵa “okalamba anali kuonedwa monga osunga miyambo ya nzeru ndi chidziŵitso chapamwamba, chimene chinali chifukwa chake achichepere analangizidwa kuyanjana nawo ndi kuphunzira kwa iwo.” Smith’s Bible Dictionary ikulongosola kuti: “Mu moyo wa mtseri [okalamba] anali kulemekezedwa monga nkhokwe za chidziŵitso . . . [Achichepere] anawalola iwo kupereka malingaliro awo choyamba.”
Kulemekeza okalamba kunasonyezedwa m’Chilamulo cha Mose pa Levitiko 19:32: “Pali aimvi uziwagwadira, nuchitire ulemu munthu wokalamba.” Chotero okalamba anali ndi malo a thayo m’chitaganya ndipo anaonedwa monga chuma chamtengo wake. Mwachionekere mmenemu ndi mmene Rute Mmoabu anaonera apongozi ake Achiisrayeli, a Naomi.
Rute anasankha motsimikiza kutsagana ndi Naomi kuchoka ku Moabu kumka ku Israyeli, pambuyo pake anamvetsera mosamalitsa uphungu wa Naomi. Pamene anafika ku Betelehemu, anali Naomi amene anaona kuti dzanja la Yehova linali kutsogoza zochitika ndipo ndi amene panthaŵiyo analangiza Rute za mmene adzikhalira. (Rute 2:20; 3:3, 4, 18) Moyo wa Rute unaumbidwa m’njira yateokratiki pamene anaphunzira kwa Naomi wachidziŵitsoyo. Apongozi ake anatsimikizira kukhala nkhokwe ya chidziŵitso.
Mwa njira yofananayo, akazi achichepere Achikristu lerolino angapindule mwa kuyanjana ndi akazi okalamba mumpingo. Mwinamwake mlongo akulingalira za kukwatiwa kapena akulimbana ndi vuto lovuta laumwini. Kukakhala kwanzeru chotani nanga kufuna uphungu ndi chichirikizo cha mlongo wokhwima wokalamba amene ali ndi chidziŵitso m’nkhaniyo!
Ndiponso, bungwe la akulu lingapindule mwa kugwiritsira ntchito chidziŵitso cha okalamba pakati pawo. Tingaphunzire pa kulephera kwa Loti kuchita zimenezi. Mkangano wokhudza abusa a ziŵeto za Abrahamu ndi Loti unachititsa kufunika kwa chosankha chimene chikayambukira aliyense. Loti anapanga chosankha chopanda nzeru. Kukanakhala bwino chotani nanga ngati akanapempha uphungu wa Abrahamu poyamba! Loti akanalandira chitsogozo chokhwima chimene chikanapulumutsa banja lake ku tsoka lomwe linatsatirapo chifukwa cha kusankha kwake mofulumira. (Genesis 13:7-13; 14:12; 19:4, 5, 9, 26, 29) Kodi mumamvetsera mosamalitsa pamene akulu okhwima akulankhula musanafikire chigamulo chanu pa nkhani yakutiyakuti?
Okalamba osaŵerengeka ali ndi changu chachikulu kaamba ka ntchito ya Yehova, monga momwe anachitira Simeoni ndi Anna m’zaka za zana loyamba. (Luka 2:25, 36, 37) Chili chizindikiro cha ulemu ndi chisonyezero cha mkhalidwe wa kusamalira okalamba oterowo kuŵaloŵetsamo m’zochita za mpingo monga momwe nyonga yawo ingawatheketsere, ngakhale kufika mu ukalamba weniweni. Mwinamwake wachichepere akufunikira thandizo kukonzekera gawo la mu Sukulu Yautumiki Wateokratiki. Mkulu waluso angaganize kuti mlangizi wabwino angakhale chiŵalo chokalamba cha mpingo, amene ali ndi nzeru zachifatse, khalidwe labwino, ndi nthaŵi yokwanira.
Komabe, kusamalira zosoŵa zapadera za okalamba kumaloŵetsamo zambiri. Ambiri amavutika ndi kusungulumwa, kuwopa upandu, ndi mavuto azandalama. Ndiponso, okalamba atadwala, mavuto ameneŵa amakulitsidwa ndi thanzi lomaipiraipira ndi kugwiritsidwa mwala ndi kuchepekera kwa nyonga yawo. Ndiyeno iwo angafunikire chisamaliro chokulira. Kodi ndimotani mmene munthu payekha ndi mpingo wonse ungathandizire?
“Kusonyeza Kudzipereka Kwaumulungu”
Mkati mwa zaka za zana loyamba, Paulo analemba mouziridwa pa 1 Timoteo 5:4, 16 kuti: “Ngati wamasiye wina ali nawo ana kapena adzukulu, ayambe aphunzire iwo [kusonyeza kudzipereka kwaumulungu, NW] m’banja lawo, ndi kubwezera [makolo awo ndi agogo awo, NW]; pakuti ichi ncholandirika pamaso pa Mulungu. Ngati mkazi wina wokhulupira ali nawo amasiye, iye awathandize, ndipo Mpingowo usalemedwe; kuti uthandize iwo amene ali amasiye ndithu.” Kusamalira okalamba kunali nkhani ya banja. Ngati chiŵalo chokalamba cha mpingo chinali chosoŵa pambuyo pogwiritsira ntchito njira zonse za m’banja lake, thayo linakhala pa mpingo. Malamulo a mkhalidwe ameneŵa sanasinthe.
Kodi nchiyani chimene chathandiza Akristu kusonyeza chikondi Chachikristu kwa okalamba mwa kusonyeza kudzipereka kwaumulungu m’mabanja awo? Taonani ndemanga zotsatirazi za Mboni zambiri zimene zili ndi chidziŵitso cha kusamalira awo amene ali a mvula zakale.
Chisamaliro cha Nthaŵi Zonse cha Zosoŵa Zauzimu
“Kukambitsirana lemba la tsiku pamodzi kunali chithandizo chopindulitsa,” akukumbukira motero Felix, amene anathandiza mkazi wake kusamalira makolo ake. “Zokumana nazo zaumwini ndi zonulirapo zinaphatikizidwa ndi malamulo a mkhalidwe a Yehova.” Ndithudi, potenga ntchito ya kusamalira achibale okalamba, mfundo yoyamba ndiyo kusamalira moyenerera mphamvu yawo yauzimu. Zimenezi nzanzeru polingalira za mawu a Yesu pa Mateyu 5:3 akuti: “Odala ali osauka mumzimu.” Pa lemba la tsiku pangawonjezeredwe programu ya kuŵerenga Baibulo, kukambitsirana zofalitsidwa zozikidwa pa Baibulo, ndi pemphero. “Kukuoneka kuti okalamba amakonda mlingo winawake wa kukhazikika,” akutero Peter.
Inde, kukhazikika nkofunika m’zinthu zauzimu. Osati m’zinthu zauzimu zokha komanso m’moyo wa tsiku ndi tsiku okalamba amayamikira dongosolo lokhazikika. Ngakhale awo amene ali odwala pang’ono angalimbikitsidwe “kudzuka ndi kuvala bwino tsiku lililonse,” akutero Ursula. Ndithudi, timafuna kupeŵa kupereka lingaliro la kulamulira okalamba. Doris akuvomereza kuti kaŵirikaŵiri zoyesayesa zake zabwino zinalakwika momvetsa chisoni. “Ndinapanga zolakwa za mtundu uliwonse. Tsiku lina ndinapempha bambo wanga kuti adzisintha malaya awo tsiku ndi tsiku. Ndiyeno amayi anga anandikumbutsa kuti: ‘Iwo adakali amunanga!’”
Okalambawo adaali achichepere panthaŵi ina, koma kuti achichepere adziike m’malo a okalamba kumakhala ntchito yaikulu kwambiri. Komabe, imeneyo ndiyo mfungulo ya kumvetsetsa zosoŵa zawo zapadera. Ukalamba umabweretsa kugwiritsidwa mwala. Gerhard akulongosola kuti: “Apongozi anga anadzikwiyira okha chifukwa chakuti sanalinso okhoza kuchita zonse zimene ankachita. Kuvomereza mkhalidwewo kunali kopweteka kwambiri. Umunthu wawo unasintha.”
Pansi pa mikhalidwe yomasintha, sikumakhala kwachilendo kwa munthu wokalamba kusonyeza malingaliro ake a kugwiritsidwa mwala mwa kusuliza ena, makamaka awo amene akumsamalira. Chifukwa chake nchokhweka. Kusamaliridwa kwawo mwachikondi kumawakumbutsa za kuchepa kwa nyonga yawo. Kodi muyenera kuchitanji ndi chisulizo kapena chidandaulo chosayenerera chimenechi?
Kumbukirani, malingaliro osamangirirawo samasonyeza lingaliro la Yehova la zoyesayesa zanu. Pitirizani kuchita zabwino, ndipo sungani chikumbumtima chabwino, ngakhale ngati kamodzikamodzi mumatuta ndemanga zosalungama. (Yerekezerani ndi 1 Petro 2:19.) Mpingo wakumaloko ungapereke chichirikizo chachikulu.
Zimene Mpingo Ungachite
Mipingo yambiri ili ndi chifukwa chakukhalira yoyamikira kwambiri kaamba ka zoyesayesa za abale ndi alongo athu okalamba okondedwa. Mwinamwake anali iwo amene anayala maziko a mpingo, kuumanga kuyamba ndi ofalitsa oŵerengeka okha zaka makumi apita. Kodi mpingowo ukanakhala pati popanda ntchito yawo yachangu yapapitapo, ndipo mwinamwake, chichirikizo chawo cha ndalama tsopano?
Pamene chisamaliro chowonjezereka chikhala chofunikira kwa wofalitsa wokalamba, thayolo silifunikira kukhala pa achibale okha. Ena angathandize mwa kuwatumikira, kuwaphikira, kuyeretsera, kupita koyenda ndi wokalambayo, kupereka choyendera kupita kumisonkhano Yachikristu, kapena kungocheza naye pa Nyumba Yaufumu. Onse angaloŵemo, ngakhale kuti kuchita bwino zinthu ndi dongosolo lokhazikika zimachitidwa bwino koposa ngati zoyesayesa zigwirizanitsidwa.
Kugwirizanitsa ndiko chinthu china chimene akulu ayenera kukumbukira pamene akulinganiza maulendo aubusa. Mipingo ina imapereka chitsanzo chabwino m’zimenezi, akulu akumatsimikizira kuti maulendo aubusa okhazikika akupangidwa kwa okalamba ndi ofooka, ngakhale kwa awo amene akusamaliridwa bwino ndi mabanja awo. Komabe, kukuonekera kuti mipingo ina iyenera kuzindikira bwino kwambiri mathayo awo kulinga kwa okalamba.
Mbale wina wokhulupirika, amene ali kumapeto kwa zaka zake za m’ma 80, anasamaliridwa ndi mwana wake wamkazi ndi mkamwini wake, amene anachoka pa Beteli kuti akachite zimenezo. Komabe, maulendo a ziŵalo zina za mpingo anali ofunikabe kwa iye. “Pamene ndinkachezera odwala,” mbaleyo anadandaula motero, “ndinali kupemphera nawo. Koma palibe amene anapempherapo nane.” Chisamaliro chachikondi cha achibale sichimachotsera akulu thayo la ‘kuŵeta gulu la Mulungu lili mwa iwo.’ (1 Petro 5:2) Ndiponso, awo amene akusamalira okalamba amafuna kumangiriridwa ndi kulimbikitsidwa kuti apitirize ntchito yawo yabwino.
“Wokalamba ndi Wokhutira”
Alexander von Humboldt, wasayansi wa ku Germany wa m’zaka za zana la 19, anali wokalamba pamene mkazi wachichepere anamfunsa ngati sanapeze kukalamba kukhala kotopetsa. “Wanena zoona,” anayankha motero mwamuna wophunzirayo. “Koma ndiyo njira yokha yokhala ndi moyo kwa nthaŵi yaitali.” M’lingaliro lofananalo, abale ndi alongo ambiri lerolino amapereka chitsanzo chabwino cha kuvomereza nsautso za ukalamba mosinthana ndi ulemu wa kukhala ndi moyo wautali. Iwo amasonyeza mkhalidwe wa maganizo wosonyezedwa ndi Abrahamu, Isake, Davide, ndi Yobu, amene anali ‘okalamba ndi okhutira.’—Genesis 25:8, NW; 35:29; 1 Mbiri 23:1; Yobu 42:17.
Ukalamba umadzetsa chitokoso cha kulandira thandizo mwaulemu ndi kupereka chiyamikiro moona mtima. Nzeru imafuna kuti aliyense azindikire malire a nyonga zake. Komabe, zimenezo sizimachititsa munthu wokalamba kukhala wosakangalika. Maria ali ndi msinkhu wa zaka zoposa 90, koma amafikabe pamisonkhano yampingo ndi kuperekapo ndemanga. Kodi iye amachita zimenezo motani? “Sindithanso kuŵerenga, koma ndimamvetsera Nsanja ya Olonda pa kaseti. Ndimaiŵala zambiri, koma kaŵirikaŵiri ndimakhozabe kupereka ndemanga.” Mofanana ndi Maria, kukhala wotanganitsidwa ndi zinthu zimene zimamangirira kumathandiza munthu kukhalabe wokangalika ndi kusunga umunthu Wachikristu.
Mu Ufumu wa Mulungu, ukalamba sudzakhalakonso. Panthaŵi imeneyo amene akalamba m’dongosolo lino ndipo mwinamwake amene anafa adzakhala ndi zikumbukiro zabwino za chisamaliro ndi chikondi chosonyezedwa kwa iwo. Pamene okalamba amenewo adzalandiranso moyo ndi nyonga, adzakhaladi ndi chikondi chachikulu kulinga kwa Yehova ndi chiyamikiro chakuya kwa awo amene anamamatira kwa iwo m’ziyeso zawo m’dongosolo lino lakale.—Yerekezerani ndi Luka 22:28.
Bwanji ponena za awo amene akusamalira okalamba tsopano? Posachedwapa, pamene Ufumu udzatenga ulamuliro wonse wa dziko lapansi, adzayang’ana m’mbuyo ndi chisangalalo ndi mpumulo kuti sanazembe thayo lawo koma anasonyeza kudzipereka kwaumulungu mwa kusonyeza chikondi Chachikristu kwa okalamba.—1 Timoteo 5:4.
[Bokosi patsamba 30]
Okalamba Adzayamikira Maulendo Anu
Zabwino zambiri zingakwaniritsidwe mwa kulinganiza kuchezera wokalamba, mwinamwake kwa mphindi 15, pambuyo pa ntchito yolalikira. Koma nkwabwino kwambiri kusapanga maulendo amenewo mwadzidzidzi, monga momwe chokumana nacho chotsatirachi chikusonyezera.
Brigitte ndi Hannelore anali kulalikira pamodzi, akumakambitsirana ndi mwamuna wokalamba pakhomo pake. Alongowo analankhula naye kwa mphindi zisanu asanazindikire kuti nayenso anali Mboni ya Yehova, chiŵalo cha mpingo umodzimodzi. Zinali zamanyazi chotani nanga! Koma chokumana nachocho chinatha bwino. Hannelore anapanga makonzedwe panthaŵi yomweyo a kuchezera mbaleyo ndi kumthandiza kufika pamisonkhano yampingo.
Kodi mumadziŵa dzina ndi keyala ya wofalitsa aliyense wokalamba amene akukhala m’gawo limene mumalalikiramo? Kodi mungapange makonzedwe a kumchezera mwachidule? Mosakayikira kudzayamikiridwa kwambiri.