Achichepere Akufunsa Kuti . . .
Kodi Kuchita Mphyotomphyoto Kuli Kowopsya Motani?
“Ndikudabwitsidwa ngati kuchita mphyotomphyoto kuli kolakwa m’maso mwa Mulungu. Kodi kungayambukire umoyo wanga wa kuthupi ndipo/kapena wa maganizo mtsogolo ndipo ngati ndingakhoze kukwatira?”—Melissa wa zaka zakubadwa 15.
MAFUNSO amenewa akhudza achichepere ambiri. Chifukwa chake? Kuchita mphyotomphyoto, kapena kudzutsa kwaumwini kwadala kwa kugalamutsa zochititsa chisembwere, kuli kofala. Mogwirizana ndi maripoti, amuna 97 ndi oposa 90 peresenti ya akazi achitapo mphyomphyoto podzafika msinkhu wa zaka 21. Ndiponso, kachitidweka katsutsidwa kaamba ka mkhalidwe uliwonse woipa—kuchokera pa zotupa pa khungu ndi kufira kwa zikope kufika ku khunyu ndi matenda a maganizo.
Palibe matenda a kuthupi, ngakhale kuli tero, omwe atsimikiziridwa ndi ofufuza za mankhwala amakono omwe akhala akuchititsidwa ndi kuchita mphyotomphyoto. Akuwonjezera ofufuza William Masters ndi Virginia Johnson: “Palibe umboni uliwonse wokhazikitsidwa mwa mankhwala kuti kuchita mphyotomphyoto, mosasamala kanthu za kubwerezabwereza, kumatsogolera ku matenda a maganizo.”
Komabe, achichepere Achikristu ambiri ali odera nkhaŵa ponena za ukulu wa chizoloŵezi chimenechi. “Pamene ndinayamba kuchita icho [mphyotomphyoto], ndinakhoza kudzimva monga kuti ndinachimwira Yehova Mulungu,” analemba tero wachichepere mmodzi. “Ndinapsyinjika kwakukulukulu nthaŵi zina.” Wachichepere wina anafunsa kuti: “Kodi kuchita mphyotomphyoto kuli chimo losakhululukidwa?”
Kodi Baibulo Limanenanji?
Ngakhale kuti machimo a kugonana onga ngati kugonana kunja kwa chikwati (dama), kugonana kwa ofanana ziwalo, chigololo, ndi kugonana ndi zinyama kuli kotsutsidwa kotheratu monga machimo akulu m’Baibulo, kuchita mphyotomphyoto sikunatchulidwe. (Genesis 39:7-9; Levitiko 18:20, 22, 23; 1 Akorinto 6:9, 10) Kuchita mphyotomphyoto kunali kofala m’dziko lolankhula Chigriki mkati mwa nthaŵi ya Baibulo, ndipo mawu osiyanasiyana a Chigriki ankagwiritsiridwa ntchito kulongosola kachitidweko. Mosangalatsa, palibe ndi liwu limodzi lomwe limene likugwiritsiridwa ntchito m’Baibulo.a
Popeza kuti kuchita mphyotomphyoto sikuli kotsutsidwa mwachindunji m’Baibulo, kodi ichi chimatanthauza kuti kuli kosavulaza? Motsimikizirika ayi! Ngakhale awo amene kwenikweni sali odera nkhaŵa ndi kawonedwe ka umulungu amadzimva kukhala osakhazikika ponena za kachitidweko. Mwachitsanzo, Dr. Aaron Hass m’kufufuza kwake kwa kachitidwe ka kugonana ka achichepere 625 anasimba kuti: “Ochulukira a achichepere omwe anachitapo mphyotomphyoto anasimba kuti anadzimva kukhala a liwongo, kuchititsidwa manyazi, uve, kupusa, kumvetsedwa chisoni, kapena kusokonezeka.” Motsimikizirika, kuchita mphyotomphyoto kuli kachitidwe kosakhala ka udongo. Koma popeza kuti “zonyansa,” kulingana ndi Baibulo, kuli katchulidwe komwe kamalola mlingo wakuya wokulira wa kuipa, kuchita mphyotomphyoto sikufunikira kugwirizanitsidwa ndi machimo oipa oterowo onga ngati dama kapena mitundu ina ya chisembwere cha kugonana kokulira.—Aefeso 4:19.
Komabe, Mulungu amazindikira kuti kulabadira kuletsa kwa Baibulo molimbana ndi chimo la chisembwere cha kugonana sikuli kopepuka. Iye, chotero, amapereka malingaliro a mmene tingapewere chisembwere cha kugonana. Iye ‘amakuphunzitsani kuti mupindule.’ (Yesaya 48:17) Malamulo a Mawu ake amasonyeza kuti “mumapindula inu eni” mwakutsutsa zolimba chizoloŵezi chodetsa chimenechi, choyambirira chifukwa chakuti icho . . .
Chimadzutsa “Chilakolako cha Kugonana”
“Fetsani, chotero, ziwalo za thupi lanu,” limafulumiza tero Baibulo, “za . . . chilakolako cha kugonana.” (Akolose 3:5, NW) “Chilakolako cha kugonana” chimenechi sichiri kudzimva kwa kufuna kugonana kwatsopano kumene achichepere ambiri amamva mkati mwa unamwali, pa chimene palibe kufunika kulikonse kwa kudzimvera chisoni. “Chilakolako cha kugonana” chimakhalapo pamene kudzimva kumeneko kwakulitsidwa kotero kuti wina alephera kukulamulira. Chilakolako cha kugonana choterocho chatsogolera ku chimo la chisembwere cha kugonana, monga momwe zalongosoledwera ndi Paulo pa Aroma 1:26, 27.b
Koma kodi kuchita mphyotomphyoto “sikumafetsa” zilakolako zimenezi? Mosiyanako, monga mmene wachichepere mmodzi analongosolera: “Pamene uchita mphyotomphyoto, umakhalirira mwamalingaliro pa zikhumbo zoipa, ndipo chonse chimene chimachitika chiri kuwonjezera chilakolako chako kaamba ka izo.” Kaŵirikaŵiri kachitidwe konyansa kamagwiritsiridwa ntchito kuwonjezera chikondwerero cha kugonana. (Mateyu 5:27, 28) Mutapatsidwa mikhalidwe yoyenerera, inu mungagwe mopepuka m’chisembwere. Wachichepere mmodzi anadzimvera chisoni pambuyo pa kuchita chisembwere: “Panthaŵi imodzi, ndinadzimva kuti kuchita mphyotomphyoto kukakhoza kuchepetsako zokhumbira popanda kudzilowetsamo inemwini ndi mkazi. Komabe ndinakulitsa chikhumbo chosakhoza kulakika cha kuchita tero.” M’chenicheni, phunziro la dziko lonse linavumbula kuti kwa achichepere amene anachita mphyotomphyoto, chiŵerengero chokulira chinkachitamo chisembwere. Iwo anaposa chiŵerengero cha aja omwe anali anamwali ndi 50 peresenti! Kachitidweko motsimikizirika sikanathetse “chilakolako cha kugonana” chawo!
Ngakhale ngati mumadzimva kuti mungakhoze kudzilamulira inumwini mu mkhalidwe woipa kwambiri, nchifukwa ninji kudziika m’ngozi ya kudzutsa chilakolako inueni mwa kuchita mphyotomphyoto? Ngati mwaŵi wa kuchita chisembwere unawoneka, kodi inu ndithudi mungakhoze kunena kuti ayi?
Zodetsa Mwamaganizo ndi Mwamalingaliro
Kuchita mphyotomphyoto kumaloŵetsanso mikhalidwe ina yake yomwe imaipitsa mwamalingaliro. (Yerekezani 2 Akorinto 11:3.) Chizoloŵezi chimenechi chimaphunzitsa wina kuchita ndi thupi lake monga kokha chiwiya chogwiritsiridwa ntchito kaamba ka zosangalatsa za kugonana. Pamene achita mphyotomphyoto, munthu amamizidwa mu zilakolako za thupi lake—kudzikonda kotheratu. Kugonana kumakhala kolekanitsidwa ku chikondi ndipo kumatsogozedwa ku tsatanetsatane wa thupi yemwe amatulutsa kukangana. Koma Mulungu analinganiza zilakolako za kugonana kuti zikhutiritsidwe mu unansi wa kugonana, kasonyezedwe ka chikondi pakati pa mwamuna ndi mkazi wake.—Miyambo 5:15-19.
Kusowa kawonedwe kameneka kungatsogolere ku mavuto m’kusintha ku unansi wabwino wa awo a ziwalo zosiyana za kugonana. Oterewa angawonedwe monga ziwiya za kugonana nazo m’malo mwa anthu okhoza kumva. Wina angakhoze kupondereza mnzake monga chiwiya chokha cha kukhutiritsira kugonana. Kachitidwe koipa kotereka kophunzitsidwa ndi kuchita mphyotomphyoto kangaipsye “mzimu” wa wina, kapena kawonedwe ka maganizo kodidikiza. Kaamba ka chifukwa chabwino, Mawu a Mulungu amatisonkhezera kuti: “Okondedwa, tidzikonzere ife tokha kuleka chodetsa cha thupi ndi cha mzimu.” (2 Akorinto 7:1) Chowona, pambuyo pa chikwati okwatirana ambiri amakhala okhoza kugwirira ntchito pa mavuto ochititsidwa ndi kuchita mphyotomphyoto. Komabe, zitsanzo zambiri zimapereka nsonga za mmene angakhalire ovuta ndi okhalitsa ena a mavuto amenewa, kaŵirikaŵiri kumayambukira kugwirizana kwa aŵiri okwatirana.
Koma bwanji ngati munthu akumenyera kugonjetsa chizoloŵezi choipa chimenechi, ndipo pamene mwachisawawa akupita patsogolo, ali ndi mavutobe ndi icho?
Kawonedwe Kolinganizika ka Liwongo
Ngakhale kuti cholakwa chiri cholakwa, Baibulo limasonyeza kuti Mulungu amawona kuchita kwathu choipa kukhala kwa ukulu wosiyanasiyana, ndipo ali wachifundo. “Pakuti inu, [Yehova NW], ndinu wabwino, ndi wokhululukira, ndi wachifundo chochulukira onse akuitana inu.” (Masalmo 86:5) Pamene Mkristu wagonjera ku kuchita mphyotomphyoto, mtima wake kaŵirikaŵiri umamtsutsa. Komabe, Baibulo limalongosola kuti “Mulungu ali wamkulu koposa mitima yathu, amazindikira zonse.” (1 Yohane 3:20) Mulungu amawona zambiri kuposa machimo athu. Ukulu wa chidziŵitso chake umamkhozetsa iye kumvetsera ndi chifundo kufunsira kwathu kwa mu mtima kaamba ka kukhululukidwa. Monga mmene mkazi wachichepere mmodzi analembera: “Ndadzimva wa liwongo ku mlingo winawake, koma kudziŵa amene Mulungu wachikondi ali ndi kuti angaŵerenge mtima wanga ndi kudziŵa zoyesayesa zanga zonse ndi zolinga kumandisunga ine kuchoka ku kukhala wopsyinjika kwambiri pamene ndalakwa nthaŵi zina.” Mwa kulimbana ndi kuchita mphyotomphyoto, sichiri chotsimikizirika kuti inu mudzachita chimo lalikulu la chisembwere.
Kope la February 15, 1954, la magazini yathu inzake, Nsanja ya Olonda, (Chingelezi) linalongosola kuti: “Ife [tingakhoze] kudzipeza ife eni tikukhumudwa ndi kukhoterera nthaŵi zambiri ku zizoloŵezi zoipa zomwe zatikoka mozama ku mkhalidwe wathu wakale wa umoyo kuposa ndi mmene tinkayembekezera. Kenaka tiri okhoterera kudzimva wokhumudwitsidwa kwambiri ndipo wosayenerera. . . . Musavutike mtima. Inu musatsirize kuti mwachita chimo losakhoza kukhululukidwa. Umu ndi mmene Satana amangofuna kuti inu mulingalire. Chenicheni chakuti inu mumadzimva achisoni ndi kukalipitsidwa ndi inueni chiri chitsimikiziro chokha chakuti simunapite patali. Musadere nkhaŵa kutembenuka modzichepetsa ndi mofunitsitsa kwa Mulungu, mukumafuna chikhululukiro chake ndi kuyeretsa ndi chithandizo. Pitani kwa iye monga mmene mwana amapitira kwa atate wake pamene ali mu vuto, mosasamala kanthu ndi kubwerezabwereza kotani kwa cholakwa chimodzimodzicho, ndipo Yehova adzakupatsani inu chithandizo mwaulemerero chifukwa cha chisomo chake ndipo, ngati muli wotsimikiza, iye adzakupatsani inu kuzindikira kwa chikumbumtima choyeretsedwa.”
[Mawu a M’munsi]
a Mulungu anapha Onani kaamba ka ‘kuwononga ubwamuna wake pansi (NW).’ Komabe, kugonana kosokonezedwa, osati kuchita mphyotomphyoto, kunaphatikizidwa. Ndiponso, kuphedwako kunali chifukwa chakuti Onani analephera mwadyera kuchita ukwati wa usuweni m’malo mofuna kupitiriza ndi mzere wa banja la mbale wake. (Genesis 38:1-10) “Kugona uipa” kotchulidwa pa Levitiko 15:16-18 mwachiwonekere kumalozera, osati ku kuchita mphyotomphyoto, koma ku kutulutsa ubwamuna usiku limodzinso ndi unansi wa kugonana kwa mu chikwati.
b Liwu la Chigriki loyambirira kaamba ka “chilakolako cha kugonana” (paʹthos) linagwiritsiridwa ntchito ndi wodziŵa mbiri yakale wa m’zana loyamba Josephus kulongosola mkazi wa Potifa, amene, chifukwa cha “chisiriro chopitirira [paʹthos],” anayesera kunyenga wachichepere Yosefe; ndi mwamuna Amunoni, amene, “atatenthetsedwa ndi chilakolako ndi kutsogozedwa ndi mphamvu za kusirira [paʹthos], anaipsya [kugwirira] mlongo wake.” Kusirira kwa onse aŵiri mkazi wa Potifa ndi kwa Amunoni kunali kosadziletsa.—Genesis 39:7-12; 2 Samueli 13:10-14.
[Chithunzi patsamba 14]
Ngakhale kuti kuchita mphyotomphyoto kungapangitse malingaliro amphamvu a liwongo, pemphero lochokera mu mtima kaamba ka chikhululukiro cha Mulungu ndi kugwira ntchito mwamphamvu kutsutsa kachitidweko kungapatse wina chikumbumtima chabwino