Yehova Atenga Ana Ambiri Aloŵe Ulemerero
“Kunamuyenera Iye [Mulungu], . . . pakutenga ana ambiri aloŵe ulemerero, kumkonza wamphumphu mtsogoleri woyamba wa chipulumutso chawo mwa zoŵaŵa.”—AHEBRI 2:10.
1. Kodi nchifukwa ninji tingakhale otsimikiza kuti chifuno cha Yehova kaamba ka mtundu wa anthu chidzakwaniritsidwa?
YEHOVA analenga dziko lapansi kuti likhale mudzi wachikhalire wa banja la munthu langwiro lokhala ndi moyo kosatha. (Mlaliki 1:4; Yesaya 45:12, 18) Zoonadi, kholo lathu Adamu anachimwa ndipo chifukwa cha zimenezo anapatsira mbadwa zake uchimo ndi imfa. Koma chifuno cha Mulungu kaamba ka mtundu wa anthu chidzakwaniritsidwa mwa Mbewu yake Yolonjezedwa, Yesu Kristu. (Genesis 3:15; 22:18; Aroma 5:12-21; Agalatiya 3:16) Chifukwa chakuti anakonda dziko la anthu, Yehova anasonkhezeredwa kupereka “Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.” (Yohane 3:16) Ndipo chikondi chinasonkhezera Yesu “kupereka moyo wake dipo la anthu ambiri.” (Mateyu 20:28) “Chiwombolo” chimenechi chimagulanso mwaŵi ndi ziyembekezo zimene Adamu anataya ndipo chimapangitsanso kuti pakhale mwaŵi wokhala ndi moyo wosatha.—1 Timoteo 2:5, 6; Yohane 17:3.
2. Kodi ntchito ya nsembe ya dipo ya Yesu inaphiphiritsiridwa motani pa Tsiku Lachitetezo la chaka ndi chaka la Israyeli?
2 Ntchito ya nsembe ya dipo ya Yesu inali kuphiphiritsiridwa pa Tsiku Lachitetezo limene linali kuchitika chaka ndi chaka. Patsikulo, choyamba mkulu wa ansembe wa Israyeli anali kupereka ng’ombe kuti ikhale nsembe yauchimo ndipo anali kuthira mwazi wake pa Likasa lopatulika m’Malo Opatulikitsa a chihema, ndipo patapita nthaŵi zimenezo zinayamba kuchitidwira m’kachisi. Mkulu wa ansembe anali kuchita zimenezi m’malo mwa iye mwini, banja lake, ndi fuko la Levi. Mofananamo, Yesu Kristu anapereka kwa Mulungu mtengo wa mwazi wake kuti choyamba uphimbe machimo a “abale” ake auzimu. (Ahebri 2:12; 10:19-22; Levitiko 16:6, 11-14) Pa Tsiku Lachitetezo, mkulu wa ansembe anali kuperekanso mbuzi kuti ikhale nsembe yauchimo ndi kupereka mwazi wake m’Malo Opatulikitsa, ndipo zimenezi zinali kutetezera mitundu 12 ya Israyeli imene sinali yaunsembe kumachimo awo. Mofananamo, Mkulu wa Ansembe Yesu Kristu adzagwiritsira ntchito mwazi wake wamoyo m’malo mwa anthu okhulupirira, ndipo udzafafaniza machimo awo.—Levitiko 16:15.
Kuloŵetsedwa mu Ulemerero
3. Malinga nkunena kwa Ahebri 2:9, 10, kodi Mulungu wakhala akuchita chiyani kwa zaka 1,900?
3 Kwa zaka 1,900, Mulungu wakhala akuchita chinthu chinachake chosangalatsa kwambiri chokhudza “abale” ake a Yesu. Ponena za chimenechi, mtumwi Paulo analemba kuti: “Timpenya Iye amene adamchepsa pang’ono ndi angelo, ndiye Yesu, chifukwa cha zoŵaŵa za imfa, wovala korona wa ulemerero ndi ulemu, kuti ndi chisomo cha Mulungu alaŵe imfa m’malo mwa munthu aliyense. Pakuti kunamuyenera Iye [Yehova Mulungu] amene zonse zili chifukwa cha Iye, ndi zonse mwa Iye, pakutenga ana ambiri aloŵe ulemerero, kumkonza wamphumphu mtsogoleri woyamba wa chipulumutso chawo mwa zoŵaŵa.” (Ahebri 2:9, 10) Mtsogoleri woyamba wa chipulumutso ndiye Yesu Kristu, amene anaphunzira kumvera mwangwiro mwa zoŵaŵa zimene anakumana nazo akali munthu padziko lapansi. (Ahebri 5:7-10) Yesu anali woyamba kudzozedwa monga mwana wauzimu wa Mulungu.
4. Kodi ndi liti ndipo ndi motani mmene Yesu anadzozedwera kuti akhale Mwana wauzimu wa Mulungu?
4 Yehova anagwiritsira ntchito mzimu wake woyera, kapena kuti mphamvu yogwira ntchito, podzoza Yesu kuti akhale Mwana wake wauzimu, ncholinga chakuti amloŵetse mu ulemerero wakumwamba. Pamene anali kwayekha pamodzi ndi Yohane Mbatizi, Yesu anamizidwa kotheratu m’madzi posonyeza kudzipereka kwake kwa Mulungu. Nkhani ya mu Uthenga Wabwino wa Luka imati: “Pamene anthu onse anabatizidwa, ndipo Yesu anabatizidwa, nalikupemphera, kuti panatseguka pathambo, ndipo mzimu woyera anatsika ndi maonekedwe a thupi lake ngati nkhunda, nadza pa Iye; ndipo munatuluka mawu m’thambo, kuti, Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa, mwa Iwe ndikondwera.” (Luka 3:21, 22) Yohane anaona mzimu woyerawo ukutsikira pa Yesu ndipo anamva Yehova akumuvomereza poyera kuti ndiye Mwana Wake wokondedwa. Panthaŵi imeneyo ndipo mwa mzimu woyera, Yehova anadzoza Yesu monga woyamba wa ‘ana ambiri oloŵetsedwa mu ulemerero.’
5. Kodi ndani amene akhala oyambirira kupindula ndi nsembe ya Yesu, nanga alipo angati?
5 “Abale” ake a Yesu akhala oyamba kupindula mwa nsembe yake. (Ahebri 2:12-18) M’masomphenya, mtumwi Yohane anaona iwo ataloŵa kale mu ulemerero pa Phiri la Ziyoni lakumwamba pamodzi ndi Mwanawankhosa, Ambuye Yesu Kristu woukitsidwayo. Yohane anatchulanso za chiŵerengero chawo, nanena: “Ndipo ndinapenya, taonani, Mwanawankhosayo alikuimirira pa Phiri la Ziyoni, ndipo pamodzi ndi Iye zikwi zana mphambu makumi anayi kudza anayi, akukhala nalo dzina lake ndi dzina la Atate wake lolembedwa pamphumi pawo. . . . Iwowa anagulidwa mwa anthu, zipatso zoundukula kwa Mulungu ndi kwa Mwanawankhosa. Ndipo m’kamwa mwawo simunapezedwa bodza; ali opanda chirema.” (Chivumbulutso 14:1-5) Choncho ‘ana ambiri oloŵa ulemerero’ wakumwamba alipo 144,001 okha—Yesu ndi abale ake auzimu.
‘Obadwa Kuchokera mwa Mulungu’
6, 7. Kodi ndani amene ali ‘obadwa kuchokera mwa Mulungu,’ ndipo zimenezi zimatanthauzanji kwa iwo?
6 Anthu odzozedwa ndi Yehova ali ‘obadwa kuchokera mwa Mulungu.’ Ponena za anthu ameneŵa, mtumwi Yohane analemba kuti: “Yense wobadwa kuchokera mwa Mulungu sachita tchimo, chifukwa mbewu yake [ya Yehova] ikhala mwa iye; ndipo sakhoza kuchimwa, popeza wabadwa kuchokera mwa Mulungu.” (1 Yohane 3:9) “Mbewu” imeneyi ndiyo mzimu woyera wa Mulungu. Mwa kugwira ntchito mogwirizana ndi mawu ake, mzimuwo wachititsa aliyense wa a 144,000 ameneŵa ‘kubadwanso’ ku chiyembekezo cha kumwamba.—1 Petro 1:3-5, 23.
7 Mwa kubadwa kwake monga munthu, Yesu anali Mwana wa Mulungu, mongadi momwe munthu wangwiro Adamu analili “mwana wa Mulungu.” (Luka 1:35; 3:38) Komabe, Yesu atabatizidwa, chinali chinthu chapadera kuti Yehova analengeza kuti: “Mwana wanga wokondedwa ndiwe, mwa Iwe ndikondwera bwino.” (Marko 1:11) Chilengezo chimenechi chotsagana ndi kutsanuliridwa kwa mzimu woyera, chinali umboni wakuti Mulungu anali atatenga Yesu kuti akhale Mwana Wake wauzimu. Panthaŵiyo Yesu ‘anabadwa mwatsopano,’ titero kunena kwake, napatsidwa mwaŵi wolandiranso moyo monga Mwana wauzimu wa Mulungu kumwamba. Mofanana ndi iye, abale ake auzimu okwanira 144,000 ali ‘obadwa mwatsopano.’ (Yohane 3:1-8; onani Nsanja ya Olonda, November 15, 1992, masamba 3-6.) Monganso momwe anachitira Yesu, iwo anadzozedwa ndi Mulungu ndi kupatsidwa ntchito yolalikira uthenga wabwino.—Yesaya 61:1, 2; Luka 4:16-21; 1 Yohane 2:20.
Umboni wa Kudzozedwa
8. Kodi kudzozedwa ndi mzimu kwa (a) Yesu (b) ophunzira ake oyambirira, kunachitiridwa umboni motani?
8 Panali umboni wakuti Yesu anadzozedwa ndi mzimu. Yohane Mbatizi anaona mzimu ukutsikira pa Yesu ndipo anamvanso chilengezo cha Mulungu chakuti Mesiya wongodzozedwa kumeneyo ndi Mwana Wake wauzimu. Koma kodi ophunzira a Yesu anadziŵa bwanji kuti iwo anadzozedwa ndi mzimu? Ndithudi, patsiku limene anakwera kumwamba, Yesu anati: “Yohane anabatizadi ndi madzi; koma inu mudzabatizidwa ndi mzimu woyera, asanapite masiku ambiri.” (Machitidwe 1:5) Ophunzira a Yesu ‘anabatizidwa ndi mzimu woyera’ patsiku la Pentekoste wa 33 C.E. Kutsanuliridwa kumeneko kwa mzimu kunatsagana ndi ‘mkokomo wochokera kumwamba wa mphepo yolimba’ ndi “malilime ogaŵanikana, onga a moto” pa aliyense wa ophunzirawo. Chinthu chimene chinali chapadera kwambiri chinali chakuti ophunzirawo ‘analankhula ndi malilime ena, monga mzimu unawalankhulitsa.’ Choncho, panali umboni wooneka ndi womveka wakuti njira ya ulemerero wakumwamba inatsegukira otsatira a Kristu amenewo ndipo anakhala ana a Mulungu.—Machitidwe 2:1-4, 14-21; Yoweli 2:28, 29.
9. Kodi ndi umboni wotani umene unasonyeza kuti Asamariya, Korneliyo, ndi anthu ena a m’zaka za zana loyamba anali atadzozedwa ndi mzimu?
9 Nthaŵi inayake zimenezi zitachitika, Filipo mlaliki anakalalikira ku Samariya. Ngakhale kuti Asamariya analandira uthengawo nabatizidwa, iwo analibe umboni wakuti Mulungu anawadzoza kuti akhale ana ake. Pamene atumwiwo Petro ndi Yohane anapemphera ndi kuika manja awo pa okhulupirirawo, iwo “analandira mzimu woyera” mwa njira inayake imene anthu oonerera anaichitira umboni. (Machitidwe 8:4-25) Umenewu unali umboni wakuti Asamariya okhulupirirawo anali atadzozedwa ndi mzimu nakhala ana a Mulungu. Mofananamo, mu 36 C.E., Korneliyo ndi Akunja ena analandira choonadi cha Mulungu. Petro ndi Ayuda okhulupirira amene anatsagana naye “anadabwa . . . , chifukwa pa amitundunso panatsanuliridwa mphatso ya mzimu woyera. Pakuti anawamva iwo alikulankhula ndi malilime, ndi kumkuza Mulungu.” (Machitidwe 10:44-48) Akristu ambiri a m’zaka za zana loyamba analandira “mphatso zauzimu” monga kulankhula m’malilime. (1 Akorinto 14:12, 32) Chotero anthu ameneŵa anali ndi umboni wonse wakuti iwo anadzozedwa. Koma kodi Akristu okhalapo pambuyo pa zimenezi anali kudzadziŵa bwanji kuti ali odzozedwa ndi mzimu kapena sali odzozedwa?
Umboni wa Mzimu
10, 11. Pamaziko a Aroma 8:15-17, kodi mungafotokoze motani pankhani yakuti mzimu umachitira umboni oloŵa nyumba anzake a Kristu?
10 Akristu onse odzozedwa okwanira 144,000 akhala ndi umboni wokwanira wakuti ali ndi mzimu wa Mulungu. Ponena za nkhani imeneyi, Paulo analemba kuti: “Munalandira mzimu wa umwana, umene tifuula nawo, kuti, Abba, Atate. Mzimu [wo]kha [u]chita umboni pamodzi ndi mzimu wathu, kuti tili ana a Mulungu; ndipo ngati ana, pomweponso oloŵa nyumba; inde oloŵa nyumba ake a Mulungu, ndi oloŵa anzake a Kristu; ngatitu ife timva zoŵaŵa pamodzi naye, kuti tikalandirenso ulemerero pamodzi ndi iye.” (Aroma 8:15-17) Akristu odzozedwa ali ndi mkhalidwe wina wapadera kwambiri mogwirizana ndi Atate wawo wakumwamba, umboni wakuti alidi ana ake. (Agalatiya 4:6, 7) Iwo ali otsimikiza kotheratu kuti anadzozedwa ndi Mulungu kuti akhale ana ake auzimu monga oloŵa nyumba anzake a Kristu mu Ufumu wakumwamba. Pokwaniritsa zimenezi, mzimu woyera wa Yehova umagwira ntchito yofunika kwambiri.
11 Mwa chisonkhezero cha mzimu woyera wa Mulungu, mzimu, kapena kuti mkhalidwe wapadera kwambiri, wa odzozedwa umawasonkhezera kuti azichita mogwirizana ndi zimene Mawu a Mulungu amanena mokhudzana ndi chiyembekezo cha kumwamba. Mwachitsanzo, pamene iwo aŵerenga zimene Malemba amanena zokhudza ana auzimu a Yehova, iwo amavomereza nthaŵi yomweyo kuti mawu amenewo akunena za iwo. (1 Yohane 3:2) Iwo amadziŵa kuti ‘anabatizidwa mwa Kristu Yesu’ ndiponso mwa imfa yake. (Aroma 6:3) Iwo ali ndi chitsimikizo chachikulu chakuti ali ana auzimu a Mulungu, amene adzafa ndi kuukitsidwira ku ulemerero wakumwamba, monga momwe anachitira Yesu.
12. Kodi mzimu wa Mulungu wakhazikitsa chiyani mwa Akristu odzozedwa?
12 Kudzozedwa ndi kukhala mwana wauzimu sikuchitika chifukwa cha chikhumbo cha munthu. Anthu odzozedwa ndi mzimu salingalira zopita kumwamba chifukwa chakuti akusweka maganizo ndi mavuto amene ali padziko lapansi lerolino ayi. (Yobu 14:1) M’malo mwake, mzimu wa Yehova wakhazikitsa mwa odzozedwa enieni ameneŵa chiyembekezo ndi chikhumbo chimene anthu ena onse alibe. Anthu odzozedwa ameneŵa amadziŵa kuti moyo wosatha monga anthu angwiro okhala padziko lapansi la paradaiso pamodzi ndi mabanja ndi mabwenzi achimwemwe ungakhale moyo wosangalatsa kwambiri. Komabe, moyo umenewo sindiwo chikhumbo chachikulu cha m’mitima mwawo. Odzozedwa ali ndi chiyembekezo champhamvu chakumwamba kotero kuti amadzimana mofunitsitsa ziyembekezo zonse ndi zochita za padziko lapansi.—2 Petro 1:13, 14.
13. Malinga nkunena kwa 2 Akorinto 5:1-5, kodi Paulo ‘anakhumbitsa’ chiyani, ndipo kodi zimenezi zimasonyezanji ponena za anthu odzozedwa ndi mzimu?
13 Chiyembekezo chopatsidwa ndi Mulungu cha moyo wakumwamba nchamphamvu kwambiri mwa ameneŵa kotero kuti malingaliro awo ali ofanana ndi aja a Paulo, amene analemba kuti: “Tidziŵa kuti ngati nyumba ya pansi pano ya msasa wathu ipasuka, tili nacho chimango cha kwa Mulungu, ndiyo nyumba yosamangidwa ndi manja, yosatha, m’mwamba. Pakutinso m’menemo tibuula, ndi kukhumbitsa kuvekedwa ndi chokhalamo chathu chochokera kumwamba; ngatitu povekedwa sitidzapezedwa amaliseche. Pakutinso ife okhala mu msasawu tibuula, pothodwa; sikunena kuti tifuna kuvulidwa, koma kuvekedwa, kuti chaimfacho chimezedwe ndi moyo. Ndipo wotikonzera ife ichi chimene, ndiye Mulungu, amene anatipatsa ife chikole cha mzimu.” (2 Akorinto 5:1-5) Paulo ‘anakhumbitsa’ kuti adzaukitsidwe ndi kutengedwera kumwamba monga cholengedwa chauzimu chosakhoza kufa. Ponena za thupi laumunthu, iye anagwiritsira ntchito fanizo la msasa umene umatha kupasuka, malo okhalamo amene ali osalimba ndi akanthaŵi powayerekezera ndi nyumba. Ngakhale kuti akukhala padziko lapansi m’thupi lanyama, lokhoza kufa, Akristu amene ali ndi mzimu monga chikole cha moyo wakumwamba umene ukudzawo akuyembekezera “chimango cha kwa Mulungu,” thupi lauzimu losakhoza kufa ndi losakhoza kuvunda. (1 Akorinto 15:50-53) Mofanana ndi Paulo, iwo anganene motsimikiza kuti: “Tilimbika mtima, ndipo tikondwera makamaka kusakhala m’thupi [laumunthu], ndi kukhala kwathu kwa Ambuye [kumwamba].”—2 Akorinto 5:8.
Kuloŵetsedwa m’Mapangano Apadera
14. Pamene anayambitsa Chikumbutso, kodi ndi pangano liti limene Yesu anatchula choyamba, nanga kodi limagwira ntchito yotani mogwirizana ndi Israyeli wauzimu?
14 Akristu odzozedwa ndi mzimu ali otsimikiza kuti analoŵetsedwa m’mapangano aŵiri apadera. Yesu anatchula limodzi la ameneŵa pamene anagwiritsira ntchito mkate wopanda chotupitsa ndi vinyo poyambitsa Chikumbutso cha imfa yake imene inali kuyandikira, pamene anati ponena za chikho: “Chikho ichi ndi pangano latsopano m’mwazi wanga wothiridwa chifukwa cha inu.” (Luka 22:20; 1 Akorinto 11:25) Kodi ndani amene ali oloŵetsedwa m’pangano latsopanoli? Yehova Mulungu ndi mamembala a Israyeli wauzimu—anthu amene Yehova akufuna kuwaloŵetsa mu ulemerero wakumwamba. (Yeremiya 31:31-34; Agalatiya 6:15, 16; Ahebri 12:22-24) Pangano latsopano limagwira ntchito kudzera mwa mwazi wokhetsedwa wa Yesu ndipo limatenga mwa amitundu anthu a dzina la Yehova ndiponso limapanga Akristu odzozedwa ndi mzimu ameneŵa kukhala mbali ya “mbewu” ya Abrahamu. (Agalatiya 3:26-29; Machitidwe 15:14) Pangano latsopano limapatsa mwaŵi anthu onse a Israyeli wauzimu kuti aloŵetsedwe mu ulemerero mwa kuukitsidwira ku moyo wosakhoza kufa wakumwamba. Pokhala “chipangano chosatha,” mapindu ake adzakhala kosatha. Zidzadziŵika mtsogolo muno ngati pangano limeneli lidzagwiranso ntchito zina mu Ulamuliro Wazaka Chikwi ndi pambuyo pake.—Ahebri 13:20.
15. Mogwirizana ndi Luka 22:28-30, kodi otsatira odzozedwa a Yesu anayamba kuloŵetsedwa m’pangano lina liti, nanga zimenezi zimachitika liti?
15 Aliyense wa “ana ambiri” amene Yehova akufuna ‘kuwaloŵetsa mu ulemerero’ waloŵetsedwanso payekha m’pangano la Ufumu wakumwamba. Ponena za pangano limeneli lapakati pa iye mwini ndi otsatira mapazi ake, Yesu anati: “Inu ndinu amene munakhala ndi Ine chikhalire m’mayesero anga; ndipo Ine ndikuikirani [“ndipangana nanu pangano la,” NW] ufumu, monganso Atate wanga anandiikira [“anapangana pangano ndi,” NW] Ine, kuti mukadye ndi kumwa kugome kwanga mu Ufumu wanga; ndipo mudzakhala pa mipando yachifumu ndi kuweruza mafuko khumi ndi aŵiri a Israyeli.” (Luka 22:28-30) Pangano la Ufumu linakhazikitsidwa pamene ophunzira a Yesu anadzozedwa ndi mzimu woyera pa Pentekoste wa 33 C.E. Pangano limenelo lidzagwirabe ntchito mpaka muyaya pakati pa Kristu ndi mafumu anzake. (Chivumbulutso 22:5) Nchifukwa chake Akristu odzozedwa ndi mzimu ali otsimikiza kuti iwo ali m’pangano latsopano ndiponso m’pangano la Ufumu. Choncho, paphwando la Chakudya Chamadzulo cha Ambuye, otsalira ochepa a odzozedwa okhawo amene adakali padziko lapansi ndiwo amadya mkate, kuimira thupi laumunthu la Yesu lopanda uchimo, ndi kumwa vinyo, kuimira mwazi wake wangwiro wothiridwa paimfa ndiponso umene umapangitsa pangano latsopano kuti likhale logwira ntchito.—1 Akorinto 11:23-26; onani Nsanja ya Olonda, February 1, 1989, masamba 17-20.
Oitanidwa, Osankhika, ndi Okhulupirika
16, 17. (a) Kuti aloŵetsedwe mu ulemerero, kodi onse a 144,000 ayenera kuchita chiyani? (b) Kodi “mafumu khumi” ndani, nanga kodi iwo akuchita chiyani kwa otsalira a padziko lapansi a “abale” a Kristu?
16 Ntchito yoyamba ya nsembe ya dipo ya Yesu ikuchititsa kuti a 144,000 aitanidwire kumoyo wakumwamba ndi kusankhidwa mwa kudzozedwa ndi mzimu wa Mulungu. Ndithudi, kuti aloŵetsedwe mu ulemerero, iwo ayenera ‘kuchita changu kukhazikitsa maitanidwe ndi masankhulidwe awo,’ ndiponso ayenera kukhaladi okhulupirika kufikira imfa. (2 Petro 1:10; Aefeso 1:3-7; Chivumbulutso 2:10) Otsalira ochepa a odzozedwa amene adakali padziko lapansi akusungabe kukhulupirika kwawo ngakhale kuti akutsutsidwa ndi “mafumu khumi” amene amaimira maulamuliro onse a ndale. “Iwo adzachita nkhondo pa Mwanawankhosa,” anatero mngelo, “ndipo Mwanawankhosa adzawalaka, chifukwa ali Mbuye wa ambuye, ndi Mfumu ya mafumu; ndipo adzawalakanso iwo akukhala naye, oitanidwa, ndi osankhika ndi okhulupirika.”—Chivumbulutso 17:12-14.
17 Olamulira aumunthu sangachite chilichonse motsutsana ndi Yesu, “Mfumu ya mafumu,” popeza kuti iye ali kumwamba. Koma iwo amadana ndi otsalira a “abale” ake amene adakali padziko lapansi. (Chivumbulutso 12:17) Zimenezo zidzatha pankhondo ya Mulungu ya Armagedo, pamene kudzakhaladi chilakiko cha “Mfumu ya mafumu” ndi “abale” ake—“oitanidwa, ndi osankhika ndi okhulupirika.” (Chivumbulutso 16:14, 16) Tsopano lino, Akristu odzozedwa ndi mzimu ali otanganika kwambiri. Kodi iwo akuchita chiyani tsopano, asanaloŵetsedwe mu ulemerero ndi Yehova?
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi ndani amene Mulungu ‘amawaloŵetsa mu ulemerero wakumwamba’?
◻ Kodi ‘kubadwa kuchokera mwa Mulungu’ kumatanthauzanji?
◻ Kodi mzimu ‘umachitira umboni’ motani kwa Akristu ena?
◻ Kodi anthu odzozedwa ndi mzimu aloŵetsedwa m’mapangano ati?
[Chithunzi patsamba 15]
Pa Pentekoste wa 33 C.E., panaperekedwa umboni wakuti njira yoloŵera mu ulemerero wakumwamba inatseguka