Kodi Ndimotani Mmene Yesu Kristu Analiri Mneneri Wofanana ndi Mose?
YEHOVA MULUNGU samanama. (Tito 1:2; Ahebri 6:18) Chotero, maulosi a Mawu ake, Baibulo, ali odalirika ndi owona. Iwo adzakwaniritsidwadi.
Pakati pa maulosi ouziridwa mwaumulungu ameneŵa pali umodzi umene mneneri Wachihebri Mose analemba ponena za Mesiya. Pogwira mawu Yehova, Mose anati: ‘Ndidzawaukitsira [Aisrayeli] mneneri wa pakati pa abale awo, wonga iwe [Mose]; ndipo ndidzampatsa mawu anga m’kamwa mwake, ndipo adzanena nawo zonse ndimuuzazi.’—Deuteronomo 18:17, 18.
Mtumwi Petro anagwiritsira ntchito ulosiwu kwa Yesu Kristu pamene adanena kuti: ‘Mosetu anati, [Yehova, NW] Mulungu adzaukitsira inu mneneri mwa abale anu, ngati ine; mudzamvera iye m’zinthu ziri zonse akalankhula nanu.’ (Machitidwe 3:22) Kwenikweni, Yesu iyemwini adanena kuti: ‘Pakuti mukadakhulupirira Mose, mukadakhulupirira ine, pakuti iyeyu analembera za ine.’ (Yohane 5:46) Kodi ndi m’njira zotani mmene Yesu ndi Mose analiri ofanana?
Ofanana m’Chiyambi cha Ntchito Zawo
Onse aŵiri Mose ndi Yesu anapulumuka kuphedwa kwa ana aamuna aang’ono kwambiri. Mose wakhanda anabisidwa pakati pa mabango m’mbali mwa mtsinje wa Nile ndipo motero anapulumuka kuphedwa kwa makanda aamuna Achiisrayeli monga momwe kunalamulidwa ndi Farao wa Igupto. Monga mwana wachichepere, Yesu nayenso anapulumuka kuphedwa kwa ana aamuna kufika ku azaka ziŵiri m’Betelehemu ndi zigawo zake. Kupha kumeneku kunalamulidwa ndi Mfumu Herode Wamkulu, amene, mofanana ndi Farao, anali mdani wa Mulungu ndi anthu Ake.—Eksodo 1:22–2:10; Mateyu 2:13-18.
Mzimu wofatsa, kapena wodzichepetsa, unasonyezedwa ndi onse aŵiri Mose ndi Yesu. Ngakhale kuti analeredwa monga mwana wa m’nyumba ya mfumu yamphamvu ya Igupto, Mose anadzakhala “wofatsa woposa anthu onse a pa dziko lapansi.” (Numeri 12:3) Moyerekezera, Yesu anatumikira monga Mikayeli kalonga wamphamvu kumwamba koma modzichepetsa anatsikira ku dziko lapansi. (Danieli 10:13; Afilipi 2:5-8) Ndiponso, Yesu anali ndi chifundo kwa anthu ndipo anakhoza kunena kuti: ‘Senzani gori langa, ndipo phunzirani kwa ine; chifukwa ndiri wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu.’—Mateyu 11:29; 14:14.
Kaamba ka utumiki wa Yehova, onse aŵiri Mose ndi Yesu anasiya kumbuyo malo apamwamba ndi chuma chambiri. Kuti atumikire Yehova ndi anthu Ake, Mose anasiya chuma ndi malo okwezeka mu Igupto. (Ahebri 11:24-26) Mofananamo, Yesu anasiya kumbuyo malo olemekezeka kwambiri ndi chuma kumwamba kotero kuti atumikire Mulungu ndi anthu Ake padziko lapansi.—2 Akorinto 8:9.
Onse aŵiri Mose ndi Yesu anakhala odzozedwa a Mulungu. Mneneri Mose anatumikira monga wodzozedwa wa Yehova ku mtundu wa Israyeli. Monga momwe mtumwi Paulo ananenera, Mose ‘anaŵerenga thonzo la [kukhala] Kristu [wodzozedwayo] chuma choposa zolemera za Aigupto.’ (Ahebri 11:26; Eksodo 3:1–4:17) Kodi nliti pamene Yesu anakhala Kristu, kapena Wodzozedwayo? Ichi chinachitika pamene anadzozedwa ndi mzimu woyera wa Mulungu, kapena mphamvu yogwira ntchito, atabatizidwa. Kwa mkazi Wachisamariya pachitsime cha Yakobo ku Sukari ndiponso pamaso pa mkulu wansembe wa Israyeli pamene ankazengedwa mlandu, Yesu anapereka umboni wakuti iye anali Mesiya, kapena Kristu.—Marko 14:61, 62; Yohane 4:25, 26.
Onse aŵiri Mose ndi Yesu anasala kudya kwa masiku 40. Kuchiyambi kwa ntchito yake monga wolankhulira Mulungu, Mose anasala kudya kwa masiku 40 pamene anali m’phiri la Sinai. (Eksodo 34:28) Yesu anasala kudya kwa masiku 40 m’chipululu ndiyeno anatsutsa chiyeso cha Satana kuchiyambi kwa ntchito yake monga Mesiya wolonjezedwayo.—Mateyu 4:1-11.
Amuna Onse Aŵiriwo Analemekeza Yehova
Yehova anagwiritsira ntchito onse aŵiri Mose ndi Yesu kukweza dzina Lake lopatulika. Mulungu anauza Mose kupita kwa Aisrayeli m’dzina la ‘Yehova, Mulungu wa makolo awo.’ (Eksodo 3:13-16) Mose anaimira Mulungu pamaso pa Farao, amene analoledwa kukhalabe ndi moyo kotero kuti mphamvu ya Yehova isonyezedwe ndikuti dzina Lake lilengezedwe padziko lonse lapansi. (Eksodo 9:16) Mofananamo Yesu anabwera m’dzina la Yehova. Mwachitsanzo, Kristu ananena kuti: ‘Ndadza ine m’dzina la Atate wanga, ndipo simundilandira ine.’ (Yohane 5:43) Yesu analemekeza Atate wake, nadziŵikitsa dzina la Yehova kwa anthu amene Mulungu adampatsa, ndipo analidziŵikitsa bwino lomwe padziko lapansi.—Yohane 17:4, 6, 26.
Mwamphamvu yaumulungu, onse aŵiri Mose ndi Yesu anachita zozizwitsa zimene zinalemekeza Mulungu. Mose anachita zozizwitsa kutsimikizira kuti anatumidwa ndi Yehova Mulungu. (Eksodo 4:1-31) Kupyola m’ntchito yake yonse, Mose, yemwe anagwiritsiridwa ntchito ndi Mulungu kugaŵa Nyanja Yofiira, anapitiriza kuchita zozizwitsa zimene zinalemekeza Yehova. (Eksodo 5:1–12:36; 14:21-31; 16:11-18; 17:5-7; Salmo 78:12-54) Mofananamo, Yesu anadzetsa ulemerero kwa Mulungu mwakuchita zozizwitsa zambiri. Zinali zazikulu kwakuti Yesu anati: ‘Khulupirirani ine, kuti ine ndiri mwa Atate ndi Atate ali mwa ine; koma ngati si chomwecho, khulupirirani ine chifukwa cha ntchito zomwe.’ (Yohane 14:11) Pakati pa zozizwitsa zake panali chija chopangitsa namondwe wamphamvu kutonthola, kotero kuti Nyanja ya Galileya inakhala bata.—Marko 4:35-41; Luka 7:18-23.
Zofanana Zina Zofunika
Onse aŵiri Mose ndi Yesu anagwirizanitsidwa ndi kuperekedwa kwa chakudya kozizwitsa. Mose anali mneneri wa Yehova pamene chakudya chinaperekedwa mozizwitsa kwa Aisrayeli. (Eksodo 16:11-36) Mofananamo, pazochitika ziŵiri za cholembedwa cha Baibulo, Yesu anawadyetsa mozizwitsa makamu ndi chakudya chakuthupi.—Mateyu 14:14-21; 15:32-38.
Mana ochokera kumwamba anagwirizanitsidwa ndi utumiki wa onse aŵiri Mose ndi Yesu. Mose ankatsogolera Aisrayeli pamene anagaŵiridwa mana ochokera kumwamba, titero kunena kwake. (Eksodo 16:11-27; Numeri 11:4-9; Salmo 78:25) Mwanjira yoyerekezera koma yofunika koposa, Yesu anapereka thupi lake lenilenilo monga mana ochokera kumwamba kaamba ka moyo wa anthu omvera.—Yohane 6:48-51.
Onse aŵiri Mose ndi Yesu anatsogolera anthu kutuluka m’nsinga kuloŵa ufulu. Mose anagwiritsiridwa ntchito ndi Mulungu kutsogolera Aisrayeli kutuluka m’nsinga ya Aigupto ndi kuloŵa ufulu monga anthu Ake. (Eksodo 12:37-42) Mofananamo, Yesu Kristu wakhala akutsogolera otsatira ake kuloŵa ufulu. Kristu adzatsogoleranso anthu kuloŵa ufulu womasuka ku nsinga ya gulu la Satana Mdyerekezi, limodzinso ndi ya uchimo ndi imfa.—1 Akorinto 15:24-26; Akolose 1:13; 1 Yohane 5:19.
Onse aŵiri Mose ndi Yesu anachita unkhoswe wa mapangano. Mose anali nkhoswe ya pangano la Chilamulo, pakati pa Yehova Mulungu ndi Aisrayeli. (Eksodo 19:3-9) Yesu ndi Nkhoswe ya pangano latsopano, pakati pa Mulungu ndi Israyeli wauzimu.—Yeremiya 31:31-34; Luka 22:20; Ahebri 8:6-13.
Kuŵeruza kunapatsidwa kwa onse aŵiri Mose ndi Yesu Kristu. Mose anatumikira monga woweruza ndi wopereka malamulo kwa Israyeli wakuthupi. (Eksodo 18:13; Malaki 4:4) Yesu akutumikira monga Woweruza ndipo wapereka malamulo ake ndi ziweruzo kwa “Israyeli [wauzimu] wa Mulungu.” (Agalatiya 6:16; Yohane 15:10) Kristu iyemwini ananena kuti: ‘Atate saweruza munthu aliyense, koma anapereka kuweruza konse kwa Mwana; kuti onse akalemekeze Mwana, monga alemekeza Atate. Wosalemekeza Mwana salemekeza Atate amene anamtuma iye.’—Yohane 5:22, 23.
Onse aŵiri Mose ndi Yesu anaikiziridwa umutu wa pa nyumba ya Mulungu. Mose anali wokhulupirika monga mutu pa nyumba ya Mulungu mu Israyeli wakale. (Numeri 12:7) Moyerekezera, Yesu anapangidwa kukhala Mutu wa nyumba yauzimu ya ana a Yehova ndipo watsimikizira kukhala wokhulupirika pa iyo. Ndithudi, Yesu anakhala ‘wokhulupirika kwa Iye adamuikayo, monganso Mose m’nyumba yake yonse. Pakuti ameneyo wayesedwa woyenera ulemerero woposa Mose, monga momwe iye amene anaimanga nyumba ali nawo ulemerero woposa nyumbayi. . . . Mosetu anali wokhulupirika m’nyumba yake yonse, monga mnyamata, achitire umboni izi zidzalankhulidwazi; koma Kristu monga Mwana, wosunga nyumba Yake; ndife nyumba Yake, ngati tigwiritsa kulimbika mtima ndi kudzitamandira kwa chiyembekezocho, kuchigwira kufikira chitsiriziro.’—Ahebri 3:2-6.
Ngakhale ponena za imfa, Mose ndi Yesu anali ofanana. Motani? Eya, Yehova anachotsa thupi la Mose, motero kuchinjiriza anthu kaya kulichitira chitonzo kapena kulipanga fano. (Deuteronomo 34:5, 6; Yuda 9) Mofananamo, Mulungu anachotsa thupi la Yesu, kusalilola kuwona chivundi ndipo motero kulichinjiriza kukhala chokhumudwitsa ku chikhulupiriro.—Salmo 16:10; Machitidwe 2:29-31; 1 Akorinto 15:50.
Perekani Chisamaliro ku Ulosi
Izi ziri pakati pa njira zimene Yesu Kristu anatsimikizira kukhala mneneri wofanana ndi Mose. Ha, ndimodabwitsa chotani nanga mmene mawu a Mulungu kwa Mose onena za kubwera kwa mneneri ameneyo anakwaniritsidwira!
Palibe chikaikiro chirichonse kuti Yehova anakwaniritsa malonjezo ake aulosi akudzutsa mneneri wofanana ndi Mose. Mawu a Deuteronomo 18:18 anakwaniritsidwa m’moyo ndi zokumana nazo za Yesu Kristu. Ndipo kukwaniritsidwa koteroko kumatipatsa chifukwa chokhalira achidaliro m’mbali zina zaulosi za Mawu a Mulungu. Chifukwa chake, tiyeni tipereketu chisamaliro nthaŵi zonse ku ulosi wa Baibulo.