Sekemu Mzinda wa m’Chigwa
CHAPAKATIKATI pa dziko limene Mulungu anasankhira anthu ake, lochingidwa ndi mapiri a Ebali ndi Gerizimu, panali mzinda wa Sekemu. Kunali kuno—pafupifupi zaka zikwi zinayi zapitazo—kumene Yehova analonjeza Abrahamu kuti: “Ndidzapatsa mbewu yako dziko lino.”—Genesis 12:6, 7.
Mogwirizana ndi lonjezo limeneli, mdzukulu wa Abrahamu, Yakobo anamanga msasa pa Sekemu ndi kumanga guwa lansembe lomwe anatcha “Mulungu ndiye Mulungu wa Israyeli.” Mwinamwake Yakobo anakumba chitsime pamalo aŵa chomwapo banja lake ndi zifuyo zake, chitsime chimene zaka mazana ambiri chinatchedwa “chitsime cha Yakobo.”—Genesis 33:18-20 NW, mawu amtsinde; Yohane 4:5, 6, 12.
Komabe, si ziŵalo zonse za banja la Yakobo zimene zinasonyeza changu cha kulambira koona. Dina, mwana wake wamkazi, anakafuna mabwenzi pakati pa atsikana achikanani a m’Sekemu. Dina, yemwe panthaŵiyo anali wachicheperebe, anasiya chisungiko cha mahema a banja lake ndi kuyamba kumakacheza kumzinda wapafupiwo akumapeza mabwenzi kumeneko.
Kodi anyamata amumzinda anamuona bwanji namwali ameneyu yemwe anachezera mzinda wawo kaŵirikaŵiri—mwachionekere ali yekha? Mwana wa kalonga “anamuona iye . . . anamtenga nagona ndi iye, namuipitsa.” Kodi nchifukwa ninji Dina anadziloŵetsa m’ngozi mwa kugwirizana ndi Akanani achisembwere? Kodi kungakhale kwakuti anafuna kucheza ndi atsikana ausinkhu wake? Kodi anali wouma khosi ndi wodzigangira monga ena a alongo ake? Taŵerengani nkhani ya m’Genesis, ndi kuyesa kumvetsetsa nsautso ndi manyazi amene Yakobo ndi Leya anawamva chifukwa cha maulendo a mwana wawo okacheza ku Sekemu ndi zotulukapo zake zatsoka.—Genesis 34:1-31; 49:5-7; onaninso Nsanja ya Olonda, June 15, 1985, tsamba 31.
Pafupifupi zaka 300 pambuyo pake, zotulukapo zakunyalanyaza zitsogozo zateokrase zinaonekeranso poyera. Ku Sekemu, Yoswa analinganiza umodzi wa misonkhano yosaiŵalika m’mbiri ya Aisrayeli. Taonani m’maganizo mwanu chochitikachi m’chigwacho. Anthu oposa miliyoni imodzi—amuna, akazi, ndi ana—amafuko asanu ndi limodzi a Israyeli ataimirira pandunji pa phiri la Gerizimu. Patsidya la chigwacho pafupifupi chiŵerengero chofanana cha mafuko ena asanu ndi limodzi ataimirira pandunji pa phiri la Ebali.a Ndipo cha m’tsinde mwakemo, pambali pa likasa lachipangano ndi pakati pa makamu aŵiri a Aisrayeliwo, paimirira ansembe ndi Yoswa. Nchochitika chotani nanga!—Yoswa 8:30-33.
Mapiri aatali aŵiriwo pamwamba pa khamu lalikulu limeneli akusonyeza kusiyana kwakukulu pakati pa nthaka yokongola ndi youma. Kumtunda kwa Gerizimu kukuoneka nthaka yobiriŵira ndi yachonde, pamene ija ya Ebali njouma ndi yopanda kanthu. Kodi mukumva kunong’onezanako mmene Aisrayeli akudikira nthaŵi yoti Yoswa alankhule? Phokoso lililonse likumveka pamalo abata amenewo.
Maola anayi kapena asanu ndi limodzi amene Yoswa akuŵerenga ‘buku lachilamulo cha Mose,’ anthuwonso akutengamo mbali. (Yoswa 8:34, 35) Mwachionekere, Aisrayeli omwe ali pandunji pa Gerizimu akuti Amen! pambuyo pa dalitso lililonse, pamene kuli kwakuti Amen! wa aja ali pandunji pa Ebali akugogomezera themberero lililonse. Kapena maonekedwe ouma a phiri la Ebali akukumbutsa anthuwo za zotulukapo zatsoka za kusamvera.
“Wotembereredwa iye wakupeputsa atate wake kapena mayi wake,” Yoswa akuchenjeza choncho. Mogwirizana, mawu oposa miliyoni imodzi akuyankha: “Amen!” Yoswa akudikira kuti mfuu yaikulu ya kuyankhako iti zii asanapitirize: “Wotembereredwa iye wakusendeza malire a mnansi wake.” Kachiŵirinso mafuko asanu ndi limodziwo, pamodzi ndi alendo ambiri, akufuula kuti: “Amen!” (Deuteronomo 27:16, 17) Mukanakhalapo pamenepo, kodi mukanaiŵala msonkhanowo umene unachitikira pakati pamapiriwo? Kodi kufunika kwa kumvera sikukanakhomerezeka m’maganizo anu?
Ali pafupi kumwalira pambuyo pa zaka 20, kachiŵirinso Yoswa anausonkhanitsa pamodzi mtunduwo ku Sekemu kuti adzatsimikizire chosankha chawo. Anawapatsa chosankha chimene aliyense ayenera kupanga. “Mudzisankhire lero amene mudzamtumikira,” anatero. “Koma ine, ndi a m’nyumba yanga, tidzatumikira Yehova.” (Yoswa 24:1, 15) Mwachionekere, misonkhano yolimbikitsa chikhulupiriro imeneyi ku Sekemu inagwira mitima. Zaka zambiri pambuyo pa imfa ya Yoswa, Aisrayeli anatsanzira chitsanzo chake chokhulupirika.—Yoswa 24:31.
Zaka mazana 15 pambuyo pake pamene Yesu anali kupuma mumthunzi wa phiri la Gerizimu, makambitsirano osangalatsa mtima anachitika. Atatopa ndi ulendo wautali, Yesu anali khale pachitsime cha Yakobo pamene mkazi wachisamariya ali ndi mtsuko wamadzi anafika. Mkaziyo anadabwa kwambiri pamene Yesu anampempha madzi, pakuti Ayuda sankalankhula ndi Asamariya ngakhale kumwera madzi m’ziŵiya zawo. (Yohane 4:5-9) Mawu a Yesu otsatira anangowonjezera kudabwa kwake.
“Yense wakumwako madzi awa adzamvanso ludzu; koma iye wakumwa madzi amene Ine ndidzampatsa sadzamva ludzu nthaŵi zonse; koma madzi amene Ine ndidzampatsa adzakhala mwa iye kasupe wa madzi otumphukira ku moyo wosatha.” (Yohane 4:13, 14) Talingalirani mmene mkaziyo anakondera lonjezo limenelo, pakuti kudzatunga madzi m’chitsime ichi kunali ntchito yaikulu. Yesu anafotokozanso kuti ngakhale kuti Yerusalemu ndi phiri la Gerizimu anali malo otchuka m’mbiri, sanali malo olambirira ofunika pomfikira Mulungu. Chimene chinali nkanthu ndicho mkhalidwe wamtima ndi khalidwe, osati malo. “Olambira oona adzalambira Atate mumzimu ndi m’choonadi,” anatero. “Pakuti Atate afuna otere akhale olambira ake.” (Yohane 4:23) Mawu amenewo anali otonthoza bwanji nanga! Kachiŵirinso chigwa chimenechi chinakhala malo kumene anthu anali kulimbikitsidwa kutumikira Yehova.
Lero mzinda wa Nablus uli chapafupi ndi mabwinja a Sekemu wakale. Mapiri a Gerizimu ndi Ebali angotibe tolo m’chigwacho, monga mboni zaphee zoona ndi maso zochitika zamakedzana. Chitsime cha Yakobo, mmunsi mwa mapiriwo chingakaonedwebe. Pamene tisinkhasinkha zochitika zimene zinachitika kumeneko, timakumbutsidwa kufunika kwa kuchirikiza kulambira koona, monga mmene Yoswa ndi Yesu anatiphunzitsira.—Yerekezerani ndi Yesaya 2:2, 3.
[Mawu a M’munsi]
a Mafuko asanu ndi limodziwo pandunji pa phiri la Gerizimu ndiwo Simeoni, Levi, Yuda, Isakara, Yosefe, ndi Benjamini. Mafuko asanu ndi limodzi pandunji pa phiri la Ebali ndiwo Rubeni, Gadi, Aseri, Zebuloni, Dani, ndi Nafitali.—Deuteronomo 27:12, 13.
[Mawu a Chithunzi patsamba 31]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.