Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
◼ Kodi nchifukwa ninji Maliro 4:10 amalozera kwa amayi omwe anadya ana awo kukhala “akazi achisoni”?
Akulongosola mkhalidwe wosoŵa chochita wa Ayuda mkati mwa kuzingidwa kwa Chibabulo pa Yerusalemu mu 607 B.C.E., Yeremiya analemba kuti: “Manja a akazi achisoni anaphika ana awo awo; anali chakudya chawo poonongeka mwana wamkazi wa anthu a mtundu wanga.”—Maliro 4:10.
Mazana angapo kumbuyoko, Mose anali atachenjeza Aisrayeli kuti mtsogolo mwawo mukazindikiritsidwa ndi “dalitso” kapena “temberero.” Iwo akasangalala ndi madalitso ngati akasunga malamulo a Mulungu, koma akabweretsa kuvutika pa iwo eni ngati anakana njira zake zolungama. Chimodzi cha zotulukapo zowopsya chinali chakuti Aisrayeli akachepetsedwa ku kudya ana awo awo. (Deuteronomo 28:1, 11-15, 54, 55; 30:1; Levitiko 26:3-5, 29) Ichi m’chenicheni chinachitika pambuyo pakuti Yehova anakana mtundu wosakhulupirikawo, wosamvera kuupereka m’dzanja la Ababulo.
Pa Maliro 4:10 mneneri Yeremiya analozera pa nsonga yodziŵika bwino koposa yakuti mayi mwachibadwa amakhala wofewa mtima, wachisoni, ndi wotetezera kulinga kwa ana ake. (1 Mafumu 3:26, 27; 1 Atesalonika 2:7) Komabe, njala yomwe inali mu Yerusalemu wozingidwa inali yokulira kwenikweni ndipo kusoŵa chakudya kotulukapo kunali kokakamiza kotero kuti amayi omwe mwachibadwa akanakhala achisoni anaphika ndi kudya mbadwa zawo.—Yerekezani ndi Maliro 2:20.
Mkhalidwe wofananawo unachitika pambuyo pakuti Ayuda anakana Mesiya, yemwe anachenjeza za kudza kwa kuzingidwa kwa Yerusalemu. (Mateyu 23:37, 38; 24:15-19; Luka 21:20-24) Katswiri wa mbiri yakale Josephus analongosola chimodzi cha zowopsya za kuzingidwa kwa mu 70 C.E.: “Mary mwana wamkazi wa Eleazar . . . anapha mwana wake wamwamuna, kenaka kumuwotcha iye ndi kudya theka limodzi, kubisa ndi kusunga mbali yotsalayo.”—The Jewish War, lotembenuzidwa ndi G. A. Williamson, mutu 20, tsamba 319.
Zowonadi, kukana malamulo ndi njira za Mulungu siiri njira yanzeru.