Levitiko
26 “‘Musapange milungu yopanda pake,+ chifaniziro,+ kapena chipilala chopatulika kuti muzichilambira. Musaike mwala wogoba+ mʼdziko lanu kuti muziugwadira,+ chifukwa ine ndine Yehova Mulungu wanu. 2 Muzisunga masabata anga ndipo muzilemekeza* malo anga opatulika. Ine ndine Yehova.
3 Mukapitiriza kutsatira malangizo anga ndi kusunga malamulo anga,+ 4 ndidzakugwetserani mvula pa nthawi yake.+ Nthaka idzakupatsani chakudya,+ ndipo mitengo yamʼmunda idzakupatsani zipatso zake. 5 Mudzakhala mukupuntha zimene mwakolola mpaka kufika nyengo yokolola mphesa, ndipo mudzakhala mukukolola mphesa mpaka kufika nyengo yofesa mbewu. Mudzadya mkate wanu nʼkukhuta, ndipo mudzakhala otetezeka mʼdziko lanu.+ 6 Ndidzakupatsani mtendere mʼdzikolo,+ moti mudzagona pansi popanda wokuopsezani.+ Ndidzachotsa zilombo zoopsa zakutchire mʼdziko lanu, ndipo palibe amene adzachite nanu nkhondo. 7 Mudzathamangitsa adani anu ndi kuwagonjetsa ndi lupanga. 8 Anthu anu 5 adzathamangitsa adani 100, ndipo anthu 100 adzathamangitsa adani 10,000, moti mudzagonjetsa adani anu ndi lupanga.+
9 Ndidzakudalitsani,* kukuchititsani kuti mubereke ana ambiri komanso kukuchulukitsani.+ Ndipo ndidzasunga pangano langa ndi inu.+ 10 Pamene mukudya chakudya cha chaka chapita, mudzafunika kuchitulutsa kuti mupeze malo oikapo chatsopano. 11 Ine ndidzaika chihema changa pakati panu,+ ndipo sindidzakukanani. 12 Ine ndidzayenda pakati panu ndipo ndidzakhala Mulungu wanu,+ inuyo mudzakhala anthu anga.+ 13 Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakutulutsani mʼdziko la Iguputo kuti musakhale akapolo a Aiguputo. Ndinathyola goli lanu ndi kukuchititsani kuyenda mowongoka.*
14 Koma ngati simudzandimvera kapena kutsatira malamulo onsewa,+ 15 ndipo mukadzakana malangizo anga,+ nʼkunyansidwa ndi zigamulo zanga mpaka kukana kutsatira malamulo anga onse, nʼkufika pophwanya pangano langa,+ 16 ine ndidzakuchitani zotsatirazi: Ndidzakulangani pokupangitsani kukhala ndi mantha, kudwala chifuwa chachikulu ndi kutentha kwa thupi koopsa, zimene zidzachititsa maso anu khungu ndi kukufooketsani. Simudzapindula ndi mbewu zimene mwafesa, chifukwa adani anu adzadya zokolola zanuzo.+ 17 Ine ndidzakukanani, ndipo adani anu adzakugonjetsani+ ndi kukuponderezani,+ moti muzidzathawa popanda munthu wokuthamangitsani.+
18 Koma ngati simudzandimverabe pambuyo poona zinthu zimenezi, ndidzakulangani kuchulukitsa maulendo 7 kuposa poyamba chifukwa cha machimo anu. 19 Ndidzakuchititsani kuti musiye kunyada ndipo ndidzachititsa kumwamba kukhala ngati chitsulo+ ndi nthaka yanu ngati kopa.* 20 Mphamvu zanu zidzathera pachabe, chifukwa nthaka yanu siidzakupatsani chakudya,+ ndipo mitengo yamʼmunda mwanu siidzakupatsani zipatso.
21 Koma mukapitirizabe kuchita zosemphana ndi zofuna zanga, osafuna kundimvera, ndidzakulangani kuchulukitsa maulendo 7 mogwirizana ndi machimo anu. 22 Ndidzatumiza zilombo zakutchire pakati panu,+ ndipo zidzakupherani ana anu+ ndi ziweto zanu nʼkuchepetsa chiwerengero chanu, moti mʼmisewu yanu mudzakhala mopanda anthu.+
23 Ngati pambuyo pa zimenezi simudzasintha+ nʼkupitirizabe kuyenda motsutsana ndi ine, 24 inenso ndidzatsutsana nanu, ndipo ndidzakulangani maulendo 7 chifukwa cha machimo anu. 25 Ndidzabweretsa lupanga lobwezera chilango pa inu chifukwa chophwanya pangano.+ Mukadzathawira mʼmizinda yanu, ndidzabweretsa matenda pakati panu+ ndipo mudzaperekedwa mʼdzanja la mdani.+ 26 Ndikadzawononga njira* zanu zopezera chakudya,+ akazi 10 adzaphika mkate mu uvuni umodzi wokha, ndipo pokugawirani mkatewo, adzachita kukuyezerani+ nʼkukupatsani wochepa. Choncho mudzadya koma simudzakhuta.+
27 Koma ngati pambuyo pa zonsezi simudzandimvera, nʼkupitirizabe kuyenda motsutsana ndi ine, 28 inenso ndidzatsutsana nanu koopsa,+ ndipo ineyo ndidzakukwapulani maulendo 7 chifukwa cha machimo anu. 29 Choncho mudzadya ana anu aamuna ndi ana anu aakazi.+ 30 Ndidzawononga malo anu opatulika olambirirako+ ndipo ndidzagwetsa maguwa anu ofukizirapo zonunkhira. Ndidzaunjika mitembo yanu pamwamba pa mafano anu onyansa* opanda moyowo,+ ndipo ndidzachoka pakati panu monyansidwa.+ 31 Mizinda yanu ndidzaiwononga+ ndi lupanga ndipo malo anu opatulika adzakhala opanda anthu, komanso sindidzalandira nsembe zanu za kafungo kosangalatsa.* 32 Dziko lanu ndidzalisandutsa bwinja,+ ndipo adani anu amene azidzakhala mʼdzikolo adzaliyangʼanitsitsa modabwa.+ 33 Ine ndidzakubalalitsani pakati pa anthu a mitundu ina,+ ndipo ndidzakusololerani lupanga ndi kukuthamangitsani.+ Dziko lanu lidzakhala bwinja, ndipo mizinda yanu idzawonongedwa.+
34 Pa masiku onse amene dzikolo lidzakhale bwinja, lidzabweza masabata ake, inu muli mʼdziko la adani anu. Nthawi imeneyo, dziko lidzapuma* chifukwa likuyenera kubweza masabata ake.+ 35 Masiku onse amene dzikolo lidzakhale bwinja lidzakhala likupuma, chifukwa silinapume, pa nthawi imene munkayenera kusunga masabata anu mukukhala mʼdzikolo.
36 Ndidzaika mantha mʼmitima ya anthu amene adzapulumuke+ omwe akukhala mʼdziko la adani awo, moti adzathawa phokoso la tsamba louluka. Iwo adzathawa ngati munthu amene akuthawa lupanga, moti adzagwa popanda wowathamangitsa.+ 37 Iwo adzagwetsana okhaokha ngati anthu amene akuthawa lupanga, koma popanda munthu wowathamangitsa. Simudzatha nʼkomwe kulimbana ndi adani anu.+ 38 Ambiri mwa inu mudzafa mʼdziko la anthu a mitundu ina,+ ndipo dziko la adani anu lidzakumezani. 39 Anthu amene adzatsale pakati panu adzazunzika mʼmayiko a adani awo+ chifukwa cha zolakwa zanu. Iwo adzazunzika chifukwa cha zolakwa za makolo awo.+ 40 Kenako adzavomereza zolakwa zawo+ komanso kusakhulupirika ndi zolakwa za makolo awo. Ndipo adzavomereza kuti anachita zinthu mosakhulupirika poyenda motsutsana nane.+ 41 Atatero, inenso ndinayenda motsutsana nawo+ ndipo ndinawapititsa kudziko la adani awo.+
Izi zinachitika kuti mwina mitima yawo yosadulidwayo ingadzichepetse+ nʼkulipira chifukwa cha zolakwa zawo. 42 Choncho ndidzakumbukira pangano limene ndinachita ndi Yakobo,+ Isaki+ komanso Abulahamu.+ Ndidzakumbukiranso dzikolo. 43 Pa nthawi imene iwo anasiya kukhala mʼdzikomo, dzikolo linkabweza masabata ake+ ndipo linakhala bwinja iwowo kulibe. Iwo anapereka malipiro a zolakwa zawo, chifukwa anakana zigamulo zanga ndipo ananyansidwa ndi malamulo anga.+ 44 Koma ngakhale kuti padzachitika zonsezi, iwo akamadzakhala mʼdziko la adani awo, sindidzawakana mpaka kalekale+ kapena kunyansidwa nawo moti nʼkuwawonongeratu, zomwe zingaphwanye pangano langa+ ndi iwo, chifukwa ine ndine Yehova Mulungu wawo. 45 Ndipo kuti zinthu ziwayendere bwino ndidzakumbukira pangano limene ndinachita ndi makolo awo+ amene ndinawatulutsa mʼdziko la Iguputo, anthu a mitundu ina akuona.+ Ndidzachita zimenezi kuti ndiwasonyeze kuti ndine Mulungu wawo. Ine ndine Yehova.’”
46 Amenewa ndi malangizo, zigamulo komanso malamulo amene Yehova anakhazikitsa pakati pa iye ndi Aisiraeli mʼphiri la Sinai, kudzera mwa Mose.+