NKHANI YOPHUNZIRA 24
“Ndipatseni Mtima Wosagawanika Kuti Ndiope Dzina Lanu”
“Ndipatseni mtima wosagawanika kuti ndiope dzina lanu. Ndikukutamandani inu Yehova Mulungu wanga ndi mtima wanga wonse.”—SAL. 86:11, 12.
NYIMBO NA. 7 Yehova Ndiye Mphamvu Zathu
ZIMENE TIPHUNZIREa
1. Kodi kuopa Mulungu n’kutani? Ndipo n’chifukwa chiyani anthu amene amamukonda amafunikiranso kumuopa?
AKHRISTU amakonda Mulungu komanso kumuopa. Ena angadabwe kuti zingatheke bwanji kuopa munthu amene umam’konda. Koma kuopa kumeneku si mantha amene munthu amakhala nawo akamva kapena kuona chinthu chinachake choopsa. Munkhaniyi tikambirana za mantha apadera omwe munthu amakhala nawo chifukwa cholemekeza kwambiri Mulungu. Anthu amene amaopa Mulungu mwanjira imeneyi, safuna kukhumudwitsa Atate wawo wakumwamba poopa kusokoneza ubwenzi wawo ndi iye.—Sal. 111:10; Miy. 8:13.
2. Mogwirizana ndi pemphero la Mfumu Davide lopezeka pa Salimo 86:11, kodi tikambirana zinthu ziwiri ziti?
2 Werengani Salimo 86:11. Tikaganizira mawu a mulembali, tingathe kuona kuti Mfumu Davide inkadziwa kufunika koopa Mulungu. Tsopano tikambirana mmene tingagwiritsire ntchito zomwe Davide ananena m’pempheroli. Choyamba, tikambirana zifukwa zotichititsa kulemekeza kwambiri dzina la Mulungu. Chachiwiri, tikambirana mmene tingasonyezere kuti timalemekeza kwambiri dzina la Mulungu.
N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KULEMEKEZA KWAMBIRI DZINA LA MULUNGU?
3. Kodi n’chiyani chinathandiza Mose kuti azilemekeza kwambiri dzina la Mulungu?
3 Taganizirani mmene Mose anamvera ataona masomphenya osonyeza ulemerero wa Mulungu. Pa nthawiyi iye anabisala kuphanga lathanthwe. N’kutheka kuti palibe aliyense amene anaonapo zinthu zoopsa ngati zimenezi. Mose anamva mawu akuti: “Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wosakwiya msanga ndiponso wodzaza ndi kukoma mtima kosatha ndi choonadi. Wosungira mibadwo masauzande kukoma mtima kosatha, wokhululukira zolakwa ndi machimo.” (Eks. 33:17-23; 34:5-7) N’zosakayikitsa kuti mawuwa analankhulidwa ndi mngelo. N’kutheka kuti nthawi zonse Mose akangotchula za dzina la Yehova ankakumbukira zomwe zinachitika panthawiyi. N’zosadabwitsa kuti patapita nthawi Mose anachenjeza mtundu wa Isiraeli kuti “uziopa dzina laulemerero ndi lochititsa manthali.”—Deut. 28:58.
4. Kodi tiyenera kuganizira za makhalidwe ati kuti tizilemekeza kwambiri Yehova?
4 Tikamaganizira za dzina la Yehova, tingachitenso bwino kuganizira makhalidwe omwe ali nawo. Tiyenera kuganizira za makhalidwe ake monga mphamvu, nzeru, chilungamo komanso chikondi. Tikamaganizira za makhalidwewa komanso ena, zingatithandize kuti tizimulemekeza kwambiri.—Sal. 77:11-15.
5-6. (a) Kodi dzina la Mulungu limatanthauza chiyani? (b) Mogwirizana ndi Ekisodo 3:13, 14 komanso Yesaya 64:8, kodi Yehova amachititsa bwanji zinthu kuchitika?
5 Kodi tikudziwa zotani zokhudza tanthauzo la dzina la Mulungu? Akatswiri ambiri amanena kuti n’kutheka kuti dzina la Mulungu loti Yehova limatanthauza kuti “Amachititsa Zinthu Kuchitika.” Tanthauzo limeneli limatikumbutsa mfundo yoti palibe chimene chingalepheretse Yehova kuchita zimene akufuna. Kodi zimenezi zimatheka bwanji?
6 Yehova amachititsa zinthu kuchitika pokhala chilichonse chimene akufunikira, kuti akwaniritse cholinga chake. (Werengani Ekisodo 3:13, 14.) Nthawi zambiri timalimbikitsidwa kuti tiziganizira mfundo yochititsa chidwi imeneyi. Yehova angachititsenso atumiki ake opanda ungwiro kuti akhale chilichonse chimene akufunikira kuti amutumikire komanso kukwaniritsa cholinga chake. (Werengani Yesaya 64:8.) Mwa njira imeneyi, palibe chimene chingalepheretse Yehova kukwaniritsa zolinga zake.—Yes. 46:10, 11.
7. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tiziyamikira Atate wathu wakumwamba?
7 Kuganizira mozama zimene Yehova wachita komanso zimene watithandiza kuchita, kungatithandize kuti tiziyamikira kwambiri Atate wathu wakumwambayu. Mwachitsanzo, tikamaganizira za zinthu zodabwitsa zomwe analenga, timagoma kwambiri. (Sal. 8:3, 4) Komanso tikamaganizira zimene Yehova watithandiza kuchita kuti tikwaniritse cholinga chake, timayamba kumulemekeza kwambiri. Kunena zoona dzina la Yehova ndi lochititsa mantha. Tanthauzo lake limatiuza zonse zokhudza mmene Atate wathu alili, zonse zimene anachita komanso zonse zimene adzachite m’tsogolo.—Sal. 89:7, 8.
“NDIDZALENGEZA DZINA LA YEHOVA”
8. Mogwirizana ndi Deuteronomo 32:2, 3, kodi Yehova amafuna kuti atumiki ake azichita chiyani ndi dzina lake?
8 Aisiraeli atangotsala pang’ono kulowa m’Dziko Lolonjezedwa, Yehova anaphunzitsa Mose mawu anyimbo inayake. (Deut. 31:19) Ndiyeno Mose anafunika kuti aphunzitse anthu onse nyimboyo. (Werengani Deuteronomo 32:2, 3.) Tikamaganizira mawu a m’vesi 2 ndi 3, tikhoza kuona kuti Yehova safuna kuti dzina lake lisadziwike n’kumaoneka ngati lapadera kwambiri moti siliyenera n’komwe kutchulidwa. Iye amafuna kuti aliyense alidziwe. Zinali zosangalatsa kwambiri pamene Mose anaphunzitsa anthu za Yehova komanso dzina lake. Zimene anawaphunzitsazo zinawalimbikitsa komanso kuwatsitsimula ngati mmene mvula imathandizira zomera. Kodi tingatani kuti nafenso tiziphunzitsa mwanjira imeneyi?
9. Kodi tingathandize bwanji kuyeretsa dzina la Mulungu?
9 Tikamalalikira kunyumba ndi nyumba kapena m’malo opezeka anthu ambiri, tizigwiritsa ntchito Baibulo posonyeza anthu dzina lenileni la Mulungu loti Yehova. Tingawapatse mabuku athu, mavidiyo komanso zinthu zina za pawebusaiti yathu zimene zimalemekeza Yehova. Tiziyesetsanso kupeza mwayi wouza ena za Mulungu wathu komanso makhalidwe ake tikakhala kuntchito, kusukulu kapena paulendo. Tingawauze zokhudza zinthu zodabwitsa zimene Yehova adzatichitire m’tsogolo. Akamva zimenezi akhoza kudziwa kuti Yehova amatikonda kwambiri, ndipo mwina aka kakhoza kukhala koyamba kumva zimenezi. Tikamauza ena choonadi chokhudza Atate wathu wachikondi, timathandiza kuyeretsa dzina la Mulungu. Timawathandiza kudziwa kuti zinthu zimene anaphunzitsidwa zokhudza Yehova ndi zabodza. Mfundo za m’Baibulo zimene timawaphunzitsazi zimawalimbikitsa komanso kuwatsitsimula.—Yes. 65:13, 14.
10. Tikamaphunzitsa anthu Baibulo, n’chifukwa chiyani tiyenera kuchita zambiri osati kungowaphunzitsa malamulo a Mulungu?
10 Tikamaphunzitsa anthu Baibulo, tiziwathandiza kuti adziwe dzina la Yehova n’kumaligwiritsa ntchito. Komanso tifunika kuwathandiza kuti adziwe zimene dzinali limatanthauza. Koma kodi tingakwanitse kuchita zimenezi tikamangowaphunzitsa malamulo a Mulungu? Zimenezi zingathandizedi wophunzirayo kudziwa malamulo a Mulungu n’kumawaona kuti ndi abwino. Koma kodi angamamumvere chifukwa choti amamukonda? Tisaiwale kuti Hava ankadziwa lamulo la Mulungu, koma iye ndi Adamu sankakonda Mulungu yemwe anawapatsa lamulolo. (Gen. 3:1-6) Choncho tiyenera kuchita zambiri osati kungophunzitsa anthu zimene Mulungu amafuna.
11. Tikamaphunzitsa munthu malamulo a Mulungu, kodi tingamuthandize bwanji kuti ayambe kukonda Wopereka Malamuloyo?
11 Nthawi zonse malamulo a Yehova ndi abwino. (Sal. 119:97, 111, 112) Koma anthu amene timaphunzira nawo Baibulo sangawaone choncho ngati sitinawathandize kudziwa kuti Yehova anapereka malamulowo chifukwa choti amatikonda. Choncho tingachite bwino kuwafunsa kuti: “Kodi mukuganiza kuti n’chifukwa chiyani Mulungu amafuna kuti atumiki ake azichita zinazake kapena asamachite zinazake? Kodi zimenezi zikutiuza chiyani za iyeyo?” Tikamathandiza amene timaphunzira nawo kuganizira za Yehova ndi kuyamba kukonda kwambiri dzina lake, tingawafikedi pamtima. Iwo angayambe kukonda malamulo ake komanso Wopereka Malamuloyo. (Sal. 119:68) Ndipo adzakhala ndi chikhulupiriro cholimba komanso zidzawathandiza kuti adzapirire mayesero ovuta m’tsogolo.—1 Akor. 3:12-15.
“TIDZAYENDA M’DZINA LA YEHOVA”
12. Kodi nthawi ina Davide analephera bwanji kukhala ndi mtima wosagawanika, nanga panali zotsatirapo zotani?
12 Pa Salimo 86:11 pali mawu ofunika akuti “ndipatseni mtima wosagawanika.” Mfumu Davide ndi amene anauziridwa kulemba mawu amenewa. Iye ankadziwa bwino kuti n’zosavuta kukhala ndi mtima wogawanika. Pa nthawi ina ali padenga lanyumba yake, anaona mkazi wina dzina lake Batiseba akusamba. Mkaziyu anali wa mwiniwake. Ndiye kodi pa nthawiyi Davide anakhalabe ndi mtima wosagawanika? Iye ankadziwa lamulo la Yehova lakuti: “Usalakelake mkazi wa mnzako.” (Eks. 20:17) Koma n’zachidziwikire kuti iye anapitirizabe kuyang’anitsitsa mkaziyo. Apatu mtima wake unagawanika. Anafunika kusankha kusangalatsa Yehova kapena kupitirizabe kulakalaka mkaziyo. Ngakhale kuti kwa nthawi yaitali Davide ankaopa komanso kukonda Yehova, pa nthawiyi anangotsatira zofuna za mtima wake mpaka anachita zinthu zoipa kwambiri. Zimenezi zinanyozetsa dzina la Mulungu. Komanso anapweteketsa anthu a m’banja lake ndiponso anthu ena osalakwa.—2 Sam. 11:1-5, 14-17; 12:7-12.
13. Kodi tikudziwa bwanji kuti Davide anayambiranso kukhala ndi mtima wosagawanika?
13 Yehova anapereka chilango kwa Davide. Ndipo Davide anakhalanso pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. (2 Sam. 12:13; Sal. 51:2-4, 17) Davide sanaiwale mavuto omwe anakumana nawo atasiya kukhala ndi mtima wosagawanika. Kodi Yehova anamuthandizanso kuti akhale ndi mtima wosagawanika? Inde. Tikutero chifukwa Mawu a Yehova amanena za Davide kuti ‘anatumikira Yehova Mulungu wake ndi mtima wathunthu.’—1 Maf. 11:4; 15:3.
14. Kodi tiyenera kudzifunsa funso lotani, nanga n’chifukwa chiyani?
14 Chitsanzo cha Davide chomwe takambiranachi ndi cholimbikitsa komanso chotichenjeza. Zimene zinamuchitikirazi ndi chenjezo kwa atumiki a Mulungu masiku ano. Kaya tangoyamba kumene kutumikira Yehova kapena tamutumikira kwa zaka zambiri, tingachite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndimayesetsa kupewa mayesero a Satana amene angachititse kuti ndikhale ndi mtima wogawanika?’
15. Kodi kuopa Yehova kungatiteteze bwanji tikaona zithunzi zomwe zingatichititse kuganizira zinthu zolakwika?
15 Mwachitsanzo, kodi mumatani mukaona chithunzi pa TV kapena pa intaneti chimene chingakuchititseni kuyamba kuganizira zinthu zolakwika? Mwina zingakhale zosavuta kuganiza kuti sikuti chithunzicho kapena filimuyo ndi yolaula. Koma kodi mwina ingakhale njira ya Satana yofuna kukulepheretsani kukhala ndi mtima wosagawanika? (2 Akor. 2:11) Zimenezi tingaziyerekezere ndi nkhwangwa imene munthu amagwiritsira ntchito akafuna kuwaza nkhuni. Powazapo mbali yakuthwa yankhwangwayo ndi imene imalowa m’chikunicho. Ndiyeno mbali yakuthwayo ikamalowa, chikunicho chimawazika. Zithunzi ndi mafilimuwo zingakhale ngati mbali yakuthwa yankhwangwa. Zinthu zowoneka ngati zazing’ono komanso zabwinobwino, zikhoza kuchititsa munthu kuti achite tchimo lomwe lingamulepheretse kukhala ndi mtima wosagawanika komanso kumulepheretsa kukhala wokhulupirika kwa Yehova. Choncho tiyenera kupewa choipa chilichonse kulowa mumtima mwathu, kuti tipitirize kuopa Yehova ndi kukhala ndi mtima wosagawanika.
16. Tikakumana ndi mayesero, kodi tiyenera kudzifunsa mafunso ati?
16 Kuwonjezera pazithunzi zokopa, Satana amagwiritsanso ntchito zinthu zina pofuna kutiyesa kuti tichite zoipa. Ndiye kodi timatani zimenezi zikachitika? N’zosavuta kuganiza kuti zinthu zimenezi si zoipa kwenikweni. Mwachitsanzo, mwina tingaganize kuti: ‘Zinthuzi sizolakwika moti mpaka ndingachotsedwe nazo mumpingo.’ Kaganizidwe kameneka n’kolakwika kwambiri. Tingachite bwino kudzifunsa mafunso monga: ‘Kodi pamenepa Satana sakundiyesa kuti ndisiye kukhala ndi mtima wosagawanika? Ngati nditachita zinthu zoipazi, kodi sindinganyozetse dzina la Yehova? Kodi kuchita zimenezi kungandithandize kuti ndikhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova kapena ayi?’ Tiyenera kuganizira mafunso amenewa. Tizipempha Mulungu kuti atipatse nzeru zimene zingatithandize kuti tiyankhe mafunsowa moona mtima. (Yak. 1:5) Zimenezi zingatiteteze chifukwa zingatithandize kukana mayesero mwamphamvu ngati mmene Yesu anachitira. Paja iye nthawi ina ananena kuti: “Choka Satana!”—Mat. 4:10.
17. N’chifukwa chiyani kukhala ndi mtima wogawanika n’kosathandiza? Perekani chitsanzo.
17 Kukhala ndi mtima wogawanika n’kosathandiza. Tayerekezerani kuti pali timu inayake yomwe osewera ake sagwirizana. Osewera ena akungofuna kutchuka, ena safuna kutsatira malamulo komanso ena salemekeza mphunzitsi wawo. N’zokayikitsa kuti timu yotereyi ingapambane masewera. Mosiyana ndi zimenezi, timu yomwe osewera ake ndi ogwirizana ingapambane. Mtima wanu ungafanane ndi timu imene ingapambaneyi ngati zimene mumaganiza, kulakalaka komanso mmene mumamvera n’zogwirizana ndi kutumikira Yehova. Musaiwale kuti Satana amafuna mukhale ndi mtima wogawanika. Iye amafuna kuti zimene mumaganiza, kulakalaka komanso mmene mumamvera zizisemphana ndi mfundo za Yehova. Koma kuti muzitumikira Yehova, mumafunika kuti mukhale ndi mtima wosagawanika. (Mat. 22:36-38) Choncho musalole kuti Satana akuchititseni kukhala ndi mtima wogawanika.
18. Mogwirizana ndi Mika 4:5, kodi mwatsimikiza mtima kuchita chiyani?
18 Tizipemphera kwa Yehova ngati mmene anachitira Davide kuti: “Ndipatseni mtima wosagawanika kuti ndiope dzina lanu.” Ndiyeno tiziyesetsa mmene tingathere kuti tizichita zinthu mogwirizana ndi pemphero lathulo. Tsiku lililonse tiziyesetsa kuti zosankha zathu zonse zizisonyeza kuti timaopa dzina loyera la Yehova. Monga Mboni zake, tikamachita zimenezi tingathandize kuti ena azilemekeza dzina lake. (Miy. 27:11) Ndipotu tingalankhule ngati mneneri Mika yemwe ananena kuti: “Ife tidzayenda m’dzina la Yehova Mulungu wathu mpaka kalekale, inde mpaka muyaya.”—Mika 4:5.
NYIMBO NA. 41 Mulungu Imvani Pemphero Langa
a Munkhaniyi tikambirana mawu ena a m’pemphero la Mfumu Davide opezeka pa Salimo 86:11, 12. Kodi kuopa dzina la Yehova kumatanthauza chiyani? N’chifukwa chiyani tiyenera kuopa dzinali? Kodi kuopa Mulungu kungatiteteze bwanji tikamayesedwa kuti tichite zinthu zoipa?
b MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Mose anaphunzitsa anthu nyimbo yolemekeza Yehova.
c MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Hava analephera kukana maganizo olakwika. Mosiyana ndi zimenezi, ifeyo sitilola kuona zithunzi kapena mauthenga aliwonse amene angatichititse kulakalaka zoipa n’kunyozetsa dzina la Mulungu.