Pangani Manja Osatha a Yehova Kukhala chichirikizo Chanu
“Mulungu wamuyaya ndiye mokhalamo mwako, ndipo pansipo pali manja osatha.”—DEUTERONOMO 33:27, American Standard Version.
1, 2. Kodi nchifukwa ninji anthu a Yehova angakhale ndi chidaliro pa chichirikizo chake?
YEHOVA amasamalira anthu ake. Mwachitsanzo, m’mazunzo onse a Aisrayeli, “Iye anazunzidwa”! M’chikondi ndi chisoni, iye “anawaombola, nawabereka nawanyamula.” (Yesaya 63:7-9) Chotero ngati ndife okhulupirika kwa Mulungu, tikhoza kukhala achidaliro pa chichirikizo chake.
2 Mneneri Mose anati: “Mulungu wamuyaya ndiye mokhaliramo mwako; Ndi pansipo pali manja osatha.” (Deuteronomo 33:27) New World Translation imati: “Malo obisalamo ndiye Mulungu wakalekale, ndipo pansipo pali manja osatha ku nthaŵi yonse.” Koma kodi ndimotani mmene manja a Mulungu amachirikizira atumiki ake?
Nchifukwa Ninji Pali Zovuta Zambiri?
3. Kodi ndiliti pamene anthu omvera adzasangalala mokwanira ndi “ulemerero wa ufulu wa ana a Mulungu”?
3 Kutumikira Yehova sikumatichinjiriza ku mavuto ofala kwa anthu opanda ungwiro. Mtumiki wa Mulungu Yobu anati: ‘Munthu wobadwa ndi mkazi ngwa masiku owerengeka, nakhuta mavuto.’ (Yobu 14:1) Ponena za “masiku a zaka zathu,” wamasalmo anati: ‘Kukula kwawo kumati chivuto ndi chopanda pake.’ (Salmo 90:10) Moyo udzakhala choncho kufikira pamene ‘chilengedwe chidzamasulidwa ku ukapolo wa chivundi, ndi kuloŵa ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu.’ (Aroma 8:19-22) Chimenecho chidzachitika mkati mwa Ulamuliro Wazaka Chikwi wa Kristu. Pamaziko a nsembe yadipo ya Yesu, nzika za Ufumuwo zidzamasulidwa ku uchimo ndi imfa. Pofika kumapeto kwa Zaka Chikwi, Kristu ndi ansembe anzake okhalanso mafumu adzakhala atathandiza anthu omvera kuufikira ungwiro, ndipo maina a okhulupirika kwa Mulungu mkati mwa chiyeso chomalizira cha Satana ndi ziŵanda zake adzalembedwa kunthaŵi yonse ‘m’bukhu la moyo.’ (Chibvumbulutso 20:12-15) Ndiyeno iwo adzasangalala mokwanira ndi ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu.
4. Mmalo modandaula ndi mkhalidwe wa moyo, kodi tiyenera kuchitanji?
4 Pakali pano, mmalo modandaula ponena za mkhalidwe wathu wa moyo, tiyeni tidalire Yehova. (1 Samueli 12:22; Yuda 16) Tiyeni tikhalenso achiyamikiro kwa Mkulu Wansembe wathu, Yesu, kupyolera mwa amene tikhoza kumfikira Mulungu ‘kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo cha kutithandiza nthaŵi yakusoŵa.’ (Ahebri 4:14-16) Sitiyenera konse kukhala ngati Adamu. Kwenikweni, iye molakwa anaimba Yehova mlandu wakumpatsa mkazi woipa, mwakunena kuti: “Mkazi amene munandipatsa ine kuti akhale ndi ine, ameneyo anandipatsa ine za mtengo, ndipo ndinadya.” (Genesis 3:12) Mulungu amapatsa zinthu zabwino ndipo samabweretsa zovuta pa ife. (Mateyu 5:45; Yakobo 1:17) Kaŵirikaŵiri mavuto amakhala chotulukapo cha kusoŵa nzeru kwathu kapena zolakwa za winawake. Akhoza kutigweranso chifukwa ndife ochimwa ndipo timakhala m’dziko logona m’ulamuliro wa Satana. (Miyambo 19:3; 1 Yohane 5:19) Komabe, manja osatha a Yehova nthaŵi zonse amachirikiza atumiki ake okhulupirika amene amadalira mwapemphero pa iye ndipo mwaumwini amagwiritsira ntchito uphungu wa Mawu ake.—Salmo 37:5; 119:105.
Kuchirikizidwa m’Nthaŵi Yakudwala
5. Kodi ndichilimbikitso chotani chimene odwala angachipeze pa Salmo 41:1-3?
5 Kudwala kumapangitsa ambirife kupsinjika nthaŵi zina. Komabe, Davide anati: ‘Wodala iye amene asamalira wosauka: Tsiku la tsoka Yehova adzampulumutsa: Yehova adzamsunga, nadzamsunga ndi moyo, ndipo adzadalitsika pa dziko lapansi; ndipo musampereke ku chifuniro cha adani ake. Yehova adzamgwiriziza pa kama wodwalira; Podwala iye mukonza pogona pake.’—Salmo 41:1-3.
6, 7. Kodi ndimotani mmene Mulungu anathandizira Davide pamene anali pa kama wodwalira, ndipo kodi ndimotani mmene chimenechi chingalimbikitsire atumiki a Yehova lerolino?
6 Munthu wolingalira ena amathandiza osoŵa. “Tsiku la tsoka” likhoza kukhala chochitika chirichonse chatsoka kapena nyengo yaitali ya vuto limene limafooketsa munthu. Iye amadalira mwa Mulungu kumchinjiriza posakhoza iye, ndipo ena ‘adzamdalitsa pa dziko lapansi’ mwakubukitsa mbiri ya zochita zachifundo za Yehova kwa iye. Mulungu anamchirikiza Davide ‘pa kama wodwalira,’ mwinamwake mkati mwa nthaŵi yakupsinja pamene Abisalomu mwana wamwamuna wa Davide anafuna kulanda mpando wachifumu wa Israyeli.—2 Samueli 15:1-6.
7 Popeza kuti Davide anasonyeza kulingalira osauka, iye analingalira kuti Mulungu akamthandiza pamene akhala wopanda chochita m’kama wodwalira. (Salmo 18:24-26) Ngakhale kuti anali wodwala kowopsa, iye anali ndi chidaliro chakuti Mulungu ‘akakonza pogona iye,’ osati mwakuchotsa matendawo mozizwitsa, koma mwakumlimbitsa ndi malingaliro otonthoza. Kukakhala ngati kuti Yehova anali kusintha kama wake kuchoka ku wodwalira kukhala wochirira. Mofananamo, ngati tikudwala monga atumiki a Mulungu, manja osatha a Yehova adzatichirikiza.
Chitonthozo kwa Opsinjika
8. Kodi ndimotani mmene Mkristu wodwala wina anasonyezera chidaliro chake pa Mulungu?
8 Matenda angachititse kupsinjika kwamaganizo. Mkristu wodwala kwambiri amene nthaŵi zina amasoŵa nyonga ngakhale yoŵerengera akusimba kuti: “Ichi chimandipsinja maganizo kwambiri, ndimadzimva kukhala wopanda pake, ndipo ngakhale kugwetsa misozi.” Podziŵa kuti Satana akufuna kumfooketsa ndi malingaliro a kugwiritsidwa mwala, iye akulimbana, akudziŵa kuti ndi chithandizo cha Yehova sakhoza kulephera. (Yakobo 4:7) Mwamuna ameneyu ali chilimbikitso kwa ena amene amadziŵa kuti amadalira pa Mulungu. (Salmo 29:11) Ngakhale pamene akudwala m’chipatala, amawatumira foni odwala ndi ena kuwalimbikitsa mwauzimu. Iye mwiniwake amalimbikitsidwa mwakumvetsera ku nyimbo za Ufumu ndi nkhani za m’magazini ano ndi magazini anzake a Galamukani! zojambulidwa pakaseti ndi mwakuyanjana ndi Akristu anzake. Mbaleyu amanena kuti: “Ndimalankhula kwa Yehova nthaŵi zonse m’pemphero, kumpempha kundipatsa nyonga, chitsogozo, chitonthozo, ndi chithandizo kuti ndipirire.” Ngati ndinu Mkristu wokhala ndi mavuto owopsa athanzi, dalirani Yehova nthaŵi zonse ndipo pangani dzina lake losatha kukhala chichirikizo chanu.
9. Kodi ndi zitsanzo zotani zimene zimasonyeza kuti anthu opembedza nthaŵi zina amavutika ndi kupsinjika kwamaganizo?
9 Kupsinjika kuli vuto lakalekale. Pamene anali pansi pachiyeso, Yobu analankhula monga munthu wosiidwa ndi Mulungu. (Yobu 29:2-5) Nkhaŵa ya mzinda wa Yerusalemu wosakazidwa ndi malinga ake inapangitsa Nehemiya kukhala wachisoni, ndipo Petro anapsinjika kwambiri chifukwa chokana Kristu kwakuti analira moŵaŵidwa mtima. (Nehemiya 2:1-8; Luka 22:62) Epafrodito anapsinjika chifukwa chakuti Akristu ku Filipi anamva kuti iye anadwala. (Afilipi 2:25, 26) Kupsinjika kunakantha Akristu ena mu Tesalonika, popeza kuti Paulo anafulumiza abalewo ‘kulimbikitsa amantha mtima.’ (1 Atesalonika 5:14) Chotero kodi ndimotani mmene Mulungu amathandizira anthu oterowo?
10. Kodi nchiyani chimene chingakhale chothandiza m’kuyesa kulaka kupsinjika kwamaganizo?
10 Payenera kukhala chosankha chaumwini ponena za kuchiritsa kwaukatswiri kwa kupsinjika kwakukulu.a (Agalatiya 6:5) Kupumula kokwanira ndi ntchito yolinganizika zingathandize. Mmalo mwakuwona mavuto angapo monga chitsoka chimodzi chachikulu, munthu wopsinjika angakupeze kukhala kothandiza kugwirira ntchito pa kuwathetsa limodzi panthaŵi imodzi. Chithandizo chotonthoza chochokera kwa akulu mumpingo chingakhale chopindulitsa, makamaka ngati vuto lamalingaliro limeneli likuchititsa nkhaŵa yauzimu. (Yakobo 5:13-15) Pamwamba pa zonse, kuli kofunika kudalira pa Yehova, ‘kutaya nkhaŵa zathu zonse pa iye, pakuti iye amatisamala.’ Pemphero loumirira ndi la mtima wonse likhoza kupatsa munthu ‘mtendere wa Mulungu umene udzasunga mtima ndi maganizo mwa Kristu Yesu.’—1 Petro 5:6-11; Afilipi 4:6, 7.
Yehova Amatithandiza Kupirira Chisoni
11-13. Kodi nchiyani chimene chingatithandize kuthetsa chisoni chathu cha imfa ya wokondedwa?
11 Chokumana nacho china chosautsa maganizo ndicho imfa ya wokondedwa. Abrahamu analira imfa ya mkazi wake, Sara. (Genesis 23:2) Pamene mwana wake Abisalomu anafa, Davide anakanthidwa ndi chisoni. (2 Samueli 18:33) Eya, ngakhale munthu wangwiro Yesu “analira” pa imfa ya bwenzi lake Lazaro! (Yohane 11:35) Chotero pamakhala chisoni pamene imfa itenga wokondedwa. Koma kodi nchiyani chimene chingathandize kuthetsa chisoni choterocho?
12 Mulungu amathandiza anthu ake kupirira chisoni chachikulu cha kuferedwa. Mawu ake amanena kuti padzakhala chiukiriro. Chifukwa chake, sitimalira ‘monganso otsalawo, amene alibe chiyembekezo.’ (1 Atesalonika 4:13; Machitidwe 24:15) Mzimu wa Yehova umatithandiza kukhala ndi mtendere ndi chikhulupiriro ndi kusinkhasinkha ponena za mtsogolo mwabwino koposa molonjezedwa m’Mawu ake, kotero kuti sitikugonjetsedwa kotheratu ndi malingaliro achisoni a wokondedwa wakufayo. Chitonthozo chimachokeranso m’kuŵerenga Malemba ndi kupemphera kwa ‘Mulungu wa chitonthozo chonse.’—2 Akorinto 1:3, 4; Salmo 68:4-6.
13 Tikhoza kupeza chitonthozo m’chiyembekezo cha chiukiriro monga momwe anachitira Yobu wopembedza, yemwe analengeza kuti: ‘Ha! mukadandibisa kumanda [Yehova], Mukadandisunga m’tseri, mpaka wapita mkwiyo wanu. Mukadandiikira nthaŵi, ndi kundikumbukira. Atafa munthu, adzakhalanso ndi moyo kodi? Ndikadayembekeza masiku onse a nkhondo yanga, mpaka kwafika kusandulika kwanga. Mukadaitana, ndipo ndikadakuyankhani; Mukadakhumba ntchito ya manja anu.’ (Yobu 14:13-15) Sipamakhala chisoni chachikulu nthaŵi zonse pamene bwenzi lokondedwa lipita paulendo, popeza kuti timayembekezera kuliwonanso. Chisoni chachikulu cha kutaikiridwa wokondedwa chingachepetsedwe ngati tilingalira imfa ya Mkristu wokhulupirika mwanjira yofananayo. Ngati iye anali ndi chiyembekezo cha padziko lapansi, adzaukitsidwa ku tulo ta imfa pano pa dziko lapansi mkati mwa Ulamuliro Wazaka Chikwi wa Kristu. (Yohane 5:28, 29; Chibvumbulutso 20:11-13) Ndipo ngati tikuyembekezera kukhala padziko lapansi kosatha, tingadzakhalepo kudzalandira okondedwa athu oukitsidwa.
14. Kodi ndimotani mmene akazi amasiye Achikristu aŵiri analakira imfa ya amuna awo?
14 Pambuyo pa imfa ya mwamuna wake, mlongo wina anadziŵa kuti anafunikira kupitiriza ndi moyo muutumiki wa Mulungu. Pambali pokhala ‘wakuchuluka m’ntchito ya Ambuye,’ iye anasoka nsalu yazigambazigamba yokhala ndi zidutswa 800. (1 Akorinto 15:58) “Imeneyi inali projekiti yabwino,” iye anatero, “chifukwa chakuti nthaŵi zonse pamene ndinkasoka ndinali kumvetsera ku nyimbo za Ufumu ndi matepi a Baibulo, amene anatangwanitsa maganizo anga.” Iye amakonda kukumbukira nthaŵi imene mkulu wofikapo anamchezera ndi mkazi wake. Kuchokera m’Baibulo, mkuluyo anasonyeza kuti Mulungu amasamaladi akazi amasiye. (Yakobo 1:27) Mkazi wina Wachikristu sanalefuke mwakudzimverera chisoni pamene mwamuna wake anamwalira. Iye anayamikira chichirikizo cha mabwenzi ndipo anakhala ndi chikondwerero chachikulu mwa ena. “Ndinapemphera kaŵirikaŵiri ndi kukulitsa unansi wathithithi ndi Yehova,” iye anatero. Ndipo ndidalitso lotani nanga kukhala ndi chichirikizo cha manja osatha a Mulungu!
Chithandizo Pamene Tilakwa
15. Kodi ndimfundo yaikulu yotani yokhala m’mawu a Davide pa Salmo 19:7-13?
15 Ngakhale kuti timakonda lamulo la Yehova, nthaŵi zina timalakwa. Mosakaikira chimenechi chimatipsinja, monga momwe Davide anachitira, amene anawona malamulo a Mulungu, zikumbutso, zitsogozo, ndi ziweruzo kukhala zokhumbirika kuposa golidi. Iye anati: ‘Kapolo wanu achenjezedwa nazo: M’kuzisunga izo muli mphotho yaikulu. Adziŵitsa zolowereza zake ndani? Mundimasule kwa zolakwa zobisika. Ndiponso muletse kapolo wanu pa zodzitama; zisachite ufumu pa ine: pamenepo ndidzakhala wangwiro, ndi wosachimwa cholakwa chachikulu.’ (Salmo 19:7-13) Tiyeni tiwapende mawuŵa.
16. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kupeŵa kudzitama?
16 Machitidwe odzitama ali machimo owopsa koposa zophophonya. Sauli anakanidwa monga mfumu chifukwa chopereka nsembe modzitama ndi chifukwa cha kupulumutsa Agagi, mfumu ya Amaleki ndi zofunkha, ngakhale kuti Mulungu analamula kuti Amaleki aperekedwe ku chiwonongeko. (1 Samueli 13:8-14; 15:8-19) Mfumu Uziya anakanthidwa ndi khate chifukwa chakudzitengera mathayo a ansembe modzitama. (2 Mbiri 26:16-21) Pamene likasa la chipangano linkaperekedwa ku Yerusalemu ndipo ng’ombe zokoka garetalo zinatsala pang’ono kuligubudula, Mulungu anakantha Uza nafa chifukwa chopanda mantha ndi kugwira Likasalo kuti alichirikize. (2 Samueli 6:6, 7) Chotero, ngati sitidziŵa chochita kapena ngati taloledwa kuchita chinachake, tiyenera kusonyeza kudekha ndi kufunsa odziŵa. (Miyambo 11:2; 13:10) Ndithudi, ngati tinakhalapo odzitama, tiyenera kupempherera chikhululukiro ndi kupempha Mulungu kutithandiza kuchenjera ndi kudzitama mtsogolo.
17. Kodi kubisa machimo kungamyambukire motani munthu, komabe kodi ndimotani mmene angapezere chikhululukiro ndi mpumulo?
17 Machimo obisidwa angachititse kupsinjika. Malinga ndi Salmo 32:1-5, Davide anayesa kubisa tchimo lake, koma anati: ‘Pamene ndinakhala chete mafupa anga anakalamba ndi kubuula kwanga tsiku lonse. Chifukwa usana ndi usiku dzanja lanu linandilemera ine; Uwisi wanga unasandulika kuuma kwa malimwe.’ Kuyesa kudidikiza chikumbumtima cha liŵongo kunamtopetsa Davide, ndipo kuvutika mtima kunamfooketsa monga momwe mtengo umataira chinyontho choupatsa moyo m’nthaŵi ya chilala kapena m’kutentha kwa chirimwe. Mwachiwonekere iye anavutika ndi ziyambukiro zamaganizo ndi zakuthupi ndipo anataya chimwemwe chifukwa cha kulephera kuulula. Kuululira Mulungu ndiko kokha kukabweretsa chikhululukiro ndi mpumulo. Davide anati: ‘Wodala munthuyo wokhululukidwa chimo lake; Wokwiriridwa choipa chake. . . . Ndinavomera choipa changa kwa inu; ndipo mphulupulu yanga sindinaibisa. Ndinati, Ndidzaululira Yehova machimo anga; ndipo munakhululukira choipa cha kulakwa kwanga.’ Chithandizo chachikondi chochokera kwa akulu Achikristu chikhoza kutithandiza kuchira mwauzimu.—Miyambo 28:13; Yakobo 5:13-20.
18. Kodi pali umboni wotani wakuti tchimo likhoza kukhala ndi ziyambukiro zokhalitsa, komabe kodi nchiyani chingabweretse chitonthozo m’mikhalidwe yoteroyo?
18 Tchimo lingakhale ndi ziyambukiro zokhalitsa. Linatero kwa Davide, yemwe anachita chigololo ndi Bateseba, kuchititsa imfa ya mwamuna wake, ndi kukwatira mkazi wamasiye wokhala ndi pathupiyo. (2 Samueli 11:1-27) Ngakhale kuti Mulungu anasonyeza chifundo chifukwa cha pangano la Ufumu, kulapa kwa Davide, ndi kuchitira ena mwachifundo, Davide anawona ‘choipa chotulutsidwa m’nyumba yake.’ (2 Samueli 12:1-12) Mwana wobadwa m’chigololoyo anamwalira. Amoni, mwana wamwamuna wa Davide, anagwirira chigololo Tamara, mchemwali wake wopeza ndipo anaphedwa molamulidwa ndi Abisalomu, mchimwene wake. (2 Samueli 12:15-23; 13:1-33) Abisalomu anachititsa manyazi Davide pamene anagonana ndi akazi aang’ono a Davide. Iye anayesa kulanda mpando wachifumu koma anaphedwa. (2 Samueli 15:1–18:33) Tchimo limakhalabe ndi zotulukapo. Mwachitsanzo, wochimwa wochotsedwa angalape ndi kubwezeredwa mumpingo, koma kungatenge zaka zambiri kuti alake vuto la malingaliro la mbiri yake yoipitsidwa ndi tchimolo. Pakali pano, nkotonthoza chotani nanga kukhululukidwa ndi Yehova ndi kukhala ndi chichirikizo chake cha manja ake osatha!
Kuwonjoledwa ku Zipsinjo Zotigwera
19. Kodi ndimotani mmene mzimu wa Mulungu ungakhalire wothandiza pamene tikuyang’anizana ndi ziyeso zowopsa?
19 Pamene tiyesedwa mowopsa, tingasoŵe nzeru yokwanira ndi nyonga kuti tipange chosankha ndi kuchichita. M’chochitika choterocho, mzimu wa Mulungu ‘uthandiza kufooka kwathu; pakuti chimene tizipempha monga chiyenera, sitidziŵa; koma mzimuwo utipempherera ndi zobuula zosatheka kuneneka.’ (Aroma 8:26) Ngati Yehova abweretsa kusintha kwa mikhalidwe, tiyenera kukhala oyamikira. Komabe, dzanja lake lingatithandize mwa njira ina. Ngati tipempherera nzeru, Yehova angatisonyeze mwa mzimu wake chimene tiyenera kuchita ndi kutipatsa nyonga yofunikira kuchichita. (Yakobo 1:5-8) Ndi chithandizo chake, tikhoza kupirira pamene ‘tichita chisoni ndi mayesero a mitundu mitundu’ ndi kutulukamo ndi chikhulupiriro choyesedwa ndi cholimbitsidwa.—1 Petro 1:6-8.
20. Kodi tidzasangalala ndi chiyani ngati tipangadi manja osatha a Yehova kukhala chichirikizo chathu?
20 Tiyeni tisatope konse kutembenukira kwa Mulungu m’pemphero. ‘Maso anga alinga kwa Yehova kosaleka; pakuti iye adzawonjola mapazi anga muukonde,’ anatero Davide. ‘Cheukirani ine ndipo ndichitireni chifundo; pakuti ndiri wosungulumwa ndi wozunzika. Masautso a mtima wanga akula: Munditulutse m’zondipsinja. Penyani mazunzo anga ndi zovuta zanga; ndipo khululukirani zolakwa zanga zonse.’ (Salmo 25:15-18) Mofanana ndi Davide, tidzasangalala ndi chimasuko, chiyanjo, ndi chikhululukiro zaumulungu ngati tipangadi manja osatha a Yehova kukhala chichirikizo chathu.
[Mawu a M’munsi]
a Onani nkhani pa kupsinjika maganizo mu Awake! ya October 22, 1987, masamba 2-16, ndi November 8, 1987, masamba 12-16.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi ndimotani mmene Yehova amathandizira atumiki ake odwala?
◻ Kodi nchiyani chimene chingakhale chothandiza pamene tikuyesa kulaka kupsinjika kwamaganizo?
◻ Kodi nchiyani chimene chingathandize kuthetsa chisoni cha imfa ya wokondedwa?
◻ Kodi amene amabisa machimo awo angapeze motani mpumulo?
◻ Kodi pamakhala chithandizo chotani pamene anthu a Yehova akuyesedwa mowopsa?
[Chithunzi pamasamba 16, 17]
Tikhoza kupeza chitonthozo m’chiyembekezo cha chiukiriro, monga momwe anachitira Yobu wopembedzayo