Makolo Khalani Chitsanzo Chabwino kwa Ana Anu
“NDI BWINO kuti tsopano, patatha zaka zambirimbiri, akatswiri a zamaganizo asiye kuvutika kufunafuna chinsinsi cholelera bwino ana. Osati chifukwa choti achipeza kale, koma chifukwa choti palibe chinsinsi choterechi.” Inatero nkhani ina ya m’magazini ya Time yofotokoza za maleredwe a ana. Nkhaniyo inati ana amatengera kwambiri zochita za anzawo, osati za makolo awo.
Sitingatsutse kuti ana amatengera kwambiri zochita za anzawo. (Miyambo 13:20; 1 Akorinto 15:33) William Brown, yemwe amalemba nkhani m’nyuzipepala inayake, anati: “Ngati pali chinthu chimene chili chofunika kwambiri kwa achinyamata onse, ndiye kuti chinthu chake ndicho kufuna kukhala wofanana ndi anzako. . . . Achinyamata amaopa kukhala osiyana ndi anzawo koposa mmene amaopera imfa imene.” Chifukwa cha moyo wopanikiza wa masiku anowu, makolo ena sakhala ndi ana awo kwa nthawi yokwanira ndipo amachititsa kuti moyo wapakhomo ukhale wosasangalatsa, motero ana awo amangotengera zochita za anzawo.
Kuphatikizanso apo, “masiku otsiriza” ano, mabanja ali pavuto chifukwa, monga Baibulo linaneneratu, anthu akuganizira kwambiri za ndalama, zosangalatsa, ndi za zofuna zawo basi. Motero sitiyenera kudabwa kuona ana ali “osamvera akuwabala, osayamika, osayera mtima, opanda chikondi chachibadwidwe.”—2 Timoteo 3:1-3.
Mawu akuti “chikondi chachibadwidwe,” m’Baibulo amatanthauza chikondi chimene munthu umakhala nacho pa anthu a m’banja lako. Ichi n’chikondi chachibadwa chimene chimachititsa kuti makolo azisamalira ana ndiponso kuti ana azikonda kwambiri makolo awo. Koma makolo akasoweka chikondi choterechi, ana amapita kwa anthu ena kuti aziwakonda m’njira yotereyi, ndipo nthawi zambiri anthuwo amakhala anzawo. Motero anawo amatengera zochita za anzawozo. Koma zimenezi zingapewedwe ngati makolo atalola mfundo za m’Baibulo kuyendetsa moyo wawo wabanja.—Miyambo 3:5, 6.
Mulungu Ndiye Anayambitsa Banja
Atamangitsa banja la Adamu ndi Hava, Mulungu anawauza lamulo ili: “Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi.” Apa m’pamene panabwerera banja, lomwe limakhala ndi bambo, mayi, ndi ana. (Genesis 1:28; 5:3, 4; Aefeso 3:14, 15) Pofuna kuthandiza anthu kulera ana awo, Yehova anapanga anthu ndi chibadwa choti azitha kulera ana. Koma mosiyana ndi zinyama, anthu amafunikira thandizo linanso, motero Yehova anawalembera malangizo. M’malangizowo muli mfundo zokhudza makhalidwe abwino ndiponso moyo wauzimu komanso muli mfundo zokhudza kalangidwe kabwino ka ana.—Miyambo 4:1-4.
Polangiza makamaka atate, Yehova anati: “Mawu awa ndikuuzani lero, azikhala pamtima panu; ndipo muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala pansi m’nyumba zanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pouka inu.” (Deuteronomo 6:6, 7; Miyambo 1:8, 9) Onani kuti malangizowa akusonyeza kuti makolo anayenera kuyamba ndi iwowo kuika lamulo la Mulungu mumtima mwawo. N’chifukwa chiyani izi zinali zofunika? Chifukwa choti maphunziro amene amakhudzadi mtima wa ena si maphunziro ongonena pakamwa ayi koma ndi ochokera pansi pamtima. Makolo angawaphunzitse ana awo mowafika pamtima pokhapokha ngati makolowo akuphunzitsa mochoka pansi pamtima. Makolo otere amakhalanso zitsanzo zabwino kwambiri kwa ana awo, chifukwatu ana amaona msanga ngati makolo akuchita zinthu mwachiphamaso.—Aroma 2:21.
Makolo achikristu amauzidwa kuti aziphunzitsa ana awo kuyambira ali makanda “m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.” (Aefeso 6:4; 2 Timoteo 3:15) Kodi n’zoona kuti azitero kuyambira ali makanda? Inde! Mayi wina analemba kuti: “Nthawi zina makolofe timaderera zimene ana athu angachite. Komatu ana angathe kuchita zinthu zambiri. Makolofe tiyenera kugwiritsa ntchito bwino luso la ana athuwa.” Inde, ana amakonda kuphunzira zinthu, ndipo akamaphunzitsidwa ndi makolo okonda Mulungu, angaphunzirenso kukhala achikondi. Ana otere amaona kuti ndi otetezeka ndi malamulo a makolo awo owaletsa kuchita zinazake. Motero, makolo olera bwino ana awo amayesetsa kukondana ndi ana awowo, kulankhulana nawo bwino, ndiponso kukhala aphunzitsi oleza mtima koma osalekerera. Zimenezi zimathandiza anawo kuti akule bwino.a
Tetezani Ana Anu
Poda nkhawa, hedimasitala wina ku Germany analembera makolo kalata n’kunena kuti: “Tikufuna kukulimbikitsani makolo kuti ndi ntchito yanu kulera ana anu kukhala anthu olongosoka. Musaisiyire TV kapena anzawo kuti ndiwo achite ntchitoyi, chifukwa choti inuyo ndi amene kwenikweni muli ndi [udindo] umenewu.”
Kusiya ana kuti aleredwe ndi TV kapena anzawo, kwenikweni n’kulola kuti mzimu wa dziko uwalowerere. (Aefeso 2:1, 2) Mzimu wa dziko umatsutsana ndi mzimu wa Mulungu, ndipo monga mphepo yamphamvu, umatenga maganizo ‘adziko achibadwidwe a ziwanda’ n’kuwadzaza m’mutu ndi mu mtima wa anthu osadziwa zambiri pamoyo kapena opusa. (Yakobo 3:15) Pamapeto pake maganizo amenewa, omwe ali owononga ngati tchire lomera m’munda, amawononga mtima. Yesu anapereka fanizo la mmene zinthu zodzalidwa mumtima zimakhudzira munthu ponena kuti: “Munthu wabwino atulutsa zabwino m’chuma chokoma cha mtima wake; ndi munthu woipa atulutsa zoipa m’choipa chake: pakuti m’kamwa mwake mungolankhula mwa kuchuluka kwa mtima wake.” (Luka 6:45) Motero, Baibulo limatilimbikitsa kuti: “Chinjiriza mtima wako koposa zonse uzisunga; pakuti magwero a moyo atulukamo.”—Miyambo 4:23.
Inde, ana ndi ana basi, ndipo ena n’ngosamva ndipo mwinanso amatha kulowerera. (Genesis 8:21) Kodi makolo angatani? Baibulo limati: “Utsiru umangidwa mumtima mwa mwana; koma ntyole yom’langira idzauingitsira kutali.” (Miyambo 22:15) Anthu ena amaona kuti kulanga mwana m’njira imeneyi ndi nkhanza ndipo kuti n’kwachikale. N’zoona kuti Baibulo limadana ndi zachiwawa ndiponso kuzunza munthu m’njira ina iliyonse. Komano nthawi zina mawu akuti “ntyole” amatanthauza udindo umene makolo ali nawo womwe amaugwiritsa ntchito mosalekerera koma mwachikondi komanso moyenerera pofuna kuti ana awo adzakhale ndi moyo wosatha.—Ahebri 12:7-11.
Sangalalani Limodzi ndi Ana Anu
Aliyense amadziwa kuti ana amakula bwino ngati akusewera ndi kuchita zosangalatsa. Makolo anzeru amayesetsa kuti azigwirizana kwambiri ndi ana awo pochita nawo zinthu zosangalatsa nthawi iliyonse imene angakwanitse kutero. Motero, makolowo amatha kuwathandiza anawo kusankha bwino zosangalatsa komanso amawasonyeza kuti amasangalala kwambiri kucheza nawo.
Bambo wina wa Mboni anati nthawi zambiri akaweruka kuntchito ankasewera mpira ndi mwana wake. Mayi wina amakumbukira kuti ana ake ankakonda masewera monga tchesi ndi dilafuti. Munthu wina amakumbukira kuti iye adakali kamtsikana kakang’ono anthu a m’banja mwawo ankakonda kukwerera njinga pamodzi. Ana onse tawatchulawa panopo anakulakula, koma amakondabe kwambiri makolo awo ndiponso Yehova.
Ndithu, makolo amene m’zonena zawo ndiponso zochita zawo amasonyeza kuti amakonda ana awo ndi kuti amasangalala akakhala nawo, amakhudza mtima kwambiri anawo kwa moyo wawo wonse. Mwachitsanzo, anthu ambiri omaliza maphunziro a Sukulu ya Gileadi Yophunzitsa Baibulo analongosola kuti anayamba kufuna utumiki wa nthawi zonse chifukwa cha chitsanzo ndiponso chilimbikitso cha makolo awo. Ichitu ndi cholowa chosangalatsa kwambiri kwa anawo ndiponso ndi dalitso lalikulu kwa makolowo. N’zoona kuti si kuti ana onse angathe kulowa utumiki wa nthawi zonse akakula, komabe ana angapindule kwambiri potsanzira ndi kulemekeza makolo oopa Mulungu ndipo izi zingatheke ngati makolo akugwirizana kwambiri ndi ana awo.—Miyambo 22:6; Aefeso 6:2, 3.
Makolo Olera Okha Ana Angachite Bwino
Masiku ano, ana ambiri amakula ndi mayi kapena bambo wawo yekha basi. Zimenezi zimawonjezera vuto lolera ana, komabe n’zotheka kulera anawo bwinobwino. Makolo olera okha ana angakhazike mtima pansi poganizira chitsanzo cha m’Baibulo za anthu monga Yunike, Mkristu wachiyuda wa m’nthawi ya atumwi. Iyeyu anakwatiwa ndi munthu wosakhulupirira moti n’zoonekeratu kuti mwamuna wake sankamuthandiza mkaziyu. Komabe, mayiyu anaphunzitsa bwino kwambiri Timoteo. Chitsanzo chake chabwino kwa Timoteo kuyambira ali wamng’ono, komanso chitsanzo cha Loisi, agogo a Timoteo, chinathandiza kwambiri Timoteo kuti asatengere makhalidwe oipa amene mwina anzake anali nawo.—Machitidwe 16:1, 2; 2 Timoteo 1:5; 3:15.
Achinyamata ambiri masiku ano, omwe aleredwa ndi mayi kapena bambo wosakhulupirira kapena omwe aleredwa ndi mayi kapena bambo wawo yekha, amasonyeza makhalidwe abwino angati a Timoteo. Mwachitsanzo, Ryan, yemwe tsopano ali ndi zaka 22, ndipo ndi mtumiki wa nthawi zonse, anakulira pa khomo la kholo limodzi pamodzi ndi azichimwene ake ndi azilongo ake aakulu. Bambo ake anali munthu wokonda mowa kwambiri ndipo mmene amachoka pabanjapo n’kuti Ryan ali ndi zaka zinayi. Ryan akukumbikira kuti: “Nthawi zonse mayi anga ankafunitsitsa kuti banja lathu lipitirire kutumikira Yehova, ndipo ankayesetsa ndi mtima wonse kuchita khama kuti zimenezi zitheke.”
Ryan anati: “Mwachitsanzo, mayi ankaonetsetsa kuti ana amene tinkasewera nawo anali ana olongosoka. Sankatilola kucheza ndi anthu amene Baibulo limawatcha kuti mayanjano oipa, kaya ndi a kumpingo kapenanso a kunja kwa mpingo. Mayi anatithandizanso kuona bwino nkhani ya maphunziro.” Ngakhale kuti mayi a Ryan anali n’zochita zambiri ndiponso ankatopa chifukwa cha ntchito, iwo sanaleke kusonyeza chikondi ana awo pochita nawo chidwi. Ryan anati: “Nthawi zonse iwo ankafuna kukhala nafe pamodzi ndi kutilankhulitsa. Ankatiphunzitsa moleza mtima koma mosalekerera, ndipo ankaonetsetsa kuti tikuphunzira Baibulo nthawi zonse. Pankhani zokhudza mfundo za m’Baibulo mayi sankaganizako n’komwe zogonjera.”
Akamaganizira moyo wake ali mwana, Ryan amaona kuti munthu amene iyeyo ndiponso azibale ake anatengera kwambiri zochita zake ndi mayi awo omwe ankakonda kwambiri Mulungu ndiponso ana awo. Motero inu makolo achikristu, kaya muli pabanja kapena ndinu amasiye, kaya mwamuna kapena mkazi wanu ndi Mkristu kapena ayi, yesetsani kuti pantchito yophunzitsa ana anu musafooke kapena kubwerera m’mbuyo ngakhale pang’ono. Komabe nthawi zina, ana ena, amatha kuchoka m’choonadi ngati mwana wosakaza wotchulidwa m’Baibulo uja, koma akaona kuti dzikoli n’lachabe komanso n’lankhanza, amatha kubwerera. Inde, ‘wolungama amayenda mwangwiro ndipo ana ake adala pambuyo pake.’—Miyambo 20:7; 23:24, 25; Luka 15:11-24.
[Mawu a M’munsi]
a Kuti mumve tsatanetsatane wa mfundo zimenezi, onani tsamba 55 mpaka 59 m’buku la Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
[Bokosi/Zithunzi patsamba 11]
Makolo A Yesu Anachita Kusankhidwa Ndi Mulungu
Pamene anatumiza Mwana wake Yesu kudzabadwa ngati munthu padziko lapansi, Yehova anasankha mosamala kwambiri anthu odzakhala makolo a Yesuyo. N’zochititsa chidwi kuti anasankha mwamuna ndi mkazi odzichepetsa komanso oopa Mulungu, omwe sanam’lekerere Yesu koma anam’phunzitsa Mawu a Mulungu ndipo anam’phunzitsanso kukhala munthu wazintchito. (Miyambo 29:21; Maliro 3:27) Yosefe anaphunzitsa Yesu ntchito ya ukalipentala, ndipo n’zosakayikitsa kuti Yosefe ndi Mariya yemwe ankam’tuma Yesu, monga mwana wawo woyamba, kuti azithandiza kusamalira ana awo ena, omwe mwina analipo sikisi.—Marko 6:3.
Mungathe kuganizira anthu a m’banja mwa Yosefe akugwira ntchito limodzi pa nthawi ya Paskha kukonzekera ulendo wawo wa chaka n’chaka wopita ku Yerusalemu, womwe unali ulendo wokwana makilomita 200 kupita ndi kubwera, popanda njira zamakono za kayendedwe. N’zosakayikitsa kuti banja lawoli, lomwe mwina linali ndi anthu naini kapena kuposa pamenepo linayenera kukonzekera bwino kwambiri kuti liyende ulendo wautali choncho. (Luka 2:39, 41) Ngakhale kuti panali zovuta zonsezi, n’zosakayikitsa kuti Yosefe ndi Mariya ankasangalala kwambiri ndi maulendo amenewa, ndipo mwina ankapezerapo mwayi wophunzitsa ana awo nkhani za m’Baibulo zomwe zinachitika kale.
Ali panyumba pa makolo akewa Yesu ‘ankamvera’ makolo ake, ndipo nthawi zonse “anakulabe m’nzeru ndi mumsinkhu, ndi m’chisomo cha pa Mulungu ndi cha pa anthu.” (Luka 2:51, 52) Inde, zochita za Yosefe ndi Mariya zinaonetsa kuti mpake Yehova kuwakhulupirira. Iwowatu n’chitsanzo chabwino kwambiri kwa makolo masiku ano!—Salmo 127:3.