Makolo, Pezerani A M’banja Lanu Zosowa Zawo
“Ngati wina sadzisungiratu mbumba yake ya iye yekha, . . . aipa koposa wosakhulupira.”—1 TIMOTEO 5:8.
1, 2. (a) N’chifukwa chiyani zili zolimbikitsa kuona mabanja akupezeka pamisonkhano ali limodzi? (b) Kodi ndi zovuta ziti zimene mabanja amakhala nazo poyesetsa kuti akafike ku misonkhano panthawi yake?
MUKAMWAZA maso mumpingo wachikristu misonkhano isanayambe, mungaone ana ovala bwino akukhala pansi limodzi ndi makolo awo. Kodi sizosangalatsa kuona chikondi m’mabanja oterowo, chikondi chawo kwa Yehova ndi kwa wina ndi mnzake? Ndipo kawirikawiri sitiganizira n’komwe za ntchito yaikulu imene imakhalapo pokonzekeretsa banja kuti lifike kumisokhano panthawi yake.
2 Nthawi zambiri, makolo amakhala otanganidwa tsiku lonse, koma tsiku la misonkhano m’pamene banja limakhaladi pa mpanipani. Chakudya chimafunika kuti chiphikidwe, ntchito zapakhomo izi ndi izi, komanso homuweki. Makamaka makolo ndiwo amakhala ndi ntchito yaikulu, poonetsetsa kuti onse aoneke bwino, adye, ndiponso akonzeke panthawi yake. Koma poti ana ndi ana, chinachake chikhoza kusokonezeka panthawi yolakwika kwambiri. Mwana wokulirapo akhoza kung’amba kabudula wake posewera. Mwana wam’ng’ono akhoza kukhutula pansi chakudya. Kapena anawo angayambe kukangana. (Miyambo 22:15) Mapeto ake? Ngakhale kukonzekera kwakhama kwa makolo kungasokonezeke. Komabe, mabanja oterowo nthawi zambiri amafikabe pa Nyumba ya Ufumu misonkhano isanayambe. N’zolimbikitsa kwambiri kuwaona kumisonkhano mlungu ndi mlungu, chaka ndi chaka, pamene anawo akukula ndi kuyamba kutumikira Yehova!
3. Kodi timadziwa bwanji kuti Yehova amaona mabanja kukhala ofunika kwambiri?
3 Ngakhale kuti ntchito yanu monga kholo nthawi zina imakhala yovuta, ngakhalenso yotopetsa, dziwani kuti Yehova amayamikira kwambiri kuyesetsa kwanu. Yehova ndiye anayambitsa dongosolo la banja. Ndiye chifukwa chake Mawu ake amanena kuti banja lililonse “alitcha dzina,” kutanthauza kuti ndi Yehova anapangitsa kuti likhalepo. (Aefeso 3:14, 15) Choncho, pamene makolonu muyesetsa kukwaniritsa udindo wanu m’banja m’njira yoyenerera, mumakhala mukulemekeza Ambuye wa chilengedwe chonse. (1 Akorinto 10:31) Umenewo si mwayi waukulu nanga? Ndiye chifukwa chake, mpake kuti tikambirane za udindo umene Yehova anapatsa makolo. Udindo umene tikambirane m’nkhani ino, ndi udindo wopezera a m’banja zosowa zawo. Tiyeni tikambirane njira zitatu zimene Mulungu amayembekezera makolo kupezera a m’banja zosowa zawo.
Kuwapezera Zosowa Zakuthupi
4. M’banja, kodi Yehova anakhazikitsa dongosolo lotani pankhani yopezera ana zosowa zawo?
4 Mtumwi Paulo analemba kuti: “Koma ngati wina sadzisungiratu mbumba yake ya iye yekha, makamaka iwo a m’banja lake, wakana chikhulupiriro iye, ndipo aipa koposa wosakhulupira.” (1 Timoteo 5:8) Kodi “wina” amene Paulo anali kunena pano ndani? Anali kunena mutu wa banja, yemwe amakhala mwamuna. Mulungu anapatsanso mkazi udindo wolemekezeka ngati wothandiza mwamuna wake. (Genesis 2:18) Akazi a m’nthawi za m’Baibulo kawirikawiri anathandiza amuna awo kupezera a m’banja zosowa zawo. (Miyambo 31:13, 14, 16) Lerolino, mabanja a kholo limodzi akuchuluka. Makolo ambiri achikristu omwe alibe mwamuna kapena mkazi akuchita bwino kwambiri posamalira mabanja awo. Komabe, n’zoona kuti zimakhala bwino koposa pakakhala makolo onse awiri, kuti bambo azitsogolera banja.
5, 6. (a) Kodi amene amayesa kupezera a m’banja lawo zosowa zakuthupi amakumana ndi zovuta zina zotani? (b) Kodi Akristu opezera banja zosowa ayenera kuona ntchito motani kuti azitha kupirira?
5 Pa 1 Timoteo 5:8, kodi Paulo anali kunena za kupezera banja zosowa zotani? Nkhaniyo ikusonyezeratu kuti anali kunena zosowa za banja zakuthupi. M’dziko la masiku ano, pali zovuta zambiri zimene mutu wa banja ungakumane nazo pofuna kupezera banja zosowa. Mavuto azachuma ali padziko lonse. Palinso vuto la kuchotsedwa ntchito, ulova, ndi kukwera mtengo kwa zinthu. Kodi n’chiyani chingathandize wopezera banja zosowa kupirira mavuto oterowo?
6 Wopezera banja zosowa ayenera kukumbukira kuti akusamalira udindo wochokera kwa Yehova. Mawu ouziridwa a Paulo amasonyeza kuti munthu amene angathe kukwaniritsa lamulo limeneli, koma akulinyalanyaza, amafanana ndi munthu amene “wakana chikhulupiriro.” Mkristu ayenera kuchita zonse zimene angathe kuti asakhale wotero pamaso pa Mulungu. Komabe n’zomvetsa chisoni kuti anthu ambiri m’dzikoli masiku ano alibe “chikondi chachibadwidwe.” (2 Timoteo 3:1, 3) Ndithudi, pali abambo ambiri omwe sasamalira udindo wawo, amene amasiya mabanja awo ali opanda chithandizo. Amuna achikristu sakhala ouma mtima chotero, ndipo sapeputsa udindo wawo wopezera banja lawo zosowa. Mosiyana ndi apantchito anzawo, Akristu opezera banja zosowa amaona ngakhale ntchito zotsika kwenikweni kukhala zolemekezeka ndi zofunika. Amaziona kukhala njira yokondweretsera Yehova Mulungu, chifukwa zimawathandiza kupeza zosowa za okondedwa awo.
7. N’chifukwa chiyani kuli koyenerera kuti makolo azisinkhasinkha chitsanzo cha Yesu?
7 Amene ali mitu ya mabanja amathandizikanso posinkhasinkha chitsanzo changwiro cha Yesu. Kumbukirani kuti, Baibulo limatcha Yesu mwaulosi kuti “Atate Wosatha.” (Yesaya 9:6, 7) Pokhala “Adamu wotsirizayo,” Yesu analowa m’malo mwa “munthu wayamba, Adamu” monga atate wa anthu onse okhala ndi chikhulupiriro. (1 Akorinto 15:45) Mosiyana ndi Adamu, yemwe anachita zinthu mwadyera posamalira zofuna za iye mwini, Yesu ndiye atate wodziwa kusamalira banja lake. Baibulo limati za iye: “Umo tizindikira chikondi, popeza Iyeyu anapereka moyo wake chifukwa cha ife.” (1 Yohane 3:16) Inde, ndi mtima wonse, Yesu anapereka moyo wake kaamba ka ena. Komanso, tsiku ndi tsiku anaika zosowa za ena patsogolo pa za iye mwini ngakhale m’zinthu zazing’ono. Makolonu, muchita bwino kutengera mzimu wodzipereka umenewo.
8, 9. (a) Kodi makolo angaphunzire chiyani poona mmene mbalame imadziperekera popezera ana ake zosowa? (b) Kodi makolo achikristu ambiri amasonyeza motani mzimu wodzipereka?
8 Makolo akhoza kuphunzira zambiri za chikondi chopanda dyera kuchokera pa mawu amene Yesu anawalankhula kwa anthu opandukira Mulungu. Iye anati: “Ine ndinafuna kangati kusonkhanitsa pamodzi ana ako, inde monga thadzi lisonkhanitsa anapiye ake m’mapiko ake.” (Mateyu 23:37) Yesu pano anapereka chithunzi choonekera bwino cha nkhuku imene ikuteteza ana ake m’mapiko. Kunena zoona, makolo angaphunzire zambiri kuchokera pa chibadwa cha mbalame yaikazi, imene imaika moyo wake pachiswe pofuna kuteteza ana ake. Komanso, zimene mbalame zimachitira ana ake tsiku ndi tsiku n’zochititsa chidwi kuona. Zimauluka kukasaka chakudya n’kubwera, kupitanso n’kubwera, choncho! Ngakhale zitatopa, zimagwetserabe chakudya m’makamwa oyasamula a anapiye, omwe amachimeza ndi kuyasamulanso kufuna china. Ndithudi, zolengedwa za Yehova zambiri “zipambana kukhala zanzeru” mmene zimapezera zosowa za ana awo.—Miyambo 30:24.
9 Mofananamo, makolo achikristu padziko lonse lapansi mumasonyeza mzimu wotamandika wodzipereka. Mumalolera kuvutika kusiyana n’kuti ana anu avutike. Komanso, mumadzipereka tsiku ndi tsiku kuti mupezere zosowa banja lanu. Ambiri mumalawirira m’mamawa kukagwira ntchito zotopetsa kapena zosasangalatsa kwenikweni. Mumagwira ntchito zolimba kuti mupezere banja lanu chakudya chopatsa thanzi. Mumagwira ntchito molimbika kuti ana anu avale zovala zoyera, akhale m’nyumba yoyenerera, ndi kuti apeze maphunziro abwino. Ndipo mumalimbikirabe motero tsiku ndi tsiku, chaka ndi chaka. Kunena zoona, kudzipereka ndi kupirira koteroko Yehova amakondwera nako kwabasi! (Ahebri 13:16) Komabe kumbukirani kuti palinso mitundu ina ya zosowa zofunika koposa, zimene muyenera kupezera banja lanu.
Kuwapezera Zosowa Zauzimu
10, 11. Kodi zosowa zofunika koposa za anthu ndi ziti, ndipo kodi makolo achikristu ayenera kuchitanji choyamba asanapezere ana awo zosowazo?
10 Kupezera a m’banja lanu zosowa zauzimu n’kofunika kuposa zakuthupi. Yesu anati: “Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mawu onse akutuluka m’kamwa mwa Mulungu.” (Mateyu 4:4; 5:3) Kodi inu makolo, mungachite chiyani kuti mupezere banja lanu zosowa zauzimu?
11 Pankhani imeneyi, mwina palibe lemba lina limene timaligwira mawu kuposa Deuteronomo 6:5-7. Tatsegulani Baibulo lanu muwerenge mavesiwo. Onani kuti choyamba makolo akuuzidwa kulimbitsa moyo wawo wauzimu, kukulitsa chikondi chawo pa Yehova ndi kumvera mawu ake. Inde, muyenera kukhala wophunzira Mawu a Mulungu wakhama, kuwerenga Baibulo nthawi zonse ndi kusinkhasinkha zimene mumawerenga. Zimenezi zidzakuthandizani kumvetsa ndi kukonda njira za Yehova, mfundo zake za makhalidwe abwino, ndi malamulo ake. Zotsatira zake n’zakuti, mtima wanu udzadzala ndi mfundo za choonadi cha m’Baibulo zimene zidzakupangitsani kukhala wosangalala, wolemekeza Yehova ndi kum’konda. Mudzakhala ndi zophunzitsa ana anu zabwino komanso zambiri.—Luka 6:45.
12. Kodi makolo angatengere motani chitsanzo cha Yesu pophunzitsa ana awo mfundo za choonadi cha m’Baibulo?
12 Makolo olimba mwauzimu amatha kugwiritsa ntchito uphungu wopezeka pa Deuteronomo 6:7, wa ‘kuphunzitsa’ ana awo Mawu a Yehova pampata uliwonse. ‘Kuphunzitsa’ kumene akutanthauza pa lembali ndiko kukhomereza mwa kubwereza zinthu. Yehova amadziwa bwino kuti tonsefe, ana makamaka, amayenera kuwabwerezera zinthu kuti aphunzire. Ndiye chifukwa chake Yesu anali kubwereza zinthu m’maulaliki ake. Mwachitsanzo, pophunzitsa ophunzira ake mfundo ya kudzichepetsa, m’malo modzikweza ndi kupikisana, iye anapeza njira zosiyanasiyana zobwerezera mfundo imodzimodziyo. Anaphunzitsa mwa kulingalira nawo, mwa fanizo, ngakhale mwa chitsanzo. (Mateyu 18:1-4; 20:25-27; Yohane 13:12-15) Koma chosangalatsa n’chakuti, Yesu sanali konse wosaupeza mtima. Mofananamo, makolo ayenera kupeza njira zophunzitsira ana awo mfundo zoyambirira za choonadi. Ayenera kumabwereza moleza mtima mfundo za makhalidwe abwino za Yehova mpaka anawo atafika pozimvetsa ndi kuyamba kuzigwiritsa ntchito.
13, 14. Kodi ndi nthawi ziti zimene zingapereke mipata yoti makolo aphunzitse ana awo mfundo za choonadi cha m’Baibulo, ndipo angagwiritse ntchito nkhani zotani?
13 Nthawi za phunziro la banja zimapereka mipata yabwino yophunzitsira ana. Ndithudi, phunziro la banja la nthawi zonse, lolimbikitsa ndi losangalatsa, ndilo chinsinsi chomangira moyo wauzimu wa banja. Mabanja achikristu padziko lonse amasangalala ndi maphunziro oterowo. Amagwiritsa ntchito mabuku operekedwa ndi gulu la Yehova. Ndipo amagwirizanitsa phunzirolo ndi zosowa za ana awo. Buku lakuti Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso lakhala dalitso lalikulu pambali imeneyi. Chimodzimodzinso buku lakuti Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza.a Komabe, nthawi ya phunziro la banja si ndiyo nthawi yokha yophunzira ndi ana.
14 Monga limasonyezera lemba la Deuteronomo 6:7, mipata ilipo yambiri imene makolo mungakambirane zinthu zauzimu ndi ana anu. Kaya ndi pamene muli nawo paulendo, pogwira ntchito za pakhomo, kapena pocheza, mungapeze mipata yoperekera zosowa zauzimu kwa ana anu. Komabe, sikuti nthawi zonse muzingokhalira kuphunzitsa ana anu m’fundo za choonadi cha m’Baibulo ayi. M’malo mwake, monga banja yesani kumakhala ndi macheza auzimu ndiponso olimbikitsa. Mwachitsanzo, magazini ya Galamukani! imakhala ndi nkhani zambiri zosiyanasiyana. Nkhani zoterozo zingatsegule mpata wokambirana za zinyama zimene Yehova analenga, malo okongola achilengedwe m’madera osiyanasiyana a dziko lapansi, ndi zikhalidwe za anthu zosangalatsa ndi moyo wawo. Makambirano oterowo angalimbikitse achichepere kumawerenga mabuku ambiri operekedwa ndi gulu la kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.—Mateyu 24:45-47.
15. Kodi makolo angachite chiyani kuti athandize ana awo kuona ulaliki wachikristu kukhala wosangalatsa ndi wopindulitsa?
15 Kukhala ndi makambirano olimbikitsana ndi ana anu kudzakuthandizani kuwapezera chosowa chinanso chauzimu. Ana achikristu ayenera kuphunzira kuuzako ena mogwira mtima za chikhulupiriro chawo. Pokambirana mfundo zina zosangalatsa za mu Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!, mungayese kupeza mipata yogwirizanitsira nkhanizo ndi ulaliki. Mwachitsanzo, mungafunse kuti: “Kodi sizingakhale zosangalatsa kuti anthu ambiri adziwe zimenezi ponena za Yehova? Muganiza munthu tingamuuze bwanji nkhani imeneyi kuti imusangalatse?” Makambirano oterowo angalimbikitse chidwi mwa ana chofuna kuuzako ena zimene amaphunzira. Ndiyeno, pamene ana anu apita nanu ku ulaliki, amaona zenizeni zimene mumakambirana. Angaonenso kuti ulaliki ndi ntchito yabwino, yokhutiritsa ndi yosangalatsa kwambiri.—Machitidwe 20:35.
16. Kodi ana angaphunzire chiyani pomvetsera mapemphero a makolo awo?
16 Makolo amapezeranso ana awo zosowa zauzimu popemphera. Yesu anaphunzitsa ophunzira ake mmene angapempherere, komanso anapemphera nawo limodzi nthawi zambiri. (Luka 11:1-13) Taganizani kuchuluka kwa zimene iwo anaphunzira pamene Mwana weniweni wa Yehova anali kupemphera nawo. Ana anunso angaphunzire zambiri kuchokera ku mapemphero anu. Mwachitsanzo, angadziwe kuti Yehova amafuna kuti tizilankhula naye momasuka mochokera pansi pamtima, ndi kutinso tikhoza kum’fikira ndi vuto lathu lililonse limene tingakhale nalo. Inde, mapemphero anu angathandize ana anu kuphunzira mfundo ina yauzimu yofunika kwambiri: Yakuti iwo akhoza kukhala paubwenzi ndi Atate wawo wakumwamba.—1 Petro 5:7.
Kuwapezera Zosowa Zokhudza Maganizo
17, 18. (a) Kodi Baibulo limasonyeza motani kuti kusonyeza ana chikondi n’kofunika? (b) Kodi atate angatengere motani chitsanzo cha Yehova posonyeza ana awo chikondi?
17 Ananso amakhala ndi zosowa zokhudza maganizo. Mawu a Mulungu amauza makolo za kufunika kowapezera zosowa pambali imeneyinso. Mwachitsanzo, akazi aang’ono akulimbikitsidwa kuti “akonde ana awo.” Inde, n’zimene akazi aang’ono akulangizidwa. (Tito 2:4) Zimenezi zimaphunzitsa mwana kukonda ena ndipo zimadzetsa mapindu okhalitsa. Koma kulephera kuphunzitsa mwana chikondi n’kupanda nzeru. Kumadzetsa mavuto aakulu ndipo kumatanthauza kulephera kutsanzira Yehova, yemwe amatisonyeza chikondi chachikulu ngakhale tili opanda ungwiro.—Salmo 103:8-14.
18 Yehova ndiye amayamba kukonda ana ake a padziko lapansi. N’zimene lemba la 1 Yohane 4:19 limanena kuti, “anayamba Iye kutikonda.” Makamaka inuyo atate, muyenera kutengera chitsanzo cha Yehova. Yambani inuyo kulimbikitsa ubale wachikondi kwa ana anu. Baibulo limalangiza atate kuti asamakwiyitse ana awo, “kuti angataye mtima.” (Akolose 3:21) Chimene chimawakwiyitsa kwambiri ana ndicho kuona kuti kholo lawo siliwakonda kapena kuwaganizira. Atate amene amazengereza kuuza ana awo kuti amawakonda ayenera kukumbukira chitsanso cha Yehova. Iye anachita kulankhula kuchokera kumwamba kuti amakondwera ndi Mwana wake ndipo amam’konda. (Mateyu 3:17; 17:5) Zimenezo ziyenera kuti zinam’limbikitsa Yesu bwanji! Mofananamo, zimawapatsa mphamvu ana ndipo zimawalimbikitsa, pamene makolo awo awauza mochokera pansi pa mtima kuti amawakonda ndipo amakondwera nawo.
19. N’chifukwa chiyani chilango chili chofunika, ndipo makolo achikristu ayenera kuyesetsa kusamala chiyani?
19 N’zoona kuti chikondi cha makolo si mawu chabe ayi. Timasonyeza chikondi makamaka m’zochita. Kupezera ana zosowa zakuthupi ndi zauzimu ndi njira imodzi imene makolo angasonyezere chikondi chawo kwa ana, makamaka pamene makolowo asonyeza kuti akuchita zimenezo chifukwa chowakondadi anawo. Komanso, kulanga ana ndi njira inanso imene makolo angasonyezere chikondi chawo kwa ana. Zoona, “amene Ambuye am’konda am’langa.” (Ahebri 12:6) Koma kulephera kulanga ana kumasonyeza kuti mumawada. (Miyambo 13:24) Yehova nthawi zonse ‘amalanga’ pamlingo woyenerera. (Yeremiya 46:28) Koma kwa makolo opanda ungwiro, si nthawi zonse pamene amatha kulanga pamlingo woyenerera. Komabe, muyenera kuyesetsa kulanga mwana pamlingo woyenerera. Chilango chokhwima koma chachikondi chimathandiza mwana kukula bwino ndi kukhala ndi moyo wosangalala ndi wopindulitsa. (Miyambo 22:6) Kodi si zimene kholo lachikristu lililonse limafunira mwana wake?
20. Kodi makolo angapatse bwanji ana awo mwayi wabwino koposa ‘wosankha moyo’?
20 Pamene makolonu muchita ntchito yofunika imene Yehova wakugawirani, yopezera ana anu zosowa zakuthupi, zauzimu, ndi zokhudza maganizo, mapindu ake amakhala aakulu. Mukatero mumapatsa ana anu mwayi wabwino koposa ‘wosankha moyo’ ndi ‘kukhala ndi moyo.’ (Deuteronomo 30:19) Ana amene amasankha kutumikira Yehova ndi kuyendabe m’njira ya ku moyo pamene akukula, amapangitsa makolo awo kukhala osangalala kwambiri. (Salmo 127:3-5) Chisangalalo choterocho chidzakhala ku nthawi yonse! Komabe, kodi ndi motani mmene ana angatumikirire Yehova tsopano lino? Nkhani yotsatira ikufotokoza zimenezo.
[Mawu a M’munsi]
a Ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
Kodi Mungayankhe Kuti Chiyani?
Kodi makolo angachite chiyani kuti apezere ana awo zosowa
• zakuthupi?
• zauzimu?
• zokhudza maganizo?
[Chithunzi patsamba 18]
Mbalame zambiri sizitopa kupezera ana chakudya
[Chithunzi patsamba 20]
Makolo ayenera choyamba kulimbitsa moyo wawo wauzimu
[Zithunzi pamasamba 20, 21]
Makolo angapeze mipata yambiri yophunzitsira ana awo za Mlengi
[Chithunzi patsamba 22]
Ana amapeza nyonga ndi chilimbikitso ngati makolo awo amawauza kuti amakondwera nawo