“Mayendedwe Anu Ayenere Uthenga Wabwino”
“Mayendedwe anu ayenere uthenga wabwino wa Kristu.”—AFILIPI 1:27.
1. Chochitika cha posachedwapa mu Mzinda wa New York chinabweretsa ndemanga zoyanjidwa zotani kuchokera kwa mkulu wa mzinda? (Aroma 13:3)
“MBONI zoposa 1,000” zinabwera ku City Hall kunsi kwa Manhattan pa September 29, 1988, inasimba tero The New York Times. Izo zinabwera m’kuchirikiza kuyambitsidwa kwa chimango chomwe chinaperekedwa kaamba ka kupededwa ndi Bungwe Losanthula la mzindawo. Ngakhale kuti kuyambitsidwa kwakulola chimango chogonamo chatsopano pa malikulu a Mboni za Yehova kunakanidwa, mkulu wa mzinda “anatamanda Mbonizo kukhala ‘zaudongo modabwitsa’ ndipo ananena kuti izo ‘zinalidi zokhumbirika.’”
2. Ndi m’njira yotani mmene mayendedwe a Mboni aliri osiyana, ndipo nchifukwa ninji?
2 Mwa nthaŵi zonse, pamene anthu oposa chikwi chimodzi asonkhana pamodzi kusonyeza chirikizo kaamba ka chochititsa chosatchuka, nchiyani chomwe chingayembekezeredwe? Kukankha, kufuula, ngakhale kasonyezedwe ka mphamvu zenizeni ndi chiwawa sizimakhala zachilendo. Nchifukwa ninji Mboni ziri zosiyana? Chiri chifukwa chakuti izo zimazindikira kuti nthaŵi zonse khalidwe lawo limawunikira pa chikhulupiriro chawo. Izo zimakumbukira bwino lomwe uphungu wa Malemba wakuti: “Ndipo mayendedwe anu mwa amitundu akhale okoma, kuti, mmene akamba za inu ngati ochita zoipa, akalemekeze Mulungu pakuwona ntchito zanu zabwino, m’tsiku la kuyang’anira.”—1 Petro 2:12.
Mayendedwe Okoma Amalemekeza Yehova
3. Ndi mbali yotani imene mayendedwe athu amachita m’kulemekeza Yehova?
3 Kulemekeza Yehova Mulungu ndi mayendedwe okoma mwachiwonekere kuli mbali ya thayo lathu Lachikristu. (Mateyu 5:16) Machitidwe okoma, ndithudi, amaphatikizapo zinthu zambiri—mwachitsanzo, kuwona mtima, khama, ndi makhalidwe abwino. Ngakhale kuli tero, mikhalidwe imeneyi kaŵirikaŵiri imayamikiridwa kokha ndi awo omwe amatidziŵa bwino lomwe kapena awo omwe tiri nawo ndi zochita zokhazikika, onga ngati mabwenzi athu, achibale, otilemba ntchito, ogwira nawo ntchito, ndi aphunzitsi. Bwanji ponena za unyinji wokulira wa anthu amene tiri nawo ndi kokha kugwirizana kwachisawawa? Apa ndi pamene mayendedwe anthu amaloŵetsedwamo kwenikweni. Popeza kuti mofanana ndi chokulungira chokhumbirika chomwe chimabweretsa chikondwerero cha mphatso ya mtengo wake, mayendedwe abwino amapanga chomwe tikufuna kugawira kukhala chosangalatsa mowonjezereka. Mosasamala kanthu za mikhalidwe ina yokoma Yachikristu yomwe tingakhale nayo kapena mosasamala kanthu za kukhumbirika kumene zolinga zathu zingakhalire, izo zidzachita zochepera ngati mayendedwe athu ali oipa. Chotero ndimotani mmene mayendedwe athu angabweretsere ulemerero kwa Yehova?
4. Ndi m’mbali zotani za moyo m’zimene tiyenera kupereka chisamaliro ku mayendedwe athu?
4 “Mayendedwe anu ayenere uthenga wabwino,” akutero Paulo. (Afilipi 1:27) Ichi, ndithudi, chimaphatikizapo utumiki wathu wapoyera. Koma mkhalidwe wathu ndi mayendedwe pa malo athu a kulambira, pa malo athu okhala, pa ntchito, mu sukulu, inde, m’mbali iriyonse ya miyoyo yathu, alinso ndi chiyambukiro chachindunji pa kukhutiritsa kwa utumiki wathu. “Osapatsa chokhumudwitsa konse m’chinthu chirichonse, kuti utumikiwo usanenezedwe,” akulemba tero Paulo. (2 Akorinto 6:3) Ndimotani mmene tingakhalire otsimikizira kuti tikugwiritsira ntchito uphungu umenewo? Nchiyani chomwe tingachite kuthandizana wina ndi mnzake, makamaka achichepere pakati pathu, kusonyeza mayendedwe Achikristu pa nthaŵi zonse?
Pa Nyumba ya Ufumu
5. Nchiyani chomwe tiyenera kuzindikira pamene tiri pa Nyumba ya Ufumu?
5 Nyumba ya Ufumu iri malo athu a kulambira. Timakhala kumeneko pa chiitano cha Yehova ndi Mwana wake, Yesu Kristu. M’lingaliro limenelo, tiri alendo panyumba ya Yehova. (Salmo 15:1; Mateyu 18:20) Kodi muli mlendo wabwino pamene mubwera ku Nyumba ya Ufumu? Kuti tikhale tero, tiyenera kusonyeza kulingalira koyenera ndi ulemu osati kokha kwa wotiitanayo komanso kwa alendo ena. Kodi chimenecho chimaphatikizapo chiyani?
6. (a) Kukhala wochedwa mwachizoloŵezi pa misonkhano kumasonyeza kusoweka kwa chiyani? (b) Nchiyani chomwe chingachitidwe kulaka vutolo?
6 Choyamba nacho, pali nkhani ya kubwera pa nthaŵi yake. Chiri movomerezeka chosapepuka nthaŵi zonse kuchita tero. Ena amakhala kutali; ena ali ndi banja ndi ana ofunikira kukonzekeretsa. Kuyesayesa kumene amaika kubwera ku misonkhano Yachikristu mokhazikika kuli koyamikirika mowonadi. Chawonedwa, ngakhale kuli tero, kuti ena agwera m’chizoloŵezi cha kufika mochedwa kaamba ka misonkhano. Nchiyani chomwe iwo angachite kuti awongolere chimenechi? Wina ayenera kuzindikira choyamba kuti kuchedwa mwachizoloŵezi pa misonkhano Yachikristu sikumawunikira nthaŵi zonse kusoŵeka kwa chiyamikiro kaamba ka phindu la misonkhano. Ena omwe amachedwa kaŵirikaŵiri amawoneka kukhala akusangalala ndi misonkhano mofanana ndi wina aliyense—pamene afika kumeneko. M’malomwake, vuto lingatulukepo kuchokera ku kukonzekera kosakwanira ndi kusoŵeka kwa kulingalira kaamba ka Akristu anzawo. Chimodzi cha zifukwa zimene tikulangizidwa ‘kusaleka kusonkhana kwathu pamodzi’ chiri kuti tingakhoze “kulingalirana wina ndi mnzake ku ntchito zokoma.” (Ahebri 10:24, 25) Sitingakhoze konse kuchita tero ngati, nthaŵi ndi nthaŵi, tifika mochedwa ndipo mwakutero kupanga kucheutsa kapena msokonezo. Kuti tikhale osachedwa, akatswiri alingalira kuti, tiyenera kukhala ndi cholinga cha kufika nthaŵi isanakwane m’malo mofika kumeneko kokha pa nthaŵi yake. Kodi mukufuna kuika ichi m’kugwira ntchito?
7. Longosolani chimene kupereka chisamaliro pa misonkhano kumachita ndi mayendedwe abwino.
7 Mayendedwe abwino amafuna kuti tipereke chisamaliro chathu kwa anthu pamene akulankhula kwa ife. (Miyambo 4:1, 20) Ichi chimagwiranso ntchito ku misonkhano Yachikristu, kumene atumiki a Mulungu amalankhula kotero kuti apereke mphatso ina yauzimu kutimangirira. Chikakhala ndithudi kasonyezedwe ka mayendedwe oipa kwambiri ku mbali yathu ngati tikawodzera, kunong’oneza mobwerezabwereza kwa wina wokhala chifupi ndi ife, kutafuna chingamu kapena masiwiti, kuŵerenga nkhani zina, kapena kusamalira nkhani zina mkati mwa msonkhano. Elihu wachichepere sanangokhala modekha kupyola m’kukambitsirana kwakutali kochitidwa ndi Yobu ndi mabwenzi atatu komanso “anatcherera khutu” ku chimene iwo ananena ndipo anapereka “chisamaliro [chake]” kwa iwo. (Yobu 32:11, 12) Mayendedwe abwino Achikristu adzatisonkhezera ife kusonyeza ulemu woyenerera kaamba ka mlankhuli ndi uthenga wake wozikidwa m’Baibulo mwa kupereka kwa iye chisamaliro chathu chosagawanika ndi chichirikizo.
8. Ndimotani mmene timasonyezera kuti ndife ophunzira anzake a Yesu Kristu?
8 Misonkhano isanakhale ndi pambuyo pake, mayendedwe Achikristu amaphatikizapo kukhala ndi chikondwerero chokangalika mwa ena opezeka pa Nyumba ya Ufumu. Paulo anawona kuti ziŵalo zodzozedwa za mpingo Wachikristu “salinso alendo ndi ogonera, komatu ali . . . abanja la Mulungu.” (Aefeso 2:19) Kodi mumachitira Mboni zinzanu monga alendo ndi ogonera kapena monga ziŵalo za banja limodzimodzilo? Kupatsa moni kwaubwenzi, kugwirana chanza kotentha, kumwetulira kokoma mtima—zinthu zonsezo zazing’ono, mwinamwake, koma ziri mbali ya umboni wakuti ndife ophunzira anzake a Yesu Kristu. Ngati tipanga zisonyezero zoterozo pamene tikumana ndi alendo, kodi sitiyenera kuchita tero “makamaka kwa iwo apabanja la chikhulupiriro”?—Agalatiya 6:10.
9. Ndimotani mmene ana angaphunzitsidwire kusonyeza chikondwerero mwa anthu osati awo a msinkhu wawo?
9 Kodi ana angaphunzitsidwe kusonyeza mtundu umenewo wachikondwerero mwa anthu osati awo a msinkhu wawo? Achikulire ena angalingalire kuti ana afunikira kupita ndi kuseŵera ndi mabwenzi awo achichepere pambuyo pa kukhala kwa ora limodzi kapena aŵiri akumvetsera pa misonkhano. Koma Nyumba ya Ufumu siiri malo kaamba ka kuseŵera. (Mlaliki 3:1, 17) Pamene mnyamata wa zaka zakubadwa zinayi ndi theka anafunsidwa ndi mphunzitsi wake unyinji wa abale ndi alongo omwe anali nawo, iye anayankha kuti: “Ali ambiri chotero kotero kuti sindingathe kuwaŵerenga onse.” Pambuyo pake, pamene makolo ake anamfunsa iye ponena za ichi, mnyamatayo analongosola kuti: “Sindikudziŵa unyinji wa abale ndi alongo amene ndiri nawo. Pamene ndipita ku Nyumba ya Ufumu, iwo ali ambiri koposa.” Kwa iye, onse opezekapo ali abale ndi alongo ake.
Mu Utumiki Wathu Wapoyera
10. Ndi chilangizo chotani chochokera kwa Yesu chimene chingatithandize ife kuchita “mayendedwe oyenera uthenga wabwino” pamene tiri mu utumiki wathu?
10 Kuti tichite “mumayendedwe oyenera uthenga wabwino” mwachibadwa chimaloŵetsamo utumiki wathu wapoyera. Tiyenera kusunga m’maganizo kuti chomwe tiri nacho chiri uthenga wa mtendere, ndipo mayendedwe athu ayenera kuwunikira chimenecho. (Aefeso 6:15) Malangizo ochokera kwa Yesu ali akuti: “Poloŵa mnyumba muwalankhule. Ndipo ngati nyumbayo iri yoyenera, mtendere wanu udze pa iwo.” Mwakukhala otentha, aubwenzi, ndi aulemu, timalola mwininyumba kudziŵa kuti tiri ndi chikondwerero chake chenicheni pa mtima. Pa nthaŵi zina, ngakhale ndi tero, munthu yemwe timakumana naye pakhomo angakhale wopanda ubwenzi, ngakhale wandewu. Kodi tiyenera kukhala osokonezedwa ndi kuyamba kuchita mumayendedwe ofananawo? Onani chimene Yesu anapitiriza kunena: “Koma ngati [mwininyumba] sali woyenera, mtendere wanu ubwerere kwa inu.” (Mateyu 10:12, 13) Mayendedwe athu pa masitepi a khomo nthaŵi zonse ayenera kuyenerana ndi “utumiki wachiyanjanitso.”—2 Akorinto 5:18.
11. Ndimotani mmene mayendedwe athu a kavalidwe ndi mawonekedwe aumwini amayambukirira mbali yathu monga atumiki a Mulungu?
11 Mayendedwe anthu amalankhula ponena za ife m’njira zinanso. Mwachitsanzo, kodi mawonekedwe athu aumwini amayenerana ndi thayo lathu monga mtumiki wa Mawu a Mulungu? Bwanji ponena za ziwiya zimene timagwiritsira ntchito—chola cha mabukhu, Baibulo, ndi mabukhu a Baibulo? Wolemba m’danga la nyuzipepala akupatsa amuna a malonda chilangizo ichi: “Valani kaamba ka malonda, osati kaamba ka phwando, kukumana wamba kwamayanjano kapena zochitika za maseŵera.” Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti kavalidwe kanu ndi mawonekedwe aumwini “ali chizindikiro cha mayanjano chomwe chimapereka kwa anthu ozungulira chidziŵitso ponena za amene inu muli ndi kumene mumayenerera mu dongosolo la zinthu.” Chotero pamene tipita mu “zochita” zathu za utumiki, kavalidwe kathu ndi kawonekedwe siziyenera kukhala zija zopanda udongo kapena zauve, osati ngakhale zokoka chisamaliro kapena zopitirira malire, koma nthaŵi zonse “kuyenerana ndi uthenga wabwino.”—Yerekezani ndi 1 Timoteo 2:9, 10.
12. Ndimotani mmene mayendedwe abwino angasonyezedwere m’chigwirizano ndi kuyenera ndi zinthu za mwininyumba?
12 Ngakhale kuti tiyenera kukhala “nthaŵi zonse okonzeka kupanga chodzikanira” cha mbiri yabwino, mayendedwe abwino Achikristu amafunikira kuti tichite tero “achifatso ndi mantha.” (1 Petro 3:15) Chimenecho chimaphatikizapo ulemu kaamba ka kuyenerera kwa mwininyumba ndi zinthu zake. Kodi timakonzekera zochitachita zathu kotero kuti tifikire pa ora lolingalirika? Kodi tiri amaso kuwona kaya ngati tikusokoneza zochita zina zofunikira kapena ntchito? Kodi tiri owolowa manja m’kugwiritsira ntchito manenedwe onga ngati “Kodi ndingakhoze?” “Chonde,” ndi “Zikomo”? Kodi timakalamira kuloŵetsa mwininyumba m’kukambitsirana, kapena kodi timalamulira iko kuwopera kuti sitingakhoze kupambana ndi zimene takonzekera kunena?
13. Chitirani chitsanzo mmene mayendedwe okoma mu utumiki kaŵirikaŵiri amabweretsera zotulukapo zabwino.
13 Mayendedwe abwino, ophatikizidwa ndi kudera nkhaŵa kowona mtima kwaumwini, kaŵirikaŵiri amatsegula njira kaamba ka umboni wokoma. Ichi ndicho chifukwa chake ana amayendedwe abwino kaŵirikaŵiri amapeza chisamaliro ndi chikondwerero cha eninyumba kumene achikulire angalephere kuchita tero. Mboni ya zaka 13 zakubadwa mu Mexico inakumana ndi mtsikana wachichepere yemwe anafuna kuphunzira. Ngakhale kuli tero, mtsikanayo ananena kuti iye akafunikira kuchita tero popanda atate wake kudziŵa ponena za icho. Koma wofalitsa wachichepereyo anadzimva kuti, mu nkhaniyi, kaamba ka ulemu wa atatewo, iye iyemwini akafunikira kupempha chilolezo chawo. Chotero anadzipereka kukalankhula ndi atatewo ndi kuwawuza kuti chomwe anafunikira kuphunzira chinali chofunika kwambiri. Atawona kutsimikiza kumene mlongo wachichepereyo anali nako ndi kuyamikira kuti iye anabwera mwachindunji kwa iye, mwamunayo ananena kuti: “Ngati chomwe mudzaphunzira chiri chofunika kwambiri chotero, kenaka onse a banja langa afunikira kuphunzira.” Chotulukapo chinali chakuti wa zaka 13 zakubadwa ameneyu anayamba phunziro la Baibulo ndi banja lonse, kuphatikizapo mwana wamwamuna wokwatira ndi mkazi wake ndi ana ena achikulire.
Mayendedwe Abwino Amayambira Panyumba
14. Ndi kuti kumene mayendedwe abwino amayambira, ndipo ndi nsonga yotani yomwe imachita mbali yofunika?
14 Mayendedwe abwino a Mboni zachichepere ali kaŵirikaŵiri umboni wokoma ku kuphunzitsidwa kumene mowonekera amalandira panyumba. Ndithudi, mayendedwe athu ali kuwunikira kwa njira yathu ya moyo. Kaamba ka chifukwa chimenechi, mosiyana ndi chimene ena angaganizire, mayendedwe abwino ayenera kukhala ndi malo ofunika panyumba. Mwa ichi, monga m’mbali zina za moyo wabanja, chitsanzo chaukholo chiri cha kufunika koyambirira. (2 Timoteo 1:5) Kuwuza ana kuti, “Chita monga ndanenera, osati monga ndachitira” motsimikizirika sikuli njira yowaphunzitsira mayendedwe. Tsatanetsatane wosaŵerengeka wa mayendedwe abwino amaphunziridwa, osati mopepuka ndi malangizo a pakamwa, koma mwa kuwona ndi kutsanzira. “Makolo sali kokha aphunzitsi omalizira; iwo alinso zitsanzo, popeza kuti ana athu amaphunzira mwa kutsanzira njira zathu,” anawona tero Beverley Feldman, mkonzi wa Kids Who Succeed. Ndi mtundu wotani wa mayendedwe omwe ana anu amawona mwa inu?
15. Ndimotani mmene makolo angathandizire ana awo kukulitsa zizoloŵezi za moyo wonse za mayendedwe abwino?
15 “Atate, musakwiyitse ana anu” uli uphungu wa Baibulo. (Aefeso 6:4) Chiri chokwiyitsa ndi chokhumudwitsa kwa ana kuwuzidwa kuti afunikira kukhala okoma mtima ndi olingalira, ndipo komabe amawona makolo awo akutsutsana, kuneneza, kuchita mwamwano, kapena kukwiyitsidwa mwamsanga. Kodi iwo angapatsidwe mlandu ngati anachita m’mayendedwe ofananawo? Ku mbali ina, lembalo likupitirizabe kunena kuti: “Komatu muwalere iwo m’maleredwe ndi chilangizo cha [Yehova, NW].” Ndipo chimenecho chimaphatikizapo zazikulu za mayendedwe abwino, zonga kunena kuti, “Tikuwoneni,” “Chonde,” “Zikomo,” ndi “Ndikhululukireni,” kusonyeza ulemu kaamba ka achikulire, ndi kugawana zinthu ndi ena. (Levitiko 19:32; Aroma 16:3-7) Mikhalidwe imeneyi yophunziridwa panyumba mkati mwa uchichepere idzakhala ya mapindu a moyo wonse.—Miyambo 22:6.
16. Ndi zoyesayesa zotani zomwe zikufunika, ndi zotulukapo zotani?
16 Chotero makolo ndi ana mofananamo ayenera kuchita mayendedwe abwino monga mbali ya zochitachita zawo za tsiku ndi tsiku m’malo mwa kuyembekezera kufikira pa nthaŵi yapadera. M’kuchita tero, makolo ayenera kukhala oleza mtima ndi olekerera a zophophonya zimene ana ali okhoterera kupanga. Aloleni iwo adziŵe ukulu umene mikhalidwe yawo yokoma imatanthauza kwa inu, ndipo khalani wofulumira kuyamikira kupita patsogolo kumene iwo akupanga. Ndithudi, ichi chimatenga kuyesayesa kokulira ku mbali yanu. Koma kodi Malemba samanena kuti kuloŵetsa maprinsipulo aumulungu mwa ana kuyenera kuchitidwa “pokhala pansi m’nyumba zanu, ndi poyenda inu pa njira, ndi pogona inu pansi, ndi powuka inu”? (Deuteronomo 6:7) Kuchita tero kumapangitsa mkhalidwe wachifundo ndi wabwino panyumba, womwe umapita patali m’kulera ana anu pamene akula kukhala achikulire othandiza, osamalira, ndi amayendedwe. Kenaka iwo adzakhala magwero a chitamando ndi chilemekezo kwa inu ndi kwa Mlengi wawo, Yehova Mulungu.
Anthu Amayendedwe Abwino
17. Nchiyani chomwe chimawonedwa pa Nyumba za Ufumu za Mboni za Yehova?
17 “Mboni zoposa 1,000” zosonkhana kunja kwa City Hall mu Mzinda wa New York masana a September amenewo zinangosonyeza kokha pa mlingo wochepera njira imene Mboni za Yehova zimachitira pa maziko okhazikika. Kwinakwake, mwamuna anabwera ku Nyumba ya Ufumu kwa nthaŵi yoyamba ndi kunena pambuyo pake kuti: “Ndinakumana ndi anthu okonda kwenikweni, alendo kotheratu, m’tsiku limodzi kuposa ndi amene ndinakumanapo nawo m’tchalitchi chimene ndinakulira.” Chotulukapo chake? “Chinali chachiwonekere kuti ndinapeza chowonadi,” iye anatero. Mwamuna ameneyu anasintha njira yake ya moyo, ndipo miyezi isanu ndi iŵiri pambuyo pake anapereka moyo wake kwa Yehova ndi kubatizidwa.—Yerekezani ndi 1 Akorinto 14:25.
18. Ndimotani mmene muyezo wa mayendedwe abwino a Mboni za Yehova wayambukira akunja?
18 Miyezo ya mayendedwe ya Mboni ndi mawonekedwe pa misonkhano yawo ya mtundu ndi ya mitundu yonse yakhala nkhani ya kuchitira ndemanga kokomera. Pa chochitika chimodzi choterocho posachedwapa mu Japan, wotsogoza pa basi ya ulendo ananena kuti: “Pamene anthu inu mutuluka m’basi, aliyense wa inu, kuphatikizapo achichepere, mosalephera ananena kwa ine, ‘Zikomo kwambiri.’ Chimenecho chinandipangitsa ine kukhala wachimwemwe kwambiri!” Pa msonkhano wina, kalinde wa pa stesheni ya sitima ya pa njanji yapafupi anawuza Mboni kuti: “Inali ngozi yowopsya pamene msonkhano wapapitapo wa anthu 12,000 unachitikira pa Osaka Castle Hall.” Koma iye anapitirizabe kunena kuti: “Anthu inu mulidi adongosolo, ndipo tapumitsidwa. Chonde perekani moni wathu kwa aliyense yemwe akulamulira.”
19. Nchiyani chomwe aliyense wa ife ayenera kugamulapo kuchita ponena za mayendedwe?
19 Kodi nchiyani chimene ndemanga zoterozo zimasonyeza? Kuti Mboni za Yehova zonse chapamodzi zimayenda “mumayendedwe oyenera uthenga wabwino.” Bwanji ponena za ife aliyense payekha? Monga ana oyang’ana kwa atate wokonda, lolani tonsefe, achichepere ndi achikulire, tiyang’ane kwa Atate wathu wakumwamba, Yehova, kotero kuti tingaphunzitsidwe kukhala anthu a mayendedwe abwino, ngakhale m’dziko lopanda mayendedwe.—Deuteronomo 8:5; Miyambo 3:11, 12.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Nchifukwa ninji mayendedwe abwino amafunikira monga mbali ya makhalidwe okoma?
◻ Ndi mayendedwe okoma ati omwe ali oyenerera pa malo athu a kulambira?
◻ Ndimotani mmene mayendedwe abwino angasonyezedwere mu utumiki wa m’munda?
◻ Ndimotani mmene makolo angathandizire ana awo kukulitsa mayendedwe abwino?
◻ Ndi muyezo wapamwamba wotani wa mayendedwe womwe tiyenera kukalamira kusungirira?